M’Cheyne Bible Reading Plan
Senakeribu Aopseza Yerusalemu
32 Zitatha zonse zimene Hezekiya anachita mokhulupirika, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anabwera ndi kuthira nkhondo dziko la Yuda. Iye anazinga mizinda yotetezedwa ya Yuda, kuganiza kuti ayigonjetsa. 2 Pamene Hezekiya anaona kuti Senakeribu wabwera ndipo wakonzeka kuchita nkhondo ndi Yerusalemu, 3 iye anakambirana ndi akuluakulu ake pamodzi ndi atsogoleri a gulu lankhondo za kutseka akasupe ochoka ku kasupe amene anali kunja kwa mzinda, ndipo iwo anamuthandiza. 4 Gulu lalikulu la anthu linasonkhana, ndipo anatseka akasupe onse pamodzi ndi mtsinje umene umayenda mʼkati mwa nthakamo. Iwo ankanena kuti, “Nʼchifukwa chiyani mafumu a Asiriya akabwera kuno adzapeze madzi ambiri?” 5 Kenaka iye anagwira ntchito molimbika kukonza madera ogumuka a khoma ndi kumangapo msanja. Anamanganso mpanda wina kunja kwa mpanda winawo ndipo anamanga zolimbitsa Milo ku mzinda wa Davide.
6 Iye anasankha atsogoleri a ankhondo olamulira anthu ndipo anawasonkhanitsa pamaso pake pa bwalo la chipata cha mzinda ndi kuwalimbikitsa ndi mawu awa: 7 “Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite mantha kapena kutaya mtima chifukwa cha mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lalikulu lankhondo limene ali nalo, pakuti ife tili ndi mphamvu yayikulu kuposa imene ili ndi iye. 8 Iye ali ndi mphamvu ya anthu basi, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kutithandiza ndi kuchita nkhondo zathu.” Ndipo anthu anapeza chilimbikitso kuchokera pa zimene Hezekiya mfumu ya Yuda ananena.
9 Nthawi ina, pamene Senakeribu mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo anali atazinga Lakisi, iye anatumiza atsogoleri ake ankhondo ku Yerusalemu ndi uthenga uwu kwa Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a ku Yuda amene anali kumeneko:
10 “Senakeribu mfumu ya ku Asiriya akuti: Kodi inu mukukhulupirira chiyani, kuti mukukhalabe mu Yerusalemu mutazingidwa? 11 Pamene Hezekiya akunena kuti ‘Yehova Mulungu wathu adzatipulumutsa kuchoka mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya,’ iye akukusocheretsani, kuti mufe ndi njala ndi ludzu. 12 Kodi si Hezekiya amene anachotsa malo opembedzerapo Mulungu ameneyu ndi maguwa ansembe ndi kunena kwa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe limodzi ndi kupserezapo nsembe?’
13 “Kodi inu simukudziwa zimene ine ndi makolo anga tachita kwa anthu a mitundu ina? Kodi milungu ya mitundu imeneyi inatha kupulumutsa dziko lawo kuchoka mʼdzanja langa? 14 Kodi ndi milungu iti mwa milungu ya mitundu ina ya anthuwo, imene makolo anga anayiwononga kotheratu, inatha kupulumutsa anthu ake mʼdzanja langa? Nanga tsono Mulungu wanuyo adzakupulumutsani mʼdzanja langa motani? 15 Choncho inu musalole kuti Hezekiya akunamizeni ndi kukusocheretsani motere. Musamukhulupirire, pakuti palibe mulungu wa mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse umene unatha kupulumutsa anthu ake kuchoka mʼdzanja langa kapena mʼdzanja la makolo anga. Nanga bwanji Mulungu wanuyo, sadzatha kukupulumutsani kuchoka mʼdzanja langa!”
16 Atsogoleri a ankhondo a Senakeribu anapitiriza kuyankhula zotsutsana ndi Yehova Mulungu ndi mtumiki wake Hezekiya. 17 Mfumunso inalemba makalata onyoza Yehova, Mulungu wa Israeli, ndipo inanena zotsutsana naye izi: “Monga momwe milungu ya anthu a mayiko ena sinathe kuwapulumutsa kuchoka mʼdzanja langa, chonchonso Mulungu wa Hezekiya sadzapulumutsa anthu ake kuchoka mʼdzanja langa.” 18 Kenaka iwo anafuwula mu Chihebri kwa anthu a mu Yerusalemu amene anali pa khoma, kuwaopseza ndi kuwachititsa mantha ndi cholinga choti alande mzindawo. 19 Iwo anayankhula za Mulungu wa Yerusalemu monga anayankhulira za milungu ya anthu ena a pa dziko lapansi, ntchito ya manja a anthu.
20 Mfumu Hezekiya ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi anafuwulira kumwamba mʼpemphero chifukwa cha zimenezi. 21 Ndipo Yehova anatumiza mngelo amene anadzapha anthu onse odziwa nkhondo ndi atsogoleri ndiponso oyangʼanira misasa ya mfumu ya ku Asiriya. Choncho Senakeribu anabwerera kwawo wamanyazi. Ndipo atalowa mʼnyumba ya mulungu wake, ena mwa ana ake anamupha ndi lupanga.
22 Kotero Yehova anapulumutsa Hezekiya ndi anthu a ku Yerusalemu kuchoka mʼdzanja la Senakeribu mfumu ya ku Asiriya ndi mʼdzanja la anthu ena. Yehova anawateteza ku mbali zonse. 23 Anthu ambiri anabweretsa zopereka kwa Yehova ku Yerusalemu ndi mphatso zamtengowapatali kwa Hezekiya mfumu ya Yuda. Kuyambira nthawi imeneyo Hezekiya ankalemekezedwa kwambiri ndi mitundu ina yonse.
Kunyada, Kupambana ndi Imfa ya Hezekiya
24 Pa nthawi imeneyo Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Iye anapemphera kwa Yehova, amene anamuyankha ndi kumupatsa chizindikiro chodabwitsa. 25 Koma Hezekiya anali ndi mtima wonyada ndipo sanachite molingana ndi kukoma mtima kumene Mulungu anamuonetsera. Choncho mkwiyo wa Yehova unali pa iye ndi pa Yuda ndi Yerusalemu. 26 Koma kenaka Hezekiya analapa za kunyada kwakeko, monga anachitanso anthu a mu Yerusalemu. Choncho mkwiyo wa Yehova sunafike pa iwo pa nthawi ya Hezekiya.
27 Hezekiya anali ndi chuma ndi ulemu wambiri ndipo anamanga nyumba zosungiramo chuma cha siliva wake ndi golide ndi za miyala yokongola, zokometsera zakudya, zishango ndi mtundu uliwonse wa zinthu zamtengowapatali. 28 Iye anamanganso nyumba zosungiramo tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta a olivi, ndiponso anamanga nyumba zodyeramo ngʼombe zosiyanasiyana, ndi makola a nkhosa. 29 Iyeyo anamanga midzi ndipo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, pakuti Mulungu anamupatsa chuma chambiri.
30 Ndi Hezekiya amene anatseka ku mtunda kwa kasupe wa Gihoni, ndi kumuwongolera kuti madzi ake apite mbali ya kumadzulo kwa Mzinda wa Davide. Iye ankachita bwino pa ntchito iliyonse imene ankagwira. 31 Koma pamene nthumwi zotumizidwa ndi atsogoleri a ku Babuloni zinabwera kudzamufunsa za chizindikiro chozizwitsa chimene chinachitika mʼdzikomo, Mulungu anamusiya yekha, kumuyesa kuti adziwe zonse zimene zinali mu mtima mwake.
32 Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Hezekiya ndi ntchito za kudzipereka kwake zalembedwa mʼmasomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli. 33 Hezekiya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pa phiri pamene pali manda a zidzukulu za Davide. Ayuda onse ndi anthu a mu Yerusalemu anamulemekeza atamwalira. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Kugwa kwa Babuloni
18 Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero. 2 Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti:
“ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’
Wasandulika mokhalamo ziwanda
ndi kofikako mizimu yonse yoyipa
ndi mbalame zonse zonyansa
ndi zodetsedwa.
3 Pakuti mayiko onse amwa
vinyo ozunguza mutu wazigololo zake.
Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo,
ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.”
Awachenjeza kuti Athawe Chiweruzo cha Babuloni
4 Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti:
“ ‘Anthu anga tulukani, mwa iye,’
mungachimwe naye
kuti musadzalandire nawo gawo lililonse la miliri yake;
5 pakuti machimo ake awunjikana mpaka kumwamba,
ndipo Mulungu wakumbukira milandu yake.
6 Bwezerani Iye monga momwe iye anakuchitirani.
Mubwezereni mowirikiza pa zimene anachita.
Mumusakanizire magawo awiri kuchokera mʼchikho chake.
7 Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambiri
monga mwaulemerero ndi zolakalaka
zimene anadzaza mu mtima mwake. Iye anadzikuza nʼkumati,
‘Ndinakhala monga mfumu yayikazi,
ine sindine wamasiye
ndipo sindidzalira maliro.’
8 Chifukwa chake miliri yake idzamugonjetsa tsiku limodzi;
imfa, kulira maliro ndi njala.
Iye adzanyeka ndi moto
pakuti wamphamvu ndi Mulungu Ambuye amene wamuweruza.
Tsoka la Babuloni
9 “Mafumu a dziko lapansi, amene anachita naye chigololo nachita naye pamodzi zosangalatsa moyo uno, akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzalira nakhuza maliro ake. 10 Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake.
“ ‘Tsoka! Tsoka mzinda waukulu
iwe, Babuloni mzinda wamphamvu!
Mu ora limodzi chiwonongeko chako chafika!’
11 “Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo, 12 katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira; 13 zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo.
14 “Iwo adzanena kuti, ‘Chipatso chimene unachilakalaka chakuchokera. Chuma chako chonse ndi ulemerero zatha, sizidzapezekanso.’ 15 Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro 16 ndipo adzalira mokuwa kuti,
“ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu,
iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira,
ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale!
17 Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’
“Oyendetsa sitima ndi onse oyenda pa sitima ya pamadzi, ogwira ntchito mʼsitima ndi onse amene amadalira nyanja pamoyo wa tsiku ndi tsiku adzayima patali potero. 18 Akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzakuwa kuti, ‘Kodi panalinso mzinda wina ngati mzinda waukuluwu?’ 19 Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti,
“Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe,
kumene onse anali ndi sitima pa nyanja
analemera kudzera mʼchuma chake!
Mu ora limodzi wawonongedwa.
20 “Kondwerani chifukwa cha iye inu kumwamba!
Kondwerani oyera mtima
ndi atumwi ndi aneneri!
Mulungu wamuweruza iye
monga momwe anakuchitirani inu.”
Chiwonongeko Chotsiriza cha Babuloni
21 Kenaka mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati mphero yayikulu nawuponya mʼnyanja nanena kuti,
“Mwa mphamvu chonchi
mzinda waukulu wa Babuloni udzaponyedwa pansi,
sudzapezekanso.
22 Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba,
oyimba zitoliro, ndi lipenga.
Mwa iwe simudzapezekanso
mʼmisiri wina aliyense.
Mwa iwe simudzapezekanso
phokoso la mphero.
23 Kuwala kwa nyale
sikudzawunikanso mwa inu.
Mawu a mkwati ndi mkwatibwi
sadzamvekanso mwa iwe.
Amalonda anu anali akuluakulu a dziko lapansi.
Mitundu yonse inasokonezedwa ndi zamatsenga zako.
24 Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima,
ndi onse amene anaphedwa pa dziko lapansi.”
Yehova Akubwera ndipo Akulamulira
14 Taonani tsiku la Yehova likubwera pamene zinthu zimene adani ako anakulanda azidzagawana iwe ukuona.
2 Ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu; mzindawu udzalandidwa, nyumba zidzaphwasulidwa, ndipo akazi adzagwiriridwa. Theka la anthu a mu mzindamu lidzapita ku ukapolo, koma ena onse otsala mu mzindamu sadzachotsedwa.
3 Pamenepo Yehova adzabwera kudzamenyana ndi mitundu ya anthu imeneyi, ngati mmene amachitira pa nthawi ya nkhondo. 4 Tsiku limenelo adzayimirira pa Phiri la Olivi, kummawa kwa Yerusalemu, ndipo Phiri la Olivilo lidzagawikana pawiri kuyambira kummawa mpaka kumadzulo, kupanga chigwa chachikulu, kuchititsa kuti theka la phiri lisunthire kumpoto ndi linalo kummwera. 5 Inu mudzathawa podzera mʼchigwa chapakati pa phirilo, pakuti chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa monga munachitira pa tsiku la chivomerezi nthawi ya Uziya mfumu ya Yuda. Kenaka Yehova Mulungu wanga adzabwera, pamodzi ndi oyera ake onse.
6 Tsiku limenelo sipadzakhala kuwala, kuzizira kapena chisanu. 7 Lidzakhala tsiku lapaderadera, silidzakhala usana kapena usiku; tsiku limeneli akulidziwa ndi Yehova yekha. Ikadzafika nthawi ya madzulo, kudzakhala kukuwalabe.
8 Tsiku limenelo madzi amoyo adzatuluka mu Yerusalemu, theka lidzapita ku nyanja ya kummawa ndipo theka lina ku nyanja ya kumadzulo, nthawi yachilimwe ndi nthawi yozizira yomwe.
9 Ndipo Yehova adzakhala mfumu pa dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo padzakhala Ambuye mmodzi yekha, ndipo dzina lidzakhala limodzi lomwelo.
10 Dziko lonse, kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kummwera kwa Yerusalemu, lidzakhala ngati Araba. Koma Yerusalemu adzakwezedwa ndipo adzakhala pamalo pakepo, kuyambira ku Chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene ali ku Chipata Choyamba, ku Chipata Chapangodya, ndipo kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku malo opsinyira mphesa za mfumu. 11 Mʼmenemo mudzakhala anthu; sadzawonongedwanso. Yerusalemu adzakhala pa mtendere.
12 Mliri umene Yehova adzakanthire nawo mitundu yonse ya anthu imene inkamenyana ndi Yerusalemu ndi uwu: Matupi awo adzawola iwo eni akuyenda, maso awo adzawola ali mʼmalo mwake, ndipo malilime awo adzawola ali mʼkamwa mwawo. 13 Pa tsiku limenelo Yehova adzasokoneza anthu akuluakulu. Munthu aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndi kuyamba kumenyana okhaokha. 14 Yuda nayenso adzachita nkhondo ku Yerusalemu. Chuma chonse cha anthu a mitundu yozungulira adzachisonkhanitsa pamodzi; golide, siliva ndi zovala zochuluka kwambiri. 15 Mliri womwewo udzapha akavalo ndi nyulu, ngamira ndi abulu, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku misasako.
16 Kenaka opulumuka ochokera mwa mitundu yonse ya anthu amene anathira nkhondo Yerusalemu, azidzapita chaka ndi chaka kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, ndiponso kukachita Chikondwerero cha Misasa. 17 Ngati mitundu ina ya anthu pa dziko lapansi sidzapita ku Yerusalemu kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, idzakhala wopanda mvula. 18 Ndipo ngati anthu a ku Igupto sadzapita ndi kukakhala nawo kumeneko, adzakhala wopanda mvula. Yehova adzabweretsa pa iwo mliri umene analangira mitundu ina ya anthu imene sinapite ku Chikondwerero cha Misasa. 19 Chimenechi chidzakhala chilango cha Igupto ndiponso mitundu ina yonse imene sidzapita ku Chikondwerero cha Misasa.
20 Pa tsiku limenelo pa maberu a akavalo padzalembedwa mawu oti wopatulikira Yehova, ndipo miphika ya mʼNyumba ya Yehova idzakhala yopatulika ngati mbale za ku guwa. 21 Mʼphika uliwonse ku Yerusalemu ndi ku Yuda udzakhala wopatulikira Yehova Wamphamvuzonse, ndipo onse amene adzabwera kudzapereka nsembe adzatenga miphika ina ndi kuphikiramo. Ndipo nthawi imeneyo simudzakhalanso Akanaani mʼNyumba ya Yehova Wamphamvuzonse.
Yesu Adzipempherera Yekha
17 Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera:
“Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. 2 Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. 3 Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. 4 Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. 5 Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe.
Yesu Apempherera Ophunzira Ake
6 “Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. 7 Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. 8 Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. 9 Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. 10 Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. 11 Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 12 Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe.
13 “Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. 14 Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 15 Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. 16 Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 17 Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. 18 Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. 19 Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni.
Yesu Apempherera Okhulupirira Onse
20 “Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. 21 Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 22 Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 23 Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine.
24 “Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
25 “Atate wolungama, ngakhale kuti dziko lapansi silikudziwani Inu, Ine ndimakudziwani, ndipo iwo amadziwa kuti Inu munandituma Ine. 26 Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.