Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 36

36 Tsono anthu a mʼdzikomo anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namuyika kukhala mfumu mu Yerusalemu mʼmalo mwa abambo ake.

Yehowahazi Mfumu ya Yuda

Yowahazi anali wa zaka 23 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa miyezi itatu. Mfumu ya Igupto inamuchotsa pa udindo wa ufumu mu Yerusalemu ndipo inakhometsa msonkho dziko la Yuda wa makilogalamu 3,400 asiliva ndi agolide. Mfumu ya Igupto inakhazika Eliyakimu, mʼbale wake wa Yehowahazi kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu ndipo anasintha dzina la Eliyakimu kukhala Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yowahazi mʼbale wake wa Eliyakimu ndi kupita naye ku Igupto.

Yehoyakimu Mfumu ya Yuda

Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wake. Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anachita naye nkhondo ndipo anamumanga ndi zingwe zamkuwa ndi kumutenga kupita naye ku Babuloni. Nebukadinezara anatenganso zipangizo za ku Nyumba ya Yehova kupita nazo ku Babuloni ndipo anaziyika mʼnyumba ya Mulungu wake kumeneko.

Zochitika zina za pa ulamuliro wa Yehoyakimu, zinthu zonyansa zimene anachita ndi zonse zinapezeka kuti zinali zomutsutsa zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda. Ndipo Yehoyakini mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Yehoyakini Mfumu ya Yuda

Yehoyakini anali ndi zaka 21 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa miyezi itatu ndi masiku khumi. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. 10 Nthawi ya mphukira, mfumu Nebukadinezara inayitanitsa Yehoyakini ndipo inapita naye ku Babuloni, pamodzi ndi ziwiya zamtengowapatali za mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova, ndipo anayika Zedekiya malume wake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.

Zedekiya Mfumu ya Yuda

11 Zedekiya anali ndi zaka 21 pamene ankakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. 12 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wake ndipo sanadzichepetse yekha pamaso pa mneneri Yeremiya amene ankayankhula mawu a Yehova. 13 Iye anawukiranso mfumu Nebukadinezara amene anamulumbiritsa mʼdzina la Mulungu. Iyeyo anali wosamva ndipo anawumitsa mtima wake. Sanatembenukire kwa Yehova Mulungu wa Israeli. 14 Kuwonjezera apo, atsogoleri onse a ansembe ndi anthu ena anapitirapitira kukhala osakhulupirika, kutsatira machitidwe onse onyansa a mitundu ina ndi kudetsa Nyumba ya Yehova Mulungu wawo, imene anayipatula mu Yerusalemu.

Kugwetsedwa kwa Yerusalemu

15 Yehova, Mulungu wa makolo awo, ankatumiza mawu kwa iwo kudzera kwa amithenga ake kawirikawiri, chifukwa ankawamvera chisoni anthu ake ndi malo ake okhalapo. 16 Koma iwo ananyoza amithenga a Mulungu, anapeputsa mawu awo ndipo ankaseka aneneri ake mpaka anawutsa mkwiyo wa Yehova pa anthu ake ndipo panalibenso mankhwala owachiritsa. 17 Yehova anabweretsa mfumu ya anthu a ku Babuloni, imene inapha anyamata awo ndi lupanga ku malo opatulika, ndipo sanasiye kaya mnyamata kapena mtsikana, wamkulu kapena wokalamba. Mulungu anapereka onsewo kwa Nebukadinezara. 18 Iye ananyamula kupita nazo ku Babuloni zipangizo zonse za mʼNyumba ya Yehova Mulungu wawo, zazikulu ndi zazingʼono zomwe, ndi chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso chuma cha mfumu ndi akuluakulu ake. 19 Iwo anayatsa moto Nyumba ya Mulungu, ndipo anagwetsa makoma a Yerusalemu. Anatentha moto nyumba zonse zaufumu ndipo anawononga chilichonse chimene chinali chofunika.

20 Iye anagwira ukapolo anthu otsala amene anapulumuka ku lupanga ndi kupita nawo ku Babuloni, ndipo anakhala antchito ake ndi ana ake mpaka pamene ufumu wa Peresiya unakhazikitsidwa. 21 Dziko linakondwera ndi masabata ake. Pa nthawi yonse ya chipasuko chake nthaka inapuma, mpaka zaka 70 zinakwana pokwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya.

22 Mʼchaka choyamba cha Koresi mfumu ya Peresiya, pofuna kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anakhudza mtima wa mfumu ya Peresiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse ndipo anazilemba:

23 Chimene mfumu Koresi ya Peresiya ikunena ndi ichi:

“Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa ine mafumu onse a dziko lapansi ndipo wandisankha kuti ndimumangire Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ku Yuda. Aliyense wa anthu ake pakati panu, Yehova Mulungu wake akhale naye, ndipo apite.”

Chivumbulutso 22

Mtsinje Wamoyo

22 Ndipo mngeloyo anandionetsa mtsinje wamadzi amoyo, oyera ngati mwala wa krustalo ukutuluka ku mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa, Ukuyenda pakati pa msewu waukulu wa mu mzindawo. Mbali iliyonse ya mtsinjewo kunali mtengo wamoyo, utabala zipatso khumi ndi ziwiri. Kubereka zipatso mwezi uliwonse. Ndipo masamba a mtengowo ndi mankhwala wochiritsa anthu a mitundu ina. Sipadzakhalanso temberero lililonse. Mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa udzakhala mu mzindawo, ndipo atumiki ake adzamutumikira. Iwo adzaona nkhope yake ndipo dzina lake lidzalembedwa pa mphumi zawo. Sipadzakhalanso usiku. Sadzafuna kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuwala kwawo. Ndipo adzalamulira kwamuyaya.

Mngeloyo anandiwuza kuti, “Mawu awa ndi okhulupirika ndi owona. Ambuye Mulungu wa mizimu ya aneneri anatumiza mngelo wake kudzaonetsa atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.”

Yesu Akubweranso

“Taonani, ndikubwera posachedwa! Wodala ndi amene asunga mawu oneneratu za kutsogolo a mʼbuku ili.”

Ine Yohane, ndine amene ndinamva ndi kuona zinthu izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kuona izi ndinagwa pansi kuti ndipembedze mngelo amene amandionetsa zimenezi. Koma mngeloyo anandiwuza kuti, “Usatero ayi! Ine ndine wotumikira monga iwe pamodzi ndi abale ako aneneri ndi onse amene amasunga mawu a mʼbuku pembedzani Mulungu.”

10 Kenaka anandiwuza kuti, “Usabise mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili chifukwa nthawi yayandikira. 11 Wochita zoyipa apitirire kuchita zoyipazo; wochita zonyansa apitirire kuchita zonyansazo; wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo; ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.”

Mawu Otsiriza: Kuyitanidwa ndi Chenjezo

12 “Taonani, ndikubwera posachedwa! Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense malinga ndi zimene anachita. 13 Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimaliziro ndine.

14 “Odala amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wopita ku mtengo wamoyo ndi kuti akalowe mʼzipata za mu mzindawo. 15 Kunja kuli agalu, amatsenga, achiwerewere, akupha anthu, opembedza mafano ndi aliyense amene amakonda bodza ndi kulichita.

16 “Ine Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti achitire umboni uwu ku mipingo. Ine ndine Muzu ndi Chipatso cha Davide ndipo ndine Nthanda Yonyezimira.”

17 Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.

18 Ndikuchenjeza aliyense amene akumva mawu onena zamʼtsogolo a mʼbukuli kuti, “Ngati wina awonjezerapo kalikonse, Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mʼbuku ili. 19 Ndipo wina akachotsapo mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili, Mulungu adzachotsa gawo lake pa mtengo wamoyo ndi la mu mzinda woyera zimene zanenedwa mʼbuku ili.”

20 Iye amene akuchitira umboni pa zinthu izi akuti, “Inde, Ine ndikubwera posachedwa.”

Ameni. Bwerani Ambuye Yesu.

21 Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi anthu onse. Ameni.

Malaki 4

Tsiku la Yehova

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi. Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola. Tsiku limenelo inu mudzapondereza anthu oyipa; adzakhala phulusa ku mapazi anu pa tsiku limene Ine ndidzachite zinthu zimenezi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Kumbukirani zophunzitsa za mtumiki wanga Mose, malamulo ndi malangizo amene ndinamupatsa pa Horebu kuti awuze Aisraeli onse.

“Taonani, ndidzakutumizirani mneneri Eliya lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. Iye adzabweza mitima ya makolo kwa ana awo, ndi mitima ya ana kwa makolo awo. Kupanda kutero ndidzabwera kudzakantha dziko lanu ndi temberero.”

Yohane 21

Yesu Aonekera kwa Ophunzira ku Nyanja ya Tiberiya

21 Zitatha izi Yesu anaonekeranso kwa ophunzira ake, mʼmbali mwa nyanja ya Tiberiya. Anadzionetsera motere: Simoni Petro, Tomasi (otchedwa Didimo), Natanieli wochokera ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzira ena awiri anali limodzi. Simoni Petro anawawuza iwo kuti, “Ine ndikupita kukasodza,” ndipo iwo anati, “ife tipita nawe.” Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.

Mmamawa, Yesu anayimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzira ake sanazindikire kuti anali Yesu.

Yesu anawafunsa iwo kuti, “Anzanga, kodi muli nsomba?”

Iwo anayankha kuti, “Ayi.”

Iye anati, “Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu.” Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba.

Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, “Ndi Ambuye!” Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja. Ophunzira enawo analowa mʼbwato akukoka ukonde odzaza ndi nsomba, popeza iwo sanali kutali kuchokera ku mtunda, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi. Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi.

10 Yesu anawawuza kuti, “Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo.”

11 Simoni Petro anakwera mʼbwato ndi kukokera khoka ku gombe, lodzaza ndi nsomba zikuluzikulu 153, komabe ndi nsomba zochuluka chotero khoka silinangʼambike. 12 Yesu anawawuza kuti, “Bwerani mudzalandire chakudya chammawa.” Palibe mmodzi wa ophunzira anayesa kumufunsa Iye, “Kodi ndinu ndani?” Iwo anadziwa kuti anali Ambuye. 13 Yesu anabwera, natenga buledi ndikuwapatsa iwo, ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsomba. 14 Aka kanali tsopano kachitatu Yesu akuonekera kwa ophunzira ake Iye ataukitsidwa kwa akufa.

Yesu Abwezeretsa Petro

15 Iwo atamaliza kudya chakudya chammawa, Yesu anati kwa Simoni Petro, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda Ine kuposa mmene amandikondera awa?”

Iye anati, “Inde Ambuye, Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”

Yesu anati, “Samala ana ankhosa anga.”

16 Yesu anatinso, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”

Iye anayankha kuti, “Inde, Ambuye, Inu mukudziwa kuti ine ndimakukondani.”

Yesu anati, “Weta nkhosa zanga.”

17 Yesu anati kwa iye kachitatu, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”

Petro anadzimvera chisoni chifukwa Yesu anamufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda Ine?” Iye anati, “Ambuye, Inu mudziwa zinthu zonse. Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”

Yesu anati, “Dyetsa nkhosa zanga. 18 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngʼono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita.” 19 Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”

20 Petro anatembenuka ndi kuona kuti ophunzira amene Yesu amamukonda amawatsatira iwo. (Uyu ndi amene anatsamira pachifuwa cha Yesu pa chakudya chamadzulo ndipo iye anati, “Ambuye, kodi ndi ndani amene adzakuperekani Inu?” 21 Petro atamuona iye, anafunsa kuti, “Ambuye, nanga uyu?”

22 Yesu anayankha kuti, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo? Iwe uyenera kunditsata Ine.” 23 Chifukwa cha ichi mbiri inafala pakati pa abale kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kuti iye sadzafa. Iye anati, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo?”

24 Uyu ndi wophunzira amene akuchitira umboni ndipo ndi amene analemba. Ife tidziwa kuti umboni wake ndi woona.

25 Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anachita. Zikanalembedwa zonsezi, ndikhulupirira dziko lonse lapansi likanasowa malo osungirako mabuku onse amene akanalembedwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.