Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 15

Nyimbo ya Mose ndi Miriamu

15 Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi:

“Ine ndidzayimbira Yehova
    pakuti wakwezeka mʼchigonjetso.
Kavalo ndi wokwera wake,
    Iye wawaponya mʼnyanja.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
    ndiye chipulumutso changa.
Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda,
    Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza.
Yehova ndi wankhondo;
    Yehova ndilo dzina lake.
Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondo
    Iye wawaponya mʼnyanja.
Akatswiri ankhondo amphamvu a Farao
    amizidwa mʼNyanja Yofiira.
Nyanja yakuya inawaphimba;
    Iwo anamira pansi ngati mwala.”

Yehova, dzanja lanu lamanja
    ndi laulemerero chifukwa cha mphamvu zake.
Ndithu Yehova, dzanja lanu lamanja
    linaphwanya mdani.
Ndi ulemerero wanu waukulu,
    munagonjetsa okutsutsani.
Inu munatumiza mkwiyo wanu waukulu;
    ndipo unawapsereza ngati udzu.
Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu
    madzi anawunjikana pamodzi.
Nyanja yakuya ija inasanduka
    madzi owuma gwaa kufika pansi.

Mdaniyo anati,
    “Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira.
Ndidzagawa chuma chawo;
    ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa.
Ine ndidzasolola lupanga langa,
    ndi mkono wanga ndidzawawononga.”
10 Koma Inu munawuzira mphepo yanu,
    ndipo nyanja inawaphimba.
Iwo anamira ngati chitsulo
    mʼmadzi amphamvu.

11 Ndithu Yehova, pakati pa milungu,
    ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera,
        ndiponso wotamandika wolemekezeka,
        chifukwa cha ntchito zanu,
        zazikulu ndi zodabwitsa?
12 Munatambasula dzanja lanu lamanja
    ndipo dziko linawameza.

13 Ndi chikondi chanu chosasinthika mudzatsogolera
    anthu amene munawawombola.
Ndi mphamvu zanu munawatsogolera
    ku malo anu woyera.
14 Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha,
    mantha woopsa agwira anthu a dziko la Filisiti.
15 Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu,
    otsogolera a dziko la Mowabu akunjenjemera ndi mantha,
ndipo anthu a ku Kanaani asungunuka ndi mantha.
16     Onse agwidwa ndi mantha woopsa.
Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu,
    iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu,
Inu Yehova atadutsa;
    inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula.
17 Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa
    pa phiri lanu.
Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo;
    malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu.
18 “Yehova adzalamula
    mpaka muyaya.”

19 Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma. 20 Ndipo Miriamu mneneri wamkazi, mlongo wa Aaroni anatenga zoyimbira ndipo akazi onse anamutsatira pambuyo, akuyimba ndi zoyimbira ndi kuvina. 21 Miriamu anawayimbira nyimbo iyi:

“Imbirani Yehova,
    chifukwa iye wapambana.
Kavalo ndi wokwerapo wake
    Iye wawamiza mʼnyanja.”

Madzi a ku Mara ndi Elimu

22 Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi. 23 Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara). 24 Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?”

25 Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino.

Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa. 26 Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”

27 Kenaka anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi awiri, ndipo anamanga misasa yawo kumeneko pafupi ndi madzi.

Luka 18

Fanizo la Mayi Wakhama pa Kupempha

18 Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke. Iye anati, “Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu. Ndipo panali mkazi wamasiye mʼmudzimo amene ankabwerabwera kwa iye ndi dandawulo lake kuti, ‘Mundiweruze mlandu mwachilungamo pakati pa ine ndi otsutsana nane.’

“Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu, koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’ ”

Ndipo Ambuye anati, “Tamvani zimene woweruza wopanda chilungamoyu wanena. Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira? Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?”

Fanizo la Mfarisi ndi Wolandira Msonkho

Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse. 10 “Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho. 11 Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu. 12 Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’

13 “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’

14 “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”

Yesu Adalitsa Ana Aangʼono

15 Anthu amabweretsanso ana aangʼono kwa Yesu kuti awadalitse. Ophunzira ataona izi, anawadzudzula. 16 Koma Yesu anayitana anawo kuti abwere kwa Iye nati, “Lolani ana abwere kwa Ine ndipo musawatsekereze, pakuti ufumu wa Mulungu uli wa anthu otere. 17 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene salandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono, sadzalowamo.”

Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu

18 Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”

19 Yesu anamuyankha kuti, “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha. 20 Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”

21 Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.”

22 Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.”

23 Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri. 24 Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu! 25 Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”

26 Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?”

27 Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”

28 Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!”

29 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu 30 adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”

Yesu Aneneratu za Imfa Yake Kachitatu

31 Yesu anatengera khumi ndi awiriwo pambali ndi kuwawuza kuti, “Taonani ife tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zalembedwa ndi Aneneri za Mwana wa Munthu zidzakwaniritsidwa. 32 Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira, 33 adzamukwapula ndi kumupha. Tsiku lachitatu Iye adzaukanso.”

34 Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula.

Yesu Achiritsa Wosaona

35 Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha, 36 anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika. 37 Iwo anamuwuza kuti “Yesu wa ku Nazareti akudutsa.”

38 Iye anayitana mofuwula, “Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”

39 Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”

40 Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti, 41 “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”

Iye anayankha kuti, “Ambuye, ine ndifuna ndionenso.”

42 Yesu anati kwa iye, “Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.” 43 Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.

Yobu 33

33 “Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga;
    mutcherere khutu zonse zimene ndinene.
Tsopano ndiyamba kuyankhula;
    mawu anga ali pa msonga ya lilime langa.
Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama;
    pakamwa panga pakuyankhula zoonadi zimene ndikuzidziwa.
Mzimu wa Mulungu wandiwumba,
    mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo.
Mundiyankhe ngati mungathe;
    konzekani tsopano kuti munditsutse.
Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu;
    nanenso ndinachokera ku dothi.
Musachite mantha ndipo musandiope ayi,
    Ine sindikupanikizani kwambiri ayi.

“Koma inu mwayankhula ine ndikumva,
    ndamva mawu anuwo onena kuti,
‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo;
    ndine woyera mtima ndipo ndilibe cholakwa.
10 Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo;
    Iye akundiyesa ngati mdani wake.
11 Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo,
    akulonda mayendedwe anga onse.’

12 “Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi,
    pakuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu.
13 Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iye
    kuti sayankha mawu ena aliwonse a munthu?
14 Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana,
    ngakhale munthu sazindikira zimenezi.
15 Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku,
    pamene anthu ali mʼtulo tofa nato
    pamene akungosinza chabe pa bedi,
16 amawanongʼoneza mʼmakutu
    ndi kuwaopseza ndi machenjezo ake,
17 kumuchotsa munthu ku zoyipa,
    ndi kuthetseratu kunyada kwake,
18 kumulanditsa munthu ku manda,
    kuti moyo wake usawonongeke ndi lupanga.

19 “Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake,
    nthawiyo thupi lake lonse limangophwanya,
20 kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya,
    ndipo amanyansidwa ndi chakudya chabwino chomwe.
21 Thupi lake limawonda
    ndipo mafupa ake, omwe anali obisika, tsopano amaonekera poyera.
22 Munthuyo amayandikira ku manda,
    moyo wake umayandikira kwa amene amabweretsa imfa.

23 “Koma patakhala mngelo ngati mthandizi,
    mmodzi mwa ambirimbiri oterewa,
    adzafotokoza zimene zili zoyenera,
24 kudzamukomera mtima ndi kunena kuti,
    ‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda;
    ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’
25 pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana;
    ndipo adzabwezeretsedwanso kukhala ngati mʼmasiku a unyamata wake.
26 Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa.
    Mulungu adzamulandira mwa chimwemwe
    ndipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba.
27 Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti,
    ‘Ndinachimwa ndipo sindinachite zolungama,
    koma sindinalangidwe koyenerana ndi kuchimwa kwanga.
28 Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda,
    ndipo ndidzakhala ndi moyo ndi kuonanso kuwala kwa dzuwa.’

29 “Mulungu amachita zonsezi kwa munthu
    kawirikawiri,
30 kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda,
    kuti athe kuonanso kuwala kwa moyo.

31 “Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere;
    khalani chete kuti ndiyankhule.
32 Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni;
    yankhulani, pakuti ine ndikufuna mupezeke wolungama.
33 Koma ngati sichoncho, mundimvere;
    khalani chete ndipo ine ndidzakuphunzitsani nzeru.”

2 Akorinto 3

Akhristu ndi Kalata Yochokera kwa Khristu

Kodi tayambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi ifenso tikufuna makalata otivomereza kwa inu, kapena ochokera kwa inu monga anthu ena? Inu ndinu kalata yathu, yolembedwa pa mitima yathu, yodziwika ndi yowerengedwa ndi aliyense. Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu.

Kulimba mtima kumeneku tili nako pamaso pa Mulungu kudzera mwa Khristu. Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu. Iye watipatsa kulimba mtima kuti tikhale atumiki a pangano latsopano, osati malamulo olembedwa koma a Mzimu; pakuti malamulo olembedwa amapha koma Mzimu amapereka moyo.

Ulemerero wa Pangano Latsopano

Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala, kodi nanga utumiki wa Mzimu sudzaposa apa? Ngati utumiki umene umatsutsa anthu unali ndi ulemerero, nanga koposa kotani ulemerero wa utumiki wobweretsa chilungamo! 10 Pakuti zimene zinali ndi ulemerero, tsopano zilibenso ulemerero pofananitsa ndi ulemerero wopambanawo. 11 Ndipo ngati zosakhalitsa zinabwera ndi ulemerero, koposa kotani ulemerero wamuyayawo!

12 Choncho, popeza tili ndi chiyembekezo chotere, ndife olimba mtima kwambiri. 13 Ife sitili ngati Mose amene amaphimba nkhope yake kuopa kuti Aisraeli angaone kuti kunyezimira kwa nkhope yake kumazilala. 14 Koma nzeru zawo zinawumitsidwa, pakuti mpaka lero chophimbira chomwecho chikanalipo pamene akuwerenga Chipangano Chakale. Sichinachotsedwebe, chifukwa chimachotsedwa ngati munthuyo ali mwa Khristu yekha. 15 Ngakhale lero lomwe lino akuwerenga mabuku a Mose pali chophimbabe mitima yawo. 16 Koma pamene aliyense atembenukira kwa Ambuye, “chophimbacho chimachotsedwa.” 17 Tsono Ambuye ndi Mzimu, ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye, pali ufulu. 18 Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.