M’Cheyne Bible Reading Plan
Bokosi la Chipangano
37 Bezaleli anapanga Bokosi la Chipangano lamatabwa amtengo wa mkesha. Kutalika kwake kunali masentimita 114, mulifupi mwake munali masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. 2 Iye analikuta bokosilo ndi golide wabwino kwambiri mʼkati mwake ndi kunja komwe. Anapanganso mkombero wagolide kuzungulira bokosilo. 3 Iye anapanga mphete zinayi zagolide ndi kuzimangirira ku miyendo yake inayi ija, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. 4 Kenaka anapanga mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide. 5 Ndipo analowetsa nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira.
6 Iye anapanga chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. 7 Ndipo anapanga Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo ndi kuwayika mbali ziwiri za chivundikirocho. 8 Iye anapanga kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa anawapangira limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. 9 Mapiko a Akerubiwo anatambasukira pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo anakhala choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho.
Mapangidwe a Tebulo
10 Iwo anapanga tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. 11 Kenaka analikuta ndi golide wabwino kwambiri, ndipo anapanga mkombero wagolide mʼmbali mwake. 12 Iwo anapanga feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo anayika mkombero wagolide kuzungulira feremuyo. 13 Iwo anapanga mphete zinayi zagolide ndipo anazilumikiza ku ngodya zake zinayi, kumene kunali miyendo yake inayi. 14 Mphetezo anaziyika kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo. 15 Anapanga nsichi zamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide kuti azinyamulira tebulolo. 16 Ndipo anapanga ziwiya za pa tebulolo zagolide wabwino, mbale ndi zipande, mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe za chakumwa.
Mapangidwe a Choyikapo Nyale
17 Iwo anapanga choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zinasulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zinapangidwa kumodzi. 18 Mʼmbali mwake munali mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse. 19 Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zinali pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri panalinso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zinali chimodzimodzi ndipo zinatuluka mʼchoyikapo nyalecho. 20 Pa choyikapo nyalecho panali zikho zinayi zokhala ngati maluwa amtowo, mphukira ndi maluwa ake. 21 Mphukira yoyamba inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Mphukira yachitatu inali mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zinali nthambi zisanu ndi imodzi 22 Mphukira ndi nthambi zonse zinasulidwa kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri.
23 Iwo anapanga nyale zisanu ndi ziwiri, mbaniro ndi zowolera phulusa, zonse zinali zagolide wabwino kwambiri. 24 Iwo anapanga choyikapo nyale ndi zipangizo zake zonse zagolide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34.
Guwa Lofukizirapo Lubani
25 Iwo anapanga guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Linali lofanana mbali zonse, mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91, ndipo nyanga zake zinapangidwa kumodzi ndi guwalo. 26 Iwo anakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse ndi nyanga zake, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwalo. 27 Anapanga mphete ziwiri pansi pa mkomberowo ndi kulumikiza ku mbali zonse ziwiri kuti apisemo nsichi zonyamulira. 28 Anapanga mizati yamtengo wa mkesha ndipo anayikuta ndi golide.
29 Iwo anapanganso mafuta opatulika odzozera ndi zofukiza za fungo lokoma kwambiri. Iyi inali ntchito ya mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa.
16 “Ine ndakuwuzani zonsezi kuti musadzakhumudwe. 2 Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu. 3 Iwo adzachita zoterozo chifukwa sanadziwe Atate kapena Inenso. 4 Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”
Ntchito ya Mzimu Woyera
5 “Tsopano Ine ndikupita kwa Iye amene anandituma koma palibe wina mwa inu akundifunsa kuti, ‘Kodi mukupita kuti?’ 6 Muli ndi chisoni kwambiri chifukwa ndakuwuzani zimene. 7 Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu. 8 Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo. 9 Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine. 10 Za chilungamo, chifukwa Ine ndi kupita kwa Atate, kumene simudzandionanso. 11 Za chiweruzo, chifukwa wolamulira dziko lino lapansi waweruzidwa tsopano.
12 “Ine ndili ndi zambiri zoti ndiyankhule nanu, koma simungathe kuzilandira tsopano. 13 Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera. 14 Iye adzalemekeza Ine chifukwa adzatenga za Ine nadzakudziwitsani. 15 Zonse za Atate ndi zanga. Ichi nʼchifukwa chake Ine ndanena kuti Mzimu Woyera adzatenga kwa Ine zanga kuti muzidziwe.”
Chisoni cha Ophunzira Chisandulika Chimwemwe
16 Yesu anapitiriza kuyankhula kuti, “Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso, ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso.”
17 Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’ ” 18 Iwo anapitiriza kufunsana kuti, “Kodi akutanthauza chiyani, ‘kanthawi kochepa?’ Ife sitikumvetsetsa chimene Iye akuyankhula.”
19 Yesu anadziwa kuti ankafuna kuti amufunse za zimenezi, choncho anawafunsa kuti, “Kodi mukufunsana wina ndi mnzake chimene Ine ndimatanthauza pamene ndinati, ‘Mwa kanthawi kochepa simudzandionanso,’ ndi ‘patatha nthawi pangʼono mudzandionanso?’ 20 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti inu mudzalira ndi kubuma pomwe dziko lapansi lidzakhale likukondwera. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. 21 Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi. 22 Chimodzimodzinso ndi inu. Tsopano ino ndi nthawi yanu yomva chisoni, koma Ine ndidzakuonaninso ndipo inu mudzasangalala, ndipo palibe amene adzachotsa chimwemwe chanu. 23 Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 24 Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.
25 “Ngakhale ndakhala ndikuyankhula mʼmafanizo, nthawi ikubwera imene Ine sindidzagwiritsanso ntchito mafanizo otere koma ndidzakuwuzani momveka za Atate anga. 26 Tsiku limenelo inu mudzapempha mʼdzina langa. Ine sindikunena kuti ndidzapempha Atate mʼmalo mwanu ayi. 27 Atate mwini anakukondani chifukwa inu mwandikonda Ine ndipo mwakhulupirira kuti Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate. 28 Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate ndi kulowa mʼdziko lapansi. Tsopano ndikulisiya dziko lapansi kubwerera kwa Atate.”
29 Kenaka ophunzira ake anati, “Tsopano mukuyankhula momveka bwino ndi mopanda mafanizo. 30 Tsopano ife tikuona kuti Inu mumadziwa zinthu zonse ndi kuti sipafunika wina aliyense kukufunsani. Mwa ichi ife takhulupirira kuti Inu munachokera kwa Mulungu.”
31 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi tsopano mwakhulupirira?” 32 Koma nthawi ikubwera ndipo yafika, pamene inu mudzabalalitsidwa, aliyense ku nyumba yake. Inu mudzandisiya ndekhandekha. Koma Ine sindili ndekha, pakuti Atate anga ali nane.
33 “Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”
13 Mwana wanzeru amamvera malangizo a abambo ake,
koma mwana wonyoza samamvetsera chidzudzulo.
2 Munthu amapeza zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake,
koma anthu osakhulupirika amalakalaka zachiwawa basi.
3 Iye amene amagwira pakamwa pake amateteza moyo wake,
koma amene amayankhula zopanda pake adzawonongeka.
4 Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu,
koma munthu wakhama adzalemera.
5 Munthu wolungama amadana ndi zabodza,
koma zochita za munthu woyipa zimanyansa ndiponso zimachititsa manyazi.
6 Chilungamo chimateteza munthu wangwiro,
koma tchimo limagwetsa munthu wochimwa.
7 Wina amadziyesa kuti ndi wolemera chonsecho alibe kanthu kalikonse;
munthu wina amaoneka ngati wosauka chonsecho ali ndi chuma chambiri.
8 Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake,
koma munthu wosauka amamva chidzudzulo.
9 Nyale ya munthu wolungama ndi yokondweretsa,
koma nyale ya munthu woyipa imazimitsidwa.
10 Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano,
koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru.
11 Chuma chochipeza mofulumira chidzatha pangʼonopangʼono
koma chuma chosonkhanitsidwa pangʼonopangʼono chidzachulukirachulukira.
12 Chinthu chochiyembekezera chikalephereka chimalefula mtima,
koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi chimakhala ngati mtengo wamoyo.
13 Amene amanyoza malangizo adzawonongeka,
koma amene amasamala lamulo amalandira mphotho.
14 Malangizo a munthu wanzeru ali ngati kasupe wamoyo;
amathandiza munthu kuti asakondwe mu msampha wa imfa.
15 Munthu wa nzeru zabwino amapeza kuyanja pakati pa anthu,
koma munthu wosakhulupirika adzawonongeka.
16 Munthu wochenjera amachita zinthu mwanzeru,
koma chitsiru chimaonetsa poyera uchitsiru wake.
17 Wamthenga woyipa amagwetsa anthu mʼmavuto,
koma nthumwi yodalirika imabweretsa mtendere.
18 Wokana mwambo adzasauka ndi kunyozedwa,
koma wosamala chidzudzulo adzalemekezedwa.
19 Chinthu chochilakalaka chikachitika chimasangalatsa mtima,
koma zitsiru zimadana ndi kuleka zoyipa.
20 Woyenda ndi anthu anzeru nayenso adzakhala wanzeru;
koma woyenda ndi zitsiru adzapwetekeka.
21 Choyipa chitsata mwini,
koma wochita zolungama adzalandira mphotho yabwino.
22 Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake cholowa,
koma chuma cha munthu wochimwa amachilandira ndi olungama.
23 Tsala la munthu wosauka limalola chakudya chambiri,
koma anthu opanda chilungamo amachilanda.
24 Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda,
koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.
25 Munthu wolungama amakhala ndi zakudya zoti adye nʼkukhuta,
koma mʼmimba mwa munthu woyipa mumakhala pululu ndi njala.
Ana ndi Makolo Awo
6 Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. 2 “Lemekeza abambo ndi amayi ako.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. 3 Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, “zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi.” 4 Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.
Antchito ndi Mabwana Awo
5 Inu antchito, mverani mabwana anu mwaulemu ndi mwamantha ndi moona mtima, monga momwe mungamvere Khristu. 6 Musawamvere pamene akukuonani kuti akukomereni mtima, koma ngati akapolo a Khristu ochita chifuniro cha Mulungu kuchokera mu mtima mwanu. 7 Tumikirani ndi mtima wonse, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu. 8 Inu mukudziwa kuti Ambuye adzamupatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene anagwira, kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.
9 Ndipo inu mabwana, muziwachitiranso chimodzimodzi antchito anu. Musamawaopseze, popeza mukudziwa kuti Mbuye wawo ndi wanunso, nonse Mbuye wanu ali kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho.
Zida Zankhondo za Mulungu
10 Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu. 11 Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. 12 Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga. 13 Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu. 14 Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. 15 Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato. 16 Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo. 17 Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu. 18 Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.
19 Mundipempherere inenso, kuti nthawi iliyonse pamene nditsekula pakamwa panga, andipatse mawu kuti ndiwulule zinsinsi za Uthenga Wabwino mopanda mantha. 20 Ndine kazembe wa Uthenga Wabwinowu ngakhale ndili womangidwa mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire mopanda mantha, monga ndiyenera.
Mawu Otsiriza
21 Tukiko, mʼbale wanga wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye, adzakuwuzani zonse kuti inunso mudziwe mmene ndilili ndi zimene ndikuchita. 22 Ine ndikumutumiza kwa inu, kuti mudziwe za moyo wathu, ndi kuti akulimbikitseni.
23 Mtendere, chikondi pamodzi ndi chikhulupiriro kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi abale onse. 24 Chisomo kwa onse amene amakonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosatha.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.