Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 21

21 Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yehoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Abale ake a Yehoramu, ana aamuna a Yehosafati, anali Azariya, Yehieli, Zekariya, Azariyahu, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Israeli. Abambo awo anawapatsa mphatso zambiri za siliva, golide ndi zinthu zina zamtengowapatali komanso mizinda yotetezedwa ya Yuda. Koma iye anapereka ufumu kwa Yehoramu chifukwa anali mwana wake woyamba kubadwa.

Yehoramu Mfumu ya Yuda

Yehoramu atakhazikika pa ufumu wa abambo ake, iye anapha abale ake ndi lupanga pamodzi ndi atsogoleri ena a Israeli. Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, pakuti anakwatira mwana wa Ahabu. Ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Komabe, chifukwa cha pangano limene Yehova anachita ndi Davide, Yehova sanafune kuwononga banja la Davide. Iye analonjeza kusungira nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.

Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira Yuda ndipo anadzisankhira mfumu. Choncho Yehoramu anapita kumeneko pamodzi ndi atsogoleri ake ndi magaleta ake onse. Aedomu anamuzungulira pamodzi ndi atsogoleri ake koma iye ananyamuka ndi kuthawa usiku. 10 Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira ulamuliro wa Yuda.

Pa nthawi yomweyi, mzinda wa Libina unawukiranso chifukwa Yehoramu anasiya Yehova, Mulungu wa makolo ake. 11 Iye anamanganso malo opembedzerapo mafano mʼmapiri a Yuda ndipo anachititsa anthu a mu Yerusalemu kukhala osakhulupirika. Choncho anasocheretsa anthu a ku Yuda.

12 Yehoramu analandira kalata yochokera kwa mneneri Eliya yonena kuti,

“Yehova Mulungu wa Davide abambo ako akuti, ‘Iwe sunayende mʼnjira ya Yehosafati abambo ako kapena Asa mfumu ya Yuda. 13 Koma wayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo watsogolera anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kukhala osakhulupirika, monga linachitira banja la Ahabu. Waphanso abale ako, abale a banja la abambo ako, anthu amene anali abwino kuposa iweyo. 14 Kotero tsono Yehova ali pafupi kukantha anthu ako, ana ako, akazi ako ndi zinthu zako zonse, ndi chilango chachikulu. 15 Ndipo iwe udzadwala nthenda yoopsa yamʼmimba, mpaka nthendayo idzachititsa matumbo ako kutuluka.’ ”

16 Yehova anamuutsira Yehoramuyo mkwiyo wa Afilisti ndi Aarabu amene amakhala pafupi ndi Akusi. 17 Iwo anathira nkhondo Yuda. Analowanso ndi kutenga katundu yense amene anamupeza mʼnyumba ya mfumu pamodzi ndi ana ake ndi akazi ake. Palibe mwana amene anatsala kupatula mwana wake wamngʼono kwambiri, Ahaziya.

18 Izi zonse zitachitika, Yehova anakantha Yehoramu ndi nthenda yamʼmimba imene inali yosachiritsika. 19 Patapita nthawi, kumapeto kwa chaka chachiwiri, matumbo ake anatuluka chifukwa cha nthendayo, ndipo anafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu ake sanasonkhe moto kumuchitira ulemu, monga anachitira ndi makolo ake.

20 Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu. Iyeyo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo anamwalira popanda odandawula, nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati mʼmanda a mafumu.

Chivumbulutso 9

Mngelo wachisanu anayimba lipenga lake, ndipo ndinaona nyenyezi ikugwa pa dziko lapansi kuchokera ku thambo. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi ya ku chidzenje chakuya. Nyenyeziyo itatsekula pa chidzenje chakuyacho panatuluka utsi ngati wochokera mʼngʼanjo yayikulu. Dzuwa ndi thambo zinada chifukwa cha utsi ochokera mʼdzenjemo. Ndipo mʼkati mwa utsimo munatuluka dzombe kukalowa mʼdziko lapansi ndipo linapatsidwa mphamvu zoluma ngati za zinkhanira pa dziko lapansi. Dzombelo linalamulidwa kuti lisawononge udzu wa pa dziko lapansi, kapena chomera chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu okhawo amene analibe chizindikiro cha Mulungu pa mphumi zawo. Silinapatsidwe mphamvu yowapha koma yowazunza kwa miyezi isanu. Ndipo ululu umene anthuwo anawumva unali ngati wa chinkhanira chikaluma munthu. Masiku amenewo anthu adzafunafuna imfa koma sadzayipeza. Adzalakalaka kufa koma imfa izidzawathawa.

Dzombe linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pawo panali ngati zipewa zaufumu zagolide ndipo nkhope zawo ngati za anthu. Tsitsi lawo linali ngati la amayi, mano awo ngati a mikango. Dzombelo linavala za pachifuwa zachitsulo. Phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magaleta ankhondo ambiri okokedwa ndi akavalo othamangira ku nkhondo. 10 Linali ndi michira ngati zinkhanira ndi mbola. Mʼmichira yake munali mphamvu yozunza nayo anthu kwa miyezi isanu. 11 Mfumu yawo inali mngelo wolamulira Chidzenje chakuya chija. Mʼchihebri dzina lake ndi Abadoni ndipo mʼChigriki ndi Apoliyoni (tanthauzo lake ndiye kuti, Wowononga).

12 Tsoka loyamba lapita; matsoka ena awiri akubwerabe.

13 Mngelo wachisanu ndi chimodzi anayimba lipenga lake, ndipo ndinamva liwu lochokera ku ngodya zinayi za guwa lansembe lagolide lija lokhala pamaso pa Mulungu. 14 Liwulo linati kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi amene anali ndi lipenga uja, “Masula angelo anayi amene anamangidwa pa mtsinje waukulu wa Yufurate.” 15 Ndipo anamasulidwadi angelo anayi aja amene anasungidwa kukonzekera ora ili, tsiku ili, mwezi uwu ndi chaka ichi kuti aphe limodzi la magawo atatu a anthu. 16 Ndinamva chiwerengero cha ankhondo a pa akavalo aja, kuti chinali 200 miliyoni.

17 Akavalo ndi okwerapo amene ndinaona mʼmasomphenya anga ankaoneka motere: Zovala za pachifukwa pawo zinali zofiira ngati moto, zobiriwira ngati utsi, ndi zachikasu ngati miyala ya sulufule. Mitu ya akavalowo inali ngati ya mikango ndipo mʼkamwa mwawo munkatuluka moto, utsi ndi sulufule. 18 Gawo limodzi la magawo atatu a anthu linaphedwa ndi miliri yamoto, utsi ndi sulufule zimene zinkachoka mʼkamwa mwawo. 19 Mphamvu za akavalowo inali mʼkamwa mwawo ndi mʼmichira mwawo; pakuti michira yawo inali ngati njoka; ndi mitu imene inkalumira.

20 Anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi sanalapebe kuti asiye ntchito zawo zoyipa. Iwo sanasiye kupembedza ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, amwala ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva kapena kuyankhula. 21 Sanalapenso kuleka zakupha, zamatsenga awo, zachigololo zawo kapena umbava wawo.

Zekariya 5

Chikalata Chowuluka

Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona chikalata chimene chimawuluka.

Mngelo uja anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?”

Ndinayankha kuti, “Ndikuona chikalata chikuwuluka, mulitali mwake mamita asanu ndi anayi ndipo mulifupi mwake mamita anayi ndi theka.”

Ndipo mngeloyo anandiwuza kuti, “Awa ndi matemberero amene akupita pa dziko lonse lapansi; potsata zimene zalembedwa mʼkati mwa chikalatamo, aliyense wakuba adzachotsedwa, ndipo potsata zomwe zalembedwa kunja kwake, aliyense wolumbira zabodza adzachotsedwanso. Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza, ndipo lidzalowa mʼnyumba ya munthu wakuba ndi munthu wolumbira zabodza mʼdzina langa. Lidzakhala mʼnyumbamo mpaka kuyiwonongeratu, matabwa ake ndi miyala yake yomwe.’ ”

Mkazi mu Dengu

Kenaka mngelo amene amayankhula nane uja anabwera patsogolo panga ndipo anandiwuza kuti, “Kweza maso ako tsopano kuti uwone kuti ndi chiyani chikubwerachi.”

Ndinafunsa kuti, “Kodi chimenechi nʼchiyani?”

Mngeloyo anayankha kuti, “Limeneli ndi dengu loyezera.” Ndipo anawonjezera kunena kuti, “Umenewu ndi uchimo wa anthu mʼdziko lonse.”

Pamenepo chovundikira chake chamtovu chinatukulidwa, ndipo mʼdengumo munali mutakhala mkazi. Mngeloyo anati, “Chimenechi ndi choyipa,” ndipo anamukankhira mkaziyo mʼdengu muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.

Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona akazi awiri akuwuluka kubwera kumene kunali ine; akuwuluzika ndi mphepo. Iwo anali ndi mapiko ngati a kakowa, ndipo ananyamula dengu lija, kupita nalo pakati pa mlengalenga ndi dziko lapansi.

10 Ine ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Dengulo akupita nalo kuti?”

11 Iye anayankha kuti, “Ku dziko la Babuloni kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzayikamo dengulo.”

Yohane 8

Koma Yesu anapita ku phiri la Olivi. Mmamawa Iye anaonekeranso ku Nyumba ya Mulungu kumene anthu onse anamuzungulira ndipo Iye anakhala pansi nawaphunzitsa. Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Iwo anamuyimiritsa patsogolo pa anthu ndipo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo. Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?” Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye.

Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake. Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.” Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.

Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo. 10 Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?”

11 Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.”

“Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”

Za Umboni wa Yesu

12 Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”

13 Afarisi anamutsutsa Iye nati, “Iwe ukudzichitira umboni wa Iwe mwini, umboni wako siwoona.”

14 Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita. 15 Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense. 16 Koma Ine ndikati ndiweruze, ndimaweruza molondola, chifukwa Ine sindili ndekha koma ndili ndi Atate amene anandituma. 17 Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka. 18 Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”

19 Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?”

Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.” 20 Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.

Mkangano Woti Yesu Ndani

21 Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”

22 Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’ ”

23 Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino. 24 Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”

25 Iwo anafunsa kuti, “Ndinu ndani?”

Yesu anayankha kuti, “Monga Ine ndakhala ndikunena nthawi yonseyi, 26 ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”

27 Iwo sanazindikire kuti Iye amawawuza za Atate ake. 28 Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa. 29 Iye amene anandituma Ine ali nane pamodzi. Iye sanandisiye ndekha popeza nthawi zonse ndimachita zomwe zimamukondweretsa Iye.” 30 Pamene Iye ankayankhula zimenezi, ambiri anamukhulupirira.

Ana a Abrahamu

31 Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga. 32 Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”

33 Iwo anamuyankha Iye kuti, “Ife ndife zidzukulu za Abrahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Kodi mukunena bwanji kuti, ‘Ife tidzamasulidwa?’ ”

34 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. 35 Pajatu kapolo alibe malo wokhazikika mʼbanja, koma mwana ndi wa mʼbanjamo nthawi zonse. 36 Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu. 37 Ine ndikudziwa kuti inu ndinu zidzukulu za Abrahamu. Chonsecho inu mwakonzeka kundipha Ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. 38 Ine ndikukuwuzani zimene ndaziona pamaso pa Atate, ndipo inu mukuchita zimene mwazimva kwa abambo anu.”

39 Iwo anayankha kuti, “Ife abambo athu ndi Abrahamu.”

Yesu anati, “Inu mukanakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zinthu zimene Abrahamuyo ankachita. 40 Koma mmene zililimu, inu mwatsimikiza kundipha Ine, munthu amene ndinakuwuzani choonadi chimene Ine ndinachimva kuchokera kwa Mulungu. Abrahamu sanachite zinthu zoterezi. 41 Inu mukuchita zinthu zimene abambo anu amachita.”

Iwo anatsutsa kuti, “Ife si ana amʼchigololo, Atate amene tili nawo ndi Mulungu yekha.”

Ana a Mdierekezi

42 Yesu anawawuza kuti, “Mulungu akanakhala Atate anu, inu mukanandikonda Ine, pakuti Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo tsopano ndili pano. Ine sindinabwere mwa Ine ndekha. 43 Nʼchifukwa chiyani simukumvetsetsa mawu anga? Chifukwa chake nʼchakuti simungathe kumva zoyankhula zanga. 44 Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza. 45 Koma chifukwa ndikuwuzani choonadi, inu simukundikhulupirira Ine! 46 Ndani mwa inu angatsimikize kuti ndine wochimwa? Ngati Ine ndikunena choonadi, nʼchifukwa chiyani simukundikhulupirira? 47 Munthu wochokera kwa Mulungu amamva zimene Mulungu amanena. Chifukwa chimene simumvera nʼchakuti, inuyo sindinu ochokera kwa Mulungu.”

Zomwe Yesu Ananena za lye Mwini

48 Ayuda anamuyankha Iye kuti, “Kodi ife sitikulondola ponena kuti Inu ndi Msamariya ndi wogwidwa ndi chiwanda?”

49 Yesu anati, “Ine sindinagwidwe ndi chiwanda, koma ndimalemekeza Atate anga, koma inu mukundinyoza. 50 Ine sindidzifunira ndekha ulemu; koma alipo wina amene amandifunira, ndipo Iyeyo ndiye woweruza. 51 Ine ndikukuwuzani choonadi, munthu akasunga mawu anga, sadzafa konse.”

52 Pamenepo Ayuda anafuwula kuti, “Tsopano ife tadziwadi kuti Inu ndi wogwidwa ndi chiwanda! Abrahamu anafa ndiponso aneneri, koma Inu mukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga, sadzafa.’ 53 Kodi ndinu wa mkulu kuposa abambo athu Abrahamu? Iye anafa, ndiponso aneneri onse. Inu mukuganiza kuti ndinu yani?”

54 Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemu wangawo ndi wosatanthauza kanthu. Atate anga amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, ndiye amene amandilemekeza Ine. 55 Ngakhale kuti inuyo simukumudziwa, Ineyo ndikumudziwa. Ngati Ine nditanena kuti sindikumudziwa, Ineyo nditha kukhala wabodza ngati inuyo, koma Ine ndimamudziwa ndipo ndimasunga mawu ake. 56 Abambo anu Abrahamu anakondwera poyembekezera kubwera kwanga. Iwo anandiona ndipo anasangalala.”

57 Ayuda anati kwa Iye, “Inu sumunafike nʼkomwe zaka makumi asanu, ndipo mukuti munamuona Abrahamu!”

58 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani choonadi, Abrahamu asanabadwe, Ine Ndine!” 59 Pamenepo iwo anatola miyala kuti amugende, koma Yesu anabisala, nachoka mozemba mʼNyumba ya Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.