Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 35

Yosiya Achita Chikondwerero cha Paska

35 Yosiya anachita chikondwerero cha Paska wa Yehova mu Yerusalemu, ndipo mwana wankhosa wa Paska anaphedwa pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba. Iye anasankha ansembe pa maudindo awo ndipo anawalimbikitsa pa ntchito ya mʼnyumba ya Yehova. Iye anati kwa Alevi amene amalangiza Aisraeli onse omwe anadzipatula kwa Yehova: Ikani bokosi lopatulika mʼNyumba ya Mulungu amene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli anamanga. Lisamanyamulidwe pa mapewa anu. Tsopano tumikirani Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisraeli. Mukhale mʼmagulu anu molingana ndi mabanja anu, molingana ndi momwe analembera Davide mfumu ya Israeli ndiponso mwana wake Solomoni.

“Muziyima ku malo opatulika pamodzi ndi gulu la Alevi oyimira gulu lililonse lalingʼono la mabanja a abale anu amene ndi anthu wamba. Muzipha ana ankhosa a Paska, muzidzipatula nokha ndi kuwakonzera abale anu ana ankhosa awo, kuchita zimene Yehova analamulira mwa Mose.”

Yosiya anapereka kwa anthu wamba onse ana ankhosa ndi ana ambuzi okwanira 30,000 ndi ngʼombe zazimuna 3,000, zopereka za Paska zonse zochokera pa chuma chake cha mfumu.

Akuluakulu akenso anapereka mwaufulu kwa anthu ndi kwa ansembe ndi Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehieli oyangʼanira ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu anapereka kwa ansembe zopereka za Paska 2,600 ndi ngʼombe 300. Konaniya nayenso pamodzi ndi Semaya ndi Netaneli, abale ake ndi Hasabiya, Yeiyeli ndi Yozabadi, atsogoleri a Alevi, anapereka nsembe za Paska 5,000 ndi ngʼombe 500 kwa Alevi.

10 Mwambo unakonzedwa ndipo ansembe anayima pamalo pawo pamodzi ndi Alevi mʼmagulu awo monga mfumu inalamulira. 11 Ana ankhosa a Paska anaphedwa ndipo ansembe anawaza magazi amene anaperekedwa kwa iwo pamene Alevi anali kusenda nyamazo. 12 Iwo anayika padera nsembe zopsereza kuti azipereke kwa magulu angʼonoangʼono a mabanja a anthu kuti apereke kwa Yehova monga zinalembedwa mʼbuku la Mose. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi ngʼombe. 13 Anawotcha nyama za Paska monga momwe zinalembedwera ndi kuwiritsa zopereka zopatulika mʼmiphika, mʼmitsuko ndi mʼziwaya ndipo anazipereka mofulumira kwa anthu onse. 14 Izi zitatha, anakonza zawo ndi za ansembe chifukwa ansembe, zidzukulu za Aaroni, anali otanganidwa kupereka nsembe zopsereza ndi mafuta a nyama mpaka madzulo. Choncho Alevi amakonza zawo ndi za ansembe, ana a Aaroni.

15 Anthu oyimba nyimbo, zidzukulu za Asafu, anali pa malo awo potsata zomwe analemba Davide, Asafu, Hemani ndi Yedutuni mlosi wa mfumu. Alonda apazipata anali pa chipata chilichonse ndipo kunali kosafunika kuti achoke pa ntchito yawo, poti abale awo Alevi ankawakonzera zonse.

16 Kotero pa nthawi imeneyi ntchito yonse ya Yehova ya chikondwerero cha Paska ndi nsembe zopsereza pa guwa la Yehova inachitika monga analamulira mfumu Yosiya. 17 Aisraeli amene analipo anachita chikondwerero cha Paska pa nthawi imeneyi ndi kuchita mwambo wa chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti, kwa masiku asanu ndi awiri. 18 Paska yofanana ndi iyi sinachitikepo ku Israeli kuyambira nthawi ya Samueli ndipo palibe mmodzi mwa mafumu a Israeli anachitapo chikondwerero cha Paska ngati anachitira Yosiya pamodzi ndi ansembe, Alevi ndi Ayuda onse ndi Aisraeli amene anali pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu. 19 Chikondwerero cha Paska ichi chinachitika mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya.

Imfa ya Yosiya

20 Zimenezi zitachitika, pamene Yosiya anakonzanso Nyumba ya Mulungu, Neko mfumu ya Igupto inapita kukachita nkhondo ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate, ndipo Yosiya anapita kukamenyana naye. 21 Koma Neko anatumiza amithenga kwa iye kunena kuti, “Kodi pali mkangano wanji pakati pa iwe ndi ine, iwe mfumu ya Yuda? Ine sindikuthira nkhondo iwe pa nthawi ino, koma nyumba imene ndili nayo pa nkhondo. Mulungu wandiwuza kuti ndifulumize choncho leka kutsutsana ndi Mulungu amene ali ndi ine, mwina adzakuwononga.”

22 Komabe Yosiya sanatembenuke kumusiya iyeyo, koma anadzizimbayitsa ndi kukalowa mʼnkhondo. Iye sanamvere zimene Neko ananena molamulidwa ndi Mulungu koma anapita kukamenyana naye ku chigwa ku Megido.

23 Anthu oponya mivi analasa mfumu Yosiya, ndipo iye anawuza akuluakulu ake, “Chotseni. Ndavulazidwa kwambiri.” 24 Choncho anamuchotsa iye mʼgaleta lake, ndipo anamuyika mʼgaleta lina limene anali nalo ndipo anabwera naye ku Yerusalemu kumene anamwalirira. Iye anayikidwa mʼmanda a makolo ake. Ndipo Ayuda ndi Yerusalemu yense anamulira.

25 Yeremiya anapeka nyimbo za maliro chifukwa cha Yosiya, ndipo mpaka lero lino amuna ndi akazi onse oyimba amakumbukira Yosiya pa nyimbo zawo za maliro. Izi zinakhala mwambo mu Israeli ndipo zinalembedwa mʼNyimbo za Maliro.

26 Zochitika zina za ulamuliro wa Yosiya ndi ntchito za kudzipereka kwake, monga zinalembedwa mʼMalamulo a Yehova, 27 zochitika zonse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda.

Chivumbulutso 21

Kumwamba ndi Dziko Lapansi Zatsopano

21 Kenaka ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinapita ndipo kunalibenso nyanja ina iliyonse. Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. ‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”

Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, “Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!” Ndipo anati, “Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona.”

Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo. Iye amene adzapambane adzalandira zonsezi, ndipo ndidzakhala Mulungu wake ndi Iye adzakhala mwana wanga. Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.”

Mzinda wa Yerusalemu Watsopano

Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja, anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri anandiwuza kuti, “Bwera, ine ndidzakuonetsa mkwatibwi wa Mwana Wankhosa.” 10 Ndipo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku phiri lalikulu ndi lalitali nandionetsa mzinda wopatulika, Yerusalemu ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu. 11 Unawala ndi ulemerero wa Mulungu, ndipo kuthwanima kwake kunali ngati mwala wamtengowapatali, ngati jasipa; woyera ngati krustalo. 12 Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali, unali ndi zipata khumi ndi ziwiri, ndipo panali angelo khumi ndi awiri. Pa chipata chilichonse panayima mngelo. Pa chipata chilichonse panalembedwa dzina la fuko la Israeli. 13 Kummawa kunali zipata zitatu, kumpoto zitatu, kummwera zitatu ndi kumadzulo zitatu. 14 Mpanda wa mzindawu unali ndi maziko khumi ndi awiri ndipo pa mazikopo panali mayina khumi ndi awiri a atumwi a Mwana Wankhosa.

15 Mngelo amene ankayankhula nane uja anali ndi ndodo yagolide yoyezera mzindawo, zipata zake ndi mpanda wake. 16 Mzindawo unamangidwa mofanana kutalika kwake, mulitali ndi mulifupi munali mofanana. Anayeza mzindawo ndi ndodo ija ndipo anapeza kuti mulitali, mulifupi ndi msinkhu wake kutalika kwake kunali makilomita 2,200. 17 Anayesa mpanda uja ndipo kuchindikala kwake kunali kopitirirapo mamita 65 monga mwa muyeso wa anthu umene mngelo anagwiritsa ntchito. 18 Mpandawo unapangidwa ndi yasipa, ndipo mzindawo unali wagolide oyengeka owala ngati galasi. 19 Maziko a mpanda wa mzindawo anali okongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali ya mtundu uliwonse. Maziko oyamba anali yasipa, achiwiri anali safiro, achitatu ndi kalikedo, achinayi ndi simaragido, 20 achisanu ndi sardiyo, achisanu ndi chiwiri ndi krusolito, achisanu ndi chitatu ndi berulo, achisanu ndi chinayi ndi topaziyo, a khumi ndi krusoprazo, a khumi ndi chimodzi ndi huakito, a khumi ndi chiwiri ndi emetusto. 21 Zipata khumi ndi ziwiri zija zinapangidwa ndi ngale, chipata chilichonse chinapangidwa ndi ngale imodzi. Misewu ya mzindawo inali yopangidwa ndi golide oyengeka, owala ngati galasi.

22 Ine sindinaone Nyumba ya Mulungu iliyonse mu mzindawo chifukwa Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse ndi Mwana Wankhosa ndiwo Nyumba yake. 23 Palibe chifukwa choti dzuwa kapena mwezi ziwale popeza mu mzindawo ulemerero wa Mulungu ndiwo umawalamo ndipo nyale yake ndi Mwana Wankhosa uja. 24 Mitundu ya anthu idzayenda mʼkuwala kwake ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mu mzindamo. 25 Zipata zake sizidzatsekedwa ngakhale tsiku limodzi lomwe pakuti sikudzakhala usiku kumeneko. 26 Ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu adzapita nazo kumeneko. 27 Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.

Malaki 3

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga amene adzakonza njira pamaso panga. Kenaka mwadzidzidzi Ambuye amene mukumufunafuna adzafika ku Nyumba yake. Mthenga wapangano amene mukumuyembekezera adzabwera.”

Koma ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Ndani adzatha kuyima pamene Iye wafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wa pa ngʼanjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa. Iye adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri woyenga ndi woyeretsa siliva. Iye adzayeretsa Alevi ndi kuwayenga ngati golide ndi siliva. Pamenepo Yehova adzakhala ndi anthu amene azidzabweretsa zopereka mwachilungamo, ndipo Yehova adzalandira zopereka za Yuda ndi Yerusalemu, ngati masiku akale, masiku amakedzana.

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsono ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Mosataya nthawi ndidzanena mawu otsutsa mfiti, achigololo, a umboni wonama, amene salipira bwino antchito awo, amene amazunza akazi ndi ana amasiye, amene saweruza alendo mwachilungamo, komanso amene sandiopa Ine.”

Kuba za Mulungu

“Ine ndine Yehova, ndipo sindisintha. Choncho inu zidzukulu za Yakobo, simunawonongedwe. Kuyambira nthawi ya makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga ndipo simunawatsatire. Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Tibwerere motani kwa Yehova?’

“Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera.

“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’

“Pa zakhumi ndi pa zopereka. Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. 10 Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga.” Akutero Yehova Wamphamvuzonse, “Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo. 11 Ndidzaletsa tizirombo kuti tisawononge mbewu zanu, ndipo mpesa wa mʼminda mwanu zipatso zake sizidzayoyoka,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 12 “Motero anthu amitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

13 Yehova akuti, “Mwayankhula mawu owawa onena za Ine.

“Komabe inu mukufunsa kuti, ‘Kodi tanena chiyani chotsutsana nanu?’

14 “Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nʼkosapindulitsa. Kodi timapindulanji pochita zofuna zake, ndi kumayenda ngati anamfedwa pamaso pa Yehova Wamphamvuzonse? 15 Koma tsono ife timati anthu odzikuza ndiye odalitsika. Kunena zoona anthu oyipa ndiye amapeza bwino, ngakhale amene amanyoza Mulungu amapulumuka.’ ”

16 Ndipo woopa Yehova anayamba kukambirana, ndipo Yehova anamvetsera. Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, lonena za amene amaopa Yehova ndi kulemekeza dzina lake.

17 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, tsiku limene Ine ndidzachita izi, adzakhala angaanga. Ndidzawaleka osawalanga monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira. 18 Pamenepo mudzaonanso kusiyana pakati pa anthu olungama ndi oyipa, pakati pa amene amatumikira Mulungu ndi amene satumikira Mulungu.”

Yohane 20

Yesu Auka kwa Akufa

20 Mmamawa tsiku loyamba la sabata, kukanali kamdimabe, Mariya wa ku Magadala anapita ku manda ndipo anaona kuti mwala unali utachotsedwa pa khomo la manda. Choncho anabwerera akuthamanga kwa Simoni Petro ndi wophunzira winayo, amene Yesu anamukonda, ndipo anati, “Iwo amuchotsa Ambuye mʼmanda, ndipo ife sitikudziwa kumene iwo amuyika Iye!”

Choncho Petro ndi wophunzira winayo ananyamuka kupita ku manda. Onse awiri anathamanga pamodzi koma wophunzira winayo anamupitirira Petro, nafika ku manda moyambirira. Ndipo mmene anawerama nasuzumira mʼkati mwa manda anaona nsalu zili potero koma sanalowemo. Kenaka Simoni Petro, amene anali pambuyo pake, anafika ndi kulowa mʼmanda. Iye anaona nsaluzo zili pamenepo, pamodzinso ndi nsalu imene anakulungira nayo mutu wa Yesu. Nsaluyi inali yopindidwa pa yokha yosiyanitsidwa ndi inayo. Pomaliza wophunzira winayo, amene anafika ku manda moyambirira, analowanso mʼkati, iye anaona ndi kukhulupirira. (Iwo sanazindikire kuchokera mʼmalemba kuti Yesu anayanera kuuka kuchokera kwa akufa).

Yesu Aonekera kwa Mariya wa ku Magadala

10 Kenaka ophunzira anabwerera ku nyumba zawo, 11 koma Mariya anayima kunja kwa manda akulira. Pamene akulira, anawerama ndi kusuzumira mʼmanda 12 ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, atakhala pamene panali mtembo wa Yesu, mmodzi kumutu ndi wina kumapazi.

13 Iwo anamufunsa iye kuti, “Amayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?”

Iye anati, “Amuchotsa Mbuye wanga, ndipo ine sindikudziwa kumene iwo amuyika.” 14 Atanena izi, iye anatembenuka ndipo anaona Yesu atayima potero koma iye sanazindikire kuti anali Yesu.

15 Iye anati, “Amayi, mukulira chifukwa chiyani? Ndani amene mukumufunafuna?”

Poganiza kuti anali mwini munda, iye anati, “Bwana, ngati inu mwamuchotsa, ndiwuzeni kumene mwamuyika, ndipo ine ndikamutenga.”

16 Yesu anati kwa iye, “Mariya.”

Anatembenukira kwa Iye nafuwula mu Chiaramaiki kuti, “Raboni!” (kutanthauza Mphunzitsi).

17 Yesu anati, “Usandigwire Ine, pakuti sindinapite kwa Atate. Mʼmalo mwake pita kwa abale anga ndikukawawuza kuti, ndikupita kwa Atate ndi kwa Atate anunso, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanunso.”

18 Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzira ndi uthenga wakuti, “Ndamuona Ambuye!” Iye anawawuza iwo kuti Yesu ananena zinthu izi kwa iye.

Yesu Aonekera kwa Ophunzira ake Tomasi Palibe

19 Madzulo a tsiku limenelo limene linali loyamba la Sabata ophunzira ake ali pamodzi, atatseka ndi kukhoma zitseko chifukwa choopa Ayuda, Yesu anabwera ndi kuyima pakati pawo nati, “Mtendere ukhale nanu!” 20 Iye atatha kunena izi, anawaonetsa manja ake ndi mʼnthiti mwake. Ophunzira anasangalala kwambiri pamene anaona Ambuye.

21 Yesu anatinso, “Mtendere ukhale nanu! Monga Atate anandituma Ine, Inenso ndikukutumani.” 22 Ndi mawu amenewo Iye anawapumira ndipo anati, “Landirani Mzimu Woyera. 23 Ngati mukhululukira aliyense machimo ake, iwo akhululukidwa; ngati simuwakhululukira, iwo sanakhululukidwe.”

Yesu Aonekera kwa Tomasi

24 Koma Tomasi (otchedwa Didimo), mmodzi wa khumi ndi awiriwo, sanali ndi ophunzira pamene Yesu anabwera. 25 Ophunzira enawo atamuwuza Tomasi kuti iwo anaona Ambuye, iye ananenetsa kuti, “Pokhapokha nditaona zizindikiro za misomali mʼmanja ake ndi kuyikamo chala changa mʼmene munali misomali ndi kukhudza dzanja langa mʼnthiti mwake, ine sindidzakhulupirira.”

26 Patapita sabata, ophunzira ake analinso mʼnyumbamo ndipo Tomasi anali nawo. Ngakhale makomo anali otsekedwa, Yesu anabwera nayima pakati pawo, ndipo anati, “Mtendere ukhale nanu!” 27 Kenaka anati kwa Tomasi, “Ika chala chako apa; ona manja anga. Tambasula dzanja lako ndi kukhudza mʼnthiti mwanga. Leka kukayika, khulupirira.”

28 Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!”

29 Kenaka Yesu anamuwuza kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”

Cholinga cha Uthenga Wabwino wa Yohane

30 Yesu anachita zodabwitsa zambiri pamaso pa ophunzira ake zimene sizinalembedwe mʼbuku lino. 31 Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.