Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 18

Nkhondo za Davide ndi Kupambana Kwake

18 Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake. Iye analanda Gati ndi midzi yake yozungulira mʼmanja mwa Afilistiwo.

Davide anagonjetsanso Amowabu, nakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iye.

Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mfumu ya Zoba, mpaka ku Hamati, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate. Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.

Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000. Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.

Davide anatenga zishango zagolide zimene ankanyamula akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu. Kuchokera ku Teba ndi Kuni, mizinda ya Hadadezeri, Davide anatengako mkuwa wambiri umene Solomoni anapangira chimbiya, zipilala ndi zida zosiyanasiyana zamkuwa.

Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri mfumu ya Zoba, 10 anatumiza mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Hadoramu anabweretsa ziwiya zosiyanasiyana zagolide, zasiliva ndi zamkuwa.

11 Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko ena onse monga Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki.

12 Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere. 13 Iye anayika maboma ku Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.

Akuluakulu a Davide

14 Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse. 15 Yowabu, mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika; 16 Zadoki, mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Savisa anali mlembi; 17 Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali alangizi a mfumu.

Yakobo 5

Chenjezo kwa Achuma Opondereza Anzawo

Tsono tamverani, inu anthu achuma, lirani ndi kufuwula chifukwa cha zovuta zimene zidzakugwereni. Chuma chanu chawola ndipo njenjete zadya zovala zanu. Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza. Taonani, ndalama za malipiro zimene munakanika kulipira aganyu aja ankasenga mʼmunda mwanu zikulira mokutsutsani. Kulira kwa okololawo kwamveka mʼmakutu mwa Ambuye Wamphamvuzonse. Mwakhala pa dziko lapansi pano moyo ofewa ndipo mwalidyera dziko lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lokaphedwa. Mwaweruza kuti ndi wolakwa ndipo mwapha munthu wosalakwa, amene sakutsutsana nanu.

Kupirira Mʼmasautso

Tsono abale, pirirani mpaka kubwera kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Amadikirira kuti zipatso zabwino zioneke mʼmunda mwake. Amayembekezera mokhazikika mtima kuyambira nthawi ya mvula yoyamba mpaka yotsiriza. Inunso mukhale owugwira mtima ndi osasinthika chifukwa Ambuye ali pafupi kubwera. Abale, musamanenezane zoyipa kuopa kuti mungadzaweruzidwe. Woweruza ali pa khomo!

10 Abale, tengerani chitsanzo cha aneneri amene anayankhula mʼdzina la Ambuye. Iwowo anakumana ndi zovuta koma anapirira. 11 Monga mukudziwa, tinawatenga ngati odalitsika anthu amene anapirira. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Ambuye anamuchitira potsiriza pake. Ambuye ndi wodzaza ndi chisoni ndi chifundo.

12 Koposa zonse, abale anga, musamalumbire. Polumbira osamatchula kumwamba kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. “Inde” wanu azikhala “Inde,” ndipo “Ayi” wanu azikhala “Ayi,” kuopa kuti mungadzapezeke olakwa.

Pemphero la Chikhulupiriro

13 Kodi alipo wina mwa inu amene ali pa mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Ayimbe nyimbo zolemekeza. 14 Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. 15 Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa. 16 Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.

17 Eliya anali munthu ngati ife. Iye anapemphera mwamphamvu kuti mvula isagwe ndipo sinagwedi kwa zaka zitatu ndi theka. 18 Kenaka anapempheranso, ndipo kumwamba kunagwetsa mvula, ndipo dziko lapansi linatulutsa zomera zake. 19 Abale anga, ngati mmodzi wa inu apatuka pa choonadi ndipo wina wake ndi kumubweza, 20 kumbukirani izi: Aliyense wobweza wochimwa kuchoka ku cholakwa chake, adzamupulumutsa ku imfa ndi kukwirira machimo ambiri.

Yona 2

Pemphero la Yona

Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake. Iye anati:

“Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova,
    ndipo Iye anandiyankha.
Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo,
    ndipo Inu munamva kulira kwanga.
Munandiponya mʼnyanja yozama,
    mʼkati mwenimweni mwa nyanja,
    ndipo madzi oyenda anandizungulira;
mafunde anu onse ndi mkokomo wake
    zinandimiza.
Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa
    pamaso panu;
komabe ndidzayangʼananso
    ku Nyumba yanu yopatulika.’
Madzi wondimiza anandichititsa mantha,
    nyanja yozama inandizungulira;
    udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga.
Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri;
    mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha.
Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo,
    Inu Yehova Mulungu wanga.

“Pamene moyo wanga umachoka mwa ine,
    ine ndinakumbukira Inu Yehova,
ndipo pemphero langa linafika kwa inu,
    ku Nyumba yanu yopatulika.

“Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe
    amataya chisomo chawo.
Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe
    ndikuyimba nyimbo yamayamiko.
Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa.
    Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”

10 Ndipo Yehova analamula chinsomba chija, ndipo chinakamusanza Yonayo mʼmbali mwa nyanja.

Luka 7

Chikhulupiriro cha Kenturiyo

Yesu atamaliza kunena zonsezi pamaso pa anthu amene ankamvetsera, analowa mu Kaperenawo. Kumeneko wantchito wa Kenturiyo, amene amamukhulupirira kwambiri, anadwala ndipo anali pafupi kufa. Kenturiyo anamva za Yesu ndipo anatumiza ena a akulu Ayuda kwa Iye kuti abwere adzachiritse wantchito wakeyo. Iwo atafika kwa Yesu, anamudandaulira kwambiri, nati, “Munthuyu ayenera kuthandizidwa chifukwa amakonda mtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge wathu.” Pamenepo Yesu anapita nawo.

Iye sanali patali ndi nyumba pamene Kenturiyo anatumiza anzake kuti akamuwuze kuti, “Ambuye, musadzivutitse, pakuti ndine wosayenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga. Nʼchifukwa chake sindinadziyenereze ndi pangʼono pomwe kuti ndibwere kwa inu. Koma nenani mawu, ndipo wantchito wanga adzachira. Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita.”

Yesu atamva izi, anadabwa naye, ndipo anatembenukira gulu la anthu limene limamutsatira nati, “Ndikukuwuzani kuti, sindinapeze chikhulupiriro chachikulu ngati ichi mu Israeli.” 10 Kenaka anthu amene anatumidwawo anabwerera ku nyumba ndipo anakamupeza wantchitoyo atachira.

Yesu Aukitsa Mwana wa Mayi Wamasiye

11 Zitangotha izi, Yesu anapita ku mudzi wa Naini ndipo ophunzira ake ndi gulu lalikulu la anthu linapita naye pamodzi. 12 Akufika pa chipata cha mudziwo, anakumana ndi anthu amene ankatuluka ndi munthu wakufa amene anali mwana yekhayo wa mkazi wamasiye. Gulu lalikulu la anthu a mʼmudziwo linali naye. 13 Ambuye atamuona mayiyo, mtima wawo unagwidwa naye chifundo ndipo anati, “Usalire.”

14 Kenaka anapita nakakhudza chithatha cha maliro ndipo amene anachinyamulawo anayima. Iye anati, “Mnyamata, ndikukuwuza kuti, dzuka!” 15 Wakufayo anakhala tsonga ndi kuyamba kuyankhula, ndipo Yesu anamupereka mnyamatayo kwa amayi ake.

16 Onse anachita mantha kwambiri nalemekeza Mulungu. Iwo anati, “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu. Mulungu wabwera kudzathandiza anthu ake.” 17 Mbiriyi inafalikira ku Yudeya konse ndi ku madera ozungulira.

Yesu ndi Yohane Mʼbatizi

18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuwuza Yohaneyo zinthu zonsezi. Atayitana awiri a ophunzirawo, 19 anawatumiza kwa Ambuye kukafunsa kuti, “Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?”

20 Anthuwo atafika kwa Yesu anati, “Yohane Mʼbatizi watituma kwa Inu kuti tidzafunse kuti, ‘Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?’ ”

21 Pa nthawi yomweyo, Yesu anachiritsa ambiri amene ankavutika, odwala ndi amene anali mizimu yoyipa, ndiponso anapenyetsa anthu osaona. 22 Ndipo Iye anawayankha otumidwawo kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwaona ndi kumva: Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. 23 Odala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”

24 Anthu otumidwa ndi Yohane aja atachoka, Yesu anayamba kuyankhula ndi gulu la anthu za Yohaneyo kuti, “Kodi munkapita ku chipululu kukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo? 25 Ngati si choncho, munkapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zabwino? Ayi, ovala zovala zodula ndi okhala moyo wapamwamba ali mʼnyumba zaufumu. 26 Koma inu munkapita kukaona chiyani? Mneneri? Inde, Ine ndikukuwuzani, woposa mneneri. 27 Uyu ndi amene malemba akunena za Iye kuti,

“ ‘Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,
    amene adzakonza njira yanu.’

28 Ine ndikukuwuzani kuti pakati pa obadwa kuchokera mwa mkazi palibe wina wamkulu kuposa Yohane; komabe amene ali wamngʼono mu ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.”

29 Anthu onse, ngakhale amisonkho, atamva mawu a Yesu, anavomereza kuti njira ya Mulungu ndi yolondola, chifukwa anabatizidwa ndi Yohane. 30 Koma Afarisi ndi akatswiri amalamulo anakana cholinga cha Mulungu kwa iwo okha, chifukwa sanabatizidwe ndi Yohane.

31 “Kodi ndingawafanizire chiyani anthu a mʼbado uno? Ali ngati chiyani? 32 Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti,

“ ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro,
    koma inu simunavine.
Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro,
    koma inu simunalire.’

33 Pakuti Yohane Mʼbatizi sanabwere kudzadya buledi kapena kumwa vinyo, koma inu mumati, ‘Ali ndi chiwanda.’ 34 Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’ 35 Ndipo nzeru zimaoneka zolondola mwa ana ake onse.”

Yesu Adzozedwa ndi Mayi Wochimwa

36 Tsopano mmodzi mwa Afarisi anayitana Yesu kuti akadye naye ku nyumba kwake ndipo anapita nakakhala pa tebulo. 37 Mayi amene amakhala moyo wauchimo mu mzindawo atadziwa kuti Yesu akudya ku nyumba ya Mfarisiyo, anabweretsa botolo la mafuta onunkhira a alabasta. 38 Iye anayimirira kumbuyo kwa Yesu pa mapazi ake akulira, nayamba kumadontheza misozi pa mapazi ake. Ndipo iye anapukuta mapaziwo ndi tsitsi lake, nawapsompsona ndi kuwathira mafuta onunkhirawo.

39 Mfarisiyo anamuyitanayo ataona izi, anati mu mtima mwake, “Ngati munthuyu akanakhala mneneri, akanadziwa kuti akumukhudzayo ndi mayi otani, kuti ndi wochimwa.”

40 Yesu anamuyankha iye kuti, “Simoni, ndili ndi kanthu koti ndikuwuze.”

Iye anati, “Ndiwuzeni Aphunzitsi.”

41 “Anthu awiri anakongola ndalama kwa munthu wina wokongoletsa ndalama: mmodzi ndalama zokwana 500 ndi winayo ndalama makumi asanu. 42 Panalibe mmodzi mwa iwo anali ndi ndalama zobwezera, ndipo iye anawakhululukira ngongole zawo. Tsopano ndi ndani mwa awiriwa adzamukonde koposa?”

43 Simoni anayankha kuti, “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira ngongole yayikulu.”

Yesu anati, “Wayankha molondola.”

44 Kenaka anatembenukira kwa mayiyo nati kwa Simoni, “Ukumuona mayiyu? Ine ndabwera mʼnyumba yako. Iwe sunandipatse madzi otsukira mapazi anga, koma iyeyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake. 45 Iwe sunandipsompsone, koma mayiyu, kuyambira pamene Ine ndalowa, sanaleke kupsompsona mapazi anga. 46 Iwe sunadzoze mutu wanga mafuta, koma iye wadzoza mapazi anga mafuta onunkhira. 47 Tsono, ndikukuwuza iwe, machimo ake amene ndi ambiri akhululukidwa, monga chaonetsera chikondi chake chachikulu. Koma iye amene wakhululukidwa zochepa amakonda pangʼono.”

48 Kenaka anati kwa mayiyo, “Machimo ako akhululukidwa.”

49 Alendo enawo anayamba kumanena mʼmitima mwawo kuti, “Uyu ndi ndani amene akhululukiranso machimo?”

50 Yesu anati kwa mayiyo, “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa. Pita mu mtendere.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.