Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 1

Solomoni Apempha Nzeru

Solomoni mwana wa Davide anakhazikika molimbika mu ufumu wake, pakuti Yehova Mulungu wake anali naye ndipo anamukweza kwambiri.

Tsono Solomoni anayankhula kwa Aisraeli onse, olamulira a anthu 1,000, olamulira a anthu 100, oweruza ndiponso kwa atsogoleri onse a Israeli ndi atsogoleri amabanja. Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la anthu anapita ku malo ofunika kwambiri pachipembedzo ku Gibiyoni. Tenti ya msonkhano ya Mulungu inali kumeneko, imene Mose mtumiki wa Yehova anayipanga mʼchipululu muja. Davide anabweretsa Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriyati Yearimu, ndi kulikhazika kumalo kumene analikonzera popeza analimangira tenti mu Yerusalemu. Koma guwa lansembe lamkuwa limene Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri analipanga linali ku Gibiyoni kutsogolo kwa tenti ya Yehova. Kotero kuti Solomoni ndi gulu lonse anakapembedza kumeneko. Solomoni anapita pamene panali guwa lansembe lamkuwa pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano ndipo anapereka nsembe zopsereza 1,000.

Usiku umenewo Mulungu anaonekera kwa Solomoni ndipo anati kwa iye, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”

Solomoni anayankha Mulungu kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwakukulu kwa Davide abambo anga ndipo mwayika ine kukhala mfumu mʼmalo mwake. Tsopano Inu Yehova Mulungu, lolani kuti lonjezo lanu kwa abambo anga Davide likwaniritsidwe, pakuti mwandiyika kukhala mfumu ya anthu anu amene ndi ochuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi. 10 Mundipatse nzeru ndi luntha zolamulira anthu awa, pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”

11 Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza izi ndi zokhumba za mtima wako ndipo sunapemphe katundu, chuma kapena ulemu, kapena imfa ya adani ako, ndiponso poti sunapemphe moyo wautali koma nzeru ndi luntha kuti ulamulire anthu anga amene Ine ndakuyika kukhala mfumu yawo, 12 Ine ndidzakupatsa nzeru ndi chidziwitso. Ndipo ndidzakupatsanso katundu, chuma ndi ulemu, zinthu zoti palibe mfumu imene inali nazo iwe usanakhalepo ndipo palibe wina amene adzakhale nazo iweyo ukadzafa.”

13 Kotero Solomoni anabwerera ku Yerusalemu kuchoka kumalo opembedzerako a ku Gibiyoni, ku tenti ya msonkhano ndipo analamulira Israeli.

14 Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndi akavalo 12,000, amene anawayika mʼmizinda yosungira magaleta ndipo ena anali ndi iye mu Yerusalemu. 15 Mfumu inasandutsa siliva ndi golide kukhala ngati miyala wamba mu Yerusalemu. Inasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa. 16 Solomoni amagula akavalo ku Igupto ndi Kuwe pakuti anthu amalonda a mfumu amakawagula ku Kuwe. 17 Anthu ankagula galeta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Iwo ankazigulitsanso kwa mafumu onse a Ahiti ndi a Aramu.

1 Yohane 1

Mawu a Moyo

Tikukulalikirani za Mawu a moyo amene analipo kuyambira pachiyambi, amene tinawamva, amene tinawaona ndi maso athu, amene tinawapenyetsetsa, ndipo tinawakhudza ndi manja athu. Moyowo unaoneka, tinawuona ndipo tikuchitira umboni. Tikukulalikirani za moyo wosatha umene unali ndi Atate ndipo unaonekera kwa ife. Tikukulalikirani chimene tinachiona ndi kumva, kuti inuyo muyanjane nafe. Kuyanjana kwathu, tikuyanjana ndi Atate ndiponso ndi Mwana wawo, Yesu Khristu. Tikukulemberani zimenezi kuti chimwemwe chathu chikhale chathunthu.

Kuyenda mu Kuwunika

Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse. Tikanena kuti timayanjana naye, koma nʼkumayendabe mu mdima, tikunama ndipo sitikuchita choonadi. Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.

Kuwulula Machimo ndi Kukhululukidwa

Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi. Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse. 10 Ife tikanena kuti sitinachimwe, tikumutenga Mulungu kukhala wonama, ndipo Mawu ake sali mwa ife.

Mika 7

Chipsinjo cha Israeli

Tsoka ine!
Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe,
    pa nthawi yokolola mphesa;
palibe phava lamphesa loti nʼkudya,
    palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.
Anthu opembedza atha mʼdziko;
    palibe wolungama ndi mmodzi yemwe amene watsala.
Anthu onse akubisalirana kuti aphane;
    aliyense akusaka mʼbale wake ndi khoka.
Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa;
    wolamulira amafuna mphatso,
woweruza amalandira ziphuphu,
    anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna,
    onse amagwirizana zochita.
Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati mtengo waminga,
    munthu wolungama kwambiri pakati pawo ndi woyipa kuposa mpanda waminga.
Tsiku limene alonda ako ananena lafika,
    tsiku limene Mulungu akukuchezera.
    Tsopano ndi nthawi ya chisokonezo chawo.
Usadalire mnansi;
    usakhulupirire bwenzi.
Usamale zoyankhula zako
    ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira.
Pakuti mwana wamwamuna akunyoza abambo ake,
    mwana wamkazi akuwukira amayi ake,
mtengwa akukangana ndi apongozi ake,
    adani a munthu ndi amene amakhala nawo mʼbanja mwake momwe.

Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo,
    ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga;
    Mulungu wanga adzamvetsera.

Kuuka kwa Israeli

Iwe mdani wanga, usandiseke!
    Ngakhale ndagwa, ndidzauka.
Ngakhale ndikukhala mu mdima,
    Yehova ndiye kuwunika kwanga.
Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova,
    chifukwa ndinamuchimwira,
mpaka ataweruza mlandu wanga
    ndi kukhazikitsa chilungamo changa.
Iye adzanditulutsa ndi kundilowetsa mʼkuwunika;
    ndidzaona chilungamo chake.
10 Ndipo mdani wanga adzaona zimenezi
    nadzagwidwa ndi manyazi,
iye amene anandifunsa kuti,
    “Ali kuti Yehova Mulungu wako?”
Ndidzaona kugonjetsedwa kwake ndi maso anga;
    ngakhale tsopano adzaponderezedwa
    ngati matope mʼmisewu.

11 Idzafika nthawi yomanganso makoma anu,
    nthawi yokulitsanso malire anu.
12 Nthawi imeneyo anthu adzabwera kwa inu
    kuchokera ku Asiriya ndi mizinda ya ku Igupto,
ngakhale kuchokera ku Igupto mpaka ku Yufurate
    ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso
    kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.
13 Dziko lapansi lidzasanduka chipululu
    chifukwa cha anthu okhala mʼdzikomo, potsatira zochita za anthuwo.

Pemphero ndi Matamando

14 Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza,
    nkhosa zimene ndi cholowa chanu,
zimene zili zokha mʼnkhalango,
    mʼdziko la chonde.
Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi
    monga masiku akale.

15 “Ndidzawaonetsa zodabwitsa zanga,
    ngati masiku amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto.”

16 Mitundu ya anthu idzaona zimenezi ndipo idzachita manyazi,
    ngakhale ali ndi mphamvu zotani.
Adzagwira pakamwa pawo
    ndipo makutu awo adzagontha.
17 Adzabwira fumbi ngati njoka,
    ngati zolengedwa zomwe zimakwawa pansi.
Adzabwera akunjenjemera kuchokera mʼmaenje awo;
    mwamantha adzatembenukira kwa Yehova Mulungu wathu
    ndipo adzachita nanu mantha.
18 Kodi alipo Mulungu wofanana nanu,
    amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa
    za anthu otsala amene ndi cholowa chake?
Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya
    koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
19 Inu mudzatichitiranso chifundo;
    mudzapondereza pansi machimo athu
    ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.
20 Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo,
    ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu,
monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu
    masiku amakedzana.

Luka 16

Fanizo la Kapitawo Wosakhulupirika

16 Yesu anawuza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene kapitawo wake anzake anamuneneza kuti amawononga chuma chakecho. Choncho anamuyitana ndi kumufunsa kuti, ‘Kodi nʼchiyani chimene ndikumva za iwe? Pereka tsatanetsatane wa ntchito yako, pakuti supitirizanso kukhala kapitawo wanga.’

“Kapitawoyo analingalira kuti, ‘Kodi tsopano ndidzachita chiyani? Bwana wanga andichotsa ntchito. Ine ndilibe mphamvu zokwanira zolimira, komanso ine ndimachita manyazi kupempha. Ine ndikudziwa chimene ndidzachita kotero kuti, pamene ntchito yanga yatha pano, anthu adzandilandire mʼnyumba zawo.’

“Choncho iye anayitana aliyense amene anali ndi ngongole kwa bwana wake. Iye anafunsa woyamba, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa bwana wanga?’

“Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’

“Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’

“Kenaka iye anafunsa wachiwiri kuti, ‘Nanga iwe uli ndi ngongole yotani?’

“Iye ayankha kuti madengu a tirigu 1,000.

“Iye anati, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo ndipo ulembepo 800.’

“Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika. Ine ndikukuwuzani inu, gwiritsani ntchito chuma cha dziko lapansi kuti mudzipezere nokha abwenzi, kuti pamene chatha mudzalandiridwe mʼmalo okhala amuyaya.

10 “Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri. 11 Ndipo ngati simunakhale okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma cha dziko lapansi, ndani amene adzakusungitsani chuma chenicheni? 12 Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi chuma cha mwini wake, ndani amene adzakupatsani katundu wanuwanu?

13 “Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.”

14 Afarisi amene ankakonda ndalama atamva zimenezi anamuseka Yesu. 15 Yesu anawawuza kuti, “Inu ndi amene mumadzilungamitsa nokha pamaso pa anthu, koma Mulungu amadziwa mitima yanu. Zinthu zimene anthu amaziyesa zopambana, ndi zonyansa pamaso pa Mulungu.

Ziphunzitso Zina

16 “Malamulo ndi Aneneri zinagwira ntchito mpaka nthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ukulalikidwa, ndipo aliyense akuyesetsa mwamphamvu kuti alowemo. 17 Nʼkwapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kulekana ndi kuti kalemba kakangʼono kachoke mʼMalamulo.

18 “Aliyense amene asiya mkazi wake ndi kukakwatira mkazi wina akuchita chigololo, ndipo mwamuna amene akwatira mkazi wosiyidwayo akuchitanso chigololo.”

Za Munthu Wachuma ndi Lazaro

19 “Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse. 20 Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse 21 ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake.

22 “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda. 23 Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. 24 Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’

25 “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. 26 Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’

27 “Iye anayankha kuti, ‘Ndipo ndikupemphani inu, abambo, mutumeni Lazaro ku nyumba ya abambo anga, 28 pakuti ine ndili ndi abale asanu. Lolani iye akawachenjeze kotero kuti asadzabwere kumalo ano amazunzo.’

29 “Abrahamu anayankha kuti, ‘Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.’

30 “Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’

31 “Anati kwa iye, ‘Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’ ”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.