M’Cheyne Bible Reading Plan
Malamulo a Zachilungamo ndi Zachifundo
23 “Usafalitse mbiri yabodza. Usathandize munthu wolakwa pomuchitira umboni wonama.
2 “Usatsate gulu la anthu ndi kuchita choyipa. Pamene ukupereka umboni mʼbwalo lamilandu, usakhotetse mlandu chifukwa chofuna kukondweretsa anthu ambiri. 3 Ndipo poweruza mlandu wa munthu wosauka usamukondere.
4 “Ngati ukumana ndi ngʼombe kapena bulu wa mdani wako zitasochera, uwonetsetse kuti wazitenga kupita nazo kwa mwini wakeyo. 5 Ngati uwona bulu wa munthu wina amene amakuda atagwa ndi katundu, usamusiye pomwepo, uwonetsetse kuti wamuthandiza.
6 “Usakhotetse milandu ya anthu osauka. 7 Upewe zabodza ndipo usaphetse munthu wosalakwa ndi wolungama, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.
8 “Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa.
9 “Usamuzunze mlendo, pakuti inu nomwe mukudziwa mmene amamvera mlendo chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Igupto.
Malamulo a Nthawi Zopuma
10 “Muzidzala mbewu zanu mʼmunda ndi kumakolola mbewuzo kwa zaka zisanu ndi chimodzi. 11 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi.
12 “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri musagwire ntchito kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu apume ndiponso kuti kapolo wobadwira mʼnyumba yanu ndi mlendo yemwe apezenso mphamvu.
13 “Samalani pochita zonse zimene ine ndanena. Musamapemphere kwa milungu ina ndipo mayina awo musamawatchule.
Masiku Atatu Akulu a Chikondwerero
14 “Muzichita zikondwerero zolemekeza Ine katatu pa chaka.
15 “Muzichita Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi mwezi wa Abibu pa nthawi yomwe ndayika, pakuti mʼmwezi umenewu munatuluka mʼdziko la Igupto.
“Pasapezeke munthu wobwera pamaso panga wopanda kanthu mʼmanja.
16 “Muzichita Chikondwerero cha Masika pogwiritsa ntchito zipatso zoyambirira kucha zimene munadzala mʼmunda.
“Muzichitanso Chikondwerero cha Zokolola pakutha pa chaka, pamene mukututa zokolola zanu mʼmunda.
17 “Amuna onse azionekera pamaso pa Ambuye Yehova katatu pa chaka.
18 “Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti.
“Ndipo musasunge mafuta anyama yansembe ya pa chikondwerero mpaka mmawa.
19 “Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku Nyumba ya Yehova Mulungu wanu.
“Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.
Kutsogolera kwa Mngelo wa Mulungu
20 “Taona Ine ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu kuti akutetezeni mʼnjiramo ndi kukakufikitsani ku malo amene ndakonza. 21 Muzimumvera ndi kumvetsetsa zimene akunena. Musamuwukire chifukwa sadzakhululuka kuwukira kwanu, pakuti akuchita zimenezi mʼdzina langa. 22 Ngati mudzamvera iyeyu ndi kuchita zonse zimene Ine ndikunena, Ine ndidzakhala mdani wa adani anu ndipo ndidzatsutsana ndi onse otsutsana nanu. 23 Mngelo wanga adzakhala patsogolo panu ndipo adzakufikitsani mʼdziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanaani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawapheratu onsewo. 24 Musagwadire milungu yawo kapena kuyipembedza. Ndipo musatsatire zinthu zomwe amachita. Koma inu mukawononge milungu yawo ndi kuphwasula malo amene amapembedzerapo. 25 Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu. 26 Palibe mkazi amene adzapite padera kapena kukhala wosabereka mʼdziko mwanu. Ndidzakupatsani moyo wautali.
27 “Ine ndidzawachititsa mantha ndi kusokoneza anthu onse amene adzalimbana ndi inu ndipo adani anu onse adzakuthawani. 28 Ahivi, Akanaani ndi Ahiti adzathawa ngati kuti ndawatumizira mavu. 29 Komabe sindidzawachotseratu onse mʼchaka chimodzi chifukwa dziko lingadzakhale lopanda anthu ndipo nyama zakuthengo zidzakuchulukirani. 30 Ndidzawathamangitsa pangʼonopangʼono mpaka inu mutachuluka kokwanira mwakuti nʼkutenga dzikolo.
31 “Malire a dziko lanu adzakhala kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku nyanja ya Afilisti, ndiponso kuyambira ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Anthu onse okhala mʼdziko limeneli ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo mudzawathamangitsa. 32 Musachite pangano ndi iwo kapena ndi milungu yawo. 33 Asadzakhale mʼdziko lanu chifukwa angadzakuchimwitseni ndi kuyamba kupembedza milungu yawo. Mukadzatero ndiye kuti mwakodwa mu msampha.”
Yesu Asandutsa Madzi Kukhala Vinyo
2 Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, 2 ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo. 3 Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.”
4 Yesu anayankha kuti, “Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.”
5 Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”
6 Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
7 Yesu anati kwa antchitowo, “Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende.
8 Ndipo Iye anatinso kwa iwo, “Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.”
Iwo anachita momwemo. 9 Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali 10 ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”
11 Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.
Yesu Ayeretsa Nyumba ya Mulungu
12 Zitatha izi Iye anatsikira ku Kaperenawo pamodzi ndi amayi ake, abale ake ndi ophunzira ake. Iwo anakhala kumeneko masiku owerengeka.
13 Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu. 14 Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo. 15 Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo. 16 Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, “Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!”
17 Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.”
18 Kenaka Ayuda anamufunsa Yesu kuti, “Kodi mungationetse chizindikiro chodabwitsa chotani chotsimikizira ulamuliro wanu wochitira izi?”
19 Yesu anawayankha kuti, “Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.”
20 Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?” 21 Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake. 22 Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula.
23 Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake. 24 Koma Yesu sanawakhulupirire iwo, pakuti amadziwa anthu onse. 25 Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.
41 “Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba
kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?
2 Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake,
kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza?
3 Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo?
Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa?
4 Kodi idzachita nawe mgwirizano
kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya?
5 Kodi udzasewera nayo ngati mbalame,
kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo?
6 Kodi anthu adzayitsatsa malonda?
Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse?
7 Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga,
kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?
8 Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo,
ndipo iweyo sudzabwereranso.
9 Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza;
kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha.
10 Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa.
Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine?
11 Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere?
Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.
12 “Sindidzaleka kuyankhula za ziwalo zake za chirombocho,
za mphamvu zake ndiponso za maonekedwe a thupi lake.
13 Ndani angasende chikopa chake?
Ndani angayiyandikire kuti abowole chikopa chake cholimbacho?
14 Ndani angatsekule kukamwa kwake,
pakamwa pamene pazunguliridwa ndi mano ochititsa mantha?
15 Kumsana kwake kuli mizere ya mamba
onga zishango zolumikizanalumikizana;
16 Mambawo ndi olukanalukana
kotero kuti mpweya sungathe kulowa pakati pake.
17 Ndi olumikizanalumikizana;
ndi omatirirana kwambiri kotero kuti sangathe kulekana.
18 Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali;
maso ake amawala ngati kuwala kwa mʼbandakucha.
19 Mʼkamwa mwake mumatuluka nsakali zamoto ndipo
mumathetheka mbaliwali zamoto.
20 Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi
ngati wa mʼnkhali yowira yomwe ili pa moto wa bango.
21 Mpweya wake umayatsa makala,
ndipo malawi amoto amatuluka mʼkamwa mwake.
22 Mphamvu zake zili mʼkhosi mwake;
aliyense wokumana nayo amangoti njenjenje ndi mantha.
23 Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana ndipo
ndi yokhwima kwambiri ndi yolimba.
24 Pachifuwa pake ndi powuma ngati mwala,
ndi pa gwaa, ngati mwala wamphero.
25 Ngʼonayo ikangovuwuka,
ndi anthu amphamvu omwe amaopa; amabwerera mʼmbuyo, kuthawa.
26 Ngakhale ikanthidwe ndi lupanga, lupangalo silichita kanthu,
ngakhale mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera.
27 Chitsulo imachiyesa ngati phesi chabe
ndi mkuwa ngati chikuni chowola.
28 Muvi sungathe kuyithawitsa,
miyala imene ayilasa nayo imangoyinyenyanyenya.
29 Zibonga zimakhala ngati ziputu;
imangoseka pamene akuyibaya ndi nthungo.
30 Mamba a ku mimba kwake ali ngati chopunthira chakunthwa ndipo
imasiya mkukuluzi mʼmatope ngati galeta lopunthira tirigu.
31 Imagadutsa madzi ozama ngati madzi a mʼnkhali,
imachititsa nyanja kuti iwire ngati mbiya yoyengera mafuta.
32 Kumbuyo kwake imasiya nthubwitubwi zambee,
kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi.
33 Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho,
nʼcholengedwa chopanda mantha.
34 Chimanyoza nyama zina zonse;
icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.”
Paulo ndi Atumwi Onyenga
11 Ndikukhulupirira kuti mupirira nako pangʼono kupusa kwanga. Chonde tandipirirani! 2 Nsanje imene ndimakuchitirani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi yekha, mwamunayo ndiye Khristu, kuti ndidzakuperekeni inuyo kwa Iyeyo monga namwali wangwiro. 3 Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi kuchenjera kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu. 4 Pakuti ngati wina abwera kwa inu nalalikira Yesu wina wosiyana ndi Yesu amene tinamulalikira, kapena ngati mulandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu amene munalandira, kapena uthenga wabwino wina wosiyana ndi umene munawuvomereza, inuyo mumangolandira mosavuta.
5 Komatu sindikuganiza kuti ndine wotsika kwambiri kwa “atumwi apamwamba.” 6 Mwina ndikhoza kukhala wosaphunzitsidwa kayankhulidwe, koma ndili ndi chidziwitso. Izi tinakufotokozerani momveka bwinobwino. 7 Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere? 8 Ndinkalanda mipingo ina pomalandira thandizo kwa iwo kuti ndikutumikireni. 9 Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero. 10 Kunena moona mtima molingana ndi chilungamo cha Khristu chimene chili mwa ine, palibe amene angandiletse kudzitamandira mʼzigawo za ku Akaya. 11 Nʼchifukwa chiyani ndikutero? Kodi nʼchifukwa choti sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani!
12 Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira. 13 Pakuti anthu oterewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzizimbayitsa ngati atumwi a Khristu. 14 Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu. 15 Nʼzosadabwitsa tsono ngati atumiki ake akudzizimbayitsa ngati otumikira chilungamo. Matsiriziro awo adzalandira zoyenerana ndi ntchito zawo.
Paulo Anyadira Mazunzo Ake
16 Ndibwereze kunena kuti, wina aliyense asandiyese chitsiru. Koma ngati mutero, mundilandire monga mmene mukhoza kulandirira chitsiru, kuti ndinyadirepo pangʼono. 17 Kudzinyadira kwangaku, sindikuyankhula monga mmene Ambuye akufunira koma ngati chitsiru. 18 Popeza ambiri akudzitama monga dziko lapansi limachitira, inenso ndidzitamanso. 19 Inu mumalolera kukhala ndi zitsiru mokondwera chifukwa mumati ndinu anzeru! 20 Kunena zoona mumangololera aliyense; amene amakusandutsani akapolo, kapena amene amakudyerani masuku pamutu, kapena amene amakupezererani, kapena amene amadzitukumula, kapena amene amakumenyani khofi. 21 Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi.
Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso. 22 Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso ndine Mhebri. Kodi iwo ndi Aisraeli? Inenso ndine Mwisraeli. Kodi iwo ndi zidzukulu za Abrahamu? Inenso ndine mdzukulu wa Abrahamu. 23 Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankhula ngati wamisala. Ine ndine woposa iwowo. Ndagwira ntchito kwambiri kupambana iwo, ndakhala ndikuyikidwa mʼndende kawirikawiri, ndakwapulidwapo kwambiri, kawirikawiri ndinali pafupi kufa. 24 Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi. 25 Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja. 26 Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga. 27 Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala. 28 Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse. 29 Ndani ali wofowoka, ine wosakhala naye mʼkufowoka kwakeko? Ndani amene mnzake amuchimwitsa, ine wosavutika mu mtima?
30 Ngati nʼkoyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira pa zinthu zimene zimaonetsa kufowoka kwanga. 31 Mulungu, Atate a Ambuye Yesu, amene tiyenera kumutamanda nthawi zonse, akudziwa kuti sindikunama. 32 Ku Damasiko, bwanamkubwa woyimira Mfumu Areta, anayika alonda kuzungulira mzinda wonse kuti andigwire. 33 Koma abale anandiyika mʼdengu nanditsitsira pa chipupa kudzera pa zenera la mpandawo, motero ndinapulumuka mʼmanja mwake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.