M’Cheyne Bible Reading Plan
Yakobo Apita ku Igupto
46 Israeli anasonkhanitsa zonse anali nazo napita ku Beeriseba kukapereka nsembe kwa Mulungu wa abambo ake Isake.
2 Ndipo Mulungu anayankhula ndi Israeli mʼmasomphenya usiku nati, “Yakobo! Yakobo!”
Iye anayankha, “Ee, Ambuye.”
3 Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu. Mulungu wa abambo ako. Usachite mantha kupita ku Igupto, pakuti ndidzachulukitsa zidzukulu zako kumeneko moti zidzakhala mtundu waukulu. 4 Ine ndidzapita ku Igupto pamodzi ndi iwe ndipo mosakayika konse zidzukulu zako ndidzazibweretsa konkuno. Yosefe adzakhalapo pa nthawi yako yomwalira.”
5 Yakobo anachoka ku Beeriseba, ndipo ana ake anakweza abambo awo, ana awo, pamodzi ndi akazi awo pa ngolo zimene Farao anatumiza kuti adzakwerepo. 6 Iwo anatenganso ziweto zawo ndi katundu wawo amene anali naye ku Kanaani, ndipo Yakobo pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake anapita ku Igupto. 7 Ndiye kuti popita ku Igupto Yakobo anatenga ana aamuna, zidzukulu zazimuna, ana aakazi ndi zidzukulu zazikazi.
8 Nawa ana a Israeli (ndiye kuti Yakobo ndi ana ake) amene anapita ku Igupto:
Rubeni mwana woyamba wa Yakobo.
9 Ana aamuna a Rubeni ndi awa:
Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi.
10 Ana aamuna a Simeoni ndi awa:
Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo amene mayi wake anali wa ku Kanaani.
11 Ana aamuna a Levi ndi awa:
Geresoni, Kohati ndi Merari.
12 Ana aamuna a Yuda ndi awa:
Eri, Onani, Sela, Perezi ndi Zera. Koma Eri ndi Onani anamwalira mʼdziko la Kanaani.
Ana a Perezi anali
Hezironi ndi Hamuli.
13 Ana aamuna a Isakara ndi awa:
Tola, Puwa, Yobi ndi Simironi.
14 Ana aamuna a Zebuloni ndi awa:
Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.
15 Amenewa ndi ana aamuna a Leya amene anamubalira Yakobo ku Padanaramu. Panali mwana wamkazi dzina lake Dina. Ana onse analipo 33.
16 Ana aamuna a Gadi ndi awa:
Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.
17 Ana aamuna a Aseri ndi awa:
Imuna, Isiva, Isivi, Beriya
ndi Sera mlongo wawo.
Ana aamuna a Beriya ndi awa:
Heberi ndi Malikieli.
18 Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Zilipa amene Labani anapereka kwa mwana wake, Leya. Onse pamodzi analipo 16.
19 Ana aamuna a Rakele mkazi wa Yakobo anali:
Yosefe ndi Benjamini. 20 Ku Igupto, Asenati mwana wa Potifara wansembe wa Oni, anamuberekera Yosefe ana awa: Manase ndi Efereimu.
21 Ana aamuna a Benjamini ndi awa:
Bela, Bekeri, Asibeli, Gera, Naamani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu ndi Aridi.
22 Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa mkazi wake Rakele. Onse analipo khumi ndi anayi.
23 Mwana wa mwamuna wa Dani anali:
Husimu.
24 Ana aamuna a Nafutali ndi awa:
Yahazeeli, Guni, Yezeri ndi Silemu.
25 Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Biliha amene Labani anapereka kwa mwana wake Rakele. Onse pamodzi analipo asanu ndi awiri.
26 Onse amene anapita ndi Yakobo (iwo amene anali akeake, osawerengera akazi a ana ake), analipo 66. 27 Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70.
28 Tsopano Yakobo anatumiza Yuda kwa Yosefe kukamupempha kuti akakumane naye ku Goseni. Iwo atafika ku chigawo cha Goseni, 29 Yosefe anakonza galeta nakwerapo ndi kupita ku Goseni kukakumana ndi abambo ake, Israeli. Yosefe atangofika pamaso pa abambo ake, anawakumbatira nalira kwa nthawi yayitali.
30 Israeli anati kwa Yosefe, “Tsopano ndikhoza kumwalira poti ndaona nkhope yako kuti ukanali ndi moyo.”
31 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake pamodzi ndi a pa banja la abambo ake, “Ndipita kwa Farao ndipo ndikamuwuza kuti, ‘Abale anga pamodzi ndi onse a mʼnyumba ya abambo anga amene amakhala mʼdziko la Kanaani abwera kuno kwa ine. 32 Anthuwa ndi abusa; amaweta ziweto zawo ndipo abwera ndi nkhosa ndi ngʼombe zawo, pamodzi ndi antchito awo.’ 33 Tsono Farao akakuyitanani nakufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’ 34 Muyankhe kuti, ‘Ife, bwana ndife oweta ziweto kuyambira ubwana wathu mpaka tsopano. Takhala tikuweta ziweto monga mmene ankachitira makolo athu.’ Mukadzayankha choncho, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko la Goseni chifukwa anthu a ku Igupto amanyansidwa nawo anthu oweta ziweto.”
Kuuka kwa Yesu
16 Litapita tsiku la Sabata, Mariya Magadalena, ndi amayi ake a Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhiritsa ndi cholinga chakuti apite akadzoze thupi la Yesu. 2 Mmamawa, tsiku loyamba la Sabata, dzuwa litangotuluka kumene, anali pa ulendo wopita ku manda 3 ndipo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi akatikugudubuzira mwala pa khomo la manda ndani?”
4 Koma atakweza maso awo, anaona kuti mwala umene unali waukulu kwambiri wagubuduzidwa kale. 5 Atalowa mʼmanda, anaona mnyamata atavala mwinjiro woyera atakhala ku mbali ya kumanja, ndipo iwo anachita mantha.
6 Iye anati, “Musaope. Kodi mukufuna Yesu wa ku Nazareti, amene anapachikidwa? Wauka! Sali muno. Onani malo amene anamugonekapo. 7 Koma pitani, kawuzeni ophunzira ake ndi Petro kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona Iye monga momwe anakuwuzirani.’ ”
8 Akunjenjemera ndi kudabwa, amayiwo anatuluka ndipo anathawa ku mandako. Sananene china chilichonse kwa aliyense, chifukwa anachita mantha.
[Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe vesi 9 mpaka 20.]
Yesu Aonekera kwa Mariya Magadalena
9 Yesu atauka kwa akufa mmawa pa tsiku loyamba la Sabata, anayamba kuonekera kwa Mariya Magadalena, amene anatulutsa mwa iye ziwanda zisanu ndi ziwiri. 10 Iye anapita ndi kukawawuza amene anali ndi Yesu, amene ankakhuza maliro ndi kulira. 11 Atamva kuti Yesu ali moyo ndikuti amuona, iwo sanakhulupirire.
Yesu Aonekera kwa Ophunzira Awiri
12 Zitatha izi Yesu anaonekera mʼmaonekedwe ena kwa awiri a iwo amene anali ku dera la ku mudzi. 13 Iwo anabwerera ndi kudzawawuza enawo; koma iwo sanakhulupirirebe.
Yesu Ayankhula kwa Ophunzira Khumi ndi Mmodzi
14 Pambuyo pake Yesu anaonekera kwa khumi ndi mmodziwo pamene ankadya; anawadzudzula chifukwa chopanda chikhulupiriro ndi kukanitsitsa kwawo kuti akhulupirire amene anamuona Iye atauka.
15 Anati kwa iwo, “Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse. 16 Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa. 17 Tsono zizindikiro izi zidzawatsata amene adzakhulupirira: Mʼdzina langa adzatulutsa ziwanda; adzayankhula malilime atsopano; 18 adzanyamula njoka ndi manja awo; ndipo pamene adzamwa mankhwala akupha, sadzawapweteka nʼpangʼonongʼono pomwe; adzasanjika manja awo pa anthu odwala ndipo odwalawo adzachira.”
Yesu Apita Kumwamba
19 Ambuye Yesu atatha kuyankhulana nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu. 20 Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.
Mawu a Yobu
12 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Ndithudi inuyo ndinu anthu
ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi!
3 Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu;
ineyo sindine munthu wamba kwa inu.
Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi?
4 “Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga,
ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha.
Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa!
5 Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka.
Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.
6 Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere,
ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino,
amene amanyamula milungu yawo mʼmanja.
7 “Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa,
kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza;
8 kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa,
kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere.
9 Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa
kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?
10 Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse,
ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.
11 Kodi khutu sindiye limene limamva mawu
monga mmene lilime limalawira chakudya?
12 Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba?
Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu?
13 “Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu;
uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake.
14 Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso.
Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse.
15 Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma;
akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko.
16 Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana;
munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake.
17 Iye amalanda aphungu nzeru zawo
ndipo amapusitsa oweruza.
18 Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo
ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo.
19 Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo
ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika.
20 Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika
ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu.
21 Iye amanyoza anthu otchuka
ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu.
22 Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima
ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.
23 Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso;
amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso.
24 Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi;
amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.
25 Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira;
Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera.
Mawu Olawirana
16 Ine ndikupereka kwa inu mlongo wathu Febe, mtumiki wa mpingo wa ku Kenkreya. 2 Ine ndikukupemphani kuti mumulandire mwa Ambuye mʼnjira yoyenera oyera mtima ndi kumupatsa thandizo lililonse limene akulifuna kuchokera kwa inu, pakuti iye wakhala thandizo lalikulu kwa anthu ambiri kuphatikiza ine.
3 Perekani moni kwa Prisila ndi Akura, atumiki anzanga mwa Khristu Yesu. 4 Iwo anapereka miyoyo yawo chifukwa cha ine. Osati ine ndekha komanso mipingo yonse ya a mitundu ina ikuyamika.
5 Perekaninso moni kwa mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo.
Perekani moni kwa mʼbale wanga wokondedwa Epeneto, amene ndi woyamba kukhulupirira Khristu mʼchigawo cha Asiya.
6 Perekani moni kwa Mariya, amene wakhala akukugwirirani ntchito kwambiri.
7 Perekani moni kwa Androniko ndi Yuniya abale anga amene anali mʼndende pamodzi ndi ine. Iwo amadziwika ndi atumwi, ndipo iwo anali mwa Khristu ine ndisanakhale.
8 Perekani moni kwa Ampliato, amene ine ndimamukonda mwa Ambuye.
9 Perekani moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu mwa Khristu ndi wokondedwa wanga Staku.
10 Perekani moni kwa Apele, woyesedwa ndi wovomerezeka mwa Khristu.
Perekani moni kwa a mʼbanja la Aristobulo.
11 Perekani moni kwa Herodiona, mʼbale wanga.
Perekani moni kwa a mʼbanja la Narkiso amene ali mwa Ambuye.
12 Perekani moni kwa Trufena ndi Trufosa, amayi aja amene amagwira ntchito ya Ambuye molimbika.
Perekani moni kwa mnzanga wokondedwa Persida, mayi winanso amene wagwira ntchito kwambiri mwa Ambuye.
13 Perekani moni kwa Rufo, wosankhidwa mwa Ambuye, ndi amayi ake, amene akhala amayi anganso.
14 Perekani moni kwa Asunkrito, Felego, Herima, Patroba, Herima ndi abale amene ali nawo pamodzi.
15 Perekani moni kwa Filologo, Yuliya, Neriya ndi mlongo wake, ndi Olumpa ndi oyera mtima onse amene ali nawo pamodzi.
16 Mupatsane moni wina ndi mnzake mwachikondi choona.
Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.
17 Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo. 18 Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa. 19 Aliyense anamva za kumvera kwanu, choncho ndine odzaza ndi chimwemwe chifukwa cha inu. Koma ine ndikufuna kuti inu mukhale anzeru pa zabwino, ndi wopanda cholakwa pa zimene zili zoyipa.
20 Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana msanga pansi pa mapazi anu.
Chisomo cha Ambuye athu Yesu chikhale ndi inu.
21 Timoteyo, mtumiki mnzanga, akupereka moni. Nawonso, Lusio, Yasoni ndi Sosipatro, abale anga akutero.
22 Ine Tertio, amene ndalemba kalatayi, ndi kupereka moni mwa Ambuye.
23 Gayo, amene chifukwa cha chisamaliro chake, ine ndi mpingo wonse kuno tikusangalala, akupereka moni.
Erasto, amene ndi msungichuma wa mzinda wonse ndiponso mʼbale wathu Kwato, akupereka moni.
24 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.
25 Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali, 26 koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye, 27 kwa Mulungu yekhayo wanzeru kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu! Ameni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.