Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 3-4

Solomoni Amanga Nyumba ya Mulungu

Pamenepo Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu pa Phiri la Moriya, pamene Yehova anaonekera Davide abambo ake. Panali pabwalo lopunthirapo tirigu la Arauna Myebusi, malo amene anapereka Davide. Iye anayamba kumanga pa tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake.

Maziko amene Solomoni anayika pomanga Nyumba ya Mulungu ndi awa: Mulitali munali mamita 27, mulifupi munali mamita asanu ndi anayi (potsata miyeso yakale). Chipinda cha polowera mulitali mwake chinali mamita asanu ndi anayi ofanana ndi mulifupi mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali mamita 54.

Iye anakuta nyumbayo mʼkati mwake ndi golide woyengeka bwino. Chipinda chachikulu, khoma lake anakhomera matabwa a payini ndipo analikutira ndi golide wabwino ndi kulikongoletsa ndi zithunzi za kanjedza ndi maunyolo. Iye anakongoletsa Nyumba ya Mulunguyo ndi miyala yokongola. Ndipo golide amene anagwiritsa ntchito anali golide wa ku Paravaimu. Iye anakutira ndi golide mitanda ya ku denga, maferemu a zitseko, makoma ndi zitseko za Nyumba ya Mulungu, ndipo anajambula Akerubi mʼmakoma mwake.

Iye anamanga Malo Opatulika Kwambiri ndipo mulitali mwake munali mofanana ndi mulifupi mwa Nyumba mamita asanu ndi anayi. Anakuta mʼkati mwake ndi golide wosalala wolemera matani makumi awiri. Misomali yagolide imalemera magalamu 570. Anakutanso ndi golide zipinda zapamwamba.

10 Ku Malo Opatulika Kwambiri iye anapangako Akerubi awiri achitsulo ndipo anawakuta ndi golide. 11 Kutalika kwa mapiko onse a Akerubi kunali mamita asanu ndi anayi. Phiko la Kerubi woyamba linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza khoma la Nyumba ya Mulungu, pamene phiko linalo, lotalikanso koposerapo mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi winayo. 12 Chimodzimodzinso phiko la Kerubi wachiwiri linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza mbali ina ya khoma la Nyumba ya Mulungu, ndipo linalo limene linalinso loposera mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi woyamba uja. 13 Mapiko a Akerubiwa akawatambasula amatalika mamita asanu ndi anayi. Akerubiwa anayimirira pa mapazi awo, kuyangʼana chipinda chachikulu.

14 Solomoni anapanga nsalu zotchingira zobiriwira, zapepo ndi zofiira ndi nsalu zofewa zosalala, atajambulapo Akerubi.

15 Kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu anamangako zipilala ziwiri, zimene zonse pamodzi zinali zotalika mamita khumi ndi asanu ndi theka; chipilala chilichonse chinali ndi mutu woposera mamita awiri. 16 Iye anapanga maunyolo olumikizanalumikizana ndipo anawayika pamwamba pa zipilalazo. Anapanganso makangadza 100 ndipo anawalumikiza ku maunyolo aja. 17 Solomoni anayimika nsanamirazo kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu, imodzi mbali ya kummwera ndi inayo mbali ya kumpoto. Nsanamira ya kummwera anayitcha Yakini ndipo ya kumpoto anayitcha Bowazi.

Zipangizo za mʼNyumba ya Mulungu

Solomoni anapanga guwa lamkuwa limene mulitali mwake linali mamita asanu ndi anayi, mulifupi mwakenso mamita asanu ndi anayi ndipo msinkhu wake unali mamita anayi ndi theka. Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13. Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo zithunzi zangʼombe zazimuna mozungulira, zithunzi khumi pa theka la mita. Ngʼombezo zimajambulidwa mʼmizere iwiri ndipo anazipangira kumodzi ndi mbiyayo.

Mbiyayo anayisanjika pa ngʼombe zamkuwa khumi ndi ziwiri, zitatu zoyangʼana kumpoto, zitatu zoyangʼana kumadzulo, zitatu zoyangʼana kummwera ndipo zitatu zoyangʼana kummawa. Mbiyayo inakhazikika pamwamba pa ngʼombezo, ndipo miyendo yake yonse yakumbuyo ya ngʼombezo inkaloza mʼkati. Mbiyayo inali yochindikala ngati chikhatho ndipo mkombero wake unali ngati mkombero wa chikho, ngati duwa lokongola kwambiri. Mʼmbiyamo munkalowa madzi okwana malita 60,000.

Kenaka anapanga mabeseni khumi otsukira zinthu ndipo asanu amawayika mbali ya kummwera, asanu mbali ya kumpoto. Mʼmenemo amatsukiramo zinthu zimene zimagwiritsidwa ntchito pa nsembe zopsereza koma mbiyamo ndi mʼmene ankasambiramo ansembe.

Solomoni anapanga zoyikapo nyale khumi zagolide monga momwe kunalembedwera ndipo anaziyika mʼNyumba ya Mulungu, zisanu mbali ya kummwera, ndi zisanu mbali ya kumpoto.

Iye anapanga matebulo khumi ndipo anawayika mʼNyumba ya Mulungu, asanu mbali ya kummwera ndi asanu mbali ya kumpoto. Iye anapanganso mabeseni agolide okwanira 100.

Iye anapanga bwalo la ansembe, bwalo lalikulu ndi zitseko za bwalolo ndipo anakuta zitsekozo ndi mkuwa. 10 Anayika mbiya ija mbali yakummwera pamene mbali ya kummawa ndi kummwera zimakumana.

11 Iye anapanganso miphika ndi mafosholo ndi mabeseni owazira magazi.

Kotero Hiramu anatsiriza ntchito yonse ya ku Nyumba ya Mulungu imene ankagwirira Mfumu Solomoni:

12 Nsanamira ziwiri;

mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;

maukonde awiri okongoletsera mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;

13 makangadza 400 a maukonde awiri okongoletserawo (mizere iwiri ya makangadza pa ukonde uliwonse, kukongoletsa mbale za mitu yapamwamba pa nsanamira);

14 miyendo pamodzi ndi mabeseni ake;

15 mbiya pamodzi ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri zazimuna zosanjikapo mbiyayo.

16 Miphika, mafosholo, mafoloko otengera nyama ndi ziwiya zina zonse.

Zipangizo zonse zimene Hiramu Abi anapangira Mfumu Solomoni za mʼNyumba ya Yehova zinali zamkuwa wonyezimira. 17 Mfumu inapangitsa zimenezi mʼchigwa cha Yorodani, ku malo amtapo amene anali pakati pa Sukoti ndi Zaretani. 18 Zinthu zonse zimene Solomoni anapanga zinali zochuluka kwambiri kotero kuti kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.

19 Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Mulungu:

guwa lansembe lagolide;

matebulo pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu;

20 zoyikapo nyale zagolide ndi nyale zake zagolide weniweni, kuti ziziyaka mʼkati mwenimweni mwa malo opatulika monga analembera,

21 maluwa agolide, nyale ndi mbaniro. (Zinali zagolide mmodzi);

22 zozimitsira nyale zagolide weniweni, mbale zowazira magazi, mbale ndi zofukizira; ndiponso zitseko zagolide za Nyumba ya Mulungu, chitseko cha ku Malo Opatulika Kwambiri ndi zitseko za ku chipinda chachikulu.

1 Yohane 3

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye. Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.

Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo. Koma inu mukudziwa kuti Yesu anabwera kuti adzachotse machimo athu. Ndipo mwa Iye mulibe tchimo. Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa.

Ana okondedwa, musalole kuti aliyense akusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama, monga Khristu ali wolungama. Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi. Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu. 10 Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake.

Kukondana Wina ndi Mnzake

11 Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake. 12 Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama. 13 Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu. 14 Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. 15 Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha.

16 Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu. 17 Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu? 18 Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi. 19 Pamenepo tidzadziwa kuti tili pa choonadi ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu, 20 nthawi zonse pamene mtima wathu utitsutsa. Pakuti Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo Iye amadziwa zonse.

21 Anzanga okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pamaso pa Mulungu. 22 Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa. 23 Ndipo lamulo lake ndi ili: kukhulupirira dzina la Mwana wake, Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga Iye anatilamulira. 24 Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.

Nahumu 2

Kugwa kwa Ninive

Wodzathira nkhondo akubwera
    kudzalimbana nawe, Ninive.
    Tetezani malinga anu,
    dziyangʼanani ku msewu,
    konzekerani nkhondo,
    valani dzilimbe.
Yehova adzabwezeretsa ulemerero wa Yakobo
    ngati ulemerero wa Israeli,
ngakhale anthu owononga anawawononga kotheratu
    ndipo anawononganso mpesa wawo.

Zishango za ankhondo ake ndi zofiira;
    asilikali ake avala zovala zofiirira.
Zitsulo za pa magaleta zikunyezimira
    tsiku la kukonzekera kwake.
    Akuonetsa mikondo ya mkungudza yonoledwa.
Magaleta akuthamanga mʼmisewu
    akungothamangathamanga pa mabwalo.
Akuoneka ngati miyuni yoyaka;
    akuthamanga ngati chingʼaningʼani.

Iye akuyitanitsa asilikali ake wolemekezeka,
    koma iwo akubwera napunthwa.
Akuthamangira ku linga la mzinda;
    akuyimika chodzitchinjirizira pamalo pake.
Atsekula zipata zotchinga madzi a mu mtsinje
    ndipo nyumba yaufumu yagwa.
Zatsimikizika kuti mzinda
    utengedwa ndi kupita ku ukapolo.
Akapolo aakazi akulira ngati nkhunda
    ndipo akudziguguda pachifuwa.
Ninive ali ngati dziwe,
    ndipo madzi ake akutayika.
Iwo akufuwula kuti, “Imani! Imani!”
    Koma palibe amene akubwerera.
Funkhani siliva!
    Funkhani golide!
Katundu wake ndi wochuluka kwambiri,
    chuma chochokera pa zinthu zake zamtengowapatali!
10 Iye wawonongedwa, wafunkhidwa ndipo wavulidwa!
    Mitima yasweka, mawondo akuwombana,
    anthu akunjenjemera ndipo
    nkhope zasandulika ndi mantha.

11 Kodi tsopano dzenje la mikango lili kuti,
    malo amene mikango inkadyetserako ana ake,
kumene mkango waumuna ndi waukazi unkapitako,
    ndipo ana a mkango sankaopa kanthu kalikonse?
12 Mkango waumuna unkapha nyama yokwanira ana ake
    ndiponso kuphera nyama mkango waukazi,
kudzaza phanga lake ndi zimene wapha
    ndiponso dzenje lake ndi nyama imene waphayo.

13 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
    “Ine ndikutsutsana nawe.
Ndidzatentha magaleta ako mpaka utsi tolotolo,
    ndipo lupanga lidzapha mikango yako yayingʼono;
sindidzakusiyira chilichonse choti udye pa dziko lapansi.
Mawu a amithenga anu sadzamvekanso.”

Luka 18

Fanizo la Mayi Wakhama pa Kupempha

18 Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke. Iye anati, “Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu. Ndipo panali mkazi wamasiye mʼmudzimo amene ankabwerabwera kwa iye ndi dandawulo lake kuti, ‘Mundiweruze mlandu mwachilungamo pakati pa ine ndi otsutsana nane.’

“Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu, koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’ ”

Ndipo Ambuye anati, “Tamvani zimene woweruza wopanda chilungamoyu wanena. Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira? Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?”

Fanizo la Mfarisi ndi Wolandira Msonkho

Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse. 10 “Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho. 11 Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu. 12 Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’

13 “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’

14 “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”

Yesu Adalitsa Ana Aangʼono

15 Anthu amabweretsanso ana aangʼono kwa Yesu kuti awadalitse. Ophunzira ataona izi, anawadzudzula. 16 Koma Yesu anayitana anawo kuti abwere kwa Iye nati, “Lolani ana abwere kwa Ine ndipo musawatsekereze, pakuti ufumu wa Mulungu uli wa anthu otere. 17 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene salandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono, sadzalowamo.”

Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu

18 Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”

19 Yesu anamuyankha kuti, “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha. 20 Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”

21 Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.”

22 Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.”

23 Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri. 24 Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu! 25 Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”

26 Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?”

27 Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”

28 Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!”

29 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu 30 adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”

Yesu Aneneratu za Imfa Yake Kachitatu

31 Yesu anatengera khumi ndi awiriwo pambali ndi kuwawuza kuti, “Taonani ife tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zalembedwa ndi Aneneri za Mwana wa Munthu zidzakwaniritsidwa. 32 Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira, 33 adzamukwapula ndi kumupha. Tsiku lachitatu Iye adzaukanso.”

34 Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula.

Yesu Achiritsa Wosaona

35 Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha, 36 anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika. 37 Iwo anamuwuza kuti “Yesu wa ku Nazareti akudutsa.”

38 Iye anayitana mofuwula, “Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”

39 Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”

40 Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti, 41 “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”

Iye anayankha kuti, “Ambuye, ine ndifuna ndionenso.”

42 Yesu anati kwa iye, “Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.” 43 Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.