M’Cheyne Bible Reading Plan
19 Yehosafati, mfumu ya Yuda itabwerera mwamtendere ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, 2 mlosi Yehu, mwana wa Hanani, anatuluka kukakumana naye ndipo anati kwa mfumu, “Kodi nʼkoyenera kuthandiza oyipa ndi kukonda iwo amene amadana ndi Yehova? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Yehova uli pa inu. 3 Komabe, muli zinthu zina zabwino mwa inu, pakuti inu mwachotsa mʼdziko muno mafano a Asera ndipo mwakhazikitsa mtima wanu pa kufunafuna Mulungu.”
Yehosafati Asankha Oweruza
4 Yehosafati anakakhala ku Yerusalemu, ndipo amayenda pakati pa anthu kuchokera ku Beeriseba mpaka ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anawatembenuzira kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo. 5 Iye anasankha oweruza mʼdzikomo, mu mzinda uliwonse wotetezedwa wa Yuda. 6 Ndipo anawawuza kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, chifukwa simukuweruza mʼmalo mwa munthu koma Yehova, amene ali nanu pamene mukupereka chiweruzo. 7 Tsopano kuopsa kwa Yehova kukhale pa inu. Muweruze mosamala, pakuti ndi Yehova Mulungu wathu palibe kupotoza chilungamo kapena kukondera kapenanso kulandira ziphuphu.”
8 Mu Yerusalemu, Yehosafati anasankha Alevi ena, ansembe ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli kuti aziyangʼanira Malamulo a Yehova ndi kuweruza milandu. Ndipo iwo amakhala mu Yerusalemu. 9 Iye anawalamula kuti, “Inu mutumikire mokhulupirika ndi mtima wanu wonse moopa Yehova. 10 Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.
11 “Amariya, mkulu wa ansembe adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza Yehova, ndipo Zebadiya mwana wa Ismaeli, mtsogoleri wa fuko la Yuda, adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza mfumu ndipo Alevi adzatumikira ngati okuyangʼanirani. Muchite molimba mtima ndipo Yehova akhale ndi iwo amene adzachita bwino.”
Yehosafati Agonjetsa Mowabu ndi Amoni
20 Zitatha izi, Amowabu ndi Aamoni pamodzi ndi Ameuni ena anabwera kudzachita nkhondo ndi Yehosafati.
2 Anthu ena anabwera kudzamuwuza Yehosafati kuti, “Gulu lalikulu kwambiri lankhondo likubwera kudzachita nanu nkhondo lochokera ku Edomu, ku mbali ina ya Nyanja. Gululi lafika kale ku Hazazoni Tamara” (ndiye kuti Eni-Gedi). 3 Ndi mantha, Yehosafati anaganiza zofunsira kwa Yehova, ndipo analengeza kuti Ayuda onse asale zakudya. 4 Anthu a ku Yuda anabwera pamodzi kudzafuna thandizo kwa Yehova, ndipo anabweradi kuchokera ku mzinda uliwonse wa mu Yuda kudzafunafuna Yehova.
5 Yehosafati anayimirira pakati pa msonkhano wa Yuda ndi Yerusalemu, pa Nyumba ya Yehova patsogolo pa bwalo latsopano 6 ndipo anati:
“Inu Yehova, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu amene muli kumwamba? Inu mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu. Mphamvu ndi nyonga zili mʼmanja mwanu, ndipo palibe amene angalimbane nanu. 7 Inu Mulungu wathu, kodi simunathamangitse nzika za dziko lino pamaso pa anthu anu Aisraeli ndipo munalipereka kwa zidzukulu za Abrahamu bwenzi lanu kwamuyaya? 8 Iwo akhala mʼdzikolo ndipo anamangira Dzina lanu malo opatulika, nʼkumati, 9 ‘Ngati tsoka litigwera kaya ndi lupanga lachiweruzo, kapena mliri, kapenanso njala, ife tidzayima pamaso panu patsogolo pa Nyumba ya Mulungu ino imene imatchedwa ndi Dzina lanu ndipo tidzalirira kwa inu mʼmasautso athu, ndipo Inu mudzatimvera ndi kutipulumutsa.’
10 “Koma tsopano pano pali anthu ochokera ku Amoni, Mowabu ndi Phiri la Seiri amene dziko lawo Inu simunawalole Aisraeli kuti alithire nkhondo pamene amabwera kuchokera ku Igupto. Kotero anatembenuka ndi kuwaleka ndipo sanawawononge. 11 Taonani, mmene akutibwezera ife pobwera kudzatithamangitsa mʼdziko limene inu munatipatsa ngati cholowa chathu. 12 Inu Mulungu wathu, kodi simuwaweruza? Pakuti ife tilibe mphamvu zolimbana ndi gulu lalikulu lankhondo limene likutithira nkhondoli. Ife sitikudziwa choti tichite, koma maso athu ali pa Inu.”
13 Anthu onse a Yuda, pamodzi ndi akazi awo ndi ana ndi makanda, anayima chilili pamaso pa Yehova.
14 Ndipo Mzimu wa Yehova unabwera pa Yahazieli mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyeli, mwana wa Mataniya Mlevi, chidzukulu cha Asafu, atayimirira mu msonkhano.
15 Iye anati, “Tamverani mfumu Yehosafati ndi onse amene amakhala mu Yuda ndi Yerusalemu! Zimene Yehova akunena kwa inu ndi izi: ‘Musaope kapena kutaya mtima chifukwa cha gulu lalikulu lankhondo ili. Pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. 16 Mawa mupite mukamenyane nawo. Adzakhala akubwera mokweza kudzera Njira ya Zizi, ndipo mukawapeza kumapeto kwa chigwa cha ku chipululu cha Yeruweli. 17 Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ”
18 Yehosafati anaweramitsa nkhope yake ndi kugunda pansi, ndiponso anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anagwa pansi ndi kulambira Yehova. 19 Kenaka Alevi ena ochokera ku mabanja a Kohati ndi Kora anayimirira ndipo anatamanda Yehova Mulungu wa Israeli ndi mawu ofuwula kwambiri.
20 Mmamawa, ananyamuka kupita ku chipululu cha Tekowa. Akunyamuka, Yehosafati anayimirira ndipo anati, “Tandimverani ine anthu a Yuda ndi Yerusalemu! Khalani ndi chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu wanu ndipo mudzatchinjirizidwa, khalani ndi chikhulupiriro mwa aneneri ake ndipo mudzapambana.” 21 Atafunsira kwa anthu, Yehosafati anasankha anthu oti ayimbire Yehova ndi kumutamanda chifukwa cha ulemerero wa chiyero chake pamene amapita ali patsogolo pa gulu la ankhondo, akunena kuti:
“Yamikani Yehova
pakuti chikondi chake ndi chosatha.”
22 Atangoyamba kuyimba ndi kutamanda, Yehova anapereka mʼmanja mwawo anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu ndiponso a ku Phiri la Seiri amene amalimbana ndi Yuda, ndipo anagonjetsedwa. 23 Anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu anawukira anthu ochokera ku Phiri la Seiri, ndipo anawawononga ndi kuwatheratu. Atatsiriza kuwapha anthu ochokera ku Seiri anamenyana wina ndi mnzake mpaka kuwonongana.
24 Anthu a ku Yuda atafika pa malo oyangʼanana ndi chipululu ndi kuona kumene kunali gulu lalikulu lankhondo, iwo anangoona mitembo yokhayokha itagona pansi ndipo palibe amene anathawa. 25 Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha, ndipo pakati pawo anapeza katundu wambiri ndi zovala ndiponso zinthu zina zamtengowapatali kuposa zomwe akanatha kunyamula. Kunali katundu wambiri kotero kuti zinawatengera masiku atatu kuti amutenge. 26 Tsiku lachinayi anasonkhana ku chigwa cha Beraka kumene anatamanda Yehova. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero.
27 Tsono motsogozedwa ndi Yehosafati, anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu mokondwera pakuti Yehova anawagonjetsera adani awo. 28 Iwo analowa mu Yerusalemu ndipo anapita ku Nyumba ya Mulungu akuyimba azeze, apangwe ndi malipenga.
29 Kuopsa kwa Mulungu kunali pa maufumu onse a mayiko amene anamva mmene Yehova anamenyera adani a Aisraeli. 30 Ndipo ufumu wa Yehosafati unali pa mtendere pakuti Mulungu wake anamupatsa mpumulo ku mbali zonse.
Kutha kwa Ufumu wa Yehosafati
31 Choncho Yehosafati analamulira Yuda. Iye anali wa zaka 35 pamene anakhala mfumu ya Yuda ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 25. Dzina la amayi ake linali Azuba mwana wa Sili. 32 Iye ankayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanapatuke pa zimenezi pakuti anachita zolungama pamaso pa Yehova. 33 Komabe malo opembedzerapo mafano sanachotsedwe ndipo anthu sanaperekebe mitima yawo kwa Mulungu wa makolo awo.
34 Zochitika zina zokhudza ufumu wa Yehosafati, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la Yehu mwana wa Hanani, zomwe zikupezeka mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
35 Zitapita izi, Yehosafati mfumu ya Yuda inachita mgwirizano ndi Ahaziya mfumu ya Israeli, amene anachita zoyipa kwambiri. 36 Iye anagwirizana ndi Ahaziya kuti apange sitima zapamadzi zochitira malonda. Atazipanga zimenezi ku Ezioni-Geberi, 37 Eliezara mwana wa Dodavahu wa ku Maresa ananenera motsutsana ndi Yehosafati ndipo anati, “Chifukwa chakuti wachita mgwirizano ndi Ahaziya, Yehova adzawononga zimene mwapangazo!” Sitima za pamadzizo zinawonongeka ndipo sizinapite nʼkomwe kumene zimakachita malonda.
Kutsekulidwa kwa Chimatiro Chachisanu ndi Chiwiri
8 Atatsekula chomatira chachisanu ndi chiwiri, kumwamba kunakhala chete mphindi makumi atatu.
2 Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri aja amene amayimirira pamaso pa Mulungu, akupatsidwa malipenga asanu ndi awiri.
3 Mngelo wina amene anali ndi chofukizira chagolide anabwera nayimirira pa guwa lansembe. Anapatsidwa lubani wambiri kuti amupereke pamodzi ndi mapemphero a anthu onse oyera mtima pa guwa lansembe lagolide patsogolo pa mpando waufumu. 4 Fungo la lubani pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima zinakwera kumwamba kwa Mulungu kuchokera mʼdzanja la mngeloyo. 5 Kenaka mngeloyo anatenga chofukizira nachidzaza ndi moto wochokera pa guwa lansembe ndi kuponya pa dziko lapansi ndipo nthawi yomweyo panachitika mabingu, phokoso, mphenzi ndi chivomerezi.
Malipenga
6 Angelo asanu ndi awiri anakonzekera kuyimba malipenga asanu ndi awiri.
7 Mngelo woyamba anayimba lipenga lake ndipo kunabwera matalala ndi moto wosakanizana ndi magazi ndipo unaponyedwa pa dziko lapansi. Gawo limodzi la magawo atatu a dziko lapansi linapsa, gawo limodzi la magawo atatu a mitengo linapsa ndi gawo limodzi la magawo atatu a udzu wauwisi linapsanso.
8 Mngelo wachiwiri anayimba lipenga lake, ndipo chinthu china chooneka ngati phiri lalikulu loyaka moto, chinaponyedwa mʼnyanja. Gawo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka magazi. 9 Gawo limodzi mwa magawo atatu a zolengedwa zonse zamoyo za mʼnyanja, linafa, ndipo gawo limodzi la sitima za pamadzi linawonongedwa.
10 Mngelo wachitatu anayimba lipenga lake, ndipo nyenyezi yayikulu, yoyaka ngati muni inachoka kumwamba nigwera pa gawo limodzi la magawo atatu a mitsinje ndi pa akasupe amadzi. 11 Dzina la nyenyeziyo ndi Chowawa. Gawo limodzi la magawo atatu a madzi anasanduka owawa ndipo anthu ambiri anafa chifukwa cha madzi owawawo.
12 Mngelo wachinayi anayimba lipenga lake, ndipo chimodzi cha zigawo zitatu za dzuwa, za mwezi ndi za nyenyezi zinamenyedwa kotero chimodzi mwa zitatu za zonsezi zinada. Panalibenso kuwala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku.
13 Ndinayangʼananso ndipo ndinaona ndi kumva chiwombankhanga chimene chinkawuluka mlengalenga kwambiri chikuyankhula mofuwula kuti, “Tsoka, Tsoka! Tsoka lalikulu kwa anthu okhala mʼdziko lapansi, angelo otsala aja akangoyimba malipenga awo!”
Choyikapo Nyale cha Golide ndi Mitengo Iwiri ya Olivi
4 Kenaka mngelo amene amayankhula nane anabwerera nandidzutsa, ngati mmene amadzutsira munthu amene ali mʼtulo. 2 Anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?”
Ndinayankha kuti, “Ine ndikuona choyikapo nyale, chonse chagolide ndi mbale pamwamba pake ndi nyale zoyaka zisanu ndi ziwiri, iliyonse ili ndi zibowo zisanu ndi ziwiri zolowetsera zingwe zoyatsira. 3 Ndiponso pambali pake pali mitengo ya olivi iwiri, umodzi uli kumanja kwa mbaleyo ndipo winawo kumanzere.”
4 Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi nʼchiyani mbuye wanga?”
5 Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?”
Ndinayankha kuti, “Ayi mbuye wanga.”
6 Choncho iye anandiwuza kuti, “Mawu a Yehova kwa Zerubabeli ndi awa: ‘Osati mwa nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi Mzimu wanga,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
7 “Kodi ndiwe yani, iwe phiri lamphamvu? Pamaso pa Zerubabeli udzasanduka dziko losalala. Pamenepo adzabweretsa mwala wotsiriza. Akamadzawuyika pamwamba anthu adzafuwula kuti, ‘Mulungu adalitse Nyumbayi! Mulungu adalitse Nyumbayi!’ ”
8 Ndipo Yehova anayankhulanso nane kuti, 9 “Manja a Zerubabeli ndiwo ayika maziko a Nyumbayi; adzatsiriza ndi manja ake omwewo. Pamenepo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse ndiye anakutuma.
10 “Ndani wanyoza tsiku la zinthu zazingʼono? Anthu adzasangalala akadzaona chingwe choyezera mʼmanja mwa Zerubabeli.
(“Nyale zisanu ndi ziwirizi ndi maso a Yehova, amene amayangʼanayangʼana pa dziko lapansi.”)
11 Kenaka ndinafunsa mngelo uja kuti, “Kodi mitengo ya olivi iwiri ili kumanja ndi kumanzere kwa choyikapo nyalechi ikutanthauza chiyani?”
12 Ndinamufunsanso kuti, “Kodi nthambi ziwiri za mtengo wa olivi zomwe zili pambali pa mipopi yodzera mafuta iwiri yagolide zikutanthauza chiyani?”
13 Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?”
Ine ndinati, “Ayi mbuye wanga.”
14 Choncho iye anati, “Amenewa ndi anthu awiri amene adzozedwa kuti atumikire Ambuye pa dziko lonse lapansi.”
Yesu Apita Kuphwando Lamisasa
7 Zitatha izi Yesu anayendayenda mu Galileya, ndi cholinga chakuti asafike ku Yudeya chifukwa Ayuda kumeneko amadikira kuti amuphe. 2 Koma phwando la Ayuda lamisasa litayandikira, 3 abale a Yesu anati kwa Iye, “Inu muyenera kuchoka kuno ndi kupita ku Yudeya, kuti ophunzira anu akaone zodabwitsa zomwe mumachita. 4 Palibe wina aliyense amene amafuna kukhala wodziwika amachita zinthu mseri. Popeza Inu mukuchita zinthu izi, mudzionetsere nokha ku dziko la pansi.” 5 Pakuti ngakhale abale ake omwe sanamukhulupirire.
6 Choncho Yesu anawawuza iwo kuti, “Nthawi yanga yoyenera sinafike; kwa inu nthawi ina iliyonse ndi yoyenera. 7 Dziko lapansi silingakudeni inu, koma limandida Ine chifukwa Ine ndimachitira umboni kuti zomwe limachita ndi zoyipa. 8 Inu pitani kuphwando. Ine sindipita tsopano kuphwando ili chifukwa kwa Ine nthawi yoyenera sinafike.” 9 Atanena izi, Iye anakhalabe mu Galileya.
10 Komabe, abale ake atanyamuka kupita kuphwando, Iye anapitanso, osati moonekera, koma mseri. 11 Tsopano kuphwandoko Ayuda anakamufunafuna ndi kumafunsana kuti, “Kodi munthu ameneyu ali kuti?”
12 Pakuti pa chigulu cha anthu panali kunongʼona ponseponse za Iye. Ena ankanena kuti, “Iye ndi munthu wabwino.”
Ena ankayankha kuti, “Ayi, Iye amanamiza anthu.” 13 Koma panalibe amene ankanena kalikonse poyera za Iye chifukwa choopa Ayuda.
Yesu Aphunzitsa pa Phwando
14 Phwando lili pakatikati, Yesu anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kuphunzitsa. 15 Ayuda anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu nzeru izi anazitenga kuti popanda kuphunzira?”
16 Yesu anayankha kuti, “Chiphunzitso changa si cha Ine ndekha. Chimachokera kwa Iye amene anandituma. 17 Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha. 18 Iye amene amayankhula za Iye mwini amatero kuti adzipezere ulemu, koma amene amagwira ntchito kuti amene anamutuma alandire ulemu, ameneyo ndiye munthu woona; mu mtima mwake mulibe chinyengo chilichonse. 19 Kodi Mose sanakupatseni lamulo? Komatu palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akusunga lamulo. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kundipha Ine?”
20 Gulu la anthu linayankha kuti, “Iwe ndiye wagwidwa ndi ziwanda. Ndani akufuna kukupha?”
21 Yesu anawawuza kuti, “Ine ndinachita chodabwitsa chimodzi ndipo inu mwadabwa. 22 Koma, chifukwa chakuti Mose anakulamulani kuti muzichita mdulidwe (ngakhale kuti sunachokere kwa Mose, koma kwa makolo anu), inuyo mumachita mdulidwe mwana tsiku la Sabata. 23 Tsopano ngati mwana angachite mdulidwe pa Sabata kuti lamulo la Mose lisaswedwe, nʼchifukwa chiyani mukundipsera mtima chifukwa chochiritsa munthu pa Sabata? 24 Musamaweruze potengera maonekedwe chabe, koma weruzani molungama.”
Kodi Yesu ndi Khristu?
25 Pa nthawi imeneyi anthu ena a ku Yerusalemu anayamba kufunsana kuti, “Kodi uyu si munthu uja akufuna kumuphayu? 26 Uyu ali apa, kuyankhula poyera, ndipo iwo sakunena kanthu kwa Iye. Kodi olamulira atsimikizadi kuti Iye ndi Khristu? 27 Koma ife tikudziwa kumene achokera munthuyu; pamene Khristu adzabwere, palibe amene adzadziwa kumene akuchokera.”
28 Kenaka Yesu, akuphunzitsabe mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafuwula kuti, “Zoona, mukundidziwa Ine, ndipo mukudziwa kumene ndikuchokera. Ine sindili pano mwa Ine ndekha, koma Iye amene anandituma Ine ndi woona. Inu simukumudziwa, 29 koma Ine ndikumudziwa chifukwa ndichokera kwa Iyeyo ndipo ndiye amene anandituma Ine.”
30 Chifukwa cha izi iwo anayesa kumugwira Iye, koma palibe aliyense amene anayika dzanja lake pa Iye, chifukwa nthawi yake inali isanafike. 31 Komabe, ambiri a mʼchigulucho anamukhulupirira Iye. Iwo anati, “Kodi pamene Khristu abwera, adzachita zizindikiro zodabwitsa zambiri kuposa munthu uyu?”
32 Afarisi anamva chigulucho chikunongʼona zinthu zotere za Iye. Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anatumiza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu kuti akamumange Iye.
33 Yesu anati, “Ine ndili ndi inu kwa kanthawi kochepa chabe, ndipo kenaka ndizipita kwa Iye amene anandituma Ine. 34 Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza; ndipo kumene Ine ndili inu simungathe kubwera.”
35 Ayuda anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi munthu uyu akuganizira zoti apite kuti kumene ife sitingathe kumupeza Iye? Kodi Iye adzapita kumene anthu amakhala mobalalikana pakati pa Agriki, ndi kuphunzitsa Agriki? 36 Kodi Iye amatanthauza chiyani pamene anati, ‘Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza,’ ndi ‘Kumene Ine ndili, inu simungathe kubwera?’ ”
Mitsinje ya Madzi Opatsa Moyo
37 Pa tsiku lomaliza ndi lalikulu kwambiri laphwando, Yesu anayimirira nafuwula nati, “Ngati munthu ali ndi ludzu, abwere kwa Ine kuti adzamwe. 38 Malemba kuti ‘Aliyense amene akhulupirira Ine, mitsinje yamadzi amoyo idzatuluka kuchokera mʼkati mwake.’ ” 39 Ponena izi Iye amatanthauza Mzimu Woyera, amene adzalandire amene amakhulupirira Iye. Pa nthawiyi nʼkuti Mzimu Woyera asanaperekedwe, pakuti Yesu anali asanalemekezedwe.
40 Pakumva mawu ake, ena a anthuwo anati, “Zoonadi munthu uyu ndi mneneri.”
41 Ena anati, “Iye ndiye Khristu.”
Komanso ena anafunsa kuti, “Kodi Khristu angachokere bwanji ku Galileya? 42 Kodi Malemba samanena kuti Khristu adzachokera mʼbanja la Davide, ndi ku Betelehemu mu mzinda umene Davide anakhalamo?” 43 Kotero anthu anagawikana chifukwa cha Yesu. 44 Ena anafuna kumugwira Iye, koma palibe amene anayika dzanja pa Iye.
Kusakhulupirira kwa Atsogoleri a Ayuda
45 Pomaliza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu anabwerera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi amene anawafunsa iwo kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani simunamugwire Iye?”
46 Asilikali aja anati, “Palibe wina amene anayankhula ngati Munthu ameneyo nʼkale lonse.”
47 Afarisi anawadzudzula nati, “Kodi mukutanthauza kuti Iye anakunamizani inunso?” 48 “Kodi alipo ena a olamulira kapena a Afarisi, anamukhulupirira Iye? 49 Ayi! Koma gulu limene silidziwa malamulo ndi lotembereredwa.”
50 Nekodimo, amene anapita kwa Yesu poyamba paja ndipo anali mmodzi wa iwo, anafunsa kuti, 51 “Kodi lamulo lathu limatsutsa munthu popanda kumva mbali yake kuti tipeze chimene wachita?”
52 Iwo anayankha kuti, “Kodi ndiwenso wochokera ku Galileya? Tayangʼananso, ndipo udzapeza kuti mneneri sachokera ku Galileya.”
[Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe 7:53 mpaka 8:11]
Za Mkazi Wachigololo
53 Kenaka onse anachoka, napita kwawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.