Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 8

Ntchito Zina za Solomoni

Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga Nyumba ya Mulungu ndi nyumba yake yaufumu, Solomoni anamanganso midzi imene anapatsidwa ndi Hiramu, ndipo anakhazikamo Aisraeli. Kenaka Solomoni anapita kukalanda Hamati-zoba. Iye anamanganso Tadimori ku chipululu ndi mizinda yonse yosungiramo chuma, imene anayimanga ku Hamati. Anamanganso Beti-Horoni Wakumtunda ndi Beti-Horoni Wakumunsi, mizinda yotetezedwa yokhala ndi makoma, zitseko ndi zitsulo zotchingira, pamodzinso ndi Baalati ndi mizinda yake yonse yosungira chuma, ndiponso mizinda yonse yosungiramo magaleta ake ndi akavalo ndi chilichonse anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.

Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli). Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino. Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Aisraeli; Iwo anali anthu ake ankhondo, atsogoleri a ankhondo, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake. 10 Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za mfumu Solomoni. Onse amene ankayangʼanira anthu analipo 250.

11 Solomoni anabweretsa mwana wamkazi wa Farao mu mzinda wa Davide ku nyumba yaufumu yomwe anamumangira, pakuti iye anati, “Mkazi wanga asakhale mʼnyumba yaufumu ya Davide mfumu ya Israeli, chifukwa malo amene Bokosi la Chipangano la Yehova lafikira ndi opatulika.”

12 Solomoni anapereka nsembe zopsereza pa guwa lansembe la Yehova limene anamanga patsogolo pa khonde la polowera, 13 monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka nsembezo potsata malamulo a Mose okhudza chikondwerero cha Masabata, chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndi zikondwerero zitatu za pa chaka: Chikondwerero cha Buledi Wopanda yisiti, Chikondwerero cha Masabata ndi Chikondwerero cha Misasa. 14 Potsata malangizo a Davide abambo ake, iye anayika ansembe mʼmagulumagulu monga mwa ntchito zawo ndipo anayika Alevi kukhala otsogolera matamando ndi kuthandiza ansembe pa zofunika pa tsiku lililonse. Iye anasankhanso magulumagulu a alonda a pa zipata zosiyanasiyana, chifukwa izi ndi zimene munthu wa Mulungu, Davide analamula. 15 Anthu sanapatukepo pa zimene mfumu inalamula ansembe kapena Alevi pa china chilichonse, kuphatikiza za chuma.

16 Ntchito yonse ya Solomoni inachitika kuyambira tsiku limene maziko a Nyumba ya Mulungu anakhazikitsidwa mpaka kumaliza. Kotero Nyumba ya Yehova inamalizidwa.

17 Kenaka Solomoni anapita ku Ezioni-Geberi ndi Eloti, mʼmbali mwa nyanja ku Edomu. 18 Ndipo Hiramu anatumiza sitima zapamadzi zoyendetsedwa ndi antchito ake, antchito amene ankayidziwa bwino nyanja. Awa pamodzi ndi anthu a Solomoni, anayenda pa madzi kupita ku Ofiri ndipo anakatengako golide olemera makilogalamu 18,000 amene anabwera naye kwa mfumu Solomoni.

3 Yohane

Ndine mkulu wampingo, kulembera:

Gayo mnzanga wokondedwa, amene ndimamukonda mʼchoonadi.

Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu. Ine ndinali ndi chimwemwe chachikulu pamene abale ena anafika nʼkundifotokozera za kukhulupirika kwako pa choonadi ndiponso mmene umayendera motsata choonadi. Palibe chondikondweretsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akukhala mʼchoonadi.

Wokondedwa, ndiwe wokhulupirika pa zimene ukuchitira abale, ngakhale kuti iwowo ndi alendo. Iwo anafotokozera mpingo za chikondi chako. Chonde uwathandize kupitiriza ulendo mʼnjira yokondweretsa Mulungu. Pakuti ananyamuka ulendo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye, osalandira thandizo kwa osakhulupirira. Ife tiyenera kumathandiza anthu oterewa, kuti tigwirizane nawo pa ntchito ya choonadi.

Za Diotrefe ndi Demetriyo

Ndinalembera mpingo, koma Diotrefe, amene amafuna kukhala wotsogolera, sanafune kutimvera. 10 Tsono ndikabwera ndidzakumbutsa zimene iye amachita. Iye amafalitsa nkhani zabodza zonena ife. Ndipo sakhutira ndi zimenezo, komanso iyeyo amakana kulandira abale. Komanso amaletsa amene akufuna kutero, ndipo amawachotsa mu mpingo.

11 Wokondedwa, usatsatire zinthu zoyipa koma zinthu zabwino. Aliyense amene amachita zinthu zabwino ndi wochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amachita zoyipa sanamuonepo Mulungu. 12 Aliyense akumuchitira umboni wabwino wa Demetriyo. Ngakhale choona chomwe chimamuchitira umboni, ndipo iweyo ukudziwa kuti umboni wathu ndi woona.

13 Ndili ndi zambiri zoti ndikulembereni, koma sindikufuna kuzilemba mʼkalata. 14 Ndiyembekezera kufika kwanuko posachedwapa, ndipo tidzakambirana pamaso ndi pamaso.

15 Mtendere ukhale nawe. Abwenzi anu kuno akupereka moni. Upereke moni kwa abwenzi onse mmodzimmodzi.

Habakuku 3

Pemphero la Habakuku

Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti.

Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu;
    Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa.
Muzichitenso masiku athu ano,
    masiku athu ano zidziwike;
    mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo.

Mulungu anabwera kuchokera ku Temani,
    Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani.
            Sela
Ulemerero wake unaphimba mlengalenga
    ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.
Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa;
    kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake,
    mʼmene anabisamo mphamvu zake.
Patsogolo pake pankagwa mliri;
    nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake.
Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi;
    anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera.
Mapiri okhazikika anagumuka
    ndipo zitunda zakalekale zinatitimira.
    Njira zake ndi zachikhalire.
Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto,
    mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu.

Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje?
    Kodi munakalipira timitsinje?
Kodi munapsera mtima nyanja
    pamene munakwera pa akavalo anu
    ndiponso magaleta anu achipulumutso?
Munasolola uta wanu mʼchimake,
    munayitanitsa mivi yambiri.
            Sela
Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje;
10     mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka.
Madzi amphamvu anasefukira;
    nyanja yozama inakokoma
    ndipo mafunde ake anakwera kwambiri.

11 Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga,
    pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo,
    pa kunyezimira kwa mkondo wanu.
12 Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali,
    ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo.
13 Munapita kukalanditsa anthu anu,
    kukapulumutsa wodzozedwa wanu.
Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa,
    munawononga anthu ake onse.
            Sela
14 Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wake
    pamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa,
ankasangalala ngati kuti akudzawononga
    osauka amene akubisala.
15 Munapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu,
    kuvundula madzi amphamvu.

16 Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri,
    milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo;
mafupa anga anaguluka,
    ndipo mawondo anga anawombana.
Komabe ndikuyembekezera mofatsa,
    tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo.
17 Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,
    ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa.
Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso,
    ndipo mʼminda musatuluke kanthu.
Ngakhale nkhosa
    ndi ngʼombe zithe mʼkhola,
18 komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova,
    ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

19 Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga;
    amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi,
    amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.

Luka 22

Yudasi Avomera Kumupereka Yesu

22 Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu. Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo. Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu. Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama. Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi.

Paska Womaliza

Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe. Yesu anatuma Petro ndi Yohane nati, “Pitani kukatikonzera Paska kuti tikadye.”

Iwo anafunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonzere kuti?”

10 Iye anayankha kuti, “Taonani, mukamalowa mu mzinda, mudzakumana ndi mwamuna atanyamula mtsuko wamadzi. Mulondoleni ku nyumba imene akalowe, 11 ndipo mukamuwuze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi kufunsa kuti, chili kuti chipinda cha alendo, kumene Ine ndi ophunzira anga tikadyere Paska?’ 12 Iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala ndi zonse. Kachiteni zokonzekera mʼmenemo.”

13 Iwo anapita nakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Tsono anakonza Paska.

Za Mgonero wa Ambuye

14 Ora litakwana, Yesu ndi ophunzira ake anakhala pa tebulo. 15 Ndipo Iye anawawuza kuti, “Ine ndakhala ndikuyembekezera kudya Paska uyu ndi inu ndisanamve zowawa. 16 Pakuti Ine ndikukuwuzani kuti sindidzadyanso Paska wina mpaka Paskayi itakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.”

17 Atanyamula chikho, Iye anayamika ndipo anati, “Tengani ndipo patsiranani pakati panu. 18 Pakuti ndikukuwuzani kuti, Ine sindidzamwanso zochokera ku chipatso cha mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utabwera.”

19 Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”

20 Chimodzimodzinso, utatha mgonero, anatenga chikho nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga, amene akhetsedwa chifukwa cha inu. 21 Koma dzanja la amene akundipereka Ine lili pamodzi ndi langa pa chakudya pano. 22 Mwana wa Munthu apita monga mmene zinalembedwera, koma tsoka kwa munthu amene amupereka Iye.” 23 Iwo anayamba kufunsana pakati pawo kuti ndi ndani wa iwo amene akanachita ichi.

Mkangano Pakati pa Ophunzira

24 Komanso mkangano unabuka pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene amaganiziridwa kukhala wamkulu. 25 Yesu anawawuza kuti, “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’ 26 Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira. 27 Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani. 28 Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero. 29 Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine, 30 kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.”

Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana

31 “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu. 32 Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.”

33 Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.”

34 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza Petro, tambala asanalire lero lino, udzandikana katatu kuti sukundidziwa Ine.”

35 Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, “Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?”

Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.”

36 Iye anawawuza kuti, “Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula. 37 Zalembedwa kuti, ‘Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi anthu ochimwa,’ ndipo Ine ndikuwuzani kuti izi ziyenera kukwaniritsidwa mwa Ine. Inde, zimene zinalembedwa za Ine, zikukwaniritsidwa.”

38 Ophunzira anati, “Taonani Ambuye, awa malupanga awiri.”

Iye anayankha kuti, “Amenewa akwanira.”

Yesu Apemphera ku Phiri la Olivi

39 Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye. 40 Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti, “Pempherani kuti musagwe mʼmayesero.” 41 Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti, 42 “Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.” 43 Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa. 44 Ndipo mopsinjika mtima, anapemphera moona mtima, ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi akugwera pansi.

45 Iye atamaliza kupemphera, ndi kubwerera kwa ophunzira ake, anawapeza atagona atafowoka ndi chisoni. 46 Iye anafunsa kuti, Nʼchifukwa chiyani mukugona? “Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero.”

Amugwira Yesu

47 Pamene Iye ankayankhulabe, gulu la anthu linabwera, ndipo munthu wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo analitsogolera. Iye anamuyandikira Yesu kuti amupsompsone. 48 Koma Yesu anamufunsa kuti, “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa Munthu ndi mpsopsono?”

49 Otsatira Yesu ataona zimene zimati zichitike, anati, “Ambuye, kodi timenyane ndi malupanga athu?” 50 Ndipo mmodzi wa iwo anatema wantchito wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake lamanja.

51 Koma Yesu anayankha kuti, “Zisachitikenso zimenezi!” Ndipo Iye anakhudza khutu la munthuyo ndi kumuchiritsa.

52 Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga? 53 Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.”

Petro Akana Yesu

54 Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali. 55 Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi. 56 Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.”

57 Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.”

58 Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, “Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo.”

Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, ayi sindine.”

59 Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, “Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya.”

60 Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira. 61 Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, “Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.” 62 Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri.

Asilikali Amuchita Chipongwe Yesu

63 Anthu amene ankalonda Yesu anayamba kumuchita chipongwe ndi kumumenya. 64 Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?” 65 Ndipo iwo anamunena zachipongwe zambiri.

Yesu Pamaso pa Pilato ndi Herode

66 Kutacha, bungwe la akuluakulu, pamodzi ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anakumana pamodzi, ndipo anamuyika Yesu patsogolo pawo. 67 Iwo anati, “Tiwuze, ngati ndiwe Khristu.”

Yesu anayankha kuti, “Ine nditakuwuzani simungandikhulupirire. 68 Ine nditakufunsani inu, simungandiyankhe. 69 Koma kuyambira tsopano, Mwana wa Munthu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvu.”

70 Onse anafunsa kuti, “Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?”

Iye anayankha kuti, “Mwanena ndinu kuti Ndine.”

71 Pamenepo iwo anati, “Nanga tikufuniranjinso umboni wina? Ife tamva kuchokera pa milomo yake.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.