M’Cheyne Bible Reading Plan
Bezaleli ndi Oholiabu
31 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 2 “Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda. 3 Ndipo ndamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: 4 Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa, 5 kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja. 6 Ndasankhanso Oholiabu mwana wa Ahisamaki wa fuko la Dani. Ndiponso ndapereka nzeru kwa anthu aluso motero adzagwira ntchito zonse zimene ndakulamulira kuti zichitike monga izi: 7 Kupanga tenti ya msonkhano, bokosi laumboni pamodzi ndi chophimbira chake, ndiponso zonse za mu tenti, 8 tebulo ndi zida zake, choyikapo nyale cha golide wabwino kwambiri ndi ziwiya zake zonse, guwa lofukizirapo lubani, 9 guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, beseni ndi nsichi yake, 10 ndiponso zovala zonse zolukidwa, zovala zopatulika za Aaroni wansembe pamodzi ndi za ana ake, zovala pamene akutumikira monga ansembe, 11 ndiponso mafuta odzozera ndi lubani wonunkhira wa ku malo opatulika. Iwo azipanga monga momwe Ine ndinakulamulira.”
Za Sabata
12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 13 “Uza ana a Israeli kuti azisunga Masabata anga. Ichi chidzakhala chizindikiro pakati pa inu ndi Ine pamodzi ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo, chosonyeza kuti Ine ndine amene ndimakuyeretsani.
14 “Motero muzisunga tsiku la Sabata chifukwa ndi loyera kwa inu. Aliyense amene adetsa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake. 15 Mugwire ntchito kwa masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, lopuma, tsiku lopatulika la Yehova. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. 16 Aisraeli onse komanso zidzukulu zawo mʼtsogolo azidzasunga tsiku la Sabata ngati pangano lamuyaya. 17 Tsiku la Sabata lidzakhala chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi Aisraeli chosonyeza kuti Yehova analenga za kumwamba ndi dziko lapansi kwa masiku asanu ndi limodzi ndi kuti pa tsiku lachisanu ndi chiwiri analeka kugwira ntchito napumula.”
18 Yehova atamaliza kuyankhula ndi Mose pa phiri la Sinai, anamupatsa Mose miyala iwiri yaumboni, imene Mulungu analembapo ndi chala chake.
Mʼbusa Wabwino ndi Nkhosa Zake
10 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba. 2 Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo. 3 Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa. 4 Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake. 5 Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo.” 6 Yesu ananena mawu ophiphiritsawa, koma Afarisi sanazindikire zimene ankawawuza.
7 Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa. 8 Onse amene anadza ndisanabwere Ine ndi akuba ndi achifwamba, ndipo nkhosa sizinawamvere. 9 Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu. 10 Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.
11 “Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake. 12 Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa. 13 Munthuyo amathawa chifukwa ndi wantchito ndipo sasamalira chilichonse cha nkhosazo.
14 “Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa, 15 monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa. 16 Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi. 17 Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso. 18 Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.”
19 Pa mawu awa Ayuda anagawikananso. 20 Ambiri a iwo anati, “Iye ndi wogwidwa ndi ziwanda ndi wamisala. Chifukwa chiyani mukumvera Iye?”
21 Koma ena anati, “Awa si mawu a munthu wogwidwa ndi ziwanda. Kodi ziwanda zingathe bwanji kutsekula maso a wosaona?”
Kusakhulupirira kwa Ayuda
22 Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kupatulidwa kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nthawi yozizira, 23 ndipo Yesu ankayenda mʼbwalo la Nyumbayo ku malo a Solomoni. 24 Ayuda anamuzungulira Iye akunena kuti, “Kodi iwe udzazunguza malingaliro athu mpaka liti? Ngati iwe ndi Khristu, tiwuze momveka.”
25 Yesu anayankha kuti, “Ine ndimakuwuzani, koma inu simukhulupirira. Ntchito zimene ndikuchita mʼdzina la Atate anga zikundichitira umboni, 26 koma inu simukhulupirira chifukwa simuli a gulu lankhosa zanga. 27 Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine. 28 Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa. 29 Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga. 30 Ine ndi Atate ndife amodzi.”
31 Ayuda anatolanso miyala kuti amugende Iye, 32 koma Yesu anawawuza kuti, “Ine ndakuonetsani zinthu zambiri zabwino zodabwitsa kuchokera kwa Atate. Nʼchifukwa chiti mwa izi chimene mukundigendera?”
33 Ayuda anayankha kuti, “Ife sitikukugenda chifukwa cha izi, koma popeza ukunyoza Mulungu, chifukwa iwe, munthu wamba, ukuti ndiwe Mulungu.”
34 Yesu anawayankha kuti, “Kodi sizinalembedwa mʼmalamulo anu kuti, ‘Ine ndanena kuti ndinu milungu?’ 35 Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke, 36 nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’ 37 Musandikhulupirire Ine ngati sindichita ntchito za Atate anga. 38 Koma ngati Ine ndikuchita zimenezi, ngakhale kuti simundikhulupirira, khulupirirani ntchito zodabwitsazo, ndipo mudziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndiponso Ine ndili mwa Atate.” 39 Iwo anafuna kumugwiranso koma anawapulumuka mʼmanja mwawo.
40 Kenaka Yesu anabwereranso kutsidya la mtsinje wa Yorodani kumalo kumene Yohane ankabatiza mʼmasiku akale. Iye anakhala kumeneko 41 ndipo anthu ambiri anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Ngakhale kuti Yohane sanachite chizindikiro chodabwitsa, zonse zimene Yohane ananena za munthu uyu zinali zoona.” 42 Ndipo pamalo amenewo ambiri anakhulupirira Yesu.
Za Mkazi Wachigololo
7 Mwana wanga, mvera mawu anga;
usunge bwino malamulo angawa.
2 Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo;
samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako.
3 Uchite ngati wawamangirira pa zala zako,
ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako.
4 Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,”
ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”
5 Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo
ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo.
6 Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga
ndinasuzumira pa zenera.
7 Ndinaona pakati pa anthu opusa,
pakati pa anyamata,
mnyamata wina wopanda nzeru.
8 Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo,
kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo.
9 Inali nthawi yachisisira madzulo,
nthawi ya usiku, kuli mdima.
10 Ndipo mkaziyo anadzakumana naye,
atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.
11 (Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve,
iye ndi wosakhazikika pa khomo.
12 Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika,
ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse).
13 Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona
ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti,
14 “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano.
Lero ndakwaniritsa malumbiro anga.
15 Choncho ndinabwera kudzakumana nawe;
ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza!
16 Pa bedi panga ndayalapo
nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto.
17 Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira
za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni.
18 Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa;
tiye tisangalatsane mwachikondi!
19 Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako;
wapita ulendo wautali:
20 Anatenga thumba la ndalama
ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.”
21 Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo;
amukopa ndi mawu ake oshashalika.
22 Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo
ngati ngʼombe yopita kukaphedwa,
monga momwe mbawala ikodwera mu msampha,
23 mpaka muvi utalasa chiwindi chake,
chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe,
osadziwa kuti moyo wake uwonongeka.
24 Tsono ana inu, ndimvereni;
mvetsetsani zimene ndikunena.
25 Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu;
musasochere potsata njira zake.
26 Paja iye anagwetsa anthu ambiri;
wapha gulu lalikulu la anthu.
27 Nyumba yake ndi njira yopita ku manda,
yotsikira ku malo a anthu akufa.
Kuchita Zabwino kwa Onse
6 Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe. 2 Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu. 3 Ngati wina adziyesa kanthu pamene iyeyo sali kanthu konse, akudzinamiza yekha. 4 Munthu aliyense aziyesa yekha ntchito zake mmene zilili. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, iyeyo asadzifanizire ndi munthu wina wake, 5 pakuti aliyense ayenera kusenza katundu wake.
6 Koma munthu amene akuphunzira mawu, agawireko mphunzitsi wake zinthu zonse zabwino zimene iye ali nazo.
7 Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. 8 Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha. 9 Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa. 10 Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.
Osati Mdulidwe koma Kulengedwa Mwatsopano
11 Onani zilembo zazikulu zimene ine ndikulemba ndi dzanja langa.
12 Onse amene akufuna kuoneka abwino pamaso pa anthu akukukakamizani kuti muchite mdulidwe. Akuchita izi ndi cholinga chimodzi chokha, chakuti apewe kuzunzidwa chifukwa cha mtanda wa Khristu. 13 Pakuti ngakhale iwowa amene anachita mdulidwe satsata Malamulo, komabe akufuna kuti muchite mdulidwe kuti anyadire mdulidwe wanuwo. 14 Ine sindingathe kunyadira kanthu kena koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu, kudzera mwa mtandawo dziko lapansi linapachikidwa kwa ine ndi ine ku dziko lapansi. 15 Pakuti kaya mdulidwe kapena kusachita mdulidwe, sizitanthauza kanthu; chofunika ndi kulengedwa mwatsopano. 16 Mtendere ndi chifundo zikhale kwa onse amene amatsata chiphunzitso ichi, ndi pa Israeli wa Mulungu.
17 Pomaliza wina asandivutitse, pakuti mʼthupi mwanga muli zizindikiro za Yesu.
18 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu zikhale ndi mzimu wanu abale. Ameni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.