Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 30

Hezekiya Achita Chikondwerero cha Paska

30 Hezekiya anatumiza uthenga mʼdziko lonse la Israeli ndi ku Yuda ndiponso analemba makalata ku Efereimu ndi Manase, oyitana anthu kuti abwere ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Mfumu ndi akuluakulu ake pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu anagwirizana kuti akondwerere Paska pa mwezi wachiwiri. Iwo sanathe kukondwerera pa nthawi yake chifukwa si ansembe ambiri amene anadziyeretsa ndiponso anthu anali asanasonkhane mu Yerusalemu. Chikonzerochi chinaoneka kuti chinali chabwino kwa mfumu pamodzi ndi anthu onse. Iwo anagwirizana zoti alengeze mu Israeli monse kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani, kuyitana anthu kuti abwere ku Yerusalemu ndi kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Si ambiri amene ankachita chikondwererochi monga momwe kunalembedwera.

Molamulidwa ndi mfumu, amithenga anapita mu Israeli yense ndi Yuda ndi makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akuluakulu ake, olembedwa kuti,

“Aisraeli bwererani kwa Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Israeli, kuti abwerere kwa inu amene mwatsala, amene mwapulumuka mʼdzanja la mafumu a ku Asiriya. Musakhale ngati makolo anu ndi abale anu, amene anali osakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo kotero kuti anawachititsa kuti akhale chinthu chochititsa mantha, monga mukuoneramu. Musawumitse khosi monga anachitira makolo anu, Gonjerani Yehova. Bwerani ku malo opatulika, amene anawapatula kwamuyaya. Tumikirani Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake ukuchokereni. Ngati inu mubwerera kwa Yehova, pamenepo abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo ndi amene anawagwira ukapolo ndipo adzabwereranso ku dziko lino pakuti Yehova, Mulungu wanu ndi wokoma mtima ndi wachifundo. Iye sadzakufulatirani ngati inuyo mubwerera kwa Iye.”

10 Amithenga aja anapita mzinda ndi mzinda wa ku Efereimu ndi Manase mpaka ku Zebuloni, koma anthu anawanyoza ndi kuwachita chipongwe. 11 Komabe anthu ena a ku Aseri, Manase ndi Zebuloni anadzichepetsa ndipo anapita ku Yerusalemu. 12 Dzanja la Mulungu linalinso pa anthu a ku Yuda, kuwapatsa mtima umodzi wochita zimene mfumu ndi akuluakulu ake analamula potsata mawu a Yehova.

13 Gulu lalikulu la anthu linasonkhana mu Yerusalemu kudzachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti pa mwezi wachiwiri. 14 Anachotsa mu Yerusalemu maguwa ofukizira lubani ndipo anakawaponya mʼchigwa cha Kidroni.

15 Iwo anapha mwana wankhosa wa Paska pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anachita manyazi ndipo anadziyeretsa ndi kubweretsa nsembe zopsereza ku Nyumba ya Yehova. 16 Ndipo anakhala mʼmalo awo a nthawi zonse potsatira zolembedwa mʼmalamulo a Mose munthu wa Mulungu. Ansembe anawaza magazi amene anawapatsa Alevi. 17 Popeza ambiri mʼgululo anali asanadziyeretse, Alevi anapha ana ankhosa a Paska a iwo amene, mwa mwambo, anali osayeretsedwa ndipo sakanatha kupereka ana ankhosa awo kwa Yehova. 18 Ngakhale kuti ambiri mwa anthu ochokera ku Efereimu, Manase, Isakara ndi Zebuloni sanadziyeretse okha, komabe anadya Paska motsutsana ndi zimene zinalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, kunena kuti, “Yehova wabwino, khululukirani aliyense 19 amene wayika mtima wake kufunafuna Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale ali wosayeretsedwa molingana ndi malamulo a malo opatulika.” 20 Ndipo Yehova anamvera Hezekiya ndipo anachiritsa anthuwo.

21 Aisraeli amene anali mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti kwa masiku asanu ndi awiri akusangalala kwambiri, pamene Alevi ndi ansembe amayimbira Yehova tsiku lililonse, akuyimbira zida zamatamando za Yehova.

22 Hezekiya anayankhula molimbikitsa Alevi onse amene anaonetsa kumvetsa bwino za kutumikira Yehova. Kwa masiku asanu ndi awiri anadya gawo lawo ndi kupereka nsembe zachiyanjano ndi kutamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo.

23 Ndipo msonkhano wonse unagwirizana zopitiriza chikondwerero kwa masiku ena asanu ndi awiri. Kotero kwa masiku ena asanu ndi awiri anachita chikondwererocho mosangalala. 24 Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa ndi mbuzi 7,000 ku msonkhanoko ndipo akuluakulu ake anapereka ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa ndi mbuzi 10,000. Ansembe ambiri anadziyeretsa. 25 Gulu lonse la ku Yuda linasangalala, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ndi onse amene anasonkhana ochokera ku Israeli, kuphatikizanso alendo amene anachokera ku Israeli ndi amene amakhala ku Yuda. 26 Munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli sizinachitikepo zotere mu Yerusalemu. 27 Ansembe ndi Alevi anayimirira kudalitsa anthu, ndipo Mulungu anawamvera pakuti pemphero lawo linafika kumwamba, malo ake oyera.

Chivumbulutso 16

Mbale Zisanu ndi Ziwiri za Mkwiyo wa Mulungu

16 Kenaka ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Nyumba ya Mulungu ija kuwuza angelo asanu ndi awiri kuti, “Pitani, katsanulireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu umene uli mʼmbale zisanu ndi ziwirizi!”

Mngelo woyamba anapita natsanula mbale yake pa dziko lapansi ndipo zilonda zoyipa ndi zowawa zinabuka pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chirombo chija, napembedza fano lake.

Mngelo wachiwiri anapita natsanula mbale yake pa nyanja ndipo madzi ake anasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Chamoyo chilichonse cha mʼnyanjamo chinafa.

Mngelo wachitatu anapita natsanula mbale yake pa mitsinje ndi akasupe amadzi ndipo zinasanduka magazi. Kenaka ndinamva mngelo wolamulira madzi uja akuti,

“Inu mwachita chilungamo, Inu Woyerayo,
    amene mulipo ndipo munalipo;
pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera anu ndi aneneri anu,
    nʼchifukwa chake mwawapatsa magazi kuti amwe, zomwe zikuwayenera.”

Kenaka ndinamva mawu ochokera ku guwa lansembe akuti,

“Inde, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,
    chiweruzo chanu ndi choona ndi cholungama.”

Mngelo wachinayi anapita natsanula mbale yake pa dzuwa ndipo dzuwa linapatsidwa mphamvu yopsereza anthu ndi moto. Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza.

10 Mngelo wachisanu anapita natsanula mbale yake pa mpando waufumu wa chirombo chija ndipo mdima unagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu analuma malilime awo chifukwa cha ululu. 11 Ndipo anatukwana Mulungu wakumwamba chifukwa cha maululu awo ndi zilonda zawo koma anakana kulapa pa zimene anachita.

12 Mngelo wachisanu ndi chimodzi anapita natsanula mbale yake pa mtsinje waukulu wa Yufurate, ndipo madzi ake anaphwa kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kummawa. 13 Kenaka ndinaona mizimu yoyipa itatu imene inkaoneka ngati achule; inatuluka mʼkamwa mwa chinjoka chija, mʼkamwa mwa chirombo chija ndi mʼkamwa mwa mneneri wonyenga uja. 14 Imeneyi ndiyo mizimu ya ziwanda imene imachita zizindikiro zodabwitsa ndipo imatuluka kupita kwa mafumu a dziko lonse, kukawasonkhanitsa ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuzonse.

15 “Taonani, ndikubwera ngati mbala! Wodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuti asayende maliseche kuti angaonetse maliseche ake.”

16 Kenaka mizimu ija inasonkhanitsa pamodzi mafumu ku malo amene mʼChihebri amatchedwa Armagedo.

17 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mu mlengalenga ndipo ku Nyumba ya Mulungu kunamveka mawu ofuwula kuchokera ku mpando waufumu kuti, “Kwatha!” 18 Kenaka kunachitika mphenzi, phokoso, mabingu ndi chivomerezi choopsa. Chivomerezi ngati ichi sichinachitikepo chikhalire cha munthu pa dziko lapansi. Chinali chivomerezi choopsa kwambiri. 19 Mzinda waukuluwo unagawika magawo atatu ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Mulungu anakumbukira Babuloni Wamkulu namupatsa chikho chake chodzaza ndi vinyo wa ukali wa mkwiyo wake. 20 Chilumba chilichonse chinathawa ndipo mapiri sanaonekenso. 21 Matalala akuluakulu olemera pafupifupi makilogalamu makumi asanu anagwa kuchokera kumwamba kugwera pa anthu. Ndipo anthu anatukwana Mulungu chifukwa cha mliri wa matalala popeza unali mliri woopsa kwambiri.

Zekariya 12:1-13

Kuphedwa kwa Adani a Yerusalemu

Ulosi

12 Uthenga wa Yehova kwa Israeli. Yehova, amene amayala mlengalenga, amene amayika maziko a dziko lapansi, ndiponso amene amalenga mzimu wokhala mwa munthu, akunena kuti, “Taonani, ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala chakumwa choledzeretsa chimene chidzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomuzungulira. Yuda adzazingidwa pamodzinso ndi Yerusalemu. Pa tsiku limenelo, pamene mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi idzasonkhana kulimbana naye, ndidzasandutsa Yerusalemu thanthwe losatheka kusunthidwa ndi mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kumusuntha adzadzipweteka. Pa tsiku limenelo kavalo aliyense ndidzamuchititsa mantha kuti asokonezeke, ndipo wokwerapo wake ndidzamuchititsa misala,” akutero Yehova. “Ndidzayangʼanira nyumba ya Yuda koma ndidzachititsa khungu akavalo onse a anthu a mitundu ina. Pamenepo atsogoleri a Yuda adzayankhula mʼmitima mwawo kuti, ‘Anthu a ku Yerusalemu ndi amphamvu, chifukwa Yehova Wamphamvuzonse ndiye Mulungu wawo.’

“Pa tsiku limenelo ndidzasandutsa atsogoleri a Yuda kukhala ngati mbawula yotentha pakati pa nkhuni, ngati sakali yoyaka pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yowazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma Yerusalemu sadzasuntha pa malo ake.

“Yehova adzapulumutsa malo okhala Yuda poyamba, kuti ulemu wa nyumba ya Davide ndi wa anthu okhala mu Yerusalemu usapambane ulemu wa Yuda. Pa tsiku limenelo Yehova adzatchinjiriza onse okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anthu ofowoka kwambiri pakati pawo adzakhala ngati Davide, ndipo nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mngelo wa Yehova wowatsogolera. Pa tsiku limenelo ndidzawononga mitundu yonse yofuna kuthira nkhondo Yerusalemu.

Kulirira amene Anamulasa

10 “Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa. 11 Pa tsiku limenelo mudzakhala kulira kwakukulu mu Yerusalemu, monga kulira kwa ku Hadadi-Rimoni ku chigwa cha Megido. 12 Dziko lidzalira kwambiri, fuko lililonse pa lokha, akazi awo pa okhanso: fuko la Davide pamodzi ndi akazi awo, fuko la Natani pamodzi ndi akazi awo, 13 nyumba ya Levi pamodzi ndi akazi awo, fuko la Simei pamodzi ndi akazi awo, 14 ndiponso mafuko onse pamodzi ndi akazi awo.

Kuyeretsedwa ku Tchimo

13 “Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.

Yohane 15

Mpesa ndi Nthambi

15 “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda. Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri. Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.

“Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu. Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa. Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa. Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.

“Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. 10 Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. 11 Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. 12 Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ 13 Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14 Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. 15 Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani. 16 Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 17 Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’

Dziko Lapansi Limada Ophunzira a Yesu

18 “Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. 19 Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. 20 Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso. 21 Iwo adzakuchitani zimenezi chifukwa cha dzina langa, popeza sakudziwa amene anandituma Ine. 22 Ine ndikanapanda kubwera ndi kuyankhula nawo, sakanakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nʼkukanira mlandu wawo. 23 Iye amene amadana ndi Ine amadananso Atate anga. 24 Ine ndikanapanda kuchita pakati pawo zinthu zimene wina aliyense sanachitepo, iwo sakanakhala ochimwa. Koma tsopano aona zodabwitsa izi, komabe akundida Ine pamodzi ndi Atate anga. 25 Koma zatere kuti zikwaniritse zimene zinalembedwa mʼmalamulo awo: ‘Iwo anandida Ine popanda chifukwa.’

Ntchito ya Mzimu Woyera

26 “Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine. 27 Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.