Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 26-27

Alonda a pa Zipata

26 Magulu a alonda a pa zipata:

Kuchokera ku banja la Kora: Meselemiya mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu.

Meselemiya anali ndi ana awa:

woyamba Zekariya,

wachiwiri Yediaeli,

wachitatu Zebadiya,

wachinayi Yatinieli,

wachisanu Elamu,

wachisanu ndi chimodzi Yehohanani,

ndipo wachisanu ndi chiwiri Elihunai.

Obedi-Edomu analinso ndi ana awa:

woyamba Semaya,

wachiwiri Yehozabadi,

wachitatu Yowa,

wachinayi Sakara,

wachisanu Netaneli,

wachisanu ndi chimodzi Amieli,

wachisanu ndi chiwiri Isakara

ndipo wachisanu ndi chitatu Peuletayi.

(Pakuti Mulungu anadalitsa Obedi-Edomu).

Mwana wake Semaya analinso ndi ana amene anali atsogoleri mʼbanja la abambo awo chifukwa anali anthu amphamvu. Ana a Semaya anali: Otini, Refaeli, Obedi ndi Elizabadi; abale ake, Elihu ndi Semakiya, analinso anthu amphamvu. Onsewa anali adzukulu a Obedi-Edomu. Iwo ndi ana awo ndiponso abale awo anali anthu aluso ndi amphamvu pogwira ntchito. Zidzukulu zonse za Obedi-Edomu zinalipo 62.

Meselemiya anali ndi ana ndi abale ake amene anali aluso ndipo onse analipo 18.

10 Hosa Mmerari anali ndi ana awa: woyamba anali Simiri (ngakhale kuti iye sanali woyamba kubadwa, abambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri), 11 wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya ndipo wachinayi Zekariya. Ana ndi abale onse a Hosa analipo 13.

12 Magulu amenewa a alonda a pa zipata, motsogozedwa ndi atsogoleri awo, anali ndi ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova, monga momwe amachitira abale awo. 13 Iwo anachita maere mwa mabanja awo aangʼono ndi aakulu omwe kuti apeze mlonda pa chipata chilichonse.

14 Maere a chipata chakummwa anagwera Selemiya. Maere anachitikanso chifukwa cha mwana wake Zekariya, phungu wanzeru ndipo maere a chipata chakumpoto anagwera iye. 15 Maere a chipata chakummwera anagwera Obedi-Edomu, ndipo maere a nyumba yosungiramo katundu anagwera ana ake. 16 Maere a chipata chakumadzulo ndi chipata cha Saleketi ku msewu wa ku mtunda anagwera Supimu ndi Hosa.

Mlonda ankayangʼanana ndi mlonda mnzake: 17 Mbali ya kummawa kunkakhala Alevi 6 pa tsiku, kumpoto anayi pa tsiku, kummwera anayi pa tsiku ndipo awiri ankakhala pa nyumba yosungiramo katundu. 18 Ndipo ku bwalo cha kumadzulo, anayi amakhala mu msewu ndi awiri pabwalo penipeni.

19 Awa anali magulu a alonda a pa zipata amene anali zidzukulu za Kora ndi Merari.

Asungichuma ndi Akuluakulu Ena

20 Abale awo Alevi, motsogozedwa ndi Ahiya, anali oyangʼanira chuma cha nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Mulungu.

21 Adzukulu a Ladani, mmodzi mwa ana a Geresoni, amene anali atsogoleri a mabanja a Ageresoni, anali awa: Yehieli, 22 ana a Yehieli, Zetamu ndi mʼbale wake Yoweli. Iwo amayangʼanira chuma cha ku Nyumba ya Mulungu wa Yehova.

23 Kuchokera ku banja la Amramu, banja la Aizihara, banja la Ahebroni ndi banja la Auzieli:

24 Subaeli, chidzukulu cha Geresomu, mwana wa Mose, anali mkulu woyangʼanira chuma. 25 Abale ake obadwa mwa Eliezara, anali Rekabiya mwana wake, Yesaya mwana wake, Yoramu mwana wake, Zikiri mwana wake ndi Selomiti mwana wake. 26 Selomiti ndi abale ake amayangʼanira zinthu zonse zoperekedwa kwa Mulungu ndi mfumu Davide, atsogoleri a mabanja amene anali olamulira ankhondo 1,000, olamulira ankhondo 100, ndi olamulira ankhondo ena. 27 Zina zofunkha ku nkhondo anazipereka kuti zikhale zokonzera Nyumba ya Yehova. 28 Ndipo zonse zimene zinaperekedwa ndi Mlosi Samueli, Sauli mwana wa Kisi, Abineri mwana wa Neri ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya ndi zinthu zonse zimene zinkaperekedwa zimasungidwa ndi Selomiti ndi abale ake.

29 Kuchokera ku banja la Izihari: Kenaniya ndi ana ake anapatsidwa ntchito kutali ndi Nyumba ya Mulungu ngati akuluakulu ndi oweruza Israeli.

30 Kuchokera ku banja la Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake, anthu anzeru 1,700. Iwo ankayangʼanira ntchito zonse za Yehova ndi ntchito yonse ya mfumu cha kumadzulo kwa Yorodani. 31 Pa banja la Ahebroni, Yeriya anali mtsogoleri monga mwa mbiri ya mibado ya mabanja awo. Mʼchaka cha 40 cha ufumu wa Davide, panachitika kafukufuku ndipo ena mwa anthu aluso a banja la Hebroni anapezeka kuti anali ku Yazeri ku Giliyadi. 32 Yeriya anali ndi abale 2,700 amene anali aluso ndiponso atsogoleri a mabanja. Mfumu Davide anawayika iwowa kuti aziyangʼanira fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase pa zinthu zonse za Mulungu ndi za mfumu.

Magulu a Anthu Ankhondo

27 Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.

Amene amalamulira gulu loyamba pa mwezi woyamba anali Yasobeamu mwana wa Zabidieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Iyeyu anali chidzukulu cha Perezi ndipo anali mkulu wa atsogoleri onse a ankhondo mwezi woyamba.

Amene amalamulira gulu lachiwiri pa mwezi wachiwiri anali Dodai Mwahohi; Mikiloti ndiye anali mtsogoleri wa gulu lake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

Wolamulira ankhondo wachitatu, pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anali mtsogoleri ndipo pa gulu lake panali ankhondo 24,000. Uyu ndi Benaya uja amene anali wamphamvu pa gulu la anthu makumi atatu ndipo ndiye amatsogolera anthu makumi atatu aja. Mwana wake Amizabadi ndiye amatsogolera gulu lake.

Wachinayi pa mwezi wachinayi anali Asaheli mʼbale wake wa Yowabu; ndipo mwana wake Zebadiya ndiye analowa mʼmalo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

Wachisanu pa mwezi wachisanu anali Samihuti, mdzukulu wa Izira. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

Wa 6 pa mwezi wa 6 anali Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

10 Wa 7 pa mwezi wa 7 anali Helezi Mpeloni wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

11 Wa 8 pa mwezi wa 8 anali Sibekai Mhusati, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000

12 Wa 9 pa mwezi wa 9 anali Abiezeri wa banja la Anatoti, wa fuko la Benjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

13 Wa khumi pa mwezi wa khumi anali Mahazayi wa ku Netofa, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

14 Mtsogoleri wa 11, pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

15 Mtsogoleri wa 12, pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, wa banja la Otanieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

Akuluakulu a Mafuko a Israeli

16 Akuluakulu amene amatsogolera mafuko a Israeli ndi awa:

Mtsogoleri wa fuko la Rubeni: Eliezara mwana wa Zikiri;

mtsogoleri wa fuko la Simeoni: Sefatiya mwana wa Maaka;

17 mtsogoleri wa fuko la Levi: Hasabiya mwana wa Kemueli,

mtsogoleri wa banja la Aaroni: Zadoki;

18 mtsogoleri wa fuko la Yuda: Elihu, mʼbale wake wa Davide;

mtsogoleri wa fuko la Isakara: Omuri mwana wa Mikayeli;

19 mtsogoleri wa fuko la Zebuloni: Isimaiya mwana wa Obadiya;

mtsogoleri wa fuko la Nafutali: Yerimoti mwana wa Azirieli;

20 mtsogoleri wa fuko la Efereimu: Hoseya mwana wa Azaziya;

mtsogoleri wa fuko la theka la Manase: Yoweli mwana wa Pedaya;

21 mtsogoleri wa fuko la theka la Manase limene linali ku Giliyadi: Ido mwana wa Zekariya;

mtsogoleri wa fuko la Benjamini: Yaasieli mwana wa Abineri;

22 mtsogoleri wa fuko la Dani: Azareli mwana wa Yerohamu.

Awa anali akuluakulu a mafuko a Israeli.

23 Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kucheperapo, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisraeli ngati nyenyezi zamumlengalenga. 24 Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga amuna koma sanamalize. Mkwiyo unagwera Aisraeli chifukwa cha zimenezi ndipo chiwerengerochi sanachilowetse mʼbuku la mbiri ya mfumu Davide.

Anthu Oyangʼanira Chuma cha Mfumu

25 Azimaveti mwana wa Adieli ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa mfumu.

Yonatani mwana wa Uziya ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa maboma ozungulira, mizinda, midzi ndi malo olondera.

26 Eziri mwana wa Kelubi ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yolima ku munda.

27 Simei wa ku Rama ankayangʼanira minda ya mpesa.

Zabidi wa ku Sifamu ankayangʼanira mphesa ndi mosungiramo mwake.

28 Baala-Hanani wa ku Gederi ankayangʼanira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ya ku Sefela.

Yowasi ankayangʼanira mafuta a Olivi.

29 Sitirayi wa ku Saroni ankayangʼanira ziweto zimene amaweta ku Saroni.

Safati mwana wa Adilayi ankayangʼanira ngʼombe zakuzigwa.

30 Obili Mwismaeli ankayangʼanira ngamira.

Yehideya Mmerenoti ankayangʼanira abulu.

31 Yazizi Mhagiri akayangʼanira nkhosa ndi mbuzi.

Onsewa anali akuluakulu oyangʼanira chuma cha mfumu Davide.

32 Yonatani, malume wake wa Davide, anali phungu wake ndipo anali munthu wanzeru komanso analinso mlembi. Yehieli mwana wa Hakimoni ankasamalira ana a mfumu.

33 Ahitofele anali phungu wa mfumu.

Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu. 34 Ahitofele atamwalira mʼmalo mwake munalowa Yehoyada mwana wa Benaya ndi Abiatara.

Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.

2 Petro 1

Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu.

Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu.

Kudziwa za Mayitanidwe ndi za Kusankhidwa Kwathu

Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake. Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.

Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi. Ngati zonsezi zikhala mwa inu nʼkumachuluka, zidzakuthandizani kuti musakhale aulesi ndi osapindula ndi chidziwitso chanu cha Ambuye athu Yesu Khristu. Koma ngati wina alibe zimenezi, ndi wakhungu sangathe kuona patali, ndipo wayiwala kuti anayeretsedwa machimo ake akale.

10 Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse. 11 Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

Kukhala Oyera Mtima

12 Tsono ine ndidzakukumbutsani nthawi zonse za zinthu zimenezi, ngakhale kuti mumazidziwa ndipo kuti munakhazikika mʼchoonadi chimene muli nacho tsopano. 13 Ndikuganiza kuti nʼkoyenera ndikanali mu msasa uno, kuti ndikutsitsimutseni ndi kukukumbutsani, 14 chifukwa ndikudziwa kuti posachedwapa ndikuchoka mu msasa uno, monga Ambuye athu Yesu Khristu anandidziwitsiratu. 15 Ndipo ndidzayesetsa kuti nditachoka, mudzakumbukire nthawi zonse.

16 Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake. 17 Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.” 18 Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija.

19 Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu. 20 Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. 21 Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.

Mika 4

Phiri la Yehova

Mʼmasiku otsiriza,

phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa
    kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse.
Lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,
    ndipo anthu amitundu yonse adzathamangira kumeneko.

Mayiko ambiri adzabwera ndikunena kuti,

“Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova,
    ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.
Iye adzatiphunzitsa njira zake,
    ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”
Malangizo adzachokera ku Ziyoni,
    mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
Iye adzaweruza pakati pa anthu amitundu yambiri
    ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu amphamvu akutali ndi apafupi omwe.
Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu
    ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.
Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,
    kapena kuphunziranso za nkhondo.
Munthu aliyense adzakhala pansi pa tsinde pa mtengo wake wa mpesa
    ndi pa tsinde pa mtengo wake wamkuyu,
ndipo palibe amene adzawachititse mantha,
    pakuti Yehova Wamphamvuzonse wayankhula.
Mitundu yonse ya anthu
    itha kutsatira milungu yawo;
ife tidzayenda mʼnjira za Yehova
    Mulungu wathu mpaka muyaya.

Cholinga cha Yehova

“Tsiku limenelo, Yehova akuti,

“ndidzasonkhanitsa olumala;
    ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu ochotsedwa
    ndiponso amene ndinawalanga.
Anthu olumalawo ndidzawasandutsa anthu anga otsala.
    Anthu amene ndinawachotsa ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.
Yehova adzawalamulira mʼPhiri la Yehova
    kuyambira tsiku limenelo mpaka muyaya.
Kunena za iwe, nsanja ya ziweto zanga,
    iwe linga la mwana wamkazi wa Ziyoni,
ulamuliro wako wakale udzabwezeretsedwa kwa iwe;
    ufumu udzabwera pa mwana wamkazi wa Yerusalemu.”

Chifukwa chiyani tsopano ukulira mofuwula,
    kodi ulibe mfumu?
Kodi phungu wako wawonongedwa,
    kotero kuti ululu wako uli ngati wa mayi amene akubereka?
10 Gubuduka ndi ululu, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,
    ngati mayi pa nthawi yake yobereka,
pakuti tsopano muyenera kuchoka mu mzinda
    ndi kugona kunja kwa mzindawo.
Udzapita ku Babuloni;
    kumeneko udzapulumutsidwa,
kumeneko Yehova adzakuwombola
    mʼmanja mwa adani ako.

11 Koma tsopano mitundu yambiri ya anthu
    yasonkhana kulimbana nawe.
Iwo akuti, “Tiyeni timudetse,
    maso athu aone chiwonongeko cha Ziyoni!”
12 Koma iwo sakudziwa
    maganizo a Yehova;
iwo sakuzindikira cholinga chake,
    Iye amene amawatuta ngati mitolo ya tirigu ku malo opunthira tirigu.

13 “Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,
    pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo;
ndidzakupatsa ziboda zamkuwa
    ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.”

Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova,
    chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi.

Luka 13

Za Kutembenuka Mtima

13 Nthawi yomweyo panali ena amene analipo omwe amamuwuza Yesu za Agalileya amene magazi awo Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo. Yesu anayankha kuti, “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewa anali ochimwa kwambiri kuposa Agalileya ena onse chifukwa anavutika mʼnjira iyi? Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse. Kapena anthu 18 aja amene anafa nsanja ya Siloamu itawagwera, kodi mukuganiza kuti iwo aja anali ochimwa kwambiri kuposa onse amene amakhala mu Yerusalemu? Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.”

Kenaka Iye anawawuza fanizo kuti, “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu, umene anadzala mʼmunda wamphesa, ndipo Iye anapita kukayangʼana zipatso, koma sanazipeze. Tsono kwa munthu amene amasamalira munda wamphesawo anati, ‘Kwa zaka zitatu tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna chipatso pa mtengo uwu ndipo sindinachipeze. Udule! Nʼchifukwa chiyani ukuwononga nthaka?’

“Munthuyo anayankha kuti, ‘Bwana, tawusiyani kwa chaka chimodzi chokha ndipo ine ndikumba ngalande mozungulira ndi kuthira manyowa. Ngati udzabale zipatso chaka chamawa, zili bwino! Koma ngati sudzabala, pamenepo mudzawudule.’ ”

Mayi Wokhota Msana Achiritsidwa pa Sabata

10 Pa Sabata Yesu ankaphunzitsa mʼsunagoge ina, 11 ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe. 12 Yesu atamuona anamuyitana kutsogolo ndipo anati kwa iye, “Amayi, mwamasulidwa ku mavuto.” 13 Kenaka anasanjika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo anawongoka nayamika Mulungu.

14 Chifukwa cha kuyipidwa kuti Yesu anachiritsa pa Sabata, wolamulira sunagoge anati kwa anthu, “Pali masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Choncho bwerani kuti mudzachiritsidwe masiku amenewo osati pa Sabata.”

15 Ambuye anamuyankha kuti, “Iwe wachiphamaso! Kodi nonsenu simumasula pa Sabata ngʼombe zanu kapena bulu kumuchotsa mʼkhola ndi kupita naye kukamupatsa madzi? 16 Nanga mayiyu, amene ndi mwana wa Abrahamu, ndipo anamangidwa ndi Satana zaka 18, kodi siwoyenera kuti amasulidwe msinga imeneyi pa tsiku la Sabata?”

17 Atanena izi, onse omutsutsa anachititsidwa manyazi, koma anthu anakondwera ndi zodabwitsa zonse zimene Iye anazichita.

Fanizo la Mbewu ya Mpiru ndi la Yisiti

18 Kenaka Yesu anafunsa kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani? Kodi Ine ndingawufanizire ndi chiyani? 19 Uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Inakula, nʼkukhala mtengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinakhala mʼnthambi zake.”

20 Iye anafunsanso kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu ndingawufanizire ndi chiyani? 21 Uli ngati yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza ndi ufa wambiri mpaka anafufumitsa ufawo.”

Khomo Lopapatiza

22 Ndipo Yesu anayendayenda mʼmizinda ndi mʼmidzi, kumaphunzitsa pamene Iye ankapita ku Yerusalemu. 23 Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?”

Iye anawawuza kuti, 24 “Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero. 25 Nthawi yomwe mwini nyumba adzayimirira ndi kutseka chitseko, inu mudzayima kunja kugogoda ndi kudandaula kuti, ‘Bwana, tatitsekulirani khomo.’

“Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera.’

26 “Ndipo inu mudzati, tinkadya ndi kumwa ndi inu ndipo munkaphunzitsa mʼmisewu yathu.

27 “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera. Chokereni inu nonse ochita zoyipa!’

28 “Mudzalira ndi kukuta mano mukadzaona Abrahamu, Isake ndi Yakobo ndi aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu koma inuyo mutaponyedwa kunja. 29 Anthu adzachokera kummawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kummwera, kudzakhala pa phwando mu ufumu wa Mulungu. 30 Ndithudi otsirizira ndiye adzakhale oyambirira, ndipo oyambirira ndiye adzakhale otsirizira.”

Yesu Amvera Chisoni Yerusalemu

31 Pa nthawi imeneyo Afarisi anabwera kwa Yesu ndipo anati kwa Iye, “Chokani malo ano ndipo pitani kumalo ena aliwonse. Herode akufuna kukuphani.”

32 Iye anayankha kuti, “Pitani kawuzeni nkhandweyo, Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa ndipo tsiku lachitatu ndidzakwaniritsa cholinga changa.” 33 Mʼnjira ina iliyonse, Ine ndiyenera kupitirira ulendo wanga lero, mawa ndi mkuja. Zoona nʼzakuti mneneri sangafere kunja kwa Yerusalemu.

34 Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri ndi kuwagenda miyala anthu amene atumizidwa kwa iwe. Nthawi zambiri ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune! 35 Taona, nyumba yako yasanduka bwinja. Ine ndikukuwuza kuti, sudzandionanso mpaka pamene udzati, “Wodala amene akubwera mʼdzina la Ambuye!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.