Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 6:12-42

Pemphero la Solomoni

12 Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova patsogolo pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake. 13 Iyeyo anali atapanga nsanja yamkuwa, kutalika kwake kunali mamita awiri, mulifupi mwake munali mamita awiri, msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka ndipo nsanjayo anayimika pakati pa bwalo lakunja. Iye anayimirira pa nsanjapo nagwada pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba. 14 Iye anati,

“Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pa dziko. Inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse. 15 Inu mwasunga lonjezo lanu kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu. Inde zimene munalonjeza ndi pakamwa panu, mwazikwaniritsa ndi manja anu monga mmene tikuonera lero lino.

16 “Ndipo tsopano, Inu Yehova Mulungu wa Israeli, sungani zimene munalonjeza kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu pamene munati, ‘Sudzasowa munthu wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israeli, ngati ana ako adzasamalira mayendedwe awo ndi kusunga malamulo anga monga iwe wachitira.’ 17 Ndipo tsopano Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, lolani kuti mawu anu akwaniritsidwe amene munalonjeza mtumiki wanu Davide.

18 “Kodi Mulungu angakhaledi pa dziko lapansi ndi munthu? Mlengalenga ngakhale kumwamba kwenikweni sikungakukwaneni. Nanga kuli bwanji ndi Nyumba iyi imene ndamanga! 19 Koma Inu Yehova, Mulungu wanga, imvani pemphero ndi pembedzero la mtumiki wanu. Imvani kulira ndi pemphero la mtumiki wanu limene ndikupempha pamaso panu. 20 Maso anu azikhala otsekuka kuyangʼana Nyumba ino usana ndi usiku, malo ano amene Inu munati mudzayikamo Dzina lanu, imvani pemphero la mtumiki wanu limene akupemphera pa malo ano. 21 Imvani mapembedzero a mtumiki wanu ndi a anthu anu Aisraeli pamene akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani kumwambako, malo anu amene mumakhala; ndipo mukamva muzitikhululukira.

22 “Munthu akalakwira mnzake, nawuzidwa kuti alumbire, akabwera kudzalumbira patsogolo pa guwa lansembe la Nyumba ino, 23 imvani kumwambako ndi kuchitapo kanthu. Weruzani atumiki anuwo, wochimwa mugamule kuti ndi wolakwa ndipo alangidwe chifukwa cha zimene wachita. Wosachimwa mugamule kuti wosalakwa, ndipo muonetse kusalakwa kwakeko.

24 “Anthu anu Aisraeli akagonja kwa adani awo chifukwa akuchimwirani ndipo akatembenukira kwa Inu ndi kuvomereza Dzina lanu, kupemphera ndi kupembedzera pamaso panu mʼNyumba ino, 25 pamenepo imvani kumwambako ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraeli ndi kuwabweretsa ku dziko limene munawapatsa iwo ndi makolo awo.

26 “Pamene kumwamba kwatsekeka ndipo mvula sikugwa chifukwa anthu anu akuchimwirani, ndipo pamene apemphera akuyangʼana malo ano ndi kuvomereza Dzina lanu ndi kutembenuka kuchoka ku machimo awo chifukwa inu mwawalanga, 27 pamenepo imvani kumwambako ndipo muwakhululukire atumiki anu, anthu anu Aisraeli. Aphunzitseni makhalidwe oyenera, ndipo gwetsani mvula mʼdziko limene munapereka kwa anthu anu monga cholowa chawo.

28 “Pamene mʼdziko mwagwa njala kapena mliri, chinoni kapena chiwawu, dzombe kapena kapuchi, kapena pamene adani azungulira mzinda wawo wina uliwonse, kaya mavuto kapena matenda abwera, 29 ndipo wina aliyense mwa Aisraeli akapemphera kapena kukudandaulirani, aliyense wa iwo akadziwa masautso ake ndi ululu wake, ndi kukweza manja awo kuloza Nyumba ino, 30 pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita popeza Inu mumadziwa mtima wake, (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu), 31 motero iwo adzakuopani ndipo adzayenda mʼnjira zanu masiku onse amene adzakhale mʼdziko limene munalipereka kwa makolo athu.

32 “Ndipo kunena za mlendo amene si mmodzi wa anthu anu Aisraeli, koma wabwera kuchokera ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lotchukali, ndiponso za dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu, kudzapemphera akuyangʼana Nyumba ino, 33 pamenepo imvani kumwambako, malo anu okhalamo, ndipo muchite zonse zimene mlendoyo akukupemphani, kotero kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu ndi kukuopani monga amachitira anthu anu Aisraeli, ndipo adziwe kuti nyumba ino imene ndakumangirani imadziwika ndi dzina lanu.

34 “Anthu akapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani awo, kulikonse kumene mungawatume, ndipo akapemphera moyangʼana mzinda uno umene mwausankha ndi Nyumba yanu imene ndakumangirani, 35 pamenepo imvani kumwamba pemphero lawo ndi kupempha kwawo ndipo muwapulumutse.

36 “Pamene achimwira inu, pakuti palibe amene sachimwa, ndipo inu mwawakwiyira ndi kuwapereka kwa adani awo, amene awatenga ukapolo ku dziko lawo lakutali kapena pafupi. 37 Ngati asintha mitima yawo ku dziko limene ali akapolo ndi kulapa ndi kukudandaulirani inu mʼdziko la ukapolo wawo ndi kunena kuti, ‘Ife tachimwa, tachita zolakwa ndipo tachita moyipa kwambiri.’ 38 Ndipo ngati atembenukira kwa inu ndi mtima ndi moyo wawo wonse mʼdziko lawo la ukapolo kumene anatengedwako ndi kupemphera moyangʼana dziko limene inu munalipereka kwa makolo awo, moyangʼana Nyumba yanu imene ndakumangirani; 39 pamenepo imvani kumwamba, malo anu okhala, pemphero lawo ndi kudandaula kwawo, ndipo muwapulumutse. Ndipo mukhululukire anthu anu, amene akuchimwirani.

40 “Tsono Inu Mulungu wanga, tsekulani maso anu ndi makutu anu kuti mumve mapemphero ochitikira pa malo ano.

41 “Tsopano dzukani Inu Yehova Mulungu, ndipo bwerani ku malo anu ampumulo,
    Inu ndi Bokosi la Chipangano la mphamvu zanu.
Inu Yehova Mulungu, ansembe anu avale chipulumutso,
    oyera mtima anu akondwere ndi kukhulupirika kwanu.
42 Inu Yehova Mulungu musamukane wodzozedwa wanu.
    Kumbukirani chikondi chanu chachikulu chimene munalonjeza kwa Davide mtumiki wanu.”

1 Yohane 5

Chikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu

Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, iyeyo ndi mwana wa Mulungu, ndipo aliyense amene amakonda Atate amakondanso Mwana wake. Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nʼchakuti timakonda Mulungu ndi kusunga malamulo ake. Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa, chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.

Uyu ndiye anabwera mwa madzi ndi magazi, ndiye Yesu Khristu. Sanabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi magazi. Ndipo ndi Mzimu Woyera amene akuchitira umboni, chifukwa Mzimu Woyera ndi choonadi. Pakuti pali atatu amene amachitira umboni. Mzimu Woyera, madzi ndi magazi; ndipo atatu amavomerezana. Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana. Umboniwo ndi umene anachitira Mwana wake. 10 Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake. 11 Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. 12 Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.

Mawu Otsiriza

13 Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha. 14 Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera. 15 Ndipo ngati tikudziwa kuti amatimvera, chilichonse chimene timapempha, tikudziwanso kuti tili nacho chimene tamupempha Iye.

16 Ngati wina aona mʼbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere ndipo Mulungu adzamupatsa moyo mʼbale wakeyo. Ndikunena za ochita tchimo losadzetsa imfa. Pali tchimo lodzetsa imfa. Ine sindikunena kuti apemphere ayi. 17 Chilichonse chosalungama ndi tchimo ndipo pali tchimo losadzetsa imfa.

18 Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze. 19 Tikudziwa kuti ndife ana a Mulungu ndi kuti dziko lonse lapansi lili pansi pa ulamuliro wa woyipayo. 20 Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anafika ndipo anatipatsa nzeru, kuti timudziwe Iye amene ali woona. Ndipo ife tili mwa Iye amene ndi woona, Mwana wake, Yesu Khristu. Iye ndi Mulungu woona ndi moyo wosatha.

21 Ana okondedwa, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Habakuku 1

Uthenga umene mneneri Habakuku analandira mʼmasomphenya.

Dandawulo la Habakuku

Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani,
    koma wosayankha?
Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!”
    koma wosatipulumutsa?
Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa?
    Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa?
Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa;
    pali ndewu ndi kukangana kwambiri.
Kotero malamulo anu atha mphamvu,
    ndipo chilungamo sichikugwira ntchito.
Anthu oyipa aposa olungama,
    kotero apotoza chilungamo.

Yankho la Yehova

“Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu, ndipo penyetsetsani,
    ndipo muthedwe nazo nzeru.
Pakuti ndidzachitadi zinthu pa nthawi yanu
    zimene inu simudzazikhulupirira,
    ngakhale wina atakufotokozerani.
Pakuti taonani, Ine ndikuwutsa Ababuloni,
    anthu ankhanza ndiponso amphamvu,
amene amapita pa dziko lonse lapansi
    kukalanda malo amene si awo.
Iwowa ndi anthu ochititsa mantha, ndipo ndi owopsa;
    amadzipangira okha malamulo
    ndi kudzipezera okha ulemu.
Akavalo awo ndi aliwiro kwambiri kupambana akambuku
    ndi owopsa kupambana mimbulu yolusa nthawi ya madzulo.
Okwerapo awo akuthamanga molunjika;
    a pa akavalo awo ndi ochokera kutali,
akuwuluka ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama;
    onse akubwera atakonzekera zachiwawa.
Gulu la ankhondo likubwera ngati mphepo ya mʼchipululu
    ndi kugwira akapolo ochuluka ngati mchenga.
10 Akunyoza mafumu
    ndiponso kuchitira chipongwe olamulira.
Akupeputsa mizinda yonse yotetezedwa;
    akumanga mitumbira ndi kulanda mizindayo.
11 Kenaka amasesa mofulumira ngati mphepo nʼkumangopitirirabe,
    anthu ochimwa, amene mphamvu zawo ndiye mulungu wawo.”

Dandawulo Lachiwiri la Habakuku

12 Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire?
    Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa.
Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo;
    Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange.
13 Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa;
    Inu simulekerera cholakwa.
Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa?
    Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa
    akuwononga anthu olungama kupambana iwowo?
14 Mwasandutsa anthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja,
    ngati zolengedwa zamʼnyanja zimene zilibe wolamulira.
15 Mdani wawo woyipa amakoka anthu onse ndi mbedza,
    amawakola mu ukonde wake,
amawasonkhanitsa mu khoka lake;
    kotero iyeyo amakondwa ndi kusangalala.
16 Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake
    ndiponso kufukizira lubani khoka lake,
popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba
    ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri.
17 Kodi iye azipitirabe kugwiritsa ntchito makoka akewo,
    kuwononga mitundu ya anthu mopanda chifundo?

Luka 20

Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake

20 Tsiku lina pamene Iye ankaphunzitsa anthu mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu ndi kuphunzitsa Uthenga Wabwino, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, pamodzi ndi akuluakulu anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Mutiwuze mukuchita izi ndi ulamuliro wayani? Ndani anakupatsani ulamuliro uwu?”

Iye anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani, mundiyankhe, ‘Kodi ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena wochokera kwa anthu?’ ”

Iwo anakambirana pakati pawo ndikuti, “Ngati ife tinena kuti, ‘Kuchokera kumwamba’ Iye akatifunsa kuti, ‘chifukwa chiyani simunamukhulupirire iye?’ Koma ngati ife tinena kuti, ‘kuchokera kwa anthu,’ anthu onse atigenda miyala, chifukwa amatsimikiza kuti Yohane anali mneneri.”

Pamenepo iwo anayankha kuti, “Ife sitidziwa kumene unachokera.”

Yesu anati, “Ngakhale Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira zimenezi.”

Fanizo la Olima Mʼmunda Wamphesa

Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali. 10 Pa nthawi yokolola, iye anatumiza wantchito wake kwa alimi aja kuti amupatseko zina mwa zipatso za munda wamphesawo. Koma alimi aja anamumenya namubweza wopanda kanthu. 11 Iye anatumiza wantchito wina, koma uyunso anamumenya namuchita zachipongwe ndi kumubweza wopanda kanthu. 12 Iye anatumizanso wina wachitatu ndipo iwo anamuvulaza namuponya kunja.

13 “Kenaka mwini mundawo anati, ‘Kodi ndichite chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wamwamuna, amene ndimukonda; mwina iwo adzamuchitira ulemu.’

14 “Koma alimiwo ataona mwanayo, anakambirananso. Iwo anati, ‘Uyu ndiye wodzamusiyira chumachi. Tiyeni timuphe ndipo chumachi chikhala chathu.’ 15 Ndipo anamuponya kunja kwa mundawo ndi kumupha.

“Nanga tsono mwini munda wamphesayo adzawatani anthuwa? 16 Iye adzabwera ndi kupha alimi aja ndi kupereka mundawo kwa ena.”

Pamene anthu anamva izi, anati, “Musatero ayi.”

17 Yesu anawayangʼanitsitsa ndipo anafunsa kuti, “Kodi tanthauzo lake ndi chiyani la zimene zinalembedwa kuti,

“ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana
    wasanduka mwala wa pa ngodya.

18 Aliyense amene agwa pa mwalawu adzapweteka, koma iye amene udzamugwera udzamuphwanya.’ ”

19 Aphunzitsi amalamulo ndi akulu a ansembe amafuna njira yoti amuphe nthawi yomweyo, chifukwa anadziwa kuti ananena fanizo ili powatsutsa iwo. Koma iwo anali ndi mantha chifukwa cha anthu.

Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara

20 Pamene ankamulondalonda Iye, iwo anatumiza akazitape amene amaoneka ngati achilungamo. Iwo ankafuna kumutapa mʼkamwa Yesu mu china chilichonse chimene Iye ananena kuti amupereke Iye kwa amene anali ndi mphamvu ndi ulamuliro oweruza. 21 Potero akazitapewo anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi, tidziwa kuti mumayankhula ndi kuphunzitsa zimene zili zoonadi, ndi kuti simuonetsa tsankho koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mwachoonadi. 22 Kodi ndi bwino kwa ife kumapereka msonkho kwa Kaisara kapena kusapereka?”

23 Iye anaona chinyengo chawo ndipo anawawuza kuti, 24 “Onetseni ndalama. Chithunzi ndi malembawa ndi zayani?”

25 Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.”

Iye anawawuza kuti, “Ndiye perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zimene ndi za Mulungu.”

26 Iwo analephera kumupeza cholakwa pa zimene ankayankhula pamaso pa anthu. Ndipo pothedwa nzeru ndi yankho lake, iwo anakhala chete.

Za Kuuka kwa Akufa ndi Ukwati

27 Ena mwa Asaduki, amene ankanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Yesu ndi funso. 28 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 29 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyambayo anakwatira mkazi ndipo anafa wopanda mwana. 30 Wachiwiri 31 ndipo kenaka wachitatuyo anamukwatira iye, ndipo chimodzimodzi asanu ndi awiri aja anafa osasiya ana. 32 Pa mapeto pake mkaziyo anafanso. 33 Tsopano, pa nthawi ya kuukanso, kodi mkaziyu adzakhala wayani popeza onse asanu ndi awiri anamukwatirapo?”

34 Yesu anayankha kuti, “Anthu a mʼbado uno amakwatira ndi kukwatiwa. 35 Koma mʼmoyo umene ukubwerawo, anthu amene adzaukitsidwe kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa. 36 Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa. 37 Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’ 38 Mulungu si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo, pakuti kwa Iye onse ali ndi moyo.”

39 Ena mwa aphunzitsi amalamulo anayankha kuti, “Mwanena bwino mphunzitsi!” 40 Ndipo panalibe wina amene akanalimba mtima kumufunsa Iye mafunso ena.

Khristu ndi Mwana wa Ndani?

41 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Zikutheka bwanji kuti aziti Khristu ndi mwana wa Davide? 42 Davide mwini wake akunenetsa mʼbuku la Masalimo kuti,

“Ambuye anati kwa Ambuye anga:
    ‘Khalani ku dzanja langa lamanja,
43 mpaka Ine nditasandutsa adani anu
    chopondapo mapazi anu?’

44 Davide akumutcha Iye ‘Ambuye.’ Nanga zingatheke bwanji kuti Iye akhale mwana wake?”

Achenjeza za Aphunzitsi Amalamulo

45 Pamene anthu onse ankamvetsera, Yesu anati kwa ophunzira ake, 46 “Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando. 47 Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.