M’Cheyne Bible Reading Plan
Yakobo Akumana ndi Esau
33 Yakobo atakweza maso ake anaona Esau akubwera ndi anthu ake 400. Choncho ana ake anawagawira Leya, Rakele ndi antchito awiri aja. 2 Anayika antchito ndi ana awo patsogolo, kenaka nʼkubwera Leya ndi ana ake, ndipo pambuyo pawo Rakele ndi Yosefe. 3 Iye mwini anakhala patsogolo nawerama mpaka kukhudza pansi kasanu ndi kawiri pamene amayandikira mʼbale wake.
4 Koma Esau anathamanga kukakumana ndi Yakobo ndipo anamukupatira namupsompsona. Onse awiri ankangolira. 5 Kenaka Esau ataona amayi ndi ana awo anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi anthu amene uli nawowa ndi a ndani?”
Yakobo anayankha kuti, “Awa ndi ana amene Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, wapereka kwa mtumiki wanune.”
6 Tsono antchito aja anayandikira naweramitsa mitu pansi. 7 Kenaka, Leya ndi ana ake anabwera. Nawonso anaweramitsa mitu pansi. Potsiriza pa onse anabwera Yosefe ndi Rakele naweramitsanso mitu yawo pansi.
8 Esau anafunsa kuti, “Kodi gulu la ziweto ndakumana nalo lija ndi layani?”
Yakobo anayankha nati, “Mbuye wanga, gulu lija ndi lanu kuti mundikomere mtima.”
9 Koma Esau anati, “Mʼbale wanga, ine ndili nazo kale zambiri. Zinthu zakozi sunga.”
10 Yakobo anati, “Chonde musatero. Ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yangayi kuchokera kwa ine. Pakuti ndi mmene mwandirandira bwinomu, ine ndikamaona nkhope yanu ndikuchita ngati ndikuona nkhope ya Mulungu. 11 Chonde, landirani mphatso imene ndakutengeraniyi, popeza Mulungu wandikomera mtima kwambiri moti ndili ndi zonse zimene ndizifuna.” Ndipo popeza kuti Yakobo anamuwumiriza, Esau analandira.
12 Ndipo Esau anati, “Tiyeni tizipita; nditsagana nanu.”
13 Koma Yakobo anati kwa iye, “Mbuye wanga, inu mudziwa kuti anawa ndi a nthete ndiponso ndiyenera kusamalira nkhosa ndi ngʼombe zimene zikuyamwitsa ana awo. Ngati ndizimenya kuti zifulumire, tsiku limodzi lokha nyamazo zidzafa. 14 Choncho, mbuye wanga lolani kuti mutsogole. Ine ndiziyenda pangʼonopangʼono pambuyo pa ziwetozi ndi anawa mpaka ndikafika ku Seiri.”
15 Esau anati, “Ndiye bwanji ndikusiyireko ena mwa anthu anga.”
Koma Yakobo anati, “Koma muchitiranji zimenezi? Chachikulu nʼkuti mwandilandira bwino, mbuye wanga.”
16 Choncho tsiku limenelo Esau anayamba ulendo wobwerera ku Seiri. 17 Komabe Yakobo anapita ku Sukoti. Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa Sukoti.
18 Mmene ankabwerera kuchokera ku Padanaramu, Yakobo anafika ku Salemu, mzinda wa Sekemu ku Kanaani. Anamanga msasa pamalopo moyangʼanana ndi mzindawo. 19 Malo amenewo anagula kwa zidzukulu za Hamori, abambo a Sekemu ndi ndalama 100 zasiliva. 20 Pamalopo anamanganso guwa lansembe, nalitcha Eli Elohe Israeli.
Fanizo la Wofesa Mbewu
4 Nthawi inanso Yesu atakhala mʼmbali mwa nyanja, anayamba kuphunzitsa. Gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira kotero kuti Iye analowa mʼbwato lomwe linali pa nyanja nakhalamo, anthu onse ali pa mtunda mʼmbali mwa madzi. 2 Anawaphunzitsa zinthu zambiri mʼmafanizo, ndipo mʼchiphunzitso chake anati: 3 “Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. 4 Akufesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa njira, ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. 5 Zina zinagwa pa malo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. 6 Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinapserera, ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. 7 Mbewu zina zinagwa pa minga, ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. 8 Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.”
9 Pamenepo Yesu anati, “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”
10 Ali yekha, ophunzira ndi ena omuzungulira, anamufunsa za mafanizo. 11 Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo: 12 kotero kuti,
“ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu,
kumva mudzamva koma osamvetsetsa,
kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ”
13 Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Kodi simukulimvetsa fanizoli? Kodi nanga mudzazindikira bwanji fanizo lina lililonse? 14 Wofesa amafesa mawu. 15 Anthu ena ali ngati mbewu za mʼmbali mwa njira, mʼmene mawu amafesedwamo. Akangowamva, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu amene anafesedwa mwa iwo. 16 Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe. 17 Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira. 18 Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; 19 koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. 20 Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”
Fanizo la Nyale
21 Iye anawawuza kuti, “Kodi umatenga nyale ndi kuyiika pansi pa mbiya kapena pansi pa bedi? Mʼmalo mwake, kodi simuyika pa choyikapo chake? 22 Pakuti chilichonse chobisika chidzayenera kuwululika, ndi chilichonse chachinsinsi chidzayenera kuonekera poyera. 23 Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.”
24 Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri. 25 Amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka; amene alibe, ngakhale zimene ali nazo zidzachotsedwa kwa iwo.”
Fanizo la Mbewu Imene Ikukula
26 Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka. 27 Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira. 28 Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo. 29 Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”
Fanizo la Mbewu ya Mpiru
30 Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera? 31 Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka. 32 Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”
33 Ndi mafanizo ambiri onga awa Yesu anayankhula mawu kwa iwo, monga mmene akanatha kumvetsa. 34 Iye sananene kanthu kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. Koma ali yekha ndi ophunzira ake, ankawatanthauzira zonse.
Yesu Aletsa Namondwe
35 Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina.” 36 Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye. 37 Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. 38 Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”
39 Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.
40 Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?”
41 Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”
Chigonjetso cha Ayuda
9 Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo. 2 Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha. 3 Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai. 4 Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe.
5 Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo. 6 Ku likulu la mzinda wa Susa, Ayuda anapha ndi kuwononga anthu 500. 7 Ayuda anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata, 8 Porata, Adaliya, Aridata, 9 Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata, 10 ana khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande katundu wawo.
11 Tsiku lomwelo anawuza mfumu chiwerengero cha anthu amene anaphedwa mu likulu la mzinda wa Susa. 12 Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.”
13 Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni mfumu, apatseni chilolezo Ayuda okhala mu Susa kuti achitenso zimene achita lerozi mawa, potsata lamulo ndipo mulole kuti ana khumi a Hamani aja mitembo yawo ipachikidwe pa mtanda.”
14 Choncho mfumu inalamula kuti izi zichitike. Anapereka lamulo mu Susa ndipo mitembo ya ana khumi a Hamani anayipachika pa mtanda. 15 Ayuda a mu mzinda wa Susa anasonkhana pamodzi pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndipo anapha anthu 300 mu Susa, koma sanatenge katundu wawo.
16 Tsono Ayuda ena onse amene anali mu zigawo za mfumu anasonkhananso kudziteteza ndipo sanasautsidwenso ndi adani popeza anapha anthu 75,000 koma sanalande zofunkha zawo. 17 Zonsezi zinachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara ndipo pa tsiku la 14 anapumula ndi kupanga tsikuli kuti likhale la madyerero ndi chikondwerero.
Kukondwerera Purimu
18 Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero.
19 Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso.
20 Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali: 21 Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara, 22 ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka.
23 Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai. 24 Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, mdani wa Ayuda onse, anakonza chiwembu chakupha ndi kuwononga Ayuda ndipo anachita maere otchedwa Purimu kuti awaphe ndi kuwawononga. 25 Koma mfumu itazindikira za chiwembuchi, inalamula kuti zilembedwe mʼmakalata kuti chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda chigwere pa iye mwini, ndi kuti iye pamodzi ndi ana ake apachikidwe pa mtanda. 26 Ndi chifukwa chake masiku amenewa amatchedwa masiku a Purimu potsata dzina lakuti Purimu. Chifukwa cha kalata ya Mordekai ndiponso chifukwa cha zimene anaziona ndi kuwachitikira, 27 Ayuda onse anagwirizana kukhazikitsa lamulo lokhudza iwo, zidzukulu zawo ndi onse amene adzapanga nawo ubale kuti asalephere kusunga masiku awiri amenewa chaka chilichonse monga zinalembedweramo ndiponso potsata nthawi imene anayika. 28 Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira.
29 Choncho mfumukazi Estere, mwana wa mkazi wa Abihaili, pamodzi ndi Mordekai Myuda analemba ndi ulamuliro onse kutsimikizira kalata iyi yachiwiri yokhudza Purimu. 30 Ndipo Mordekai anatumiza makalata kwa Ayuda onse ku zigawo 127 za ufumu wa Ahasiwero. Kalatayi inali ya mawu a mtendere ndiponso a kukhulupirika 31 kuti azisunga masiku a Purimu pa nyengo imene inavomerezeka monga mmene Mordekai Myuda ndi mfumukazi Estere anawalamulira ndiponso monga anadziyikira eni okha ndi zidzukulu zawo zonena za nthawi zawo za kusala zakudya ndi kulira. 32 Lamulo la Estere linakhazikitsa mwambo wa Purimuwu ndipo zinalembedwa mʼmabuku.
Ukulu wa Mordekai
10 Mfumu Ahasiwero anakhometsa msonkho mʼdziko lake lonse mpaka ku zilumba zonse. 2 Ndipo ntchito zonse zochitika ndi mphamvu zake komanso ndi zonse zofotokoza za ukulu wa Mordekai, kukwezedwa kwake ndi mfumu, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Mediya ndi Peresiya? 3 Pakuti Mordekai Myuda uja anali wachiwiri wa mfumu Ahasiwero. Kwa Ayuda onse Mordekai anali munthu wamkulu ndipo ankamukonda chifukwa ankachitira zabwino mtundu wake ndi kufunira mtendere abale ake.
Abrahamu Analungamitsidwa Mwachikhulupiriro
4 Nanga tsono tidzati chiyani za Abrahamu kholo lathu, iyeyu anapezana ndi zotani pa nkhani imeneyi? 2 Kunena zoona, Abrahamu akanalungamitsidwa ndi ntchito zake, akanakhala nako kanthu kodzitamandira, koma osati pamaso pa Mulungu. 3 Kodi Malemba akuti chiyani? “Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.”
4 Tsopano munthu amene wagwira ntchito, malipiro ake satengedwa kukhala ngati mphatso koma zimene anayenera kulandira. 5 Koma kwa munthu amene sanagwire ntchito ndipo akhulupirira Mulungu amene amalungamitsa ochimwa, chikhulupiriro chakecho chimatengedwa kukhala chilungamo. 6 Davide ponena zomwezi pamene anayankhula za kudala kwa munthu amene Mulungu amulungamitsa osati chifukwa cha ntchito zake akuti,
7 “Odala ndi amene
zoyipa zawo zakhululukidwa;
amene machimo awo afafanizidwa.
8 Ngodala munthu amene
machimo ake Ambuye sadzawakumbukiranso.”
9 Kodi madalitso amenewa ali kwa ochita mdulidwe okha kapena kwa amene sanachitepo mdulidwe? Ife takhala tikunena kuti chikhulupiriro cha Abrahamu chinamuchititsa kukhala wolungama. 10 Kodi chinatengedwa bwanji? Kodi nʼkuti iye atachita mdulidwe kapena asanachite? Osati atachita mdulidwe koma asanachite! 11 Ndipo iye anachita mdulidwe ngati chizindikiro ndi chitsimikizo cha kulungama kumene anali nako mwachikhulupiriro pomwe anali asanachite mdulidwe. Choncho, iye ndi kholo la onse amene akhulupirira koma sanachite mdulidwe, ndi cholinga chakuti alungamitsidwe. 12 Ndipo iyenso ndiyenso kholo la ochita mdulidwe osati amene anangochita mdulidwe kokha koma amene amatsata chitsanzo cha chikhulupiriro chimene kholo lathu Abrahamu anali nacho asanachite mdulidwe.
13 Abrahamu ndi zidzukulu zake sanalandire lonjezano lakuti adzalandira dziko lapansi kudzera mu Malamulo, koma kudzera mu chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro. 14 Pakuti ngati amene amadalira Malamulo ndiye olowa mʼmalo, ndiye kuti chikhulupiriro nʼchopanda pake ndipo lonjezano ndi lopanda phindu 15 chifukwa Malamulo anabweretsa chilango. Ndipo kumene kulibe Malamulo kulibenso kuwalakwitsa.
16 Motero, timalandira lonjezo mwachikhulupiriro. Laperekedwa mwachisomo kuti patsimikizidwe kuti lonjezolo liperekedwa kwa ana ndi zidzukulu zonse za Abrahamu, osati kwa iwo okha amene amatsatira Malamulo komanso kwa iwo amene ali ndi chikhulupiriro cha Abrahamu. Iye ndiye kholo la ife tonse. 17 Monga kwalembedwa kuti, “Ine ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri.” Iye ndiye kholo lathu pamaso pa Mulungu, amene anamukhulupirira, Mulungu amene amapereka moyo kwa akufa ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo.
18 Ngakhale zinali zosayembekezeka, Abrahamu anakhulupirira ndi chiyembekezo kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri. Izi ndi monga zinanenedwa kwa iye kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.” 19 Iye sanafowoke mʼchikhulupiriro. Anadziwa choonadi cha thupi lake kuti linali lakufa popeza anali ndi zaka pafupifupi 100 ndiponso mimba ya Sara inali yowuma. 20 Komabe iye sanagwedezeke chifukwa chosakhulupirira pa zokhudzana ndi lonjezo la Mulungu. Iye analimbikitsidwa mʼchikhulupiriro chake ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu. 21 Anatsimikiza mu mtima mwake kuti Mulungu anali ndi mphamvu yochita chomwe analonjeza. 22 Nʼchifukwa chake “chinamuchititsa kukhala wolungama.” 23 Mawu akuti, “chinatengedwa kwa iye” sanalembedwe chifukwa cha iye yekha, 24 komanso chifukwa ife amene Mulungu adzatiyesa olungama, ife amene tikhulupirira mwa Iye amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu Ambuye athu. 25 Iye anaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha machimo athu ndipo anaukitsidwa ndi kukhala ndi moyo kuti tilungamitsidwe.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.