M’Cheyne Bible Reading Plan
Abrahamu Amwalira
25 Abrahamu anakwatira mkazi wina dzina lake Ketura. 2 Iyeyu anamubalira Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. 3 Yokisani anabereka Seba ndi Dedani ndipo zidzukulu za Dedani ndiwo Aasuri, Aletusi, ndi Aleumi. 4 Ana aamuna a Midiyani anali, Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali zidzukulu za Ketura.
5 Abrahamu anasiyira Isake chilichonse anali nacho. 6 Koma pamene anali ndi moyo, Abrahamu anapereka mphatso kwa ana aakazi ake ena onse. Kenaka anawatumiza ku dziko la kummawa kuti akhale kutali ndi mwana wake Isake.
7 Abrahamu anakhala ndi moyo zaka 175. 8 Abrahamu anamwalira atakalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 9 Ana ake, Isake ndi Ismaeli anamuyika mʼphanga la Makipela pafupi ndi Mamre, mʼmunda umene kale unali wa Efroni mwana wa Zohari Mhiti, 10 uwu ndi munda umene Abrahamu anagula kwa Ahiti. Kumeneko Abrahamu anakayikidwa pamodzi ndi mkazi wake Sara. 11 Atamwalira Abrahamu, Mulungu anadalitsa mwana wake Isake, amene ankakhala pafupi ndi Beeri-lahai-roi (chitsime cha Wamoyo Wondipenya).
Ana Aamuna a Ismaeli
12 Nazi zidzukulu za Ismaeli, mwana wa Abrahamu amene wantchito wa Sara, Hagara Mwigupto uja, anaberekera Abrahamu.
13 Awa ndi mayina a ana a Ismaeli monga mwa mndandanda wa mabadwidwe awo: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli; kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, 14 Misima, Duma, Masa, 15 Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema; 16 Amenewa ndi ana a Ismaeli ndi mayina awo monga mwa midzi ndi misasa yawo. Anali olamulira mafuko khumi ndi awiri. 17 Ismaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Iye anamwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 18 Zidzukulu za Ismaeli zinkakhala mʼdera la pakati pa Havila ndi Suri, kummwera kwa Igupto, mukamapita cha ku Asuri. Choncho anakhala kummawa kwa abale awo.
Yakobo ndi Esau
19 Iyi ndi mbiri ya Isake mwana wa Abrahamu.
Abrahamu anabereka Isake 20 ndipo Isake anali ndi zaka makumi anayi pamene anakwatira Rebeka mwana wa Betueli Mwaramu wa ku Padanaramu mlongo wa Labani Mwaramu.
21 Isake anapempherera mkazi wake kwa Yehova popeza iye anali wosabereka. Yehova anayankha pemphero lake ndipo mkazi wake Rebeka anatenga pathupi. 22 Koma pamene anawo amalimbana mʼmimba mwake, iye anati, “Bwanji zikundichitikira zoterezi?” Choncho anapita kukafunsa kwa Yehova.
23 Yehova anati kwa iye,
“Udzabala mafuko awiri a anthu olimbana,
ndipo magulu awiri a anthu ochokera mwa iwe adzasiyana;
fuko limodzi lidzakhala la mphamvu kuposa linzake,
ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.”
24 Pamene nthawi inakwana yakuti abeleke, Rebeka anaberekadi mapasa. 25 Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala cha ubweya; choncho anamutcha Esau. 26 Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa.
27 Anyamatawo anakula ndipo Esau anakhala katswiri wosaka, munthu wamʼthengo, pamene Yakobo anali munthu wofatsa, wokonda kukhala pa nyumba. 28 Isake ankakonda Esau chifukwa cha nyama za kutchire zomwe ankakonda kudya, koma Rebeka ankakonda Yakobo.
29 Tsiku lina pamene Yakobo ankaphika chakudya, Esau anabwera kuchokera kuthengo ali wolefuka ndi njala. 30 Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu).
31 Yakobo anayankha, “Choyamba undigulitse ukulu wako.”
32 Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?”
33 Koma Yakobo anati, “Lumbira kwa ine choyamba.” Kotero Esau analumbiradi, ndipo anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo.
34 Choncho Yakobo anamupatsa Esau buledi ndi phala lofiira lija. Iye anadya ndi kumwa, nanyamuka kumapita.
Motero Esau anapeputsa ukulu wake wachisamba uja.
Zizindikiro za Masiku Otsiriza
24 Yesu anatuluka mʼNyumba ya Mulungu ndipo akuchoka ophunzira ake anadza kwa Iye ndi kumuonetsa mamangidwe a Nyumbayo. 2 Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuona zinthu zonsezi? Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti palibe mwala pano umene udzasiyidwe pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
3 Pamene Yesu anakhala pansi pa phiri la Olivi, ophunzira ake anabwera kwa Iye mwamseri nati, “Tiwuzeni, kodi izi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kubwera kwanu ndi zizindikiro za kutha kwa dziko zidzakhala chiyani?”
4 Yesu anayankha kuti, “Onetsetsani kuti wina asakunyengeni. 5 Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati, ‘Ndine Khristu,’ ndipo adzanyenga ambiri. 6 Mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo, koma onetsetsani kuti musadzidzimuke nazo. Zotere ziyenera kuchitika, koma chimaliziro sichinafike. 7 Mtundu ndi mtundu udzawukirana, ndipo ufumu ndi ufumu udzawukirana. Kudzakhala njala ndi zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana. 8 Zonsezi ndi chiyambi chabe cha zowawa.
9 “Pamenepo adzakuperekani kuti mukazunzidwe ndi kuphedwa, ndipo mitundu yonse idzakudani chifukwa cha Ine. 10 Pa nthawi imeneyo ambiri adzasiya chikhulupiriro ndipo adzadana ndi kuperekana wina ndi mnzake, 11 ndipo aneneri onama ambiri adzaoneka ndi kunyenga anthu ambiri. 12 Chifukwa cha kuchuluka kwa zoyipa, chikondi cha ambiri chidzazirala, 13 koma wopirira kufikira chimaliziro adzapulumuka. 14 Ndipo uthenga wa ufumu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi ngati umboni kwa mitundu yonse, ndipo pomwepo chimaliziro chidzafika.”
15 “Tsono mukadzaona chinthu chonyansa chosakaza chitayima pamalo oyera chimene anayankhula mneneri Danieli, owerengayo azindikire. 16 Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire ku mapiri. 17 Yemwe ali pa denga la nyumba yake asatsike kukatulutsa chinthu chilichonse mʼnyumba. 18 Yemwe ali ku munda asapite kukatenga mkanjo wake. 19 Kudzakhala koopsa kwambiri masiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi kwa oyamwitsa! 20 Pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzachitike nthawi yozizira kapena pa Sabata. 21 Popeza kudzakhala masautso aakulu, omwe safanana ndi ena ali onse chiyambireni cha dziko lapansi mpaka lero lino ndipo sadzafanananso ndi ena. 22 Ngati masiku amenewo sakanafupikitsidwa, palibe mmodzi akanapulumuka, koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa. 23 Pa nthawi imeneyo ngati wina adzati kwa inu, ‘Onani, Khristu ali pano!’ Kapena, ‘Uyo ali ukoyo!’ Musakhulupirire. 24 Chifukwa akhristu onama ndi aneneri onama adzaoneka ndipo adzachita zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa kuti akanyenge ngakhale osankhidwawo ngati kukanakhala kotheka kutero. 25 Onani, ndakuwuzani izi nthawi isanafike.
26 “Ndiye ngati wina akuwuzani inu kuti, ‘Uyo ali ku chipululu,’ inu musapiteko; kapena akati, ‘Uyu ali kuno mʼchipinda chamʼkati,’ musakhulupirire. 27 Monga momwe mphenzi ingʼanima kuchokera kummawa kupita kumadzulo, momwemonso kudzakhala kubwera kwa Mwana wa Munthu. 28 Kulikonse kuli chinthu cha kufa, makwangwala adzasonkhanako.
29 “Akadzangotha mavuto a masiku amenewo,
“ ‘dzuwa lidzadetsedwa,
ndipo mwezi sudzawala;
nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba,
ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.’
30 “Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu. 31 Ndipo adzatuma angelo ake, ndi kulira kwa lipenga kwakukulu, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinayi, ndi kuchokera kumathero a thambo kufika mbali ina.
32 “Tsopano kuchokera ku mtengo wamkuyu phunzirani ichi: Pamene uyamba kuphukira, masamba ake akatuluka, mumadziwa kuti dzinja layandikira. 33 Momwemonso, pamene mudzaona zinthu zonsezi mudzadziwe kuti ali pafupi pa khomo penipeni. 34 Zoonadi, ndikuwuzani kuti mʼbado uwu sudzatha mpaka zinthu zonse zitachitika. 35 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Tsiku ndi Nthawi Sizidziwika
36 “Palibe amene adziwa za tsikulo kapena nthawi, angakhale angelo akumwamba, angakhale Mwana, koma Atate okha. 37 Monga momwe zinalili nthawi ya Nowa, momwemonso zidzatero pobwera kwa Mwana wa Munthu. 38 Pakuti masiku amenewo chisanafike chigumula, anthu amadya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo; 39 ndipo sanadziwe za chimene chikanachitika mpaka pamene chigumula chinafika ndi kuwamiza onse. Umu ndi mmene zidzakhalira pobwera kwa Mwana wa Munthu. 40 Amuna awiri adzakhala mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala. 41 Amayi awiri adzakhala akusinja pa mtondo; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala.
42 “Chifukwa chake yangʼanirani, popeza simudziwa tsiku lanji limene Ambuye anu adzabwera. 43 Koma zindikirani ichi: Ngati mwini nyumba akanadziwa nthawi yanji ya usiku imene mbala imabwera, sakanagona ndipo sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe. 44 Inunso tsono muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene inu simukumuyembekezera.
Wantchito Wokhulupirika ndi Wosakhulupirika
45 “Kodi wantchito wokhulupirika ndi wanzeru amene ambuye ake anamuyika kukhala woyangʼanira antchito a mʼnyumba kuti awapatse chakudya chawo pa nthawi yake ndani? 46 Chidzakhala chabwino kwa wantchitoyo ngati mbuye wake pofika adzamupeza akuchita zimenezi. 47 Zoonadi, ndikuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense. 48 Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo ndi woyipa, nati kwa iye yekha, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera,’ 49 nayamba kumenya antchito anzake, nadya ndi kumwa ndi zidakwa. 50 Mbuye wa wantchitoyo adzabwera pa tsiku limene iye samamuyembekezera ndi pa nthawi imene iye sakuyidziwa. 51 Adzamulanga koopsa ndipo adzamuyika kokhala anthu achiphamaso, kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
Vasiti Mkazi wa Mfumu Achotsedwa
1 Izi ndi zimene zinachitika pa nthawi ya ufumu wa Ahasiwero, amene analamulira zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. 2 Pa nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Ahasiwero atakhazikika pa mpando wake wa ufumu mu mzinda wa Susa, 3 ndipo mʼchaka chachitatu cha ufumu wake anakonza phwando la olemekezeka ndi nduna zake. Atsogoleri a nkhondo a ku Peresiya ndi Mediya, anthu olemekezeka pamodzi ndi nduna za mʼzigawo zonse anasonkhana kwa iye.
4 Pa nthawi yomweyi kwa masiku 180 a phwando mfumu inkaonetsa kulemera kwa ulemerero wa ufumu wake ndiponso kukongola ndi kukula kwa ufumu wake. 5 Atatha masiku amenewa, kwa masiku ena asanu ndi awiri mfumu inakonzanso phwando la anthu onse okhala mu mzinda wa Susa kuyambira anthu olemekezeka mpaka anthu wamba ku bwalo la munda la nyumba yake yaufumu. 6 Bwalo la mundali analikongoletsa ndi makatani a nsalu zoyera ndi za mtundu wamtambo zimene anazimangirira ndi zingwe za nsalu zoyera ndi zapepo ku mphete za siliva zimene anazikoloweka pa nsanamira za maburo. Anayika mipando yopumirapo yagolide ndi siliva pabwalo la miyala yoyala yamtengowapatali yofiira, ya marabulo, ndi yonyezimira. 7 Anapereka zakumwa mʼchikho zagolide zamitundumitundu, ndipo vinyo waufumu anali wochuluka kwambiri monga mwa kukoma mtima kwa mfumu. 8 Monga mwa lamulo la mfumu aliyense anamwa mʼmene anafunira, pakuti mfumu inawuza otumikira ake kuti apatse aliyense monga mwa kukonda kwake.
9 Mkazi wa mfumu Vasiti nayenso anakonzera phwando amayi ku nyumba ya ufumu ya mfumu Ahasiwero.
10 Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri, pamene mfumu Ahasiwero inaledzera ndi vinyo, inalamula adindo ofulidwa asanu ndi awiri amene ankamutumikira: Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, Abagita, Zetara, ndi Karikasi 11 kuti abwere naye mfumukazi Vasiti pamaso pa mfumu atavala chipewa chaufumu. Cholinga cha mfumu chinali choti adzamuonetse kwa anthu onse ndi olemekezeka, chifukwa anali wokongola kwambiri. 12 Koma antchito atapereka uthenga wa mfumu kwa mfumukazi, Vasiti anakana kubwera. Tsono mfumu inakwiya ndi kupsa mtima.
13 Mfumu inayankhula ndi anthu anzeru ndi ozindikira choyenera kuchita popeza chinali chikhalidwe chake kufunsa uphungu kwa akatswiri pa nkhani za malamulo ndi kuweruza kolungama. 14 Anthu amene ankakhala pafupi ndi mfumu anali awa: Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, olemekezeka asanu ndi awiri a ku Peresiya ndi Medina amene ankaloledwa mwapadera kuonana ndi mfumu ndipo anali pamwamba kwambiri mu ufumuwo.
15 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi titani naye mfumukazi Vasiti mwa lamulo, popeza sanamvere lamulo la ine mfumu Ahasiwero limene adindo ofulidwa anakamuwuza?”
16 Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero. 17 Pakuti amayi onse adzadziwa zimene wachita mfumukazi ndipo kotero adzapeputsa amuna awo ndi kunena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero analamulira kuti abwere naye mfumukazi Vasiti kwa iye koma sanapite.’ 18 Lero lomwe lino amayi olemekezeka a ku Peresiya ndi Mediya amene amva zimene wachita mfumukazi adzaganiza zochita chimodzimodzi kwa nduna zonse za mfumu. Ndipo kupeputsana ndi kukongola zidzapitirira.”
19 “Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye. 20 Ndipo lamulo la mfumuli lilengezedwa mʼdziko lake lonse ngakhale lili lalikulu, amayi onse adzapereka ulemu kwa amuna awo, amuna olemekezeka mpaka amuna wamba.”
21 Mfumu ndi nduna zake anakondwera ndi uphungu uwu, kotero mfumu inachita monga momwe ananenera Memukani. 22 Mfumu inatumiza makalata ku madera onse a ufumu wake, chigawo chilichonse mʼzilembo zawo ndi ku mtundu uliwonse mʼchiyankhulo chawochawo kulengeza kuti mwamuna ayankhule chilichonse chimene chikumukomera.
Felike Amva Mlandu wa Paulo
24 Patapita masiku asanu mkulu wa ansembe Hananiya, pamodzi ndi akuluakulu ena ndi katswiri woyankhulira anthu pa milandu wotchedwa Tertuliyo anapita ku Kaisareya ndipo anafotokoza mlandu wa Paulo kwa Bwanamkubwayo. 2 Atamuyitana Paulo, ndipo Tertuliyo anafotokozera Felike nkhani yonse ya Paulo. Iye anati, “Wolemekezeka, ife takhala pamtendere nthawi yayitali chifukwa cha inu, ndipo utsogoleri wanu wanzeru wabweretsa kusintha mʼdziko lino. 3 Wolemekezeka Felike ife timazilandira zimenezi moyamika kwambiri ponseponse ndi mwa njira iliyonse. 4 Koma kuti tisakuchedwetseni, ndikupempha kuti mwa kuleza mtima kwanu mutimvere ife.
5 “Ife tapeza kuti munthu uyu amayambitsa mavuto ndi kuwutsa mapokoso pakati pa Ayuda onse a dziko lonse lapansi. Iyeyu ndi mtsogoleri wa mpatuko wa Anazareti. 6 Anayesera ngakhale kudetsa Nyumba ya Mulungu wathu. Ndiye ife tinamugwira. 7 Koma, mkulu wa asilikali Lusiya anafika mwamphamvu namuchotsa mʼmanja mwathu. 8 Ndipo Lusiya analamula kuti amene anali naye ndi mlandu abwere kwa inu. Mukamufunsa ameneyu kwa nokha mudzadziwa choonadi cha zimene ife tikumunenera.”
9 Ayuda anavomereza nanenetsa kuti zimenezi zinali zoona.
10 Bwanamkubwayo atakodola Paulo ndi kulola kuti ayankhule, Pauloyo anati, “Ine ndikudziwa kuti inu mwakhala mukuweruza dziko lino zaka zambiri, kotero ndikukondwera kuti ndikudziteteza ndekha pamaso panu. 11 Inu mukhoza kupeza umboni wake. Sipanapite masiku khumi ndi awiri chipitireni changa ku Yerusalemu kukapembedza. 12 Amene akundiyimba mlanduwa sanandipeze mʼNyumba ya Mulungu ndi kutsutsana ndi wina aliyense kapena kuyambitsa chisokonezo mʼsunagoge kapena pena paliponse mu mzindamo. 13 Ndipo sangathe kupereka umboni wa mlandu umene akundiyimba inewu. 14 Komatu ine ndikuvomera kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu, monga wotsatira wa Njirayo, imene iwo akuyitchula mpatuko. Ine ndimakhulupirira chilichonse chimene chimagwirizana ndi malamulo ndiponso zimene zinalembedwa ndi Aneneri. 15 Ine ndili nacho chiyembekezo chomwecho chimene iwo ali nacho mwa Mulungu, kuti kudzakhala kuuka kwa akufa kwa olungama ndiponso kwa ochimwa. 16 Kotero ine ndimayesetsa kuti ndikhale ndi chikumbumtima chosanditsutsa pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.
17 “Patapita zaka zambiri, ndinabwera ku Yerusalemu kudzapereka mphatso kwa anthu osauka a mtundu wanga komanso kudzapereka nsembe. 18 Pamene ndinkachita zimenezi, iwo anandipeza mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nditachita mwambo wodziyeretsa. Panalibe gulu la anthu kapena kuti ndimachita za chisokonezo chilichonse. 19 Koma pali Ayuda ena ochokera ku Asiya, amene amayenera kukhala pano pamaso panu, kundiyimba mlandu ngati ali ndi kalikonse konditsutsa ine. 20 Kapena awa amene ali panowa anene mlandu umene anapeza mwa ine, pamene ndinayima pamaso pa Bwalo lawo Lalikulu. 21 Koma cholakwa changa chingathe kukhala chokhachi chakuti, nditayima pamaso pawo ndinafuwula kuti, ‘Mukundiweruza ine lero chifukwa ndimakhulupirira kuti akufa adzauka.’ ”
22 Kenaka Felike, amene amadziwa bwino za Njirayo, anayamba wayimitsa mlanduwo, nati, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera mkulu wa asilikali Lusiya.” 23 Iye analamulira woyangʼanira asilikali 100 kuti alondere Paulo, koma azimupatsako ufulu ndiponso kulola abwenzi ake kuti adzimusamalira.
24 Patapita masiku angapo Felike anabwera pamodzi ndi mkazi wake Drusila, amene anali Myuda. Anayitana Paulo ndipo anamvetsera zimene amayankhula za chikhulupiriro mwa Khristu Yesu. 25 Paulo atayankhula za chilungamo, za kudziretsa ndiponso za chiweruzo chimene chikubwera, Felike anachita mantha ndipo anati, “Basi tsopano! Pita. Tidzakuyitanitsa tikadzapeza mpata.” 26 Pa nthawi imeneyi amayembekeza kuti Paulo adzamupatsa ndalama, nʼchifukwa chake amamuyitanitsa kawirikawiri ndi kumayankhula naye.
27 Patapita zaka ziwiri, Porkiyo Festo analowa mʼmalo mwa Felike, koma anamusiya Paulo mʼndende, chifukwa amafuna kuti Ayuda amukonde.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.