Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 49

Yakobo Adalitsa Ana ake Aamuna

49 Pambuyo pake Yakobo anayitanitsa ana ake aamuna nati: Sonkhanani pamodzi kuti ndikuwuzeni zimene zidzakuchitikireni mʼmasiku a mʼtsogolo.

“Bwerani ndipo imvani mawu anga, inu ana a Yakobo;
    mverani abambo anu Israeli.

“Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa;
    mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga,
    wopambana pa ulemerero ndi mphamvu.
Wokokoma ngati madzi a chigumula, koma sudzakhalanso wopambana,
    iwe unagona pa bedi la abambo ako,
    ndithu unayipitsa bedi la mdzakazi wake.

“Simeoni ndi Levi ndi pachibale pawo,
    anachitira nkhanza anthu amene anachita nawo pangano.
Iwe moyo wanga, usakhale nawo pa misonkhano yawo ya mseri,
    kapena kugwirizana nawo mʼmabwalo awo,
pakuti anapha anthu mu mkwiyo wawo
    ndipo anapundula ngʼombe zamphongo monga kunawakomera.
Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi
    ndi ukali wawo wankhanza choterewu!
Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo
    ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.

“Yuda, ndiwe amene abale ako adzatamanda;
    dzanja lako lidzagwira pa khosi pa adani ako;
    abale ako adzakugwadira iwe.
Yuda ali ngati mwana wa mkango;
    umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga.
Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi,
    ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa?
10 Ndodo yaufumu sidzachoka mwa Yuda,
    udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse,
mpaka mwini wake weniweni atabwera
    ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.
11 Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa,
    ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino.
Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo;
    ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi.
12 Maso ake adzakhala akuda chifukwa cha vinyo,
    mano ake woyera chifukwa cha mkaka.

13 “Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja;
    adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi;
    malire ake adzafika ku Sidoni.

14 “Isakara ali ngati bulu wamphamvu
    wogona pansi pakati pa makola.
15 Ataona ubwino wake wa pamalo pake popumira
    ndi kukongola kwa dziko lake,
iye anaweramutsa msana kuti anyamule katundu wake
    ndipo anasanduka wogwira ntchito ya ukapolo.

16 “Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake
    monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli.
17 Dani adzakhala ngati njoka ya mʼmphepete mwa msewu,
    songo yokhala mʼnjira
imene imaluma chidendene cha kavalo
    kuti wokwerapoyo agwe chagada.

18 “Ndikuyembekeza chipulumutso chanu Yehova.

19 “Gadi adzachitidwa chiwembu ndi gulu la amaliwongo,
    koma iye adzawathamangitsa.

20 “Dziko la Aseri lidzabereka chakudya chokoma,
    ndipo iye adzapereka chakudya kwa mafumu.

21 “Nafutali ali ngati mbawala yayikazi
    yokhala ndi ana okongola kwambiri.

22 “Yosefe ali ngati mtengo wobereka zipatso,
    mtengo wobereka zipatso pafupi ndi kasupe,
    nthambi zake zimayanga pa chipupa cha mwala.
23 Alenje a uta anamuchita chiwembu mwankhanza;
    anamuthamangitsa ndi mauta awo.
24 Koma uta wake sunagwedezeke,
    ndi manja ake amphamvu aja analimbika,
chifukwa cha mphamvu za Mulungu Wamphamvu wa Yakobo,
    chifukwa ali Mʼbusa ndi Thanthwe la Israeli.
25 Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza;
    chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa
ndi mvula yochokera kumwamba,
    ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka,
    ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.
26 Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa
    madalitso a mapiri akale
    oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona.
Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe,
    pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake.

27 “Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa;
    umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha,
    ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,”

28 Onse awa ndi mafuko khumi ndi awiri a Israeli, ndipo zimenezi ndi zomwe abambo awo ananena pamene anawadalitsa, kuwapatsa aliyense madalitso ake womuyenera iye.

Kumwalira kwa Yakobo

29 Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti. 30 Ili ndi phanga la mʼmunda wa Makipela, pafupi ndi Mamre mʼdziko la Kanaani. Abrahamu anagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 31 Kumeneko kunayikidwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, Isake ndi mkazi wake Rebeka ndipo ndinayikakonso Leya. 32 Munda ndi manda amene ali mʼmenemo zinagulidwa kwa Ahiti.”

33 Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana ake, anabwezera miyendo yake pa bedi, namwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.

Luka 2

Kubadwa kwa Yesu

Mʼmasiku amenewo Kaisara Augusto anapereka lamulo kuti kalembera achitike mʼdziko lonse la Aroma. (Uyu ndi kalembera woyamba amene anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya). Ndipo aliyense anapita ku mzinda wa kwawo kukalembetsa.

Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide. Iye anapita kumeneko kukalembetsa pamodzi ndi Mariya, amene anapalana naye ubwenzi kuti akwatirane ndipo anali woyembekezera. Ali kumeneko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe, ndipo anabereka mwana wake woyamba, wamwamuna. Iye anamukulunga mʼnsalu ndi kumuyika modyera ngʼombe, chifukwa kunalibe malo mʼnyumba ya alendo.

Abusa ndi Angelo

Ndipo kunali abusa amene amakhala ku dera lomwelo, kuyangʼanira ziweto zawo usiku. Mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iwo ndipo ulemerero wa Ambuye unawala mowazungulira. Iwo anachita mantha. 10 Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse. 11 Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye. 12 Ichi chidzakhala chizindikiro kwa inu: mukapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera ngʼombe.”

13 Mwadzidzidzi gulu lalikulu la angelo linaonekera pamodzi ndi mngeloyo, kuyamika Mulungu ndi kumati,

14 “Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba,
    ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo.”

15 Angelowo atabwerera kumwamba, abusawo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni ku Betelehemu tikaone zinthu zomwe zachitika, zimene Ambuye atiwuza ife.”

16 Ndipo iwo anafulumira nyamuka nakapeza Mariya ndi Yosefe ndi mwana wakhanda, amene anagona modyera ngʼombe. 17 Pamene anamuona Iye, iwo anafotokoza zomwe anawuzidwa za mwanayo, 18 ndipo onse amene anamva zimene abusawa ananena anadabwa. 19 Koma Mariya anasunga zonsezi mu mtima mwake ndi kumazilingalira. 20 Abusa anabwerera, akulemekeza ndi kuyamika Mulungu chifukwa cha zonse anazimva ndi kuziona, zomwe zinali monga anawuzidwira ndi angelo aja.

Yesu Aperekedwa mʼNyumba ya Mulungu

21 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, tsiku loti amuchite mdulidwe anamutcha Yesu, dzina limene mngelo anamupatsa asanabadwe.

22 Nthawi yoyeretsedwa kwawo itatha, monga mwa lamulo la Mose, Yosefe ndi Mariya anapita naye ku Yerusalemu kukamupereka kwa Ambuye. 23 (Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”), 24 ndi kupereka nsembe posunga zimene zinanenedwa mulamulo la Ambuye: “Njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri.”

25 Ndipo taonani, mu Yerusalemu munali munthu wotchedwa Simeoni, amene anali wolungama ndi wodzipereka. Iye ankadikira chitonthozo cha Israeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. 26 Mzimu Woyera anamuwululira kuti sadzafa asanaone Khristu wa Ambuye. 27 Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo, 28 Simeoni anamunyamula mʼmanja mwake nayamika Mulungu, nati:

29 “Ambuye waulamuliro, monga munalonjeza,
    tsopano lolani kuti mtumiki wanu apite mu mtendere.
30 Pakuti maso anga aona chipulumutso chanu,
31     chimene Inu munakonza pamaso pa anthu onse,
32 kuwala kowunikira anthu a mitundu ina
    ndi kwa ulemerero kwa anthu anu Aisraeli.”

33 Abambo ndi amayi a Mwanayo anadabwa chifukwa cha zimene zinanenedwa za Iye. 34 Kenaka Simeoni anawadalitsa ndipo anati kwa Mariya amayi ake: “Mwana uyu wakonzedwa kukhala kugwa ndi kudzuka kwa ambiri mu Israeli, ndi kukhala chizindikiro chimene adzayankhula motsutsana nacho, 35 kotero kuti malingaliro a mitima ya ambiri adzawululidwa. Ndipo lupanga lidzabaya moyo wakonso.”

36 Panalinso mneneri wamkazi, dzina lake Ana, mwana wa Fanuelo, wa fuko la Aseri. Anali wokalamba kwambiri; anakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri atakwatiwa, 37 ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera. 38 Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.

39 Yosefe ndi Mariya atachita zonse zimene zinkafunikira ndi lamulo la Ambuye, anabwerera ku Galileya ku mudzi wa Nazareti. 40 Ndipo Mwanayo anakula nakhala wamphamvu; Iye anadzazidwa ndi nzeru, ndipo chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Yesu mʼNyumba ya Mulungu

41 Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska. 42 Iye ali ndi zaka khumi ndi ziwiri, anapita ku phwando, monga mwa mwambo. 43 Phwando litatha, pamene makolo ake ankabwerera kwawo, mnyamata Yesu anatsalira ku Yerusalemu, koma iwo sanadziwe zimenezi. 44 Poganiza kuti anali nawo mʼgulu lawo, anayenda tsiku limodzi. Kenaka anayamba kumufunafuna pakati pa abale awo ndi anzawo. 45 Atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu kukamufuna. 46 Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso. 47 Aliyense amene anamumva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake. 48 Makolo ake atamuona, anadabwa. Amayi ake anati kwa Iye, “Mwanawe, watichitira zimenezi chifukwa chiyani? Abambo ako ndi ine takhala tili ndi nkhawa kukufunafuna Iwe.”

49 Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumandifunafuna? Kodi simukudziwa kuti ndikuyenera kukhala mʼnyumba ya Atate anga?” 50 Koma iwo sanazindikire chomwe Iye amatanthauza.

51 Kenaka anapita nawo ku Nazareti ndipo anawamvera iwo. Koma amayi ake anasunga zinthu zonsezi mu mtima mwawo.

52 Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.

Yobu 15

Mawu a Elifazi

15 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,

“Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu achabechabe otere,
    kapena angakhutitse mimba yake ndi mphepo yotentha yochokera kummawa?
Kodi angathe kutsutsa ndi mawu opanda pake,
    kapena kuyankhula mawu opanda phindu?
Koma iwe ukuchepetsa zoopa Mulungu
    ndipo ukutchinga zodzikhuthulira kwa Mulungu.
Tchimo lako ndiye likuyankhulitsa pakamwa pakopo;
    ndipo watengera mayankhulidwe a atambwali.
Pakamwa pakopo ndiye pakukutsutsa osati pakamwa panga;
    milomo yakoyo ikukutsutsa.

“Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?
    Kodi unalengedwa mapiri asanalengedwe?
Kodi unali mʼgulu la alangizi a Mulungu?
    Kodi ukudziyesa wanzeru ndiwe wekha?
Kodi iwe umadziwa chiyani chimene ife sitichidziwa?
    Kodi iwe uli ndi chidziwitso chanji chimene ife tilibe?
10 Anthu a imvi ndi okalamba ali mbali yathu,
    anthu amvulazakale kupambana abambo ako.
11 Kodi mawu otonthoza mtima ochokera kwa Mulungu sakukukwanira,
    mawu oyankhula mofatsawa kwa iwe?
12 Chifukwa chiyani ukupsa mtima,
    ndipo chifukwa chiyani ukutuzula maso ako,
13 moti ukupsera mtima Mulungu
    ndi kuyankhula mawu otero pakamwa pako?

14 “Kodi munthu nʼchiyani kuti nʼkukhala woyera mtima
    kapena wobadwa mwa amayi nʼchiyani kuti nʼkukhala wolungama mtima?
15 Ngati Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake,
    ngakhale zakumwamba sizoyera pamaso pake,
16 nanga kuli bwanji munthu amene ndi wonyansa ndi wa njira zokhotakhota,
    amene kuchita zoyipa kuli ngati kumwa madzi.

17 “Mvetsera kwa ine ndipo ndidzakufotokozera;
    ndilole ndikuwuze zimene ndaziona,
18 zimene anandiphunzitsa anthu anzeru,
    sanandibisire kalikonse kamene anamva kuchokera kwa makolo awo.
19 (Ndi kwa iwowa kumene dziko lino linaperekedwa
    pamene panalibe mlendo wokhala pakati pawo).
20 Munthu woyipa amavutika ndi masautso masiku onse a moyo wake,
    munthu wankhanza adzavutika zaka zake zonse.
21 Amamva mawu owopsa mʼmakutu mwake,
    pamene zonse zikuoneka ngati zili bwino, anthu achifwamba amamuthira nkhondo.
22 Iye sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa;
    iyeyo ndi woyenera kuphedwa.
23 Amangoyendayenda pali ponse kunka nafuna chakudya;
    amadziwa kuti tsiku la mdima lili pafupi.
24 Masautso ndi nthumanzi zimamuchititsa mantha kwambiri;
    zimamugonjetsa iye monga imachitira mfumu yokonzekera kukathira nkhondo,
25 chifukwa iye amatambasula dzanja lake kuyambana ndi Mulungu
    ndipo amadzitama yekha polimbana ndi Wamphamvuzonse.
26 Amapita mwa mwano kukalimbana naye
    atanyamula chishango chochindikala ndi cholimba.

27 “Ngakhale nkhope yake ndi yonenepa
    ndipo mʼchiwuno mwake muli mnofu wambiri,
28 munthuyo adzakhala mʼmizinda yowonongeka
    ndi mʼnyumba zosayenera kukhalamo anthu,
    nyumba zimene zikugwa ndi kuwonongeka.
29 Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa,
    ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi.
30 Iyeyo sadzapulumuka mu mdimamo;
    lawi lamoto lidzawumitsa nthambi zake,
    ndipo mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu udzamusesa.
31 Asadzinyenge yekha podalira zinthu zachabechabe,
    pakuti pa mapeto pake sadzaphulapo kanthu.
32 Iye adzalandira malipiro ake nthawi yake isanakwane,
    ndipo nthambi zake sizidzaphukanso.
33 Iye adzakhala ngati mtengo wamphesa wopululidwa zipatso zake zisanapse,
    adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluwa ake.
34 Pakuti anthu osapembedza Mulungu adzakhala osabala
    ndipo moto udzapsereza nyumba za onse okonda ziphuphu.
35 Iwo amalingalira zaupandu ndipo amachita zoyipa;
    mtima wawo umakonzekera zachinyengo.”

1 Akorinto 3

Mpingo ndi Atsogoleri Ake

Ndipo abale sindikanakuyankhulani ngati auzimu koma adziko lapansi, makanda chabe mwa Khristu. Ndinakupatsani mkaka osati chakudya cholimba pakuti munali musanakonzeke kuchilandira. Zoonadi, simunakonzekebe. Mukanali adziko lapansi. Pakuti pakati panu pali kaduka ndi kukangana, kodi si inu a dziko lapansi? Kodi simukuchita ngati anthu wamba? Pamene wina anena kuti, “Ine ndimatsatira Paulo,” ndipo wina akuti, “Ine ndimatsatira Apolo,” Kodi si inu akunja?

Ndiponso kodi Apolo ndi ndani? Nanga Paulo ndi ndani? Otumikira chabe, omwe kudzera mwa iwo inu munakhulupirira monga Ambuye anawagawira aliyense ntchito yake. Ine ndinadzala mbewu, Apolo anayithirira, koma Mulungu ndiye anayikulitsa. Choncho kuphatikiza iye wodzala ndi iye wothirira, onse sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amakulitsa zinthu. Munthu wodzala ndi munthu wothirira ali ndi cholinga chimodzi, ndipo aliyense adzapatsidwa mphotho molingana ndi ntchito yake. Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; inu ndinu munda wa Mulungu, Nyumba ya Mulungu.

10 Mwachisomo chimene Mulungu wandipatsa, ine ndinayika maziko monga mmisiri waluntha, ndipo ena akumangapo. Koma aliyense ayenera kuchenjera mmene akumangira. 11 Pakuti wina sangayikenso maziko ena oposera amene anakhazikitsidwa kale, amene ndi Yesu Khristu. 12 Ngati munthu aliyense amanga pa maziko awa pogwiritsa ntchito golide, siliva, miyala yamtengowapatali, milimo yamitengo, tsekera kapena udzu, 13 ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense. 14 Ngati zimene zamangidwazo sizidzagwa, adzalandira mphotho yake. 15 Ndipo ngati zidzanyeke ndi moto, sadzalandira mphotho koma iye mwini adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wapulumuka mʼmoto.

16 Kodi inu simukudziwa kuti ndinu Nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? 17 Ngati wina aliyense awononga Nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo; popeza Nyumba ya Mulungu ndi yopatulika ndipo Nyumbayo ndi inu amene.

18 Choncho musadzinyenge. Ngati wina wa inu akuganiza kuti ndi wanzeru pa mulingo wa mʼbado uno, ayenera kukhala “wopusa” kuti athe kukhala wanzeru. 19 Pakuti nzeru ya dziko lapansi ndi yopusa pamaso pa Mulungu. Monga kwalembedwera kuti, “Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,” 20 ndiponso, “Ambuye amadziwa kuti maganizo a wanzeru ndi opandapake.” 21 Choncho, wina asanyadire anthu chabe! Zonse ndi zanu, 22 kaya Paulo kapena Apolo kapena Kefa kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena tsopano, kapena mʼtsogolo, zonse ndi zanu, 23 ndipo inu ndinu a Khristu, ndipo Khristu ndi wa Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.