Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 30

30 Rakele ataona kuti sakumuberekera Yakobo ana, anayamba kumuchitira nsanje mʼbale wake. Choncho anati kwa Yakobo, “Undipatse ana kapena apo ayi ndingofa!”

Yakobo anapsera mtima Rakele ndipo nati, “Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu amene wakulepheretsa iwe kukhala ndi ana?”

Pamenepo Rakele anati kwa Yakobo, “Mdzakazi wanga Biliha nayu. Lowana naye kuti mwina nʼkundibalira mwana, ndipo kudzera mwa iyeyu nanenso nʼkukhala ndi ana.”

Ndipo anamupatsa Yakobo wantchito wake Biliha kuti alowane naye. Choncho Yakobo analowana ndi Biliha, ndipo Bilihayo anatenga pathupi namubalira Yakobo mwana wamwamuna. Pamenepo Rakele anati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima, wamva kupempha kwanga ndipo wandipatsa mwana wa mwamuna.” Choncho anamutcha Dani.

Biliha, wantchito wa Rakele, anatenganso pathupi nabalira Yakobo mwana wa mwamuna wachiwiri. Pamenepo Rakele anati, “Ndakhala ndikulimbana kwambiri ndi mʼbale wanga ndipo ndapambana.” Choncho anamutcha Nafutali.

Pamene Leya anaona kuti waleka kubereka ana, iye anatenga wantchito wake Zilipa namupereka kwa Yakobo kuti alowane naye. 10 Zilipa, wantchito wa Leya, anaberekera Yakobo mwana wamwamuna. 11 Pamenepo Leya anati, “Mwayi wangawo!” Choncho anamutcha Gadi.

12 Zilipa, wantchito wa Leya anamubalira Yakobo mwana wa mwamuna wachiwiri. 13 Pamenepo Leya anati, “Ndakondwa bwanji! Amayi adzanditcha ine wokondwa.” Choncho anamutcha Aseri.

14 Pa nthawi yokolola tirigu, Rubeni anapita ku munda ndipo anapezako zipatso za mankhwala wobereketsa. Tsono anatengerako mayi wake Leya. Rakele anati kwa Leya, “Chonde patseko mankhwala wakupezera mwana wakowo.”

15 Koma iye anati kwa Rakele, “Kodi sizinakukwanire kulanda mwamuna wanga? Ukuti utengenso mankhwala a mwana wangawa.”

Iye anati, “Chabwino, agone ndi iwe usiku uno kuti tisinthane ndi mankhwala a mwana wakowo.”

16 Choncho pamene Yakobo ankabwera kuchokera ku munda madzulo, Leya anapita kukakumana naye nati, “Lero mukagona ku nyumba chifukwa ndakubwerekani ndi mankhwala wobereketsa a mwana wanga.” Choncho usiku umenewo Yakobo anakalowa kwa Leya.

17 Mulungu anamva pemphero la Leya ndipo anatenga pathupi nabalira Yakobo mwana wa mwamuna wachisanu. 18 Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphotho chifukwa chopereka wantchito wanga kwa mwamuna wanga.” Choncho anamutcha Isakara.

19 Leya anatenganso pathupi nabalira Yakobo mwana wa mwamuna wachisanu ndi chimodzi. 20 Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphatso yapamwamba. Tsopano mwamuna wanga adzandilemekeza chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Choncho anamutcha Zebuloni.

21 Patapita nthawi Leya anabereka mwana wamkazi ndipo anamutcha Dina.

22 Kenaka, Mulungu anakumbukira Rakele namva pemphero lake ndi kulola kuti akhale ndi mwana. 23 Rakele anatenga pathupi nabala mwana wamwamuna ndipo anati, “Mulungu wandichotsera manyazi anga.” 24 Iye anamutcha mwanayo Yosefe, ndipo anati, “Mulungu andipatsenso mwana wina.”

Nkhosa za Yakobo Zichuluka

25 Rakele atabereka Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, “Ndimasuleni kuti ndizipita ku dziko la kwathu. 26 Patseni akazi anga ndi ana anga, amene ndinakugwirirani ntchito, ndipo ndidzanyamuka ulendo. Inu mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani.”

27 Koma Labani anati kwa iye, “Chonde, ngati mungandikomere mtima musapite chifukwa ndadziwa kudzera mwa kuwombeza kwanga kuti Yehova wandidalitsa chifukwa cha inu.” 28 Anapitiriza kunena kuti, “Tchula malipiro ako ndipo ndidzakupatsa.”

29 Koma Yakobo anati kwa iye, “Inu mukudziwa mmene ine ndakugwirirani ntchito ndi mmene ziweto zanu zaswanira pamene ine ndimazisamalira. 30 Poyamba munali nazo zochepa ine ndisanabwere, koma tsopano zachuluka. Yehova wakudalitsani chifukwa cha ine. Ndi nthawi tsopano kuti nane ndisamalire banja langa.”

31 Labani anafunsa, “Ndikupatse chiyani?”

Yakobo anayankha, “Musandipatse kanthu. Koma mungondichitira izi ndipo ndidzapitiriza kusamalira nkhosa zanu ndi kuziyangʼanira: 32 Mundilole ndiyendeyende pakati pa ziweto zanu lero ndi kuchotsamo mwana wankhosa wamkazi aliyense wakuda, mbuzi iliyonse yamathothomathotho ndi yamawangamawanga. Zimenezi ndiye zikhale malipiro anga. 33 Ndipo chilungamo changa chidzaoneka mʼtsogolo, pamene inu mudzabwere kudzaona malipiro angawo. Ngati mudzapeza mbuzi mʼgulu langa imene si yamawangamawanga, kapena mwana wankhosa wamkazi amene si wakuda ndiye kuti zimenezo zidzakhala kuti ndinakuberani.”

34 Labani anati, “Ndavomera, zikhale monga mmene wayankhuliramu.” 35 Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde onse ndi mbuzi zazikazi zonse zimene zinali ndi mawangamawanga kapena zamathothomathotho, ndiponso zonse zabanga loyera. Anachotsa ana onse ankhosa aakazi akuda, napereka ziweto zonsezi kwa ana ake aamuna kuti aziweta. 36 Kenaka Labani anayenda mtunda wa masiku atatu kutalikirana ndi Yakobo koma Yakobo anapitiriza kuweta nkhosa zina zonse za Labani.

37 Tsono Yakobo anatenga nthambi zaziwisi za mitengo ya mkundi, alimoni ndi puleni nazisenda kuchotsa makungwa ake mpaka mtengo woyera wamʼkati kuonekera. 38 Atatero anayika nthambi zija mʼmagome omwera madzi molunjika ziweto zija kuti pakumwa madziwo ziweto zazikazi ziziyangʼana nthambi zija popeza kuti pakumwa madzi ziweto zija zinkakwerana. 39 Ndiye kuti nkhosa zija zinkatenga mawere pakumwa madzi molunjika nthambi zija, ndipo zinkaswa ana a mawangamawanga kapena a mathothomathotho. 40 Yakobo anayika padera ana a ziweto zija. Koma ziweto zina anaziyika kuti ziyangʼanane ndi za Labani, zimene zinali za mawangamawanga ndi zakuda. Motero anapeza ziweto zakezake, ndipo sanazisakanize ndi za Labani. 41 Yakobo ankayika nthambi zija momwera madzi pamene ziweto zamphamvu zazikazi zinkakweredwa pofuna kuti zitenge mawere pakumwa madzi moyangʼanana ndi nthambi zija. 42 Koma sankayika nthambizo pamene ziweto zofowoka zazikazi zinkakweredwa pakumwa madzi. Choncho ziweto zofowoka zonse zinakhala za Labani, ndi ziweto zamphamvu zinakhala za Yakobo. 43 Mwa njira imeneyi, Yakobo analemera kwambiri ndipo anali ndi ziweto zochuluka kwambiri, antchito aakazi ndi aamuna, ngamira ndi abulu.

Marko 1

Yohane Mʼbatizi Akonza Njira

Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya:

“Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,
    amene adzakonza njira yanu,”
“Mawu a wofuwula mʼchipululu,
‘Konzani njira ya Ambuye,
    wongolani njira zake.’ ”

Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo. Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani. Yohane amavala zovala zopangidwa ndi ubweya wangamira, ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wamthengo. Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake. Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”

Kubatizidwa ndi Kuyesedwa kwa Yesu

Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. 10 Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda. 11 Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”

12 Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu, 13 ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.

Yesu Alengeza za Uthenga Wabwino

14 Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, 15 “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”

Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba

16 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi. 17 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 18 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.

19 Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo. 20 Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.

Yesu Atulutsa Mzimu Woyipa

21 Iwo anapita ku Kaperenawo, ndipo tsiku la Sabata litafika, Yesu analowa mʼsunagoge nayamba kuphunzitsa. 22 Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo. 23 Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti, 24 “Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”

25 Yesu anadzudzula chiwandacho mwamphamvu nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye!” 26 Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.

27 Anthu anadabwa kwambiri kotero kuti anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Ichi nʼchiyani? Chiphunzitso chatsopano ndi ulamuliro! Iye akulamula, ngakhale mizimu yoyipa ikumumvera.” 28 Mbiri yake inafalikira kudera lonse la Galileya mofulumira.

Yesu Achiritsa Anthu Ambiri

29 Atangochoka mu sunagoge, Yesu pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane anakalowa mʼnyumba ya Simoni ndi Andreya. 30 Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye. 31 Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira.

32 Madzulo omwewo dzuwa litalowa anthu anabweretsa kwa Yesu anthu onse odwala ndi ogwidwa ndi ziwanda. 33 Anthu onse a mʼmudzimo anasonkhana pa khomo, 34 Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye.

Yesu Apemphera Kumalo a Yekha

35 Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera. 36 Simoni ndi anzake anapita kokamufunafuna Iye, 37 ndipo atamupeza, anamuwuza kuti, “Aliyense akukufunani!”

38 Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.” 39 Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda.

Yesu Achiritsa Wakhate

40 Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”

41 Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” 42 Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.

43 Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti, 44 “Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.” 45 Mʼmalo mwake anapita nayamba kuyankhula momasuka, nafalitsa mbiriyo. Zotsatira zake, Yesu sanathe kulowa mʼmudzi moonekera, koma anakhala kunja kumalo kopanda anthu. Komabe anthu amabwera kwa Iye kuchokera kulikonse.

Estere 6

Mordekai Apatsidwa Ulemu

Usiku umenewo mfumu inalephera kugona tulo; Choncho inayitanitsa buku limene amalembamo mbiri ya zamakedzana kuti amuwerengere. Anapeza kuti mʼbukumo munalembedwa zoti Mordekai anawulula kuti Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa a mfumu amene ankalondera pa khomo la chipinda cha mfumu ndiwo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero.

Mfumu inafunsa kuti, “Kodi Mordekai anamupatsa ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha chinthu chimene anachitachi?”

Atumiki ake anamuyankha kuti, “Palibe chimene chinachitika kwa iye.”

Mfumu inati, “Kodi ndani ali mʼbwalomo?” Tsono Hamani anali atangolowa kumene mʼbwalo lakunja la nyumba yaufumu kuti akawuze mfumu zomukhomera Mordekai pa mtanda umene anamukonzera.

Atumiki ake anamuyankha kuti, “Hamani ndiye wayima mu bwalo.”

“Mulowetseni,” Mfumu inalamulira.

Hamani atalowa, mfumu inamufunsa kuti, “Kodi timuchitire ulemu otani munthu amene mfumu ikondweretsedwa naye?”

Tsono Hamani anaganiza mu mtima kuti, “Kodi palinso ndani amene mfumu ingamulemekeze kuposa ine?” Choncho Hamani anayankha mfumuyo kuti, “Munthu amene mfumu ifuna kumuchitira ulemu, imuchitire izi: Anthu abwere ndi chovala cha ufumu ndi kavalo amene mfumu imakwerapo wokhala ndi chizindikiro chaufumu pamutu pake. Ndipo mupereke chovala cha ufumucho ndi kavalo kwa mmodzi wa akalonga a mfumu a ulemu kwambiri. Ameneyu amuveke chovalacho munthu amene mfumu yakondweretsedwa naye. Akavekedwa chovalachi amuyendetse mʼmisewu yonse ya mzinda atakwera pa kavalo wa mfumu. Kalongayu azifuwula patsogolo pa munthuyu kuti ‘Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!’ ”

10 Mfumu inalamulira Hamani kuti, “Pita msanga, katenge chovala cha ufumu ndi kavalo ndipo uchite monga wanenera kwa Mordekai Myuda, amene amakhala pa chipata cha mfumu. Usasiyeko china chilichonse chimene wanena.”

11 Choncho Hamani anatenga chovala ndi kavalo. Anamuveka Mordekai chovalacho ndipo anamuyendetsa mʼmisewu yonse ya mu mzinda atakwera pa kavalo, akufuwula kuti, “Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!”

12 Pambuyo pake Mordekai anabwerera ku chipata cha mfumu. Koma Hamani anapita msanga ku nyumba kwake, akulira, atafundira mutu wake. 13 Hamani anawuza Zeresi mkazi wake ndi abwenzi ake onse zonse zinamuchitikira.

Anthu ake anzeru ndi mkazi wake Zeresi anamuwuza kuti, “Popeza kuti Mordekai ndi Myuda amene mwayamba kale kugonja pamaso pake, ndiye kuti palibe chimene mungachitepo. Mudzagwa ndithu pamaso pake.” 14 Pamene anthuwa amayankhula nayebe, adindo a mfumu ofulidwa anabwera kudzamutenga Hamani mofulumira kupita naye ku phwando limene Estere anakonza.

Aroma 1

Ndine Paulo, mtumiki wa Khristu Yesu, woyitanidwa ndi Mulungu kukhala mtumwi. Ndinapatulidwa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Mulungu umene analonjeza kale mʼMalemba Oyera kudzera mwa aneneri ake. Uthengawu ndi wonena za Mwana wake amene mwa umunthu wake anali wochokera mwa Davide. Iyeyu ndi amene anatsimikizidwa kukhala Mwana wa Mulungu mwamphamvu za Mzimu Woyera pamene anauka kwa akufa. Kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ife tinalandira chisomo chokhala atumwi oyitana anthu a mitundu yonse kuti amukhulupirire ndi kumumvera mwachikhulupiriro kuti dzina lake lilemekezedwe. Inunso muli mʼgulu la Amitundu oyitanidwawo kukhala ake a Yesu Khristu.

Ndikulembera kwa onse okhala ku Roma amene Mulungu amakukondani nakuyitanani kuti mukhale oyera mtima.

Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.

Paulo Afunitsitsa Kukacheza ku Roma

Poyamba, ndikuthokoza Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu chifukwa cha nonsenu, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akukamba za chikhulupiriro chanu. Mulungu amene ndimamutumikira ndi mtima wanga onse polalikira Uthenga Wabwino wa Mwana wake, ndi mboni yanga kuti ndimakupemphererani nthawi zonse. 10 Mʼmapemphero anga, nthawi zonse, ndimapemphera kuti ngati nʼkotheka mwachifuniro cha Mulungu, njira inditsekukire kuti ndibwere kwanuko.

11 Ine ndikulakalaka kukuonani kuti ndikugawireni mphatso zina zauzimu kuti zikulimbikitseni 12 ndiponso kuti tonsefe tilimbikitsane mʼchikhulupiriro wina ndi mnzake. 13 Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa kuti nthawi zambiri ndakhala ndikufuna zobwera kwanuko, koma mpaka pano pali zolepheretsa, ndi cholinga choti ndidzapezeko zipatso pakati panupo monga momwe ndakhala ndikuchitira pakati pa a mitundu ina.

14 Ine ndi wokakamizidwa ndi udindo wotumikira Agriki pamodzi ndi omwe si Agriki, kwa anzeru ndi kwa opusa omwe. 15 Pa chifukwa chimenechi, ine ndikufunitsitsa kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso amene muli ku Roma.

16 Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene. 17 Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”

Mkwiyo wa Mulungu pa Mtundu wa Anthu

18 Mkwiyo wa Mulungu ukuonekera kuchokera kumwamba. Ukutsutsana ndi kusapembedza konse ndi kuyipa kwa anthu amene amapondereza choonadi mwa chikhalidwe chawo choyipa. 19 Za Mulungu zimene zingathe kudziwika, ndi zomveka bwino kwa iwo pakuti Mulungu anazionetsera kwa iwo. 20 Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula.

21 Ngakhale iwo anadziwa Mulungu, sanamulemekeze ngati Mulungu kapena kumuthokoza, koma maganizo awo anasanduka wopanda pake ndipo mʼmitima yawo yopusa munadzaza mdima. 22 Ngakhale ankadzitama kuti ndi anzeru, anasanduka opusa. 23 Iwo anasinthanitsa ulemerero wa Mulungu wosafa ndi mafano opangidwa ndi manja wooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame, ndi nyama kapena zokwawa.

24 Nʼchifukwa chake Mulungu anawasiya kuti azingochita zilakolako zochititsa manyazi zauchimo zomwe mitima yawo inkafuna. Zotsatira zake anachita za chiwerewere wina ndi mnzake kunyazitsa matupi awo. 25 Iwo anasinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza ndipo anapembedza ndi kutumikira zinthu zolengedwa mʼmalo mwa Mlengi amene ali woyenera kutamandidwa mpaka muyaya. Ameni.

26 Chifukwa cha ichi, Mulungu anawasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe anasiya machitidwe achibadwidwe pa za ukwati, namachita machitidwe ena otsutsana ndi chibadwa chawo. 27 Chimodzimodzinso amuna analeka machitidwe a ukwati ndi akazi nʼkumakhumbana amuna okhaokha. Amuna ankachita zochitisa manyazizi ndi amuna anzawo, ndipo analandira chilango choyenera molingana ndi zochita zawo zachitayikozo.

28 Ndipo popeza anaona kuti nʼchopanda nzeru kumvera Mulungu, Iye anawasiya kuti atsatire maganizo achitayiko kuti achite zosayenera kuchitazo. 29 Iwo ndi odzazidwa ndi mtundu uliwonse wa makhalidwe oyipa, zonyansa, umbombo ndi dumbo. Iwo ndi odzazidwa ndi kaduka, kupha, mikangano, chinyengo ndi udani. Iwowo ndi amiseche, 30 osinjirira, odana ndi Mulungu, achipongwe, odzitama ndi odzitukumula. Iwo amapeza njira zochitira zoyipa. Samvera makolo awo, 31 alibe nzeru, chikhulupiriro, sakhudzidwa mu mtima ndipo ndi ankhanza. 32 Ngakhale kuti amadziwa chiweruzo cholungama cha Mulungu chakuti amene amachita zinthu zotere amayenera imfa, iwo sangopitiriza chabe zimenezi, koma amavomerezanso amene amazichita zimenezi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.