M’Cheyne Bible Reading Plan
Mliri pa Ziweto
9 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao ndipo ukamuwuze kuti Yehova, Mulungu wa Ahebri akuti alole anthu anga apite kuti akandipembedze. 2 Koma ngati ukana kuti apite ndi kupitiriza kuwaletsa, 3 dzanja la Yehova lidzakantha ziweto zako zimene zili ku munda, pamodzi ndi akavalo, abulu, ngamira, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi ndi mliri woopsa kwambiri. 4 Koma Yehova adzasiyanitsa pakati pa ziweto za Israeli ndi ziweto za Igupto, kotero kuti palibe chiweto nʼchimodzi chomwe cha Aisraeli chimene chidzafe.”
5 Yehova anayika nthawi ndipo anati, “Yehova adzachita zimenezi mmawa mʼdziko muno.” 6 Ndipo mmawa mwake Yehova anachitadi zimenezi. Ziweto zonse za Aigupto zinafa, koma palibe chiweto ndi chimodzi chomwe cha Aisraeli chomwe chinafa. 7 Farao anatuma anthu kuti akafufuze ndipo anapeza kuti palibe chiweto chilichonse cha Aisraeli chomwe chinafa. Komabe mtima wake sunagonje ndipo iye sanalole kuti anthu apite.
Mliri wa Zotupa
8 Kenaka Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Tapani phulusa la pa moto lodzaza dzanja ndipo Mose aliwaze mmwamba pamaso pa Farao. 9 Phulusalo lidzasanduka fumbi pa dziko lonse la Igupto. Tsono fumbilo lidzasanduka zithupsa zomaphulika nʼkukhala zilonda pa munthu aliyense ndi pa nyama zomwe mʼdziko lonse la Igupto.”
10 Kotero anatenga phulusa la pa moto ndi kuyima pamaso pa Farao. Mose analiwaza mmwamba, ndipo panabuka zotupa zophulika zokha pa munthu aliyense ndi pa ziweto. 11 Amatsenga sanathe kumuyandikira Mose chifukwa nawonso anali ndi zithupsa monga mmene analili Aigupto ena onse. 12 Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo iye sanamvere Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.
Mliri wa Mvula ya Matalala
13 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mawa mmawa upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso ndipo ukamuwuze kuti Yehova Mulungu wa Ahebri akuti ulole anthu anga apite kuti akandipembedze. 14 Ngati suwalola, tsopano ndidzagwetsa miliri yanga yonse pa iwe ndi nduna zako ndiponso pa anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wina wofanana nane pa dziko lonse lapansi. 15 Pakuti ndikanakhala nditatukula kale dzanja langa ndikupheratu iwe pamodzi ndi anthu ako onse pa dziko lapansi. 16 Koma ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga kwa iwe ndiponso kuti dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi. 17 Komabe iwe ukudzitukumula pa anthu anga osawalola kuti atuluke. 18 Nʼchifukwa chake mawa, nthawi ngati ino, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo pa Igupto, kuyambira pachiyambi mpaka lero. 19 Tsopano lamula kuti ziweto zanu zonse ndi zinthu zonse zomwe zili ku minda kuti zilowetsedwe mʼkhola, chifukwa matalala adzagwera munthu aliyense ndi chiweto chilichonse chimene sichidzalowetsedwa mʼkhola ndipo zimene zidzakhala zili ku munda zidzafa.”
20 Nduna za Farao zinachita mantha ndi mawu a Yehova, ndipo zinalowetsa antchito awo ndi ziweto zawo mʼnyumba. 21 Koma iwo amene ananyozera mawu a Yehova anasiya akapolo ndi ziweto zawo panja.
22 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kweza dzanja lako kumwamba kuti matalala agwe pa dziko lonse la Igupto, pa munthu aliyense, pa ziweto ndi pa zonse zomera mʼminda ya Igupto.” 23 Mose ataloza ndodo yake kumwamba, Yehova anatumiza mabingu ndi matalala ndi ziphaliwali zongʼanima pa nthaka. Kotero Yehova anagwetsa matalala pa dziko la Igupto. 24 Matalala anagwa ndipo ziphaliwali zinangʼanima. Inali mphepo ya mkuntho yoopsa kwambiri imene sinakhaleponso mʼdziko lonse la Igupto chiyambire pamene Aigupto anakhala mtundu woyima pa okha. 25 Matalala anawononga dziko lonse la Igupto, munthu aliyense pamodzi ndi ziweto. Matalala aja anawononga zomera zonse za mʼmunda ndi kukhadzula mtengo uliwonse. 26 Ku malo kokhako kumene matalala sanafikeko ndi dera la Goseni kumene kunali Aisraeli.
27 Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati kwa iwo, “Tsopano ndachimwa, Yehova ndi wolungama, ine ndi anthu anga ndife olakwa. 28 Upemphere kwa Mulungu chifukwa mabingu ndi matalala atikwana. Ine ndidzakulolani kuti mupite. Simuyenera kukhalabe kuno.”
29 Mose anayankha, “Ndikangotuluka mu mzinda muno, ine ndidzakweza manja anga kwa Yehova ndi kupemphera. Mabingu ndi matalalawa adzaleka ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova ndiye akulamulira dziko lapansi. 30 Koma ine ndikudziwa kuti inu ndi nduna zanu simukuopabe Yehova Mulungu.”
31 Thonje ndi barele zinawonongeka, popeza barele anali atakhwima ndi thonje linali ndi maluwa. 32 Koma tirigu ndi mchewere sizinawonongeke chifukwa zimakhwima mochedwa.
33 Mose anasiyana ndi Farao natuluka mu mzindawo. Iye anakweza manja ake kwa Yehova. Mabingu ndi matalala zinaleka, ndipo mvula inalekeratu kugwa mʼdzikolo. 34 Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu zaleka, anachimwanso. Iye ndi nduna zake anawumitsanso mitima yawo. 35 Choncho Farao sanalole kuti Aisraeli apite monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.
Chenjezo ndi Chilimbikitso
12 Nthawi yomweyo, anthu miyandamiyanda atasonkhana, ndi kumapondanapondana, Yesu anayamba kuyankhula poyamba kwa ophunzira ake, nati, “Chenjereni ndi yisiti wa Afarisi, amene ndi chinyengo. 2 Palibe chinthu chophimbika chimene sichidzawululika, kapena chobisika chimene sichidzadziwika. 3 Chimene mwanena mu mdima chidzamveka dzuwa likuwala, ndipo zimene mwanongʼona mʼkhutu mʼchipinda chamʼkati, zidzayankhulidwa pa denga la nyumba.
4 “Ine ndikuwuzani, abwenzi anga, musachite mantha ndi amene amapha thupi chifukwa akatero sangachitenso kanthu. 5 Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye. 6 Kodi atimba asanu samagulidwa ndi ndalama ziwiri? Ngakhale zili chomwecho palibe imodzi ya izo imene imayiwalika ndi Mulungu. 7 Ndithudi, tsitsi lonse la mʼmutu mwanu ndi lowerengedwa. Musachite mantha; inu ndi oposa kwambiri mpheta zambiri.
8 “Ine ndikukuwuza kuti, aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa Munthu adzamuvomerezanso pamaso pa angelo a Mulungu. 9 Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu adzakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu. 10 Ndipo aliyense amene ayankhulira Mwana wa Munthu mawu oyipa adzakhululukidwa, koma iye wochitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa.
11 “Akadzakutengerani ku masunagoge pamaso pa oweruza ndi a maulamuliro, musadere nkhawa mmene mudzadzitchinjirizire nokha kapena chimene mudzayankhule, 12 pakuti Mzimu Woyera nthawi imeneyo adzakuphunzitsani zoyenera kunena.”
Fanizo la Munthu Wachuma Wopusa
13 Munthu wina mʼgulu la anthu anati kwa Iye, “Aphunzitsi, muwuzeni mʼbale wanga andigawireko chuma chamasiye.”
14 Yesu anayankha kuti, “Munthu iwe, ndani anandiyika Ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma pakati panu?” 15 Kenaka Iye anawawuza kuti, “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”
16 Ndipo Iye anawawuza fanizo ili, “Munda wa munthu wina wachuma unabereka kwambiri. 17 Iye anaganiza kuti, ‘Ndichite chiyani? Ndilibe malo osungiramo mbewu zanga.’
18 “Ndipo Iye anati, ichi ndi chimene ndidzachite: Ndidzaphwasula nkhokwe zanga zonse ndi kumanga zokulirapo, ndipo ndidzasungira mʼmenemo mbewu ndi katundu. 19 Ndipo ndidzawuza moyo wanga kuti, ‘Uli nazo zinthu zabwino zambiri zimene zikhalepo zaka zambiri, usapupulume; idya, imwa ndi kukondwera.’ ”
20 “Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Iwe wopusa! Usiku womwe uno moyo wako udzachotsedwa kwa iwe, ndipo ndi ndani amene adzatenge zimene iwe wadzikonzera?’
21 “Umu ndi mmene zidzakhalire ndi aliyense amene amadziwunjikira chuma, koma si wachuma pamaso pa Mulungu.”
Musadere Nkhawa
22 Kenaka Yesu anati kwa ophunzira ake, “Choncho Ine ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu, zimene mudzadya; kapena za thupi lanu, zimene mudzavala. 23 Moyo uposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. 24 Taonani makwangwala: iwo safesa kapena kukolola, alibe nyumba zosungamo zinthu kapena nkhokwe; komabe, Mulungu amawadyetsa. Koposa kotani inu amene ndi ofunikira kuposa mbalame. 25 Ndi ndani wa inu akhoza kuwonjeza ora pa moyo wake chifukwa cha kudandaula? 26 Popeza simungathe kuchita kanthu kakangʼono aka, nʼchifukwa chiyani mumadandaula ndi zinazi?
27 “Taonani mmene maluwa amakulira. Iwo sagwira ntchito kapena kusoka zovala. Koma Ine ndikuwuzani kuti, ngakhale Solomoni muulemelero wake wonse sanavalepo ngati limodzi la awa. 28 Ngati umu ndi mmene Mulungu amavekera udzu wakuthengo, umene lero ulipo ndipo mawa uponyedwa pa moto, nanga Iye adzakuvekani inu motani. Haa! Inu achikhulupiriro chochepa! 29 Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa. 30 Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi. 31 Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi.
Chuma cha Kumwamba
32 “Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu. 33 Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge. 34 Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”
Kukhala a Atcheru
35 “Khalani okonzekeratu ndipo nyale zanu ziziyaka, 36 ngati anthu oyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera kuphwando la ukwati, kuti pamene afika ndi kugogoda akhoza nthawi yomweyo kumutsekulira chitseko. 37 Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo pobwera adzawapeze akudikira. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti adzakonzekera kuwatumikira, adzakhala nawo pa tebulo ndipo adzabwera ndi kuwatumikira. 38 Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo adzawapeze ali okonzeka, ngakhale iye atabwera pa ora lachiwiri kapena lachitatu usiku. 39 Koma zindikirani izi: Ngati mwini nyumba akanadziwa ora limene mbala ibwera, sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe. 40 Inunso muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa ora limene simukumuyembekezera Iye.”
Wantchito Wokhulupirika ndi Wosakhulupirika
41 Petro anafunsa kuti, “Kodi mukunena fanizoli kwa ife, kapena kwa aliyense?”
42 Ambuye anayankha kuti, “Kodi tsono woyangʼanira wokhulupirika ndi wanzeru ndani? Kodi ndi amene mbuye wake wamuyika kukhala oyangʼanira antchito ake kuti aziwapatsa ndalama yachakudya pa nthawi yake yoyenera? 43 Zidzamukhalira bwino wantchito amene mbuye wake adzamupeza akuchita zimene pamene iye abwera. 44 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense. 45 Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo aziganiza mu mtima mwake kuti, ‘Bwana wanga akuchedwa kwambiri kubwera,’ ndipo kenaka ndi kuyamba kumenya antchito aamuna ndi aakazi ndi kudya, kumwa ndi kuledzera. 46 Mbuye wake adzabwera tsiku limene iye sakumuyembekezera ndi ora limene iye sakudziwa. Iye adzamulanga ndi kumusiya kumalo kumene kuli osakhulupirira.
47 “Wantchito amene amadziwa chifuniro cha mbuye wake koma wosakonzeka kapena wosachita chimene mbuye wake akufuna adzakwapulidwa zikwapu zambiri. 48 Koma wantchito amene sadziwa koma nʼkuchita zinthu zoyenera chilango, adzakwapulidwa zikwapu zochepa. Aliyense amene anapatsidwa zambiri, adzayenera kubwezanso zambiri; ndipo amene anamusungitsa zambiri, adzamulamula kuti abweze zambirinso.”
Za Kugawikana
49 “Ine ndabwera kudzayatsa moto pa dziko lapansi, ndipo ndikanakonda ukanayaka kale. 50 Koma Ine ndiyenera kubatizidwa, ndipo ndikusautsika mu mtima mpaka utachitika! 51 Kodi mukuganiza kuti Ine ndinabwera kudzabweretsa mtendere pa dziko lapansi? Ayi, Ine ndikukuwuzani kuti, ndinabweretsa kugawikana. 52 Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo mʼbanja limodzi mudzakhala anthu asanu ndipo adzawukirana wina ndi mnzake, atatu kuwukira awiri, ndipo awiri kuwukira atatu. 53 Anthu adzawukirana. Abambo kudzawukira mwana wawo wamwamuna, mwana wawoyo adzawukira abambo ake. Amayi adzawukira mwana wawo wamkazi, mwana wawoyo adzawukira amayi ake. Amayi adzawukira mpongozi wawo wamkazi, mpongoziyo adzawukira amayiwo.”
Kumasulira Nthawi
54 Iye anati kwa gulu la anthu, “Pamene mukuona mtambo ukukwera kummawa, nthawi yomweyo inu mumati, ‘kugwa mvula,’ ndipo imagwadi. 55 Ndipo pamene mphepo yakummwera ikuwomba, inu mumati ‘kutentha’ ndipo kumaterodi. 56 Achiphamaso inu! Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a dziko lapansi ndi thambo. Zikutheka bwanji kuti simukudziwa kumasulira kwa nthawi ino?
57 “Bwanji simukuzindikira nokha zoyenera kuchita? 58 Pamene mukupita kwa woweruza ndi amene munalakwirana naye, yesetsani kwambiri kuti muyanjane naye mʼnjiramo, chifukwa mukapanda kutero akhoza kukutengerani ku bwalo la milandu ndipo woweruzayo adzakuperekani kwa woyangʼanira ndende, ndipo woyangʼanira ndendeyo adzakuponyani mʼndende. 59 Ine ndikuwuzani kuti, simudzatulukamo mpaka mutalipira ndalama zonse.”
27 Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:
2 “Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama,
Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga,
3 nthawi zonse pamene ndili ndi moyo,
mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,
4 pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa,
lilime langa silidzayankhula zachinyengo.
5 Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona;
mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.
6 Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere;
chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga.
7 “Mdani wanga akhale ngati woyipa,
wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama!
8 Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa,
pamene Mulungu achotsa moyo wake?
9 Kodi Mulungu amamva kulira kwake
pamene zovuta zamugwera?
10 Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse?
Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?
11 “Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndipo
sindidzabisa njira za Wamphamvuzonse.
12 Inu mwadzionera nokha zonsezi.
Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake?
13 “Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa,
cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse.
14 Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipo
zidzukulu zake zidzasowa zakudya.
15 Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri,
ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.
16 Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi,
ndi kukundika zovala ngati mchenga,
17 zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale,
ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo.
18 Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche,
ili ngati msasa umene mlonda amamanga.
19 Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko;
akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita.
20 Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula;
mphepo yamkuntho imamunyamula usiku.
21 Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipo
imamuchotsa pamalo pake.
22 Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni,
pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro.
23 Mphepoyo imamuwomba ndithu
ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”
Kupambana kwa Chikondi
13 Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera. 2 Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu. 3 Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.
4 Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. 5 Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. 6 Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. 7 Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.
8 Chikondi ndi chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha. 9 Pakuti timadziwa zinthu pangʼono chabe ndipo timanenera pangʼono chabe. 10 Koma changwiro chikadzaoneka ndipo chopereweracho chidzatha. 11 Pamene ndinali mwana ndinkayankhula ngati mwana, ndinkaganiza ngati mwana, ndinkalingalira ngati mwana. Koma nditakula, zonse zachibwana ndinazisiya. 12 Pakuti tsopano tiona zinthu mosaoneka bwino ngati mʼgalasi loonera; kenaka tidzaziona maso ndi maso. Tsopano ndidziwa mosakwanira koma kenaka ndidzadziwa mokwanira, monga mmene Mulungu akundidziwira ine.
13 Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.