Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 44

Chikho Chasiliva Mʼthumba la Benjamini

44 Pambuyo pake Yosefe analamulira wantchito wa mʼnyumba mwake kuti, “Adzazire chakudya anthuwa mʼmatumba mwawo monga mmene anganyamulire, ndipo uwayikire ndalama zawo pakamwa pa matumba awowo. Tsono uyike chikho changa cha siliva chija, pakamwa pa thumba la wamngʼono kwambiriyu pamodzi ndi ndalama zake za chakudya” Ndipo iye anachita monga Yosefe ananenera.

Mmawa kutacha anthu aja analoledwa kuti apite ndi abulu awo. Atangotuluka mu mzinda muja, koma asanapite patali, Yosefe anati kwa wantchito wake, “Nyamuka atsatire anthu aja msanga. Ndipo ukawapeza, uwafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoyipa ndi zabwino? Mwaberanji chikho chimene mbuye wanga amamweramo ndi kugwiritsa ntchito akafuna kuwombeza? Chimene mwachitachi ndi chinthu choyipa.’ ”

Wantchito uja atawapeza ananena mawu anawuzidwa aja. Koma iwo anati kwa iye, “Kodi mbuye wanga mukuneneranji zimenezi? Sizingatheke ndi pangʼono pomwe kuti antchito anufe nʼkuchita zoterozo ayi! Paja ife pobwera kuchokera ku Kanaani tinatenga ndalama kubwezera zimene tinazipeza mʼmatumba mwathu. Ndiye pali chifukwa chanji kuti tikabe siliva kapena golide mʼnyumba mwa mbuye wanu? Ngati wantchito wanu wina pano atapezeka nacho chikhocho, ameneyo aphedwe ndipo ena tonsefe tidzakhala akapolo anu, mbuye wathu.”

10 Iye anati, “Chabwino, tsono zikhale monga mwaneneramu. Komatu aliyense amene angapezeke nacho chikhocho adzakhala kapolo wanga, ndipo ena nonsenu muzipita mwaufulu.”

11 Tsono onse anafulumira kutsitsa pansi aliyense thumba lake ndi kulitsekula. 12 Kenaka anayamba kufufuza, kuyambira pa wamkulu mpaka pa wamngʼono. Ndipo chikhocho chinapezeka mʼthumba mwa Benjamini. 13 Apo onse anangʼamba zovala zawo ndi chisoni. Ndipo anasenzetsa abulu katundu wawo nabwerera ku mzinda konkuja.

14 Pamene Yuda ndi abale ake ankafika ku nyumba kwa Yosefe nʼkuti Yosefe akanali komweko. Ndipo anadzigwetsa pansi pamaso pake. 15 Yosefe anafunsa kuti, “Nʼchiyani mwachitachi? Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndikhoza kuona zinthu mwakuwombeza?”

16 Yuda anayankha, “Kodi tinganenenji kwa mbuye wanga? Tinena chiyani? Tingadzilungamitse bwanji? Mulungu waulula kulakwa kwa antchito anu. Ndipo tsopano ndife akapolo a mbuye wanga, ife tonse pamodzi ndi amene wapezeka ndi chikhocho.”

17 Koma Yosefe anati, “Sindingachite choncho ayi! Yekhayo amene wapezeka ndi chikhocho ndi amene akhale kapolo wanga. Ena nonsenu, bwererani kwa abambo anu mu mtendere.”

18 Ndipo Yuda anamuyandikira iye nati, “Chonde mbuye wanga mulole kapolo wanune ndinene mawu pangʼono kwa mbuye wanga. Musandipsere mtima, kapolo wanune, popeza inu muli ngati Farao yemwe. 19 Mbuye wanga munafunsa akapolo anufe kuti, ‘Kodi muli ndi abambo anu kapena mʼbale wanu?’ 20 Ndipo ife tinayankha, ‘Inde mbuye wathu, ife tili ndi abambo athu wokalamba, ndipo pali mwana wamwamuna wamngʼono amene anabadwa abambo athu atakalamba kale. Mʼbale wake anafa ndipo ndi yekhayo mʼmimba mwa amayi ake amene watsala ndipo abambo ake amamukonda.’

21 “Ndipo inu munatiwuza kuti, ‘Mubwere naye kwa ine kuti ndidzamuone ndekha.’ 22 Ife tinati, ‘Mbuye wathu, mnyamatayo sangasiye abambo ake, akawasiya ndiye kuti abambo akewo adzafa.’ 23 Koma inu munatichenjeza kuti, ‘Pokhapokha mutabwera naye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri, simudzandionanso.’ 24 Ndiye pamene tinafika kwa kapolo wanu, abambo athu tinawawuza zonse zimene munanena.

25 “Abambo athu anatiwuza kuti, ‘Pitaninso mukagule kachakudya pangʼono.’ 26 Koma tinati, ‘Sitingathe kupitanso. Sitingapite pokhapokha mngʼono wathuyu apite nafe chifukwa munthu uja anati sitingaonane naye ngati mngʼono wathuyu sakhala nafe.’

27 “Koma kapolo wanu, abambo athu anatiwuza kuti, ‘Inu mukudziwa kuti mkazi wanga anandiberekera ana aamuna awiri. 28 Mmodzi wa iwo anandisiya. Ine ndimati anadyedwa ndi chirombo popeza sindinamuonenso mpaka lero. 29 Tsopano mukanditengeranso uyu, nakaphedwa mu njira ndiye kuti mudzandikankhira ku manda ndi chisoni.’

30 “Tsono ngati tizibwerera kwa mtumiki wanu, abambo athu popanda mnyamatayu, amene moyo wa abambo ake uli pa iyeyu, 31 ndipo akakaona kuti mnyamatayu palibe, basi akafa. Ife tidzakhala ngati takankhira abambo athu ku manda ndi chisoni. 32 Ndiponsotu ine ndinadzipereka kwa abambo anga kukhala chikole chotsimikiza kuti mnyamatayu ndidzamuteteza, ndipo ndinati, ‘Ngati sindibwerera naye mnyamatayu kwa inu, ndiye kuti ndidzakhala wochimwira inu abambo anga moyo wanga wonse.’

33 “Tsono, chonde mulole kuti ine kapolo wanu nditsalire kuno kukhala kapolo wa mbuye wathu mʼmalo mwa mnyamatayu. Koma iye apite pamodzi ndi abale akewa. 34 Ndingabwerere bwanji kwa abambo anga ngati sindingapite ndi mnyamatayu? Ayi! Sindifuna kukaona tsoka limene lingakagwere abambo anga.”

Marko 14

Yesu Adzozedwa ku Betaniya

14 Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha. Iwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.”

Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.

Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa? Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali.

Yesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino. Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. Wachita zimene akanatha. Wathira mafuta onunkhira pa thupi langa nthawi isanakwane kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.”

10 Kenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu. 11 Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke.

Mgonero wa Ambuye

12 Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”

13 Pamenepo anatumiza awiri mwa ophunzira ake, nawawuza kuti, “Pitani mu mzinda, ndipo mukakumana ndi mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi. Kamutsatireni iye. 14 Kawuzeni mwini nyumba imene iye akalowemo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa: kodi chili kuti chipinda changa cha alendo, kumene ndidyere Paska ndi ophunzira anga?’ 15 Iye adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala kale ndi zonse ndi chokonzedwa kale. Katikonzereni ife Paska kumeneko.”

16 Ophunzirawo anachoka, napita mu mzindawo ndipo anakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Choncho anakakonza Paska.

17 Ndipo kutada Yesu anafika ndi khumi ndi awiriwo. 18 Pamene ankadya pa tebulo Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka, mmodzi amene akudya ndi Ine.”

19 Iwo anamva chisoni, ndipo mmodzi ndi mmodzi anati kwa Iye, “Kodi ndine?”

20 Iye anayankha kuti, “Ndi mmodzi mwa khumi ndi awirinu, amene akusunsa buledi mʼmbale pamodzi ndi Ine. 21 Mwana wa Munthu adzapita monga momwe zinalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene adzapereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”

22 Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, ili ndi thupi langa.”

23 Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo.

24 Iye anawawuza kuti, “Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri. 25 Zoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”

26 Atayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi.

Yesu Aneneratu zakuti Petro Adzamukana

27 Yesu anati, “Nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa:

“ ‘Kantha Mʼbusa,
    ndipo nkhosa zidzabalalika.’

28 Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”

29 Petro anati, “Ngakhale onse adzakuthaweni, ine sindidzatero.”

30 Yesu anayankha kuti, “Zoona ndikukuwuza kuti lero lino, usiku uno, tambala asanalire kawiri, iweyo udzandikana katatu.”

31 Koma Petro ananenetsa kuti, “Ngakhale kutakhala kufa nanu, ine sindidzakukanani.” Ndipo ena onse ananena chimodzimodzi.

Mu Getsemani

32 Ndipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Khalani pano pamene Ine ndi kupemphera.” 33 Iye anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kumva chisoni kwambiri ndi kuvutika mu mtima. 34 Iye anawawuza kuti, “Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo musagone.”

35 Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi ndi kupemphera kuti ngati ndi kotheka oralo limupitirire. 36 Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.”

37 Kenaka anabwerera kwa ophunzira ake ndipo anawapeza akugona, Iye anati kwa Petro, “Simoni, kodi uli mtulo? Kodi simukanatha kukhala maso kwa ora limodzi? 38 Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.”

39 Kenakanso anachoka ndi kukapemphera chimodzimodzi. 40 Iye atabwerera, anawapezanso akugona, chifukwa mʼmaso mwawo munadzaza tulo. Iwo sanadziwe choti anene kwa Iye.

41 Atabweranso kachitatu, anawafunsa kuti, “Kodi mukugonabe ndi kupumula? Pakwana! Nthawi yafika. Taonani, Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa. 42 Nyamukani! Tiyeni tizipita! Uyu wondipereka Ine wafika!”

Amugwira Yesu

43 Iye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu.

44 Tsopano womupereka anapangana chizindikiro ndi iwo kuti: “Amene ndikapsompsone ndi iyeyo; mukamugwire ndi kumutenga ali womangidwa.” 45 Atapita kwa Yesu nthawi yomweyo, Yudasi anati, “Aphunzitsi,” ndipo anapsompsona. 46 Anthu anamugwira Yesu ndi kumumanga. 47 Kenaka mmodzi wa iwo amene anayima pafupipo anatulutsa lupanga lake nakhapa wantchito wa wamkulu wa ansembe, nʼkudula khutu lake.

48 Yesu anati, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira, kuti mubwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? 49 Tsiku ndi tsiku ndinali ndi inu, kuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, koma inu simunandigwire. Koma malemba ayenera kukwaniritsidwa.” 50 Pamenepo ophunzira ake onse anathawa namusiya yekha.

51 Mnyamata wamngʼono amene anangofundira nsalu yokha, wopanda chovala ankamutsatira Yesu. Atamugwira, 52 anathawa wamaliseche kusiya nsalu yake mʼmbuyo.

Yesu ku Bwalo la Milandu

53 Anamutengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo akulu a ansembe, akuluakulu ndi aphunzitsi amalamulo anasonkhana pamodzi. 54 Petro anamutsatira ali patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Kumeneko anakhala pansi ndi alonda namawotha moto.

55 Akulu a ansembe ndi onse olamulira a Ayuda ankafunafuna umboni womutsutsa Yesu kuti amuphe, koma sanapeze wina uliwonse. 56 Ambiri anamunenera Iye maumboni abodza, koma maumboni awo sanagwirizane.

57 Kenaka ena anayimirira namunenera umboni wonama womutsutsa Iye kunena kuti, 58 “Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’ ” 59 Ngakhale iwonso umboni wawo sunagwirizane.

60 Kenaka mkulu wa ansembe anayimirira pakati pawo namufunsa Yesu kuti, “Kodi suyankha? Kodi umboni uwu ndi wotani umene anthu akukuchitira?” 61 Koma Yesu anakhala chete ndipo sanayankhe.

Mkulu wa ansembe anabwereza kumufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?”

62 Yesu anati, “Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba.”

63 Mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zaunsembe zake. Iye anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani tikufuna mboni zinanso? 64 Mwamva mwanowo. Muganiza chiyani?”

Onse anavomereza kuti ndi woyenera imfa. 65 Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya.

Petro Akana Yesu

66 Petro ali chakumunsi kwa bwalo la milandu, mmodzi wa atsikana a ntchito a mkulu wa ansembe anabwera. 67 Ataona Petro akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa.

Iye anati, “Iwenso unali pamodzi ndi Mnazareti, Yesu.”

68 Koma iye anakana nati, “Sindikudziwa kapena kumvetsetsa zimene ukuyankhula.” Ndipo anachoka napita ku chipata.

69 Pamene mtsikana wantchitoyo anamuona iye, anatinso kwa iwo amene anayimirira pomwepo, “Munthu uyu ndi mmodzi mwa iwo.” 70 Anakananso kachiwiri.

Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pafupi anati kwa Petro, “Zoonadi ndiwe mmodzi wa iwo, pakuti ndiwe mu Galileya.”

71 Iye anayamba kudzitemberera, nalumbira kuti, “Sindimudziwa munthu ameneyu.”

72 Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Yesu ananena anamuwuza kuti, “Tambala asanalire kawiri, iwe udzandikana katatu.” Ndipo iye anasweka mtima nayamba kulira.

Yobu 10

10 “Ine ndatopa nawo moyo wanga;
    choncho ndidzanena zodandaula zanga momasuka
    ndipo ndidzayankhula mwa kuwawidwa mtima kwanga.
Ndidzati kwa Mulungu wanga: Musandiweruze kuti ndine wolakwa,
    koma mundiwuze chifukwa chimene Inu mukukanganira ndi ine.
Kodi mumakondwera mukamandizunza,
    kunyoza ntchito ya manja anu,
    chonsecho mukusekerera ndi zochita za anthu oyipa?
Kodi maso anu ali ngati a munthu?
    Kodi mumaona zinthu monga momwe amazionera munthu?
Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu,
    kapena zaka zanu ngati zaka za munthu,
kuti Inu mufufuze zolakwa zanga
    ndi kulondola tchimo langa,
ngakhale mukudziwa kuti sindine wolakwa
    ndiponso kuti palibe amene angandilanditse mʼdzanja lanu?

“Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu.
    Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga?
Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi,
    kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi?
10 Suja munapatsa abambo anga mphamvu zoti andibale,
    suja munandikuza bwino mʼmimba mwa amayi anga?
11 Munandikuta ndi khungu ndi mnofu
    ndi kundilumikiza pamodzi ndi mafupa ndi mitsempha?
12 Munandipatsa moyo ndi kundionetsa chifundo chanu,
    ndipo munasamalira bwino moyo wanga.

13 “Koma izi ndi zimene munabisa mu mtima mwanu,
    ndipo ndikudziwa kuti zinali mʼmaganizo anu:
14 Kuti ngati ndingachimwe mudzakhala mukundipenyetsetsa
    ndipo kuti simudzalola kuti ndisalangidwe chifukwa cha kulakwa kwanga.
15 Ngati ndili wolakwa, tsoka langa!
    Koma ngakhale ndili wosalakwa sindingathe kutukula mutu wanga,
pakuti ndagwidwa ndi manyazi
    ndipo ndamizidwa mʼmavuto anga.
16 Ndipo ndikatukula mutu wanga, Inu mumandisaka ngati mkango
    ndiponso mumandiopseza ndi mphamvu yanu.
17 Mumabweretsa mboni zatsopano potsutsana nane
    ndipo mkwiyo wanu pa ine umanka nukulirakulira ndi
    magulu anu olimbana nane amanka nachulukirachulukira.

18 “Chifukwa chiyani Inu munalola kuti ndibadwe?
    Ndi bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione.
19 Ndikanapanda kubadwa,
    kapena akanangonditenga nditabadwa kupita nane ku manda!
20 Kodi masiku anga owerengeka sali pafupi kutha?
    Ndilekeni kuti ndipumule pangʼono pokha
21 ndisanapite ku malo amene munthu sabwererako
    ku dziko la imfa ndi kwa mdima wandiweyani,
22 ku dziko la mdima wandiweyani
    ndi chisokonezo,
    kumene kuwala kumakhala ngati mdima.”

Aroma 14

Ofowoka ndi Amphamvu

14 Mulandire amene ndi ofowoka mʼchikhulupiriro, osatsutsana naye pa maganizo ake. Chikhulupiriro cha munthu wina chimamulola kudya china chilichonse koma munthu wina, amene chikhulupiriro chake ndi chofowoka, amangodya zamasamba zokha. Munthu amene amadya chilichonse sayenera kunyoza amene satero, ndipo munthu amene samadya chilichonse asaweruze munthu amene amatero, pakuti Mulungu anamulandira. Kodi ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wamwini? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza popeza kuti Mbuye wake angathe kumukhozetsa.

Munthu wina amayesa tsiku limodzi lopatulika kuposa lina. Munthu wina amayesa masiku onse ofanana. Aliyense akhale otsimikiza mʼmaganizo ake. Iye amene amaganiza kuti tsiku limodzi ndi lopambana, amatero kwa Ambuye. Iye amene amadya nyama, amadya mwa Ambuye pakuti amayamika Mulungu. Ndipo iye amene sadya, amatero kwa Ambuye ndi kuyamika Mulungu. Pakuti palibe wina wa ife amene amakhala moyo pa yekha ndiponso palibe wina wa ife amene amafa pa yekha. Ngati ife tikhala ndi moyo, ife tikhala ndi moyo kwa Ambuye. Ndipo ngati ife tifa, tifa kwa Ambuye. Choncho, ngati tikhala ndi moyo kapena kufa, ndife ake a Ambuye.

Pa chifukwa ichi, Khristu anafa ndi kuukanso kotero kuti Iye akhale ndi Ambuye wa akufa ndi amoyo. 10 Tsono nʼchifukwa chiyani iwe ukuweruza mʼbale wako? Kapena nʼchifukwa chiyani ukumunyoza mʼbale wako? Pakuti ife tonse tidzayima pa mpando wakuweruza wa Mulungu. 11 Kwalembedwa, akutero Ambuye,

“Pamene Ine ndili ndi moyo,
aliyense adzandigwadira
    ndipo lilime lililonse lidzavomereza Mulungu.”

12 Choncho tsopano, aliyense wa ife adzafotokoza yekha kwa Mulungu.

13 Motero, tiyeni tisiye kuweruzana wina ndi mnzake. Mʼmalo mwake, tsimikizani mʼmaganizo anu kuti musayike chokhumudwitsa kapena chotchinga mʼnjira ya mʼbale wanu. 14 Monga mmodzi amene ndili mwa Ambuye Yesu, ndine wotsimikiza mtima kuti palibe chakudya chimene pachokha ndi chodetsedwa. Koma ngati wina atenga china chake kukhala chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa. 15 Ngati mʼbale wako akuvutika chifukwa cha chimene umadya, iwe sukuchitanso mwachikondi. Usamuwononge mʼbale wako amene Khristu anamufera chifukwa cha chakudya chakocho. 16 Musalole kuti chimene muchiyesa chabwino achinene ngati choyipa. 17 Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani yakudya ndi kumwa, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. 18 Nʼchifukwa chake aliyense amene atumikira Khristu mʼnjira iyi akondweretsa Mulungu ndi kuvomerezedwa ndi anthu.

19 Tsono tiyeni tiyesetse kuchita zimene zidzabweretsa mtendere ndi kulimbikitsana mwachikondi. 20 Musawononge ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Chakudya chonse ndi choyera, koma munthu amalakwa ngati adya chilichonse chimene chimakhumudwitsa wina. 21 Nʼkwabwino kusadya kapena kumwa vinyo kapena kuchita chilichonse chimene chidzachititsa mʼbale wako kugwa.

22 Tsono zimene ukukhulupirira pa zinthu izi zikhale pakati pa iwe ndi Mulungu. Wodala munthu amene sadzitsutsa yekha pa zimene amazivomereza. 23 Koma munthu amene akukayika atsutsidwa ngati adya, chifukwa kudya kwake si kwa chikhulupiriro; ndipo chilichonse chosachokera mʼchikhulupiriro ndi tchimo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.