Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 4

Nsembe Yopepesera Tchimo

Yehova anayankhula ndi Mose kuti, “Awuze Aisraeli kuti, ‘Munthu akachimwa mosadziwa ndi kuchita chilichonse chimene Yehova walamula kuti asachite, azichita izi:

“ ‘Ngati wansembe wodzozedwa achimwa, ndi kuchimwitsa anthu onse, iyeyu ayenera kupereka mwana wangʼombe wamphongo wopanda chilema chifukwa cha tchimo limene wachitalo. Imeneyi ndi nsembe ya Yehova yopepesera tchimo lake. Wansembeyo abwere nayo ngʼombeyo pa khomo la tenti ya msonkhano pamaso pa Yehova. Asanjike dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo ndipo ayiphe pamaso pa Yehova. Kenaka wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano. Iye aviyike chala chake mʼmagazi, ndipo awawaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani yotchinga malo wopatulika. Kenaka wansembe apake magaziwo pa nyanga za guwa lofukizira lubani limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. Pambuyo pake achotse mafuta onse a ngʼombe yayimuna yopepesera machimoyo: mafuta okuta zamʼkati kapena mafuta onse amʼkatimo. Achotsenso ndi kubwera ndi impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta onse ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi ndi impsyo 10 monga momwe amachotsera mafuta a ngʼombe yoperekedwa kuti ikhale chopereka chachiyanjano. Tsono wansembe atenthe zimenezi pa guwa lansembe zopsereza. 11 Koma chikopa cha ngʼombe yayimunayo ndi mnofu wake wonse, pamodzi ndi mutu ndi miyendo, zamʼkati ndi matumbo, 12 kapena kuti ngʼombe yonse yotsalayo apite nayo kunja kwa msasa ku malo woyeretsedwa, kumene amatayako phulusa ndi kuyitentha pa nkhuni, pa phulusapo.

13 “ ‘Ngati gulu lonse la Aisraeli lichimwa mosadziwa, nachita chomwe ndi choletsedwa ndi Yehova, ngakhale kuti gulu lonselo silikudziwa kuti lachimwa, anthuwo ndi olakwa ndithu. 14 Akazindikira tchimo limene achita, gulu lonse lipereke mwana wangʼombe wamphongo kuti akhale chopereka chopepesera tchimo ndipo abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. 15 Akuluakulu a anthuwo asanjike manja awo pa mutu pa ngʼombe pamaso pa Yehova, ndipo ayiphe pomwepo pamaso pa Yehova. 16 Tsono wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano. 17 Aviyike chala chake mʼmagaziwo ndi kuwawaza pamaso pa Yehova kasanu ndi kawiri patsogolo pa nsalu yotchinga. 18 Pambuyo pake iye apake magaziwo pa nyanga za guwa limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. 19 Kenaka achotse mafuta onse a ngʼombeyo ndi kuwatentha pa guwa, 20 ndipo achite ndi ngʼombe yayimunayi monga anachitira ndi ngʼombe yayimuna yopepesera machimo. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera anthu, ndipo machimo awo adzakhululukidwa. 21 Kenaka atulutse ngʼombeyo kunja kwa msasa ndi kuyitentha monga anatenthera ngʼombe yoyamba ija. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo a gulu lonse.

22 “ ‘Ngati mtsogoleri achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova Mulungu wake, ndiye kuti wapalamula. 23 Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, iye abwere ndi mbuzi yayimuna yopanda chilema kuti ikhale chopereka chake. 24 Asanjike dzanja lake pa mutu wa mbuziyo ndi kuyiphera pamalo pamene amaphera zopereka zopsereza pamaso pa Yehova. Ichi ndi chopereka chopepesera tchimo. 25 Pambuyo pake wansembe atengeko magazi a chopereka chopepesera tchimocho ndi chala chake, ndipo awapake pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Athire magazi otsalawo pa tsinde la guwalo. 26 Wansembeyo atenthe mafuta onse pa guwapo monga amatenthera chopereka chachiyanjano. Pochita zimenezi, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo, ndipo adzakhululukidwa.

27 “ ‘Ngati munthu wamba achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova, ndiye kuti wapalamula. 28 Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, abweretse mbuzi yayikazi yopanda chilema kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo. 29 Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo ayiphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza. 30 Ndipo wansembe atenge magazi ndi chala chake ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza ndi kuthira magazi wotsalawo pa tsinde la guwalo. 31 Kenaka iye achotse mafuta onse monga momwe anachotsera mafuta a chopereka chachiyanjano, ndipo awatenthe pa guwa kuti akhale fungo lokomera Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo ndipo adzakhululukidwa.

32 “ ‘Ngati munthu apereka mwana wankhosa ngati chopereka chopepesera tchimo lake, abwere ndi mwana wankhosa wamkazi wopanda chilema. 33 Asanjike dzanja lake pa mutu wa mwana wankhosayo ndipo amuphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza. 34 Kenaka wansembe atengeko ndi chala chake magazi a mwana wankhosa uja ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Magazi otsalawo athire pa tsinde la guwalo. 35 Iye achotse mafuta onse, monga amachotsera mafuta a mwana wankhosa wa chopereka chachiyanjano, ndipo wansembe awatenthe pa guwa pamodzi ndi zopereka zina zopsereza za Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo limene munthuyo anachita ndipo adzakhululukidwa.

Masalimo 1-2

BUKU LOYAMBA

Masalimo 1–41

Wodala munthu
    amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa,
kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa,
    kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.
Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova
    ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.
Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,
    umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake
ndipo masamba ake safota.
    Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.
Sizitero ndi anthu oyipa!
    Iwo ali ngati mungu
    umene umawuluzidwa ndi mphepo.
Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo,
    kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama.

Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama,
    koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.
Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu?
    Akonzekeranji zopanda pake anthu?
Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;
    ndipo olamulira asonkhana pamodzi
kulimbana ndi Ambuye
    ndi wodzozedwa wakeyo.
Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo
    ndipo titaye zingwe zawo.”

Wokhala mmwamba akuseka;
    Ambuye akuwanyoza iwowo.
Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake
    ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,
“Ine ndakhazikitsa mfumu yanga
    pa Ziyoni, phiri langa loyera.”

Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula:

Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga;
    lero Ine ndakhala Atate ako.
Tandipempha,
    ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako;
    malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.
Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo;
    udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”

10 Kotero, inu mafumu, chenjerani;
    chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.
11 Tumikirani Yehova mwa mantha
    ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.
12 Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye;
    kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu,
pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa.
    Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.

Miyambo 19

19 Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro,
    aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.

Si bwino kuti munthu akhale wopanda nzeru;
    ndipo munthu woyenda mofulumira amaphonya njira.

Uchitsiru wa munthu umamubweretsera zovuta,
    mtima wake umakwiyira Yehova.

Chuma chimachulukitsa abwenzi;
    koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa.

Mboni yonama sidzalephera kulangidwa;
    ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.

Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima,
    ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense.

Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye,
    nanji abwenzi ake tsono!
Iwo adzamuthawa kupita kutali.
    Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse.

Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake.
    Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.

Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,
    ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.

10 Nʼkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wamanyado,
    nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!

11 Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga;
    ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.

12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango,
    koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.

13 Mwana wopusa ndiye tsoka la abambo ake
    ndipo mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula yamvumbi.

14 Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo;
    koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.

15 Ulesi umagonetsa tulo tofa nato
    ndipo munthu wosatakataka amakhala ndi njala.

16 Amene amamvera malangizo amasunga moyo wake,
    koma amene sasamala malamulo a Yehova adzafa.

17 Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova,
    ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.

18 Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo;
    ngati sutero udzawononga moyo wake.

19 Munthu waukali woopsa ayenera kulandira chilango;
    pakuti akamulekelera ndiye zidzayipa kuposa kale.

20 Mvera uphungu ndipo landira malangizo;
    pa mapeto pake udzakhala wanzeru.

21 Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake,
    koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.

22 Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha;
    nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.

23 Kuopa Yehova kumabweretsa moyo;
    wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.

24 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale;
    koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake.

25 Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo;
    dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso.

26 Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake,
    ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.

27 Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo,
    udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.

28 Mboni yopanda pake imanyoza cholungama,
    ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.

29 Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa,
    ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.

Akolose 2

Ndikufuna mudziwe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo pamodzi ndi anzanu a ku Laodikaya, ndi ena onse amene sitinaonane maso ndi maso. Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu. Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso. Ndikukuwuzani zimenezi kuti wina aliyense asakunamizeni ndi kukukopani ndi mawu ake. Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu.

Za Moyo Weniweni mwa Khristu

Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo. Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.

Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu.

Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu. 10 Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse. 11 Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija. 12 Mu ubatizo, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa.

13 Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse. 14 Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda. 15 Ndipo atalanda zida maufumu ndi maulamuliro, Iye anawachititsa manyazi powayendetsa pamaso pa anthu onse atawagonjetsa ndi mtanda.

Ufulu Wathu

16 Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata. 17 Zimenezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zimene zikubwera, koma choonadi chenicheni chikupezeka mwa Khristu. 18 Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu. 19 Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire.

20 Popeza munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nayo miyambo ya dziko lapansi lino, nʼchifukwa chiyani mukukhalanso ngati a dziko lapansi lino? Bwanji mukumvera malamulo monga awa: 21 “Usagwire chakuti,” “Usalawe chakuti,” “Usakhudze chakuti?” 22 Malamulo amenewa amakhudza zinthu zimene zimatha zikamagwiritsidwa ntchito, ndipo malamulo ndi zophunzitsa za anthu chabe. 23 Ndithu malamulo oterewa amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamulira anthu ambiri pa zachipembedzo ndi pa zakudzichepetsa kwa chiphamaso, ndi pa zakuzunza thupi lawo, koma alibe mphamvu zoletsa kuchita zofuna za thupilo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.