M’Cheyne Bible Reading Plan
Malamulo Khumi
20 Ndipo Mulungu anayankhula mawu onse awa nati:
2 “Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.
3 “Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.”
4 “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. 5 Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane. 6 Koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda, ndi kusunga malamulo anga.
7 “Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.
8 “Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. 9 Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi. 10 Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu. 11 Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera.
12 “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
13 “Usaphe.
14 “Usachite chigololo.
15 “Usabe.
16 “Usapereke umboni womunamizira mnzako.
17 “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”
18 Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali. 19 Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.”
20 Koma Mose anati kwa anthuwo, “Musachite mantha. Mulungu wabwera kudzakuyesani kuti mukhale ndi mtima woopa Mulungu kuti musamuchimwire.”
21 Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu.
Za Mafano ndi Maguwa Ansembe
22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Awuze izi Aisraeli: ‘Inu mwaona nokha kuti Ine ndakuyankhulani kuchokera kumwamba. 23 Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ”
24 Mundimangire guwa ladothi ndipo muziperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zanu. Pamalo paliponse pamene Ine ndidzakonza kuti muzinditamandirapo, ndidzabwera ndi kukudalitsani. 25 Ngati mudzandimangira guwa lansembe lamiyala, musagwiritse ntchito miyala yosema, pakuti mudzalidetsa mukadzagwiritsa ntchito zida. 26 Musamakwere pa makwerero popita pa guwa langa lansembe kuti mungaonetse maliseche anu.
23 Kenaka gulu lonse la anthuwo linayimirira ndi kumutengera kwa Pilato. 2 Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.”
3 Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?”
Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”
4 Kenaka Pilato anawawuza akulu a ansembe ndi gulu la anthu, “Ine sindikumupeza cholakwa munthuyu.”
5 Koma iwo analimbikirabe kuti, “Iyeyu amasokoneza anthu ku Yudeya konse ndi chiphunzitso chake, Iyeyu anayambira ku Galileya ndipo wayenda mtunda wonse mpaka kuno.”
6 Pakumva zimenezi, Pilato anafunsa ngati munthuyo ndi Mgalileya. 7 Iye atamva kuti Yesu anali pansi pa ulamuliro wa Herode, anamutumiza kwa Herodeyo, amene pa nthawi imeneyo analinso mu Yerusalemu.
8 Herode ataona Yesu, anakondwa kwambiri, chifukwa kwa nthawi yayitali, ankafunitsitsa atamuona. Kuchokera pa zimene anamva za Iye, anayembekezera kuti achita zodabwitsa. 9 Iye anamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sanayankhe. 10 Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anayimirira pamenepo ndi kumuneneza kwambiri. 11 Pamenepo Herode ndi asilikali ake anamuseka ndi kumunyoza Iye. Atamuveka mkanjo wonyezimira, anamutumizanso kwa Pilato. 12 Tsiku limenelo, Herode ndi Pilato anakhala abwenzi. Zisanachitike izi anali adani.
13 Pilato anasonkhanitsa akulu a ansembe, oweruza ndi anthu, 14 ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu. 15 Herodenso sanapeze chifukwa pakuti wamutumizanso kwa ife monga mmene mukuoneramu. Iyeyu sanachite chinthu chakuti aphedwe. 16 Nʼchifukwa chake, ine ndingomulanga, nʼkumumasula.” 17 (Pa nthawi yachikondwerero cha Paska iye ankayenera kumasula munthu mmodzi).
18 Onse pamodzi anafuwula kuti, “Muchotseni munthuyu! Timasulireni Baraba!” 19 (Baraba anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe mu mzinda ndi kupha).
20 Pofuna kumumasula Yesu, Pilato anawadandaulira iwo. 21 Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
22 Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”
23 Koma ndi mawu ofuwulitsa, analimbikirabe kuti Iye apachikidwe, ndipo kufuwulako kunapitirira. 24 Choncho Pilato anatsimikiza kuchita zofuna zawozo. 25 Iye anawamasulira munthu amene anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe ndi kupha, amene ankamufunayo, ndipo anawapatsa Yesu mwakufuna kwawo.
Kupachikidwa kwa Yesu
26 Ndipo pamene ankapita naye, anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera ku munda, namusenzetsa mtanda namuyendetsa pambuyo pa Yesu. 27 Gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye, kuphatikiza amayi amene ankabuma ndi kumulirira. 28 Yesu anatembenuka nati kwa iwo, “Ana aakazi a Yerusalemu, musandilirire Ine; dzililireni nokha ndi ana anu. 29 Pakuti nthawi idzabwera imene inu mudzati, ‘Ndi odala amayi osabereka, mimba zimene sizinabereke ndi mawere amene sanayamwitse!’ 30 Kenaka,
“adzawuza mapiri kuti tigwereni ife;
zitunda kuti tiphimbeni ife.
31 Chifukwa ngati anthu akuchita izi pa mtengo wauwisi, chidzachitike nʼchiyani ndi wowuma?”
32 Amuna ena awiri, onsewo achifwamba, anatengedwanso pamodzi ndi Yesu kukaphedwa. 33 Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere. 34 Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.
35 Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.”
36 Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa, 37 ndipo anati, “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.”
38 Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: uyu ndi mfumu ya ayuda.
39 Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, “Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!”
40 Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi? 41 Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu.”
42 Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.”
43 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”
Imfa ya Yesu
44 Linali tsopano pafupi ora lachisanu ndi chimodzi, ndipo mdima unagwa pa dziko lonse mpaka ora lachisanu ndi chinayi, 45 pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati. 46 Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.” Atanena zimenezi, anamwalira.
47 Kenturiyo, ataona zimene zinachitikazi, analemekeza Mulungu ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali munthu wolungama.” 48 Anthu onse amene anasonkhana kudzaonerera izi, ataona zinachitikazo, anadziguguda pachifuwa ndipo anachoka. 49 Koma onse amene anamudziwa Iye, kuphatikiza amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anayimirira akuona zinthu izi.
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
50 Ndipo taonani panali munthu wina wotchedwa Yosefe, mmodzi wa gulu loweruza, munthu wabwino ndi wolungama. 51 Iye sanavomereze zimene anzake abwalo anagwirizana ndi kuchita. Iye ankachokera ku mudzi wa Arimateyu wa ku Yudeya ndipo ankayembekezera ufumu wa Mulungu. 52 Atapita kwa Pilato, iye anakapempha mtembo wa Yesu. 53 Ndipo anawutsitsa, nawukulunga nsalu yabafuta nawuyika mʼmanda wosemedwa mʼmwala, amene panalibe wina amene anayikidwamo. 54 Linali tsiku lokonzekera ndipo Sabata linatsala pangʼono kuyamba.
55 Amayi amene anabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsata Yosefe ndipo anaona manda ndi momwe mtembo wake anawuyikira. 56 Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo.
Yehova Ayankhula
38 Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:
2 “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga
poyankhula mawu opanda nzeru?
3 Onetsa chamuna;
ndikufunsa
ndipo undiyankhe.
4 “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?
Ndiwuze ngati ukudziwa.
5 Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!
Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
6 Kodi maziko ake anawakumba potani,
kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
7 pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi
ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
8 “Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,
pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,
9 pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake
ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,
10 pamene ndinayilembera malire ake
ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.
11 Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire
apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’
12 “Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa,
kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake,
13 kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi
ndi kuthamangitsa anthu oyipa?
14 Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo;
zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala.
15 Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa,
ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu.
16 “Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja
kapena pa magwero ake ozama?
17 Kodi anakuonetsapo zipata za imfa?
Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani?
18 Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa?
Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi.
19 “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti?
Nanga mdima umakhala kuti?
20 Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi?
Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko?
21 Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale!
Wakhala ndi moyo zaka zambiridi!
22 “Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana
kapena unayionapo nyumba yosungira matalala,
23 zimene ndazisungira nthawi ya mavuto
ndi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo?
24 Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani
kapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi?
25 Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula,
nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi,
26 kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu,
chipululu chopandamo munthu,
27 kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa
ndi kumeretsamo udzu?
28 Kodi mvula ili ndi abambo ake?
Nanga madzi a mame anawabereka ndani?
29 Kodi madzi owundana anawabereka ndani?
Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba
30 pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala,
pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?
31 “Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi?
Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana?
32 Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake
kapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake?
33 Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa?
Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi?
34 “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo
kuti igwetse mvula ya chigumula?
35 Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime?
Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’
36 Kodi ndani anayika nzeru mu mtima,
ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu?
37 Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo?
Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo
38 pamene fumbi limasanduka matope,
ndipo matopewo amawumbika?
39 “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi
ndi kukhutitsa misona ya mikango
40 pamene ili khale mʼmapanga mwawo
kapena pamene ikubisala pa tchire?
41 Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani
pamene ana ake akulirira kwa Mulungu
ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?
Kulimbikitsa Zopereka
8 Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. 2 Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. 3 Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, 4 ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. 5 Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu. 6 Choncho tinamupempha Tito kuti atsirize poti nʼkuti atayamba kale ntchito yachisomoyi pakati panu. 7 Popeza pa zinthu zonse munachita bwino, monga pachikhulupiriro, poyankhula, pachidziwitso, pakhama lambiri ndi pachikondi chanu pa ife, onetsetsani kuti muchitenso bwino pachisomo ichi chopereka.
8 Sindikukulamulirani, koma ndikufuna kuona ngati chikondi chanu nʼchoona pofananitsa ndi changu cha anthu ena. 9 Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemera, koma chifukwa cha inuyo anasanduka wosauka, kuti umphawi wakewo, inuyo mulemere.
10 Ndipo nawa malangizo anga pa zoyenera inu kuchita pa nkhaniyi. Chaka chatha munali oyamba, osati ongofuna kupereka kokha komanso okhala ndi mtima ofuna kupereka. 11 Tsopano tsirizani ntchitoyi, ndipo changu chanu chofunitsitsa kugwira ntchitoyi ndi kuyitsiriza chichitike molingana ndi zimene muli nazo. 12 Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe.
13 Cholinga chathu sikuti tipeputse ena pamene inuyo mukuvutika, koma kuti pakhale kufanana. 14 Zambiri zimene muli nazo pakati panu muthandize nazo osowa, kuti nawonso akadzakhala nazo zambiri adzakuthandizeni pa zosowa zanu. Cholinga nʼkuchita mofanana, 15 monga kwalembedwa kuti, “Iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere.”
Tito Atumidwa ku Korinto
16 Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa Tito changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu. 17 Pakuti Tito sanangovomera kokha pempho lathu, koma yekha anafunitsitsa kwambiri kubwera kwa inu mwa iye yekha. 18 Ndipo tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale amene mipingo yonse yamuyamikira chifukwa cha utumiki wake wa Uthenga Wabwino. 19 Chowonjezera china nʼchakuti anasankhidwa ndi mipingo kuti atiperekeze pamene ife tikukapereka zopereka, zimene tikuchita pofuna kupereka ulemu kwa Ambuye mwini ndi kuonetsa kufunitsitsa kwathu pothandiza. 20 Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi. 21 Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu.
22 Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi wachangu ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu. 23 Kunena za Tito, ndiye mnzanga ndi wogwira naye ntchito pakati panu. Kunena za abale athu, ndiwo oyimirira mipingo ndi olemekezetsa Khristu. 24 Choncho anthu amenewa atsimikizireni za chikondi chanu ndipo adziwe chifukwa chimene ife timakunyadirani, kuti mipingo yonse iwone chimenechi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.