M’Cheyne Bible Reading Plan
5 “ ‘Ngati munthu anayitanidwa ku bwalo kuti akachitire umboni pa zimene anaziona kapena kuzimva koma iye nʼkukana kuchitira umboni, munthu ameneyo wachimwa ndipo ayenera kulangidwa.
2 “ ‘Munthu akakhudza chinthu chilichonse chodetsedwa, monga nyama yakufa ya mʼthengo, kapena chiweto chakufa kapenanso chokwawa chakufa, ngakhale iyeyo wachikhudza mosadziwa, wasanduka wodetsedwa ndipo wachimwa.
3 “ ‘Munthu akakhudza choyipitsa munthu cha mtundu uliwonse, ndipo pochikhudzapo ndi kuyipitsidwa nacho mosadziwa, munthuyo adzakhala wopalamula akangodziwa chimene wachitacho.
4 “ ‘Munthu akalumbira mofulumira kapena mosasamala kuti adzachita chinthu, choyipa kapena chabwino, ngakhale kuti wachita izi mosadziwa kuti nʼkulakwa, pamene wazindira kulakwa kwake, iye adzakhalabe wopalamula akangodziwa chimene wachitacho.
5 “ ‘Pamene munthu wazindikira kuti wachimwa motere, awulule tchimo limene wachitalo. 6 Pambuyo pake, munthuyo abwere kwa Yehova ndi mwana wankhosa wamkazi kapena mbuzi kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo ndipo wansembe achite mwambo wopepesera tchimo lomwe wachitalo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo.
7 “ ‘Ngati munthuyo alibe mwana wankhosa, abweretse njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri kwa Yehova ngati chopereka chopepesera tchimo lake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera tchimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. 8 Tsono abwere nazo kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayambe wapereka mbalame imodzi ngati yopepesera tchimo. Apotole khosi koma osayidula mutu, 9 kenaka awaze magazi a chopereka chopepesera tchimocho mʼmbali mwa guwa. Magazi ena onse awathire pa tsinde la guwa. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo. 10 Pambuyo pake wansembe apereke mbalame inayo kuti ikhale chopereka chopsereza potsata mwambo wake. Wansembe atatha kupereka nsembe yopepesera tchimo limene munthu uja wachita, wochimwayo adzakhululukidwa.
11 “ ‘Koma ngati munthuyo alibe njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri, abweretse ufa wosalala wokwanira kilogalamu imodzi kuti ukhale chopereka chopepesera tchimo limene wachita. Asathiremo mafuta kapena lubani chifukwa ndi chopereka chopepesera tchimo. 12 Abweretse ufawo kwa wansembe ndipo wansembeyo atapeko dzanja limodzi kuti ukhale ufa wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa pamodzi ndi chopereka chopsereza kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo. 13 Umu ndi mmene wansembe adzachitire mwambo wopepesera machimo ena aliwonse amene munthu wachita, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. Zopereka zonse zotsala zidzakhala za wansembeyo monga momwe amachitira ndi chopereka chachakudya.’ ”
Chopereka Chopepesera Kupalamula
14 Yehova anawuza Mose kuti, 15 “Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwa mosadziwa posapereka zinthu zopatulika zofunika kwa Yehova, munthuyo apereke kwa Yehova nsembe yopepesera machimo ake. Nsembeyo ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake ukhale wokwana masekeli oyenera a siliva pakawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu. Imeneyi ndi nsembe yopepesera kupalamula. 16 Munthuyo ayenera kubweza zinthu zopatulika zimene sanaperekezo. Awonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse ndi kuzipereka zonsezo kwa wansembe amene adzachita mwambo wopepesera machimo a munthuyo, popereka nkhosa yayimuna ija ngati nsembe yopepesera ndipo wochimwayo adzakhululukidwa.
17 “Ngati munthu wachimwa mosadziwa pochita chilichonse chimene Yehova salola, munthuyo ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kulangidwa. 18 Abwere kwa wansembe ndi chopereka chopepesera kupalamula kwake. Chopereka chikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake ukhale woyenera nsembe yopepesera kupalamula kumene anachimwa mosadziwako, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. 19 Imeneyi ndi nsembe yopepesera kupalamula popeza munthuyo wapezeka wolakwa pamaso pa Yehova.”
Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu.
3 Inu Yehova, achulukadi adani anga!
Achulukadi amene andiwukira!
2 Ambiri akunena za ine kuti,
“Mulungu sadzamupulumutsa.”
Sela
3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,
Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
4 Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula
ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.
Sela
5 Ine ndimagona ndi kupeza tulo;
ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
6 Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene
abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.
7 Dzukani, Inu Yehova!
Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.
Akantheni adani anga onse pa msagwada;
gululani mano a anthu oyipa.
8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.
Madalitso akhale pa anthu anu.
Sela
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide.
4 Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,
Inu Mulungu wa chilungamo changa.
Pumulitseni ku zowawa zanga;
chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.
2 Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?
Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?
Sela.
3 Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika;
Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.
4 Kwiyani koma musachimwe;
pamene muli pa mabedi anu,
santhulani mitima yanu ndi kukhala chete.
Sela
5 Perekani nsembe zolungama
ndipo dalirani Yehova.
6 Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?”
Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.
7 Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu
kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.
8 Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,
pakuti Inu nokha, Inu Yehova,
mumandisamalira bwino.
20 Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola;
aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru.
2 Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango;
amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake.
3 Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano,
koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola.
4 Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera;
kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.
5 Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi akuya,
munthu womvetsa zinthu ndiye yekha angawatunge.
6 Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo,
koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani?
7 Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino;
odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.
8 Mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo,
imapeta ndi maso ake anthu onse oyipa.
9 Ndani amene anganene kuti, “Ndawuyeretsa mtima wanga;
ndilibe tchimo lililonse?”
10 Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo
zonsezi Yehova zimamunyansa.
11 Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake,
ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.
12 Makutu amene amamva ndi maso amene amaona,
zonsezi anazilenga ndi Yehova.
13 Usakonde tulo ungasauke;
khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.
14 Munthu wogula chinthu amati, “Sichabwino, sichabwino.”
Koma akagula nʼkuchokapo amayamba kudzitama.
15 Pali golide ndi miyala yamtengowapatali,
koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi.
16 Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole;
kuti chikhale chikole chako chifukwa waperekera chikole munthu wachilendo.
17 Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu,
koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake.
18 Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu;
ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera.
19 Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi.
Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo.
20 Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake,
moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.
21 Cholowa chochipeza mofulumira poyamba,
sichidzakhala dalitso pa mapeto pake.
22 Usanene kuti, “Ine ndidzabwezera choyipa chimenechi!”
Dikira Yehova, ndipo Iye adzakupulumutsa.
23 Miyeso yosintha imamunyansa Yehova;
ndipo masikelo onyenga si abwino.
24 Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova,
tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?
25 Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,”
popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.
26 Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthu
anthu oyipa.
27 Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova;
imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.
28 Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu;
chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu.
29 Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo,
imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.
30 Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa,
ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.
Moyo Watsopano
3 Tsono popeza munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mitima yanu pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. 2 Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi. 3 Pakuti munafa, ndipo moyo wanu tsopano wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. 4 Khristu, amene ndiye moyo wanu, akadzaonekanso, pamenepo inunso mudzaoneka naye pamodzi mu ulemerero.
5 Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano. 6 Chifukwa cha zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa ana osamvera. 7 Inunso kale munkachita zomwezi, mʼmoyo wanu wakale uja. 8 Koma tsopano mukuyenera kuzichotsa zinthu zonsezi monga: mkwiyo, ukali, dumbo, chipongwe ndi mawu onyansa. 9 Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake 10 ndipo mwavala munthu watsopano, amene nzeru zake zikukonzedwanso kuti afanane ndi Mlengi wake. 11 Pano palibe kusiyana pakati pa Mgriki ndi Myuda, wochita mdulidwe ndi wosachita, wosaphunzira kapena wosachangamuka, kapolo kapena mfulu, koma Khristu yekha basi ndipo amakhala mwa onse.
12 Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira. 13 Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu. 14 Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
15 Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika. 16 Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika. 17 Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Malangizo a Moyo wa Mʼbanja la Chikhristu
18 Inu akazi, gonjerani amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.
19 Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima.
20 Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.
21 Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.
22 Inu antchito, mverani mabwana anu mu zonse, ndipo muzichita zimenezi osati nthawi yokhayo imene akukuonani kuti akukondeni, koma muzichite moona mtima ndi mopereka ulemu kwa Ambuye. 23 Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu. 24 Inu mukudziwa kuti mudzalandira mphotho monga cholowa kuchokera kwa Ambuye. Ndi Ambuye Khristu amene mukumutumikira. 25 Aliyense amene amachita zolakwa adzalandira malipiro molingana ndi kulakwa kwake, ndipo palibe tsankho.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.