M’Cheyne Bible Reading Plan
Mulungu Apatsa Mose Mphamvu Zochita Zodabwitsa
4 Mose anayankha, “Aisraeliwo sakandikhulupirira ndipo sakandimvera. Iwowo adzati, ‘Yehova sanakuonekere iwe.’ ”
2 Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?”
Mose anayankha kuti, “Ndodo.”
3 Yehova anati, “Tayiponya pansi.”
Mose anayiponya pansi ndipo inasanduka njoka ndipo anayithawa. 4 Kenaka Yehova anati kwa iye, “Igwire mtchira.” Ndipo Mose anayigwira mchira njokayo ndipo inasandukanso ndodo mʼdzanja lake. 5 Yehova anati, “Ukachite zimenezi ndipo akakukhulupirira kuti Yehova, Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo, wakuonekera iwe.”
6 Yehova anatinso, “Pisa dzanja lako mʼmalaya akowo.” Choncho Mose anapisa dzanja lake mʼmalaya ake ndipo pamene analitulutsa, linali la khate kuchita kuti mbuu ngati ufa.
7 Yehova anati, “Tsopano pisanso dzanja lako mʼmalaya.” Mose anapisanso dzanja lakelo mʼmalaya ake ndipo atalitulutsa, linali labwinobwino, ngati thupi lake lonse.
8 Tsono Yehova anati “Akakapanda kukukhulupirira, osalabadira chozizwitsa choyambacho, akakhulupirira ndithu chifukwa cha chozizwitsa chachiwiricho. 9 Koma ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwiri izi kapena kukumvera, ukatunge madzi a mu mtsinje wa Nailo ndi kuwathira pa mtunda powuma ndipo madziwo adzasanduka magazi.”
10 Mose anati kwa Yehova, “Chonde Ambuye, chikhalire ine ndakhala munthu wosatha kuyankhula bwino. Ngakhale tsopano pamene mukundiyankhula, lilime langa ndi lolemera. Ndine wachibwibwi.”
11 Yehova anati kwa iye, “Kodi anapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosayankhula kapena wosamva? Ndani amapanga munthu kukhala wopenya kapena wosaona? Kodi si Ine Yehova? 12 Tsopano pita, Ine ndidzakuthandiza kuyankhula ndipo ndidzakulangiza zoti ukanene.”
13 Koma Mose anati, “Chonde Ambuye, pepani, tumani wina kuti akachite zimenezi.”
14 Kenaka Yehova anamupsera mtima Mose ndipo anati, “Kodi suli ndi mʼbale wako Aaroni wa fuko la Levi? Ine ndikudziwa kuti iye amayankhula bwino. Iye wanyamuka kale kudzakumana nawe ndipo adzasangalala akadzakuona. 15 Iwe udzayankhula naye ndi kumuwuza mawu oti akanene. Ine ndidzakuthandizani kuyankhula nonse awirinu ndi kukulangizani zoti mukachite. 16 Iye akayankhula kwa anthu mʼmalo mwako. Iye adzakhala wokuyankhulira ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu kwa iye. 17 Koma utenge ndodo imene ili mʼdzanja lakoyo kuti ukachite nayo zizindikiro zozizwitsa.”
Mose Abwerera ku Igupto
18 Tsono Mose anabwerera kwa Yetero, mpongozi wake ndipo anati kwa Iye, “Chonde ndiloleni kuti ndibwerere ku Igupto kwa anthu anga kuti ndikaone ngati ali moyo.”
Yeteri anati, “Pitani mu mtendere.”
19 Nthawiyi Yehova anali atamuwuza kale Mose ku Midiyani kuti, “Bwerera ku Igupto, pakuti anthu onse amene amafuna kukupha aja anamwalira.” 20 Kotero Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, ndipo anawakweza pa bulu nayamba ulendo wobwerera ku Igupto. Ndipo anatenga ndodo ya Mulungu ija mʼdzanja lake.
21 Yehova anati kwa Mose, “Ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao zodabwitsa zonse zimene ndayika mphamvu mwa iwe kuti ukachite. Koma Ine ndidzawumitsa mtima wake kotero kuti sadzalola anthuwo kuti apite. 22 Ndipo iwe ukati kwa Farao, ‘Yehova akuti, Israeli ali ngati mwana wanga wachisamba.’ 23 Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ”
24 Pambuyo pake Mose ali mʼnjira, pamalo wogona, Yehova anakumana naye, ndipo anafuna kumupha. 25 Koma Zipora anatenga mwala wakuthwa nachita mdulidwe mwana wake ndipo khungulo analikhudzitsa pa mapazi a Mose. Iye anati “Zoonadi, kwa ine ndiwe mkwati wamagazi.” 26 Choncho Yehova anamuleka Mose wosamupha. Pa nthawiyo, Zipora anati, “Mkwati wa magazi,” ponena za mdulidwe.
27 Yehova anati kwa Aaroni, “Pita ku chipululu ukakumane ndi Mose.” Iye anapitadi nakakumana ndi Mose pa phiri la Mulungu namupsompsona. 28 Kenaka Mose anamufotokozera Aaroni chilichonse chimene Yehova anamutuma kuti akanene. Anamufotokozera za zizindikiro zozizwitsa zimene anamulamulira kuti akazichite.
29 Mose ndi Aaroni anapita kukasonkhanitsa pamodzi akuluakulu onse a Aisraeli. 30 Ndipo Aaroni anawafotokozera zonse zimene Yehova ananena kwa Mose. Anachita zizindikirozo pamaso pa anthu onse, 31 ndipo anakhulupirira. Iwo atamva kuti Yehova anadzawayendera ndi kuti waona mmene akuzunzikira, anaweramitsa mitu pansi napembedza.
Chikhulupiriro cha Kenturiyo
7 Yesu atamaliza kunena zonsezi pamaso pa anthu amene ankamvetsera, analowa mu Kaperenawo. 2 Kumeneko wantchito wa Kenturiyo, amene amamukhulupirira kwambiri, anadwala ndipo anali pafupi kufa. 3 Kenturiyo anamva za Yesu ndipo anatumiza ena a akulu Ayuda kwa Iye kuti abwere adzachiritse wantchito wakeyo. 4 Iwo atafika kwa Yesu, anamudandaulira kwambiri, nati, “Munthuyu ayenera kuthandizidwa 5 chifukwa amakonda mtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge wathu.” 6 Pamenepo Yesu anapita nawo.
Iye sanali patali ndi nyumba pamene Kenturiyo anatumiza anzake kuti akamuwuze kuti, “Ambuye, musadzivutitse, pakuti ndine wosayenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga. 7 Nʼchifukwa chake sindinadziyenereze ndi pangʼono pomwe kuti ndibwere kwa inu. Koma nenani mawu, ndipo wantchito wanga adzachira. 8 Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita.”
9 Yesu atamva izi, anadabwa naye, ndipo anatembenukira gulu la anthu limene limamutsatira nati, “Ndikukuwuzani kuti, sindinapeze chikhulupiriro chachikulu ngati ichi mu Israeli.” 10 Kenaka anthu amene anatumidwawo anabwerera ku nyumba ndipo anakamupeza wantchitoyo atachira.
Yesu Aukitsa Mwana wa Mayi Wamasiye
11 Zitangotha izi, Yesu anapita ku mudzi wa Naini ndipo ophunzira ake ndi gulu lalikulu la anthu linapita naye pamodzi. 12 Akufika pa chipata cha mudziwo, anakumana ndi anthu amene ankatuluka ndi munthu wakufa amene anali mwana yekhayo wa mkazi wamasiye. Gulu lalikulu la anthu a mʼmudziwo linali naye. 13 Ambuye atamuona mayiyo, mtima wawo unagwidwa naye chifundo ndipo anati, “Usalire.”
14 Kenaka anapita nakakhudza chithatha cha maliro ndipo amene anachinyamulawo anayima. Iye anati, “Mnyamata, ndikukuwuza kuti, dzuka!” 15 Wakufayo anakhala tsonga ndi kuyamba kuyankhula, ndipo Yesu anamupereka mnyamatayo kwa amayi ake.
16 Onse anachita mantha kwambiri nalemekeza Mulungu. Iwo anati, “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu. Mulungu wabwera kudzathandiza anthu ake.” 17 Mbiriyi inafalikira ku Yudeya konse ndi ku madera ozungulira.
Yesu ndi Yohane Mʼbatizi
18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuwuza Yohaneyo zinthu zonsezi. Atayitana awiri a ophunzirawo, 19 anawatumiza kwa Ambuye kukafunsa kuti, “Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?”
20 Anthuwo atafika kwa Yesu anati, “Yohane Mʼbatizi watituma kwa Inu kuti tidzafunse kuti, ‘Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?’ ”
21 Pa nthawi yomweyo, Yesu anachiritsa ambiri amene ankavutika, odwala ndi amene anali mizimu yoyipa, ndiponso anapenyetsa anthu osaona. 22 Ndipo Iye anawayankha otumidwawo kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwaona ndi kumva: Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. 23 Odala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”
24 Anthu otumidwa ndi Yohane aja atachoka, Yesu anayamba kuyankhula ndi gulu la anthu za Yohaneyo kuti, “Kodi munkapita ku chipululu kukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo? 25 Ngati si choncho, munkapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zabwino? Ayi, ovala zovala zodula ndi okhala moyo wapamwamba ali mʼnyumba zaufumu. 26 Koma inu munkapita kukaona chiyani? Mneneri? Inde, Ine ndikukuwuzani, woposa mneneri. 27 Uyu ndi amene malemba akunena za Iye kuti,
“ ‘Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,
amene adzakonza njira yanu.’
28 Ine ndikukuwuzani kuti pakati pa obadwa kuchokera mwa mkazi palibe wina wamkulu kuposa Yohane; komabe amene ali wamngʼono mu ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.”
29 Anthu onse, ngakhale amisonkho, atamva mawu a Yesu, anavomereza kuti njira ya Mulungu ndi yolondola, chifukwa anabatizidwa ndi Yohane. 30 Koma Afarisi ndi akatswiri amalamulo anakana cholinga cha Mulungu kwa iwo okha, chifukwa sanabatizidwe ndi Yohane.
31 “Kodi ndingawafanizire chiyani anthu a mʼbado uno? Ali ngati chiyani? 32 Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti,
“ ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro,
koma inu simunavine.
Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro,
koma inu simunalire.’
33 Pakuti Yohane Mʼbatizi sanabwere kudzadya buledi kapena kumwa vinyo, koma inu mumati, ‘Ali ndi chiwanda.’ 34 Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’ 35 Ndipo nzeru zimaoneka zolondola mwa ana ake onse.”
Yesu Adzozedwa ndi Mayi Wochimwa
36 Tsopano mmodzi mwa Afarisi anayitana Yesu kuti akadye naye ku nyumba kwake ndipo anapita nakakhala pa tebulo. 37 Mayi amene amakhala moyo wauchimo mu mzindawo atadziwa kuti Yesu akudya ku nyumba ya Mfarisiyo, anabweretsa botolo la mafuta onunkhira a alabasta. 38 Iye anayimirira kumbuyo kwa Yesu pa mapazi ake akulira, nayamba kumadontheza misozi pa mapazi ake. Ndipo iye anapukuta mapaziwo ndi tsitsi lake, nawapsompsona ndi kuwathira mafuta onunkhirawo.
39 Mfarisiyo anamuyitanayo ataona izi, anati mu mtima mwake, “Ngati munthuyu akanakhala mneneri, akanadziwa kuti akumukhudzayo ndi mayi otani, kuti ndi wochimwa.”
40 Yesu anamuyankha iye kuti, “Simoni, ndili ndi kanthu koti ndikuwuze.”
Iye anati, “Ndiwuzeni Aphunzitsi.”
41 “Anthu awiri anakongola ndalama kwa munthu wina wokongoletsa ndalama: mmodzi ndalama zokwana 500 ndi winayo ndalama makumi asanu. 42 Panalibe mmodzi mwa iwo anali ndi ndalama zobwezera, ndipo iye anawakhululukira ngongole zawo. Tsopano ndi ndani mwa awiriwa adzamukonde koposa?”
43 Simoni anayankha kuti, “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira ngongole yayikulu.”
Yesu anati, “Wayankha molondola.”
44 Kenaka anatembenukira kwa mayiyo nati kwa Simoni, “Ukumuona mayiyu? Ine ndabwera mʼnyumba yako. Iwe sunandipatse madzi otsukira mapazi anga, koma iyeyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake. 45 Iwe sunandipsompsone, koma mayiyu, kuyambira pamene Ine ndalowa, sanaleke kupsompsona mapazi anga. 46 Iwe sunadzoze mutu wanga mafuta, koma iye wadzoza mapazi anga mafuta onunkhira. 47 Tsono, ndikukuwuza iwe, machimo ake amene ndi ambiri akhululukidwa, monga chaonetsera chikondi chake chachikulu. Koma iye amene wakhululukidwa zochepa amakonda pangʼono.”
48 Kenaka anati kwa mayiyo, “Machimo ako akhululukidwa.”
49 Alendo enawo anayamba kumanena mʼmitima mwawo kuti, “Uyu ndi ndani amene akhululukiranso machimo?”
50 Yesu anati kwa mayiyo, “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa. Pita mu mtendere.”
Mawu a Yobu
21 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Mvetserani bwino mawu anga;
ichi chikhale chitonthozo changa chochokera kwa inu.
3 Ndiloleni ndiyankhule
ndipo ndikatha kuyankhula munditonzetonze.
4 “Kodi ine ndikudandaulira munthu?
Tsono ndilekerenji kupsa mtima?
5 Ndipenyeni ndipo mudabwe;
mugwire dzanja pakamwa.
6 Ndikamaganiza zimenezi ndimachita mantha kwambiri;
thupi langa limanjenjemera.
7 Chifukwa chiyani anthu oyipa amakhalabe ndi moyo,
amakalamba ndi kusanduka amphamvu?
8 Amaona ana awo akukhazikika pamodzi nawo,
zidzukulu zawo zikukula bwino iwo akuona.
9 Mabanja awo amakhala pa mtendere ndipo sakhala ndi mantha;
mkwapulo wa Mulungu suwakhudza nʼkomwe.
10 Ngʼombe zawo zazimuna sizilephera kubereketsa;
ngʼombe zawo zazikazi sizipoloza.
11 Amatulutsa ana awo ngati gulu la nkhosa;
makanda awo amavinavina pabwalo.
12 Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze;
amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro.
13 Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero
ndipo amatsikira ku manda mwamtendere.
14 Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’
Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu.
15 Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire?
Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo?
16 Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo,
koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa.
17 “Koma nʼkangati kamene nyale ya anthu oyipa imazimitsidwa?
Nʼkangati kamene tsoka limawagwera?
Nʼkangati kamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?
18 Nʼkangati kamene iwo amakhala ngati phesi lowuluka ndi mphepo,
ngati mungu wowuluzika ndi kamvuluvulu?
19 Paja amati, ‘Mulungu amalanga ana chifukwa cha machimo abambo awo.’
Koma Mulungu amabwezera chilango munthuyo, kuti adziwe kuti Mulungu amalangadi.
20 Mulole kuti adzionere yekha chilango chake,
kuti alawe ukali wa Wamphamvuzonse.
21 Nanga kodi amalabadira chiyani zabanja lake limene walisiya mʼmbuyo,
pamene chiwerengero cha masiku ake chatha?
22 “Kodi alipo wina amene angaphunzitse Mulungu nzeru,
poti Iye amaweruza ngakhale anthu apamwamba?
23 Munthu wina amamwalira ali ndi mphamvu zonse,
ali pa mtendere ndi pa mpumulo,
24 thupi lake lili lonenepa,
mafupa ake ali odzaza ndi mafuta.
25 Munthu wina amamwalira ali wowawidwa mtima,
wosalawapo chinthu chabwino chilichonse.
26 Olemera ndi osauka omwe amamwalira ndi kuyikidwa mʼmanda
ndipo onse amatuluka mphutsi.
27 “Ndikudziwa bwino zimene mukuganiza,
ziwembu zanu zomwe mukuti mundichitire.
28 Inu mukuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti,
matenti amene munkakhala anthu oyipa aja ali kuti?’
29 Kodi munawafunsapo anthu amene ali pa ulendo?
Kodi munaganizirapo zimene iwo amanena?
30 Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka,
kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu?
31 Kodi ndani amadzudzula munthu wochimwayo?
Ndani amamubwezera zoyipa zimene anachita?
32 Iye amanyamulidwa kupita ku manda
ndipo anthu amachezera pa manda ake.
33 Dothi la ku chigwa limamukomera;
anthu onse amatsatira mtembo wake,
ndipo anthu osawerengeka amakhala patsogolo pa chitanda chakecho.
34 “Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewo
palibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!”
Nyama ya Nsembe za Mafano
8 Tsopano za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano: Ife tidziwa kuti tonse tili ndi chidziwitso. Komatu chidziwitso chokha chimadzitukumula, koma chikondi ndicho chimapindulitsa. 2 Munthu amene amaganiza kuti amadziwa kanthu, ndiye kuti sakudziwa monga mmene amayenera kudziwira. 3 Koma munthu amene amakonda Mulungu amadziwika ndi Mulunguyo.
4 Choncho kunena za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano; ife tikudziwa kuti mafano si kanthu nʼpangʼonongʼono pomwe pa dziko lapansi, ndiponso kuti palibe Mulungu wina koma mmodzi yekha. 5 Popeza kuti ngakhale pali yotchedwa milungu, kaya ndi kumwamba kapena pa dziko lapansi (poti ilipodi milungu yambirimbiri ndi ambuye ambirimbiri), 6 koma kwa ife pali Mulungu mmodzi yekha, Atate, zinthu zonse zinachokera mwa Iye ndipo ndife ake. Komanso pali Ambuye mmodzi Yesu Khristu kumene zinthu zonse zinachokera ndipo mwa Iye ife tili ndi moyo.
7 Koma saliyense amadziwa zimenezi. Alipo ena ozolowera mafano kwambiri mwakuti akadya chakudya chotere amaganiza kuti chakudyacho chinaperekedwa nsembe kwa mafano. Ndiye poti chikumbumtima chawo nʼchofowoka chimadetsedwadi. 8 Koma chakudya sichitisendeza kufupi ndi Mulungu. Tikapanda kudya si vuto, tikadya sitisinthikanso.
9 Komabe samalani kuti ufulu wanu ochita zinthu usafike pokhumudwitsa ofowoka. 10 Pakuti ngati aliyense wachikumbumtima chofowoka akakuonani achidziwitsonu mukudya mʼnyumba yopembedzera mafano, kodi iyeyo sichidzamulimbitsa mtima kuti azidya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano? 11 Kotero kuti chifukwa cha chidziwitso chanu mʼbale wofowokayu amene chifukwa cha iye, Khristu anafa, wawonongeka chifukwa cha chidziwitso chanu. 12 Mukamachimwira abale anu motere ndikuwawonongera chikumbumtima chawo chofowokacho, mukuchimwira Khristu. 13 Nʼchifukwa chake ngati zimene ine ndimadya zichititsa mʼbale wanga kugwa mu tchimo, sindidzadyanso chakudyacho kuti mʼbaleyo ndisamuchimwitse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.