Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 7

Mwambo Wopereka Nyumba kwa Yehova

Solomoni atamaliza kupemphera, moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kutentha nsembe zopsereza ndi nsembe zina, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulunguyo. Ansembe sanathe kulowa mʼNyumba ya Mulungu chifukwa munadzaza ulemerero wa Yehova. Aisraeli onse ataona moto ukuchokera kumwamba ndi ulemerero wa Yehova pamwamba pa Nyumba ya Mulungu, anagwada poyalidwa miyalapo ndipo anagunditsa nkhope zawo pansi, ndi kulambira ndi kutamanda Yehova, ponena kuti,

“Iye ndi wabwino;
    chikondi chake chikhala chikhalire”

Tsono mfumu ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova. Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Kotero mfumu ndi anthu onse anachita mwambo wopereka Nyumba kwa Mulungu. Ansembe anayimirira mʼmalo mwawo, monganso anachitira Alevi ndi zida zoyimbira za Yehova, zimene Davide anapanga zotamandira Yehova ndipo zimagwiritsidwa ntchito pamene amatamanda, ponena kuti, “Chikondi chake chikhale chikhalire.” Moyangʼanizana ndi Alevi, ansembe amaliza malipenga, ndipo Aisraeli onse anali atayimirira.

Solomoni anapatula malo a pakati pa bwalo kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndipo pamenepo anapereka nsembe zopsereza ndi mafuta, zopereka za chiyanjano, chifukwa guwa lansembe lamkuwa limene anapanga panalibe malo woti nʼkuperekerapo nsembe zopsereza, nsembe za ufa ndi mafuta.

Choncho nthawi imeneyi, Solomoni anachita chikondwerero kwa masiku asanu ndi awiri pamodzi ndi Aisraeli onse. Unali msonkhano waukulu, kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku chigwa cha ku Igupto. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panali msonkhano, pakuti anachita mwambo wopereka guwa lansembe kwa masiku asanu ndi awiri ndi masiku enanso asanu ndi awiri achikondwerero. 10 Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Solomoni anawuza anthu aja kuti apite kwawo. Anthu anali achimwemwe ndi okondwa mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira Davide ndi Solomoni ndiponso anthu ake Aisraeli.

Yehova Aonekera Solomoni

11 Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene zinali mu mtima mwake pa Nyumba ya Yehova ndi nyumba yake yaufumu, 12 Yehova anamuonekera usiku ndipo anati:

“Ine ndamva pemphero lako ndipo ndadzisankhira malo ano kukhala Nyumba yanga yoperekeramo nsembe.

13 “Ine ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe, kapena kulamulira dzombe kuti liwononge dziko, kapena kutumiza mliri pakati pa anthu, 14 ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo. 15 Ndipo maso anga adzatsekuka ndi makutu anga adzakhala tcheru kumva mapemphero a pamalo pano. 16 Ine ndasankha ndipo ndapatula Nyumba yangayi kotero kuti ndidzakhala mʼmenemo kwamuyaya. Maso ndi mtima wanga zidzakhala pano nthawi zonse.

17 “Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula, ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga, 18 Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu, monga ndinachitira pangano ndi abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu wolamulira Israeli.’

19 “Koma ngati iwe udzapatuka ndi kutaya malangizo ndi malamulo amene ndakupatsa ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, 20 pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko langa limene ndinawapatsa, ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndadzipatulira. Ndipo udzakhala ngati mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse. 21 Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’ 22 Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova, Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’ ”

2 Yohane

Ndine mkulu wampingo, kulembera:

Mayi wosankhidwa ndi Mulungu ndi kwa ana ake amene ndimawakonda mʼchoonadi. Ndipo sindine ndekha amene ndimawakonda, komanso onse odziwa choonadi. Timakukondani chifukwa cha choonadi chimene chimakhala mwa ife ndipo chidzakhala mwa ife mpaka muyaya.

Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Yesu Khristu, Mwana wa Atate, zikhale ndi ife mʼchoonadi ndi mʼchikondi.

Choonadi ndi Chikondi

Ndinakondwera kwambiri nditapeza ana anu ena akuyenda mʼchoonadi, monga Atate anatilamulira. Ndipo tsopano, amayi wokondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lomwe lija takhala nalo kuyambira pachiyambi. Ine ndikukupemphani kuti tidzikondana wina ndi mnzake. Ndipo chikondi ndiye kuyenda momvera malamulo ake. Lamulo lake ndi lakuti mukhale moyo wachikondi monga munamva kuyambira pachiyambi.

Ndikunena zimenezi chifukwa anthu ambiri onyenga, amene savomereza kuti Yesu Khristu anabwera monga munthu, akuyenda mʼdziko lapansi. Munthu aliyense otere ndi wonyenga ndiponso wokana Khristu. Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma chitani khama kuti mukalandire mphotho yanu yonse. Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana. 10 Ngati wina aliyense abwera kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamulandire mʼnyumba mwanu kapena kumupatsa moni. 11 Aliyense wolandira munthu wotere ndiye kuti akuvomerezana nazo ntchito zake zoyipa.

12 Ndili nazo zambiri zoti ndikulembereni, koma sindikufuna kuzilemba mʼkalata. Mʼmalo mwake, ndikuyembekeza kufika kwanuko kuti tidzakambirane nanu pamaso ndi pamaso, potero chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu.

13 Ana a mlongo wanu wosankhidwa ndi Mulungu akupereka moni.

Habakuku 2

Ndidzakhala pa malo anga aulonda,
    ndi kuyima pa mitumbira ya nkhondo;
ndidzadikira kuti ndimve zimene Iye adzandiwuze,
    ndi yankho limene ndidzapatsidwe pa madandawulo anga.

Yankho la Yehova

Tsono Yehova anandiyankha, nati:

“Lemba masomphenyawa
    ndipo uwalembe mooneka bwino pa mapale
    kuti wowerenga awawerenge mosavuta.
Pakuti masomphenyawa akudikira nthawi yake;
    masomphenyawa akunena zamʼtsogolo
    ndipo sizidzalephera kuchitika.
Ngakhale achedwe kukwaniritsidwa, uwayembekezere;
    zidzachitika ndithu ndipo sadzachedwa.

“Taona, mdani wadzitukumula;
    zokhumba zake sizowongoka,
    koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
Ndithu, wasokonezeka ndi vinyo;
    ndi wodzitama ndiponso wosakhazikika.
Pakuti ngodzikonda ngati manda,
    ngosakhutitsidwa ngati imfa,
wadzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu
    ndipo wagwira ukapolo anthu a mitundu yonse.

“Kodi onse ogwidwawo sadzamunyoza ndi kumunyogodola ponena kuti,

“Tsoka kwa amene amadzikundikira katundu amene si wake
    ndipo amadzilemeretsa ndi chuma cholanda!
    Kodi izi zidzachitika mpaka liti?
Kodi angongole ako sadzakuwukira mwadzidzidzi?
    Kodi sadzadzuka ndi kukuchititsa mantha?
    Pamenepo iwe udzalandidwa kalikonse.
Pakuti unafunkha mitundu yambiri ya anthu,
    mitundu ina imene inatsala idzakufunkha iweyo.
Pakuti wakhetsa magazi a anthu;
    wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.

“Tsoka kwa amene amalemera ndi chuma chochipeza mwachinyengo,
    kukweza malo ake okhalapo,
    kuthawa mavuto!
10 Wakonzekera kuwononga mitundu yambiri ya anthu,
    kuchititsa manyazi nyumba yako yomwe ndi kuwononga moyo wako.
11 Mwala pa khoma udzafuwula,
    ndipo mitanda ya matabwa idzavomereza zimenezi.

12 “Tsoka kwa amene amanga mzinda pokhetsa magazi
    ndi kukhazikitsa mzinda pochita zoyipa!
13 Kodi Yehova Wamphamvuzonse sanatsimikize
    kuti ntchito za anthu zili ngati nkhuni pa moto,
    ndi kuti mitundu ya anthu imadzitopetsa popanda phindu?
14 Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova,
    monga momwe madzi amadzazira nyanja.

15 “Tsoka kwa amene amamwetsa anzake zakumwa zoledzeretsa,
    kutsanula mʼbotolo mpaka ataledzera,
    kuti aone umaliseche wawo.
16 Udzachita manyazi mʼmalo mokhala ndi ulemerero.
    Tsopano ino ndi nthawi yako! Imwa mpaka umaliseche wako uwonekere!
Chikho chochokera mʼdzanja lamanja la Yehova chikubwera kwa iwe,
    ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako.
17 Udzathedwa nzeru ndi chiwawa chimene unachita ku Lebanoni,
    ndiponso udzachita mantha ndi nyama zimene unaziwononga.
Pakuti wakhetsa magazi a anthu;
    wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.

18 “Kodi fano lili ndi phindu lanji, poti analisema ndi munthu,
    kapena chifanizo chimene chimaphunzitsa mabodza?
Pakuti munthu amene walipanga amakhulupirira ntchito ya manja ake;
    amapanga mafano amene samatha kuyankhula.
19 Tsoka kwa amene amawuza mtengo kuti, ‘Khala wamoyo!’
    Kapena mwala wopanda moyo kuti, ‘Dzuka!’
Kodi zimenezi zingathe kulangiza?
    Ndi zokutidwa ndi golide ndi siliva;
    mʼkati mwake mulibe mpweya.
20 Koma Yehova ali mʼNyumba yake yopatulika;
    dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.”

Luka 21

Chopereka cha Mayi Wamasiye

21 Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu. Iye anaonanso mkazi wamasiye wosauka akuyikamo timakopala tiwiri. Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa. Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.”

Zizindikiro za Masiku Otsiriza

Ena mwa ophunzira ake ankachita ndemanga za mmene Nyumba ya Mulungu anayikongoletsera ndi miyala yokongola ndiponso zinthu zina zomwe anthu anapereka kwa Mulungu. Koma Yesu anati, “Koma zimene mukuziona panozi, nthawi idzafika pamene ngakhale mwala umodzi omwe sudzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”

Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi zonsezi zidzachitika liti? Ndipo tidzaonera chiyani kuti zili pafupi kuchitika?”

Iye anayankha kuti, “Chenjerani kuti musanyengedwe. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati ‘Ine ndine Iye’ ndi kuti ‘Nthawi yayandikira.’ Musadzawatsate iwo. Mukadzamva zankhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha. Zinthu izi ziyenera kuchitika poyamba, koma chimaliziro sichidzafika nthawi yomweyo.”

10 Kenaka anawawuza kuti, “Mtundu wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu kuwukira ufumu wina. 11 Kudzakhala zivomerezi zazikulu, njala ndi miliri mʼmalo osiyanasiyana, ndi zinthu zoopsa ndi zizindikiro zamphamvu kuchokera kumwamba.

12 “Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa. 13 Umenewu udzakhala mwayi wanu ochitira umboni. 14 Koma tsimikizani mtima kuti musadzade nkhawa za momwe mudzadzitchinjirizire. 15 Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa. 16 Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani. 17 Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine. 18 Koma palibe tsitsi limodzi la mʼmutu mwanu lidzawonongeke. 19 Mukadzalimbikira ndiye mudzapeze moyo.

Kuwonongedwa kwa Yerusalemu

20 “Mukadzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, inu mudzadziwe kuti kuwonongeka kwake kuli pafupi. 21 Pamenepo amene ali ku Yudeya adzathawire ku mapiri, amene ali mu mzinda adzatulukemo, ndi amene ali ku midzi asadzalowe mu mzinda. 22 Pakuti iyi ndi nthawi yachilango pokwaniritsa zonse zimene zinalembedwa. 23 Zidzakhala zoopsa nthawi imenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! Kudzakhala masautso aakulu mʼdziko ndipo anthu onse adzawakwiyira. 24 Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndi kutengedwa ukapolo kupita ku mayiko wonse. Yerusalemu adzaponderezedwa ndi anthu a mitundu ina mpaka nthawi ya a mitundu ina itakwaniritsidwa.

25 “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja. 26 Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha, akadzamva za zimene zikubwera pa dziko lapansi, pakuti zinthu zamlengalenga zidzagwedezeka. 27 Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu. 28 Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzayimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”

Fanizo la Mtengo Wamkuyu

29 Iye anawawuza fanizo ili, “Taonani mtengo wamkuyu ndi mitengo ina yonse. 30 Ikamatulutsa masamba, mumakhoza kudzionera nokha ndi kudziwa kuti dzinja lili pafupi. 31 Chimodzimodzinso, mukadzaona zinthu zonsezi, dziwani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.

32 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika. 33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”

Za Kukhala Tcheru

34 “Samalani, kuti mitima yanu ingalemetsedwe ndi maphwando, kuledzera ndi kudera nkhawa za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingadzakupezeni modzidzimutsa ngati msampha. 35 Pakuti lidzafika pa onse okhala pa dziko lonse lapansi. 36 Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu.”

37 Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse. 38 Ndipo anthu onse amabwera mmamawa kudzamumva Iye ku Nyumba ya Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.