Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 29

Mfumu Hezekiya Ayeretsa Nyumba ya Mulungu

29 Hezekiya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Abiya mwana wa Zekariya. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide abambo ake.

Pa chaka choyamba cha ulamuliro wake, iye anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anazikonza. Iye analowetsamo ansembe ndi Alevi ndipo anawasonkhanitsa ku bwalo lakummawa ndipo anati: “Mverani, inu Alevi! Dziyeretseni tsopano ndiponso muyeretse Nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu. Muchotse zodetsa zonse ku malo opatulika. Makolo athu anali osakhulupirika ndipo anachita zoyipa pa maso pa Yehova Mulungu wathu ndi kumusiya Yehovayo. Iwo anatembenuka ndi kusiya malo okhalako Yehova ndi kumufulatira. Iwowo anatsekanso zitseko zapakhonde ndi kuzimitsa nyale. Sanafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika a Mulungu wa Israeli. Kotero, Yehova anakwiyira Yuda ndi Yerusalemu. Iye anawasandutsa chinthu chochititsa mantha, choopsa ndiponso chonyozedwa monga momwe mukuonera ndi maso anuwa lero lino. Ichi nʼchifukwa chake makolo athu anaperekedwa ku lupanga ndipo nʼchifukwa chake ana athu aamuna ndi aakazi ndi akazi athu ali ku ukapolo. 10 Tsono ine ndikuganiza zochita pangano ndi Yehova Mulungu wa Israeli, kuti mkwiyo wake woopsawu utichokere. 11 Ana anga, musanyalanyaze tsopano, pakuti Yehova wakusankhani kuti muziyima pamaso pake ndi kumutumikira Iye, kugwira ntchito pamaso pake ndi kufukiza lubani.”

12 Ndipo Alevi awa anakonzeka kugwira ntchito:

Kuchokera ku banja la Kohati,

Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya;

kuchokera ku banja la Merari,

Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli;

kuchokera ku banja la Geresoni,

Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa;

13 kuchokera kwa zidzukulu za Elizafani,

Simiri ndi Yeiyeli;

kuchokera kwa zidzukulu za Asafu,

Zekariya ndi Mataniya;

14 kuchokera kwa zidzukulu za Hemani,

Yehieli ndi Simei;

kuchokera kwa zidzukulu za Yedutuni,

Semaya ndi Uzieli.

15 Atasonkhanitsa abale awo ndi kudziyeretsa, iwo anapita kukayeretsa Nyumba ya Yehova, monga inalamulira mfumu, potsatira mawu a Yehova. 16 Ansembe analowa ku malo opatulika a Yehova kukayeretsako. Anatulutsira ku bwalo la Nyumba ya Yehova chilichonse chodetsedwa chimene anachipeza mʼNyumba ya Yehova. Alevi anatenga zimenezo ndi kupita nazo ku chigwa cha Kidroni. 17 Iwo anayamba mwambo woyeretsawu tsiku loyamba la mwezi woyamba ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo anafika pa khonde la nyumba ya Yehova. Tsono anachita mwambo woyeretsa Nyumba ya Yehova ija masiku asanu ndi atatu, ndipo anamaliza pa tsiku la 16 mwezi woyamba.

18 Ndipo anapita kwa mfumu Hezekiya ndi kukafotokoza kuti, “Ife tayeretsa Nyumba ya Mulungu yonse, guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso tebulo limene timayikapo buledi wopatulika pamodzi ndi zinthu zake zonse. 19 Takonza ndi kuyeretsa zinthu zonse zimene mfumu Ahazi anazichotsa mwa kusakhulupirika kwake pamene anali mfumu. Taziyika kutsogolo kwa guwa la Yehova.”

20 Mmamawa tsiku linalo, mfumu Hezekiya inasonkhanitsa pamodzi akuluakulu a mu mzindawo ndipo inapita ku Nyumba ya Yehova. 21 Iwo anabweretsa ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ziwiri monga nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo la ufumu, la malo opatulika ndi Yuda. Tsono mfumu inalamula ansembe, zidzukulu za Aaroni, kuti apereke zimenezi pa guwa lansembe la Yehova. 22 Choncho anthuwo anapha ngʼombe zazimunazo ndipo ansembe anatenga magazi ake ndi kuwawaza pa guwa lansembe, kenaka anapha nkhosa zazimuna zija ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe; anaphanso ana ankhosa aja ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe. 23 Mbuzi zoperekedwa chifukwa cha tchimo zija zinabweretsedwa pamaso pa mfumu ndi anthu onse, ndipo anasanjika manja awo pa izo. 24 Kenaka ansembe anapha mbuzizo ndipo anapereka magazi ake pa guwa, kuti ukhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraeli onse, pakuti mfumu inalamula kuti nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo zichitike chifukwa cha Aisraeli onse.

25 Iye anayika Alevi mʼNyumba ya Yehova ali ndi ziwaya za malipenga, azeze ndi apangwe potsata lamulo la Davide, Gadi mlosi wa mfumu ndi mneneri Natani. Pakuti Yehova ndiye analamula zimenezi kudzera mwa aneneri. 26 Kotero Alevi anayima okonzekera atanyamula zoyimbira za Davide ndiponso ansembe atanyamula malipenga awo.

27 Hezekiya analamulira kuti apereke nsembe zopsereza pa guwa. Pamene amayamba kupereka nsembezo, kuyimbira Yehova kunayambikanso, pamodzi ndi malipenga ndi zipangizo zoyimbira za Davide mfumu ya Israeli. 28 Anthu onse anawerama pansi ndi kulambira, pamene oyimba amayimba ndi malipenga. Izi zonse zinapitirira mpaka pa mapeto pa nsembe zopsereza.

29 Zopereka zitatha, mfumu ndi wina aliyense amene anali naye anagwada pansi ndi kulambira. 30 Mfumu Hezekiya ndi akuluakulu ake analamulira Alevi kuti atamande Yehova potsata mawu a Davide ndi mlosi Asafu. Kotero anayimba nyimbo zamatamando mokondwera ndipo anaweramitsa mitu yawo ndi kulambira.

31 Kenaka Hezekiya anati, “Inu mwadzipereka tsopano kwa Yehova. Bwerani ndipo mufike ndi nsembe ndi zopereka zachiyamiko ku Nyumba ya Yehova.” Choncho anthu onse anabweretsa nsembe ndi zopereka zachiyamiko, ndipo anthu onse amene anali ofuna mu mtima mwawo anabweretsa nsembe zopsereza.

32 Chiwerengero cha nsembe zopsereza chimene anthu onse anabweretsa chinali ngʼombe zazimuna makumi asanu ndi awiri, nkhosa zazimuna 100, ana ankhosa aamuna 200 ndipo zonsezi zinali za nsembe yopsereza kwa Yehova. 33 Ziweto zimene zinapatulidwa kukhala nsembe zinalipo ngʼombe zazimuna 600, nkhosa ndi mbuzi 3,000. 34 Koma ansembe anali ochepa kuti asende zonse zopsereza. Choncho abale awo Alevi anawathandiza mpaka ntchito yonse inatha ndipo mpaka ansembe ena atadziyeretsa, pakuti Alevi anachita changu kudziyeretsa kulekana ndi momwe anachitira ansembe. 35 Panali nsembe zopsereza zochuluka, pamodzi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano ndi nsembe yachakumwa imene imachitika pamodzi ndi nsembe yopsereza.

Kotero ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu inakhazikitsidwanso. 36 Hezekiya ndi anthu onse anakondwera pa zimene Mulungu anachitira anthu ake, chifukwa zinachita mwamsangamsanga.

Chivumbulutso 15

Angelo Asanu ndi Awiri Okhala ndi Miliri Isanu ndi Iwiri

15 Kumwamba ndinaona chizindikiro china chachikulu ndi chodabwitsa: angelo asanu ndi awiri ali ndi miliri isanu ndi iwiri yomaliza chifukwa Mulungu anakwiya kotheratu. Ndipo ndinaona chimene chinaoneka ngati nyanja yonyezimira yosakaniza ndi moto, ndipo pambali pa nyanjayo panayima amene anagonjetsa chirombo chija ndi fano lake, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo ananyamula azeze amene Mulungu anawapatsa. Iwo ankayimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwana Wankhosa. Nyimbo yake inkati,

“Zochita zanu ndi zazikulu ndi zodabwitsa,
    Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse
Njira zanu ndi zachilungamo ndi zoona,
    Mfumu ya mitundu yonse.
Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani,
    ndi kulemekeza dzina lanu?
Pakuti Inu nokha ndiye woyera.
Anthu a mitundu yonse adzabwera
    kudzapembedza pamaso panu,
pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”

Zitatha izi, ndinaona kumwamba Nyumba ya Mulungu imene ndi Tenti ya Umboni, atatsekula. Mʼnyumbamo munatuluka angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri. Angelowo anavala nsalu zoyera bwino zonyezimira ndi malamba agolide pa zifuwa zawo. Ndipo kenaka chimodzi cha zamoyo zinayi zija chinapereka kwa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo Nyumba ya Mulungu inadzaza ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu zake, ndipo panalibe yemwe akanalowa mʼNyumbayo mpaka miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri aja itatha.

Zekariya 11

11 Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni,
    kuti moto unyeketse mikungudza yako!
Lira mwachisoni, iwe mtengo wa payini, pakuti mkungudza wagwa;
    mtengo wamphamvu wawonongeka!
Lirani mwachisoni, inu mitengo ya thundu ya Basani;
    nkhalango yowirira yadulidwa!
Imvani kulira mwachisoni kwa abusa;
    msipu wawo wobiriwira wawonongeka!
Imvani kubangula kwa mikango;
    nkhalango yowirira ya ku Yorodani yawonongeka!

Abusa Awiri

Yehova Mulungu wanga akuti, “Dyetsa nkhosa zimene zikukaphedwa. Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo. Pakuti Ine sindidzamveranso chisoni anthu okhala mʼdziko,” akutero Yehova. “Ndidzapereka munthu aliyense mʼmanja mwa mnansi wake ndi mwa mfumu yake. Iwo adzazunza dziko, ndipo Ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.”

Choncho ine ndinadyetsa nkhosa zokaphedwa, makamaka nkhosa zoponderezedwa. Pamenepo ndinatenga ndodo ziwiri ndipo yoyamba ndinayitcha Kukoma mtima ndipo yachiwiri ndinayitcha Umodzi ndipo ndinadyetsa nkhosazo. Pa mwezi umodzi ndinachotsa abusa atatu.

Abusawo anadana nane, ndipo ndinatopa nawo. Ndinawuza gulu la nkhosalo kuti, “Sindidzakhalanso mʼbusa wanu. Imene ikufa, ife, ndipo imene ikuwonongeka, iwonongeke, zimene zatsala zizidyana.”

10 Kenaka ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Kukoma mtima ndi kuyithyola, kuphwanya pangano limene ndinachita ndi mitundu yonse ya anthu. 11 Linaphwanyidwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zosautsidwa zimene zimandiyangʼanitsitsa zinadziwa kuti anali mawu a Yehova.

12 Ndinawawuza kuti, “Ngati mukuganiza kuti zili bwino, patseni malipiro anga; koma ngati si choncho, sungani malipirowo.” Kotero anandipatsa ndalama zasiliva makumi atatu.

13 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ziponye kwa wowumba mbiya,” mtengo woyenera umene anapereka pondigula Ine! Choncho ndinatenga ndalama zasiliva makumi atatu ndi kuziponya mʼnyumba ya Yehova kwa wowumba mbiya.

14 Kenaka ndinathyola ndodo yanga yachiwiri yotchedwa Umodzi, kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israeli.

15 Pamenepo Yehova anayankhula nane kuti, “Tenganso zida za mʼbusa wopusa. 16 Pakuti ndidzawutsa mʼbusa mʼdzikomo amene sadzasamalira zotayika, kapena kufunafuna zazingʼono, kapena zovulala, kapena kudyetsa nkhosa zabwino, koma iye adzadya nyama ya nkhosa zonenepa, nʼkumakukuta ndi ziboda zomwe.

17 “Tsoka kwa mʼbusa wopandapake,
    amene amasiya nkhosa!
Lupanga limukanthe pa mkono wake ndi pa diso lake lakumanja!
    Mkono wake ufote kotheratu,
    diso lake lamanja lisaonenso.”

Yohane 14

Yesu Atonthoza Ophunzira Ake

14 “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso. Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko. Inu mukudziwa njira ya kumene Ine ndikupita.”

Yesu Njira ya kwa Atate

Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye ife sitikudziwa kumene Inu mukupita, nanga tingadziwe bwanji njirayo?”

Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine. Mukanandidziwadi Ine, mukanadziwanso Atate anga. Kuyambira tsopano, mukuwadziwa ndipo mwawaona.”

Filipo anati, “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo ife tikhutitsidwa.”

Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe Filipo, ndakhala pakati panu nthawi yonseyi ndipo iwe sukundidziwabe? Aliyense amene waona Ine, waonanso Atate. Tsono ukunena bwanji kuti, ‘Tionetseni Atate?’ 10 Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo Atate ali mwa Ine? Mawu amene Ine ndiyankhula kwa inu si mawu anga okha koma ndi mawu Atate wokhala mwa Ine, amene akugwira ntchito yake. 11 Khulupirirani Ine pamene ndi kuti Ine ndili mwa Atate ndipo Atate ali mwa Ine. Koma ngati si chomwecho, khulupiriranitu Ine chifukwa cha ntchito zanga zodabwitsa. 12 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene akhulupirira Ine adzachita zimene Ine ndakhala ndikuchita. Iye adzachita ngakhale zinthu zazikulu kuposa zimenezi, chifukwa ndikupita kwa Atate. 13 Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. 14 Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.

Lonjezo la Mzimu Woyera

15 “Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga. 16 Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. 17 Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu. 18 Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu. 19 Patsala nthawi yochepa dziko lapansi silidzandionanso koma inu mudzandiona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. 20 Tsiku limenelo inu mudzazindikira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo inu muli mwa Ine, ndipo Ine ndili mwa inu. 21 Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye.”

22 Kenaka Yudasi (osati Yudasi Isikarioti) anati, “Koma Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsa nokha kwa ife, osati ku dziko lapansi?”

23 Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. 24 Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine.

25 “Ndayankhula zonsezi ndikanali nanu. 26 Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani. 27 Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

28 “Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine. 29 Ine ndakuwuzani tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire. 30 Ine sindiyankhulanso nanu zambiri nthawi yayitali popeza wolamulira dziko lapansi akubwera. Iye alibe mphamvu pa Ine, 31 koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti Ine ndimakonda Atate ndi kuti ndimachita zokhazokha zimene Atate wandilamulira Ine.

“Nyamukani; tizipita.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.