M’Cheyne Bible Reading Plan
Za Fano la Mwana Wangʼombe Wagolide
32 Anthu ataona kuti Mose akuchedwa kutsika mʼphiri, anasonkhana kwa Aaroni ndipo anati, “Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.”
2 Aaroni anawayankha kuti, “Vulani ndolo zagolide zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi aakazi ndipo muzibweretse kwa ine.” 3 Kotero anthu onse anavula ndolo zagolide ndi kubwera nazo kwa Aaroni. 4 Choncho Aaroni analandira golideyo ndipo anamuwumba ndi chikombole ndi kupanga fano la mwana wangʼombe. Kenaka anthu aja anati, “Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.”
5 Aaroni ataona izi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa mwana wangʼombeyo ndipo analengeza kuti, “Mawa kudzakhala chikondwerero cha Yehova.” 6 Kotero tsiku linalo anthu anadzuka mmamawa ndithu ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Atatha kupereka nsembezo, anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.
7 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, “Tsika msanga, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto aja adziyipitsa kwambiri. 8 Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, ‘Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”
9 Yehova anati kwa Mose, “Ine ndikuwadziwa anthu amenewa. Iwowa ndi ankhutukumve. 10 Chifukwa chake undileke kuti mkwiyo wanga uyake pa iwo ndi kuwawononga. Ndipo Ine ndidzakusandutsa kuti ukhale mtundu waukulu.”
11 Koma Mose anapempha chifundo cha Mulungu wake ndipo anati, “Chonde Yehova, chifukwa chiyani mwakwiyira anthu awa amene munawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu. 12 Kodi mukufuna kuti Aigupto azinena kuti, ‘Munali ndi cholinga choyipa chofuna kuwaphera ku mapiri kuno ndi kuwawonongeratu pa dziko lapansi pamene munkawatulutsa ku Igupto kuja?’ Ayi, chonde mkwiyo wanu woyaka ngati motowu ubwezeni ndipo sinthani maganizo ofunira zoyipa anthu anu. 13 Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, ‘Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’ ” 14 Choncho Yehova analeka ndipo sanawachitire choyipa anthu ake monga anaopsezera.
15 Mose anatembenuka ndi kutsika phiri miyala iwiri ya pangano ili mʼmanja mwake. Miyalayi inalembedwa mbali zonse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. 16 Miyalayi anayikonza ndi Mulungu. Malembawo analemba ndi Mulungu mozokota pa miyalapo.
17 Pamene Yoswa anamva phokoso la anthu anati kwa Mose, “Ku msasa kuli phokoso la nkhondo.”
18 Mose anayankha kuti,
“Phokoso limeneli sindikulimva
ngati phokoso la opambana nkhondo,
kapena kulira kwa ongonjetsedwa pa nkhondo. Koma ndikulimva ngati phokoso la anthu amene akuyimba.”
19 Mose atayandikira msasa ndi kuona mwana wangʼombe ndiponso kuvina, anakwiya kwambiri ndipo anaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwake, ndi kuyiphwanya pa tsinde la phiri. 20 Ndipo iye anatenga mwana wangʼombe amene anthu anapanga uja ndi kumuwotcha pa moto ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi. Kenaka anawaza fumbilo mʼmadzi ndi kuwamwetsa Aisraeli madziwo.
21 Tsono Mose anafunsa Aaroni kuti, “Kodi anthu awa anakuchita chiyani kuti uwachimwitse koopsa chotere?”
22 Aaroni anayankha kuti, “Musakwiye mbuye wanga. Inu mukudziwa kuti anthu awa ndi ovuta. 23 Iwo anati kwa ine, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa ife mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.’ 24 Choncho ine ndinawawuza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.”
25 Mose anaona kuti anthuwo anali osokonezekadi chifukwa Aaroni anawalekerera mpaka kusanduka anthu osekedwa pakati pa adani awo. 26 Choncho iye anayima pa chipata cholowera mu msasa ndipo anati, “Aliyense amene ali mbali ya Yehova abwere kwa ine.” Ndipo Alevi onse anapita mbali yake.
27 Ndipo iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena, ‘Pitani ku misasa konse, mulowe ku zipata zonse ndipo aliyense akaphe mʼbale wake, kapena mnzake kapena mnansi wake.’ ” 28 Alevi anachita zomwe Mose analamula, ndipo tsiku limenelo panafa anthu pafupifupi 3,000. 29 Kenaka Mose anati, “Lero mwadzipatula nokha kukhala ansembe otumikira Yehova. Mwachita izi popeza aliyense wa inu wapha mwana wake kapena mʼbale wake. Tsono lero Yehova wakudalitsani.”
30 Mmawa mwake Mose anati kwa anthu onse, “Inu mwachita tchimo lalikulu. Koma tsopano ine ndipita ku phiri kwa Yehova mwina ndikatha kukupepeserani chifukwa cha tchimo lanu.”
31 Kotero Mose anabwereranso kwa Yehova ndipo anati, “Aa! Anthu awa achita tchimo lalikulu! Iwo adzipangira milungu yagolide. 32 Koma tsopano, chonde akhululukireni tchimo lawo. Ngati simutero, ndiye mundifute ine mʼbuku limene mwalemba.”
33 Yehova anamuyankha Mose kuti, “Ndidzafuta mʼbuku aliyense amene wandichimwira. 34 Tsopano pita ukawatsogolere anthu kumalo kumene ine ndinanena, ndipo mngelo wanga adzakutsogolerani. Komabe, nthawi yanga ikadzafika kuti ndiwalange, ndidzawalanga chifukwa cha tchimo lawo.”
35 Ndipo Yehova anawakantha anthuwo ndi mliri chifukwa anawumiriza Aaroni kuti awapangire fano la mwana wangʼombe.
Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Lazaro
11 Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anadwala. Iye anali wa ku Betaniya, mudzi wa Mariya ndi mchemwali wake Marita. 2 Mariyayo ndi yemwe uja amene anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake. Lazaro wodwalayo anali mlongo wake. 3 Choncho alongo ake anatumiza mawu kwa Yesu kuti, “Ambuye, uja amene Inu mumamukonda akudwala.”
4 Atamva izi, Yesu anati, “Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.” 5 Yesu anakonda Marita, mchemwali wake ndi Lazaro. 6 Koma atamva kuti Lazaro akudwala, Iye anakhalabe kumene anali masiku ena awiri.
7 Kenaka anati kwa ophunzira ake, “Tiyeni tibwerere ku Yudeya.”
8 Ophunzira akewo anati, “Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?”
9 Yesu anayankha kuti, “Kodi sipali maora khumi ndi awiri pa tsiku? Munthu amene amayenda masana sapunthwa, popeza akuona chifukwa cha kuwala kwa dziko lapansi. 10 Koma amene akuyenda usiku amapunthwa, chifukwa kuwalako alibe.”
11 Iye atatha kunena izi, anapitirira kuwawuza iwo kuti, “Bwenzi lathu Lazaro wagona tulo; koma Ine ndikupita kumeneko kukamudzutsa.”
12 Ophunzira ake anayankha kuti, “Ambuye, ngati wagona adzapeza bwino.” 13 Yesu ankayankhula za imfa yake koma ophunzira ake ankaganiza kuti amanena za tulo chabe.
14 Ndipo kenaka anawawuza momveka kuti, “Lazaro wamwalira. 15 Ine ndikukondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe kumeneko; koma kuti mukakhulupirire tiyeni tipiteko.”
16 Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, “Tiyeni nafenso tipite, kuti tikafere naye pamodzi.”
Yesu Atonthoza Alongo a Lazaro
17 Yesu atafika, anapeza kuti Lazaro anali atagona mʼmanda masiku anayi. 18 Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wosachepera makilomita atatu, 19 ndipo Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza pa imfa ya mʼbale wawo. 20 Pamene Marita anamva kuti Yesu akubwera, anapita kukakumana naye. Koma Mariya anatsala ku nyumba.
21 Marita anati kwa Yesu, “Ambuye, mukanakhala muli kuno, mlongo wanga sakanamwalira. 22 Koma ine ndikudziwa kuti ngakhale tsopano Mulungu adzakupatsani chilichonse chimene mudzamupempha.”
23 Yesu anati kwa iye, “Mlongo wako adzauka.”
24 Marita anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti adzauka pa kuukanso pa tsiku lomaliza.”
25 Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. 26 Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?”
27 Marita anamuwuza Iye kuti, “Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi.”
28 Ndipo iye atanena izi anabwerera ndi kukayitana mchemwali wake Mariya namuyankhula monongʼona pambali, nati, “Aphunzitsi abwera ndipo akukuyitana.” 29 Mariya atamva izi, anayimirira mofulumira napita kwa Iye. 30 Tsopano nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzi, koma anali akanali pa malo pamene Marita anakumana naye. 31 Ayuda amene ankamutonthoza Mariya mʼnyumba, anaona mmene iye anayimira mofulumira ndi kutuluka kunja, iwo anamutsata akuganizira kuti ankapita ku manda kukalirira kumeneko.
32 Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, “Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira.”
33 Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu. 34 Iye anafunsa kuti, “Kodi mwamuyika kuti?”
Iwo anayankha kuti, “Ambuye tiyeni mukaone.”
35 Yesu analira.
36 Pamenepo Ayuda anati, “Taonani mmene Iye anamukondera Lazaro!”
37 Koma ena a iwo anati, “Iye amatsekula maso a munthu wosaona, kodi sakanakhoza kuletsa kuti munthu uyu asamwalire?”
Yesu Aukitsa Lazaro
38 Yesu atakhudzidwanso kwambiri anafika ku manda. Manda akewo anali phanga ndipo anatsekapo ndi mwala. 39 Yesu anati, “Chotsani mwala.”
Marita mlongo wa womwalirayo anati, “Koma Ambuye, nthawi ino wayamba kununkha, pakuti wakhala mʼmenemu masiku anayi.”
40 Kenaka Yesu anati, “Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”
41 Choncho iwo anachotsa mwalawo. Kenaka Yesu anayangʼana kumwamba ndikuti, “Atate, Ine ndikukuthokozani chifukwa mumandimvera. 42 Ine ndimadziwa kuti Inu mumandimvera nthawi zonse, koma Ine ndanena izi chifukwa cha anthu amene ayima pano, kuti iwo akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.”
43 Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!” 44 Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu.
Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.”
Ayuda Apangana za Kupha Yesu
45 Choncho Ayuda ambiri amene anabwera kudzamuchereza Mariya ndi kuona zimene Yesu anachita anamukhulupirira Iye. 46 Koma ena a iwo anapita kwa Afarisi ndi kukawawuza zimene Yesu anachita. 47 Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anayitanitsa msonkhano wa akulu olamulira.
Iwo anafunsa kuti, “Kodi ife tikuchita chiyani? Pano pali munthu uyu akuchita zizindikiro zodabwitsa zambiri. 48 Ngati ife timuleka kuti apitirize chotere, aliyense adzamukhulupirira Iye, ndipo kenaka Aroma adzabwera ndi kudzatenga malo athu pamodzi ndi dziko lathu.”
49 Kenaka mmodzi wa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, anayankhula kuti, “Inu simukudziwa kanthu kalikonse! 50 Inu simukuzindikira kuti kuli bwino kwa inu kuti munthu mmodzi afe mʼmalo mwa anthu kusiyana ndi kuti mtundu wonse uwonongeke.”
51 Iye sananene izi mwa iye yekha, koma monga mkulu wa ansembe chaka chimenecho ananenera kuti Yesu anayanera kufera mtundu wa Ayuda, 52 ndipo osati mtundu okhawo komanso kwa ana ena a Mulungu onse obalalikana, kuti awabweretse pamodzi ndi kuwapanga kukhala amodzi. 53 Choncho kuyambira tsiku limeneli iwo anakonzekera za kuti amuphe.
54 Chifukwa cha ichi Yesu sanayendenso moonekera pakati pa Ayuda. Mʼmalo mwake Iye anapita ku chigawo cha kufupi ndi chipululu, ku mudzi wa Efereimu, kumene Iye anakhalako ndi ophunzira ake.
55 Nthawi ya Paska wa Ayuda itayandikira, ambiri anakwera kupita ku Yerusalemu kuchokera ku madera a ku midzi chifukwa cha mwambo wa kuyeretsedwa Paska asanafike. 56 Iwo anapitiriza kumufunafuna Yesu, ndipo pamene ankayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi ukuganiza chiyani? Kodi Iye sabwera konse kuphwando?” 57 Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anapereka lamulo kuti ngati wina aliyense adziwe kumene kunali Yesu, iye akawawuze kuti akamugwire.
Nzeru Ikuyitana
8 Kodi nzeru sikuyitana?
Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake?
2 Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira,
imayima pa mphambano ya misewu.
3 Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda,
pa makomo olowera imafuwula kuti,
4 Inu anthu, ndikuyitana inu;
ndikuyitanatu anthu onse.
5 Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera;
inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.
6 Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri;
ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama.
7 Pakamwa panga pamayankhula zoona
ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa.
8 Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama;
mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka.
9 Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona;
kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza.
10 Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva,
nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino.
11 Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali,
ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru.
12 Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera.
Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino.
13 Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa.
Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama,
kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.
14 Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino;
ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu.
15 Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira.
Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama.
16 Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula.
Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko.
17 Ndimakonda amene amandikonda,
ndipo amene amandifunafuna amandipeza.
18 Ine ndili ndi chuma ndi ulemu,
chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika.
19 Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala;
zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri.
20 Ndimachita zinthu zolungama.
Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo.
21 Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda
ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma.
22 “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba.
Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.
23 Ndinapangidwa kalekalelo,
pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.
24 Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi,
zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.
25 Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo,
mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,
26 lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake;
lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.
27 Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga,
pamene ankalemba malire a nyanja yozama,
28 pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga
ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,
29 pamene anayikira nyanja malire
kuti madzi asadutse malirewo,
ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.
30 Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri;
ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku,
kusangalala nthawi zonse pamaso pake.
31 Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse
ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”
32 “Ndiye tsono ana inu, ndimvereni;
odala anthu amene amasunga njira zanga.
33 Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru;
musanyozere mawu anga.
34 Wodala munthu amene amandimvera,
amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku,
kudikirira pa chitseko changa.
35 Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo
ndipo Yehova amamukomera mtima.
36 Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha;
onse amene amandida amakonda imfa.”
1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu.
Kulembera oyera mtima a ku Efeso, okhulupirika mwa Khristu Yesu:
2 Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
Madalitso Auzimu mwa Khristu
3 Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu. 4 Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake, 5 Iye anakonzeratu kuti ife titengedwe ngati ana mwa Yesu Khristu, molingana ndi kukonda kwake ndi chifuniro chake. 6 Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda. 7 Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu 8 chimene anatipatsa mosawumira. Mwa nzeru zonse ndi chidziwitso, 9 Iye watiwululira chifuniro chake chimene chinali chobisika, chimene anachikonzeratu mwa Khristu, molingana ndi kukoma mtima kwake. 10 Chimene anakonza kuti chichitike nʼchakuti, ikakwana nthawi yake asonkhanitsa pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za kumwamba ndi pa dziko lapansi.
11 Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake, 12 nʼcholinga chakuti, ife amene tinali oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu, tiyamike ulemerero wake. 13 Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza. 14 Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.
Kuyamika ndi Kupemphera
15 Choncho, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chanu mwa Ambuye Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse, 16 ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga. 17 Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni. 18 Ndimapempheranso kuti maso a mitima yanu atsekuke ndi cholinga choti mudziwe chiyembekezo chimene Iye anakuyitanirani, chuma cha ulemerero chomwe chili mwa anthu oyera mtima. 19 Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu zake zazikulu koposa zimene zili mwa ife amene timakhulupirira. Mphamvuyi ndi yofanana ndi mphamvu yoposa ija 20 imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba. 21 Anamukhazika pamwamba pa ulamuliro onse ndi mafumu, mphamvu ndi ufumu, ndiponso pamwamba pa dzina lililonse limene angalitchule, osati nthawi ino yokha komanso imene ikubwerayo. 22 Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo, 23 umene ndi thupi lake, chidzalo cha Iye amene adzaza chilichonse mu njira iliyonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.