M’Cheyne Bible Reading Plan
9 Aisraeli onse analembedwa potsata mibado yawo mʼbuku la mafumu a Aisraeli.
Anthu a ku Yerusalemu
Anthu a ku Yuda anatengedwa kunka ku ukapolo ku Babuloni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo. 2 Tsono anthu oyamba kukhala mʼmadera awo anali Aisraeli wamba, ansembe, Alevi ndi otumikira ku Nyumba ya Yehova.
3 Anthu a ku Yuda, Benjamini ndi Efereimu ndiponso Manase amene anakhala mu Yerusalemu anali awa:
4 Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, chidzukulu cha Perezi mwana wa Yuda.
5 A banja la Siloni:
Asaya mwana wake woyamba pamodzi ndi ana ake.
6 A banja la Zera:
Yeueli.
Anthu ochokera ku Yuda analipo 690.
7 A fuko la Benjamini:
Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuya;
8 Ibineya mwana wa Yerohamu; Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri; ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reueli mwana wa Ibiniya.
9 Anthu ochokera ku Benjamini monga analembedwera mwa mibado yawo, analipo 956. Anthu onsewa anali atsogoleri a mabanja awo.
10 Ansembe:
Yedaya, Yehoyaribu; Yakini;
11 Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubi, wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu;
12 Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasi-Huri, mwana wa Malikiya; ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yahizera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri.
13 Ansembe amene anali atsogoleri a mabanja awo analipo 1,760. Anali anthu amphamvu ndi odziwa kutumikira mʼnyumba ya Mulungu.
14 Alevi:
Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, wa mʼbanja la Merari; 15 Bakibakara, Heresi, Galali ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu; 16 Obadiya mwana wa Semaya mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, amene ankakhala ku midzi ya Anetofati.
17 Alonda a pa makomo:
Salumu, Akubu, Talimoni, Ahimani ndi abale awo. Mtsogoleri wawo anali Salumu. 18 Amenewa amakhala pa chipata cha mfumu kummawa mpaka lero lino. Alonda a gulu la Alevi anali awa: 19 Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja ankanyangʼanira khomo la Tenti monga ankachitira abambo awo polondera khomo la malo okhalapo Yehova. 20 Masiku oyamba Finehasi mwana wa Eliezara anali woyangʼanira alonda apakhomo ndipo Yehova anali naye. 21 Zekariya mwana wa Meselemiya anali mlonda woyangʼanira pa chipata cha tenti ya msonkhano.
22 Onse amene anasankhidwa kukhala alonda pa khonde analipo 212. Iwo analembedwa mwa mibado yawo ku midzi yawo. Davide ndi mneneri Samueli ndiwo anawayika mʼmalo awo antchito chifukwa cha kukhulupirika kwawo. 23 Iwo ndi zidzukulu zawo anali oyangʼanira zipata za nyumba ya Yehova imene imatchedwa Tenti. 24 Alonda apakhomowa anali mbali zonse zinayi: kummawa, kumadzulo, kumpoto ndi kummwera. 25 Abale awo a ku midzi yawo amabwera nthawi ndi nthawi kudzagwira ntchito yawo kwa masiku asanu ndi awiri. 26 Koma atsogoleri akuluakulu anayi a alonda, amene anali Alevi, anapatsidwa udindo woyangʼanira zipinda ndi chuma cha nyumba ya Mulungu. 27 Iwo amakhala usiku wonse atayima mozungulira Nyumba ya Mulungu, chifukwa anayenera kuyilondera. Ndipo anali ndi kiyi wotsekulira mmawa uliwonse.
28 Ena amayangʼanira zipangizo zimene amagwiritsa ntchito pa ntchito mʼNyumba ya Mulungu. Iwo amaziwerenga zikamalowetsedwa ndi potulutsidwa. 29 Ena anapatsidwa udindo wosamalira zipangizo ndi zinthu zina zonse za ku malo opatulika, pamodzi ndi ufa, vinyo, mafuta, lubani ndi zonunkhira. 30 Koma ansembe ena amasakaniza zonunkhirazo. 31 Mlevi wotchedwa Matitiya mwana woyamba wa Salumu wa mʼbanja la Kora, anapatsidwa udindo woyangʼanira zophikidwa mʼziwaya. 32 Abale ake ena a mʼbanja la Akohati amaphika buledi wa pa Sabata lililonse amene amayikidwa pa tebulo.
33 Atsogoleri a mabanja a Alevi, amene anali ndi luso loyimba, amakhala mʼzipinda za Nyumba ya Mulungu ndipo samagwira ntchito zina chifukwa ankatumikira usana ndi usiku.
34 Onsewa anali atsogoleri a mabanja a Alevi, akuluakulu monga analembedwera pa mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu.
Mibado ya Sauli
35 Yeiyeli abambo a Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni.
Dzina la akazi awo linali Maaka, 36 ndipo mwana wawo woyamba kubadwa anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu, 37 Gedori, Ahiyo, Zekariya ndi Mikiloti. 38 Mikiloti anabereka Simeamu. Iwonso ankakhala ndi abale awo ku Yerusalemu.
39 Neri anabereka Kisi, Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.
40 Mwana wa Yonatani anali
Meri-Baala, amene anabereka Mika.
41 Ana a Mika anali:
Pitoni, Meleki, Tahireya ndi Ahazi.
42 Ahazi anabereka Yara, Yara anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimiri anabereka Moza. 43 Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Refaya, Eleasa ndi Azeli.
44 Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo mayina awo anali awa:
Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Awa anali ana a Azeli.
Sauli Adzipha Yekha
10 Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa. 2 Afilisti anapanikiza kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Maliki-Suwa. 3 Nkhondo inakula kwambiri mozungulira Sauli ndipo pamene anthu amauta anamupeza, anamuvulaza.
4 Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe, kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere ndi kudzandizunza ine.”
Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo. 5 Mnyamata wonyamula zida zake uja ataona kuti Sauli wafa, nayenso anadzigwetsera pa lupanga lake nafa. 6 Motero Sauli ndi ana ake atatu anafa, pamodzi ndi banja lake lonse anafera limodzi.
7 Pamene Aisraeli onse amene anali mʼchigwa anaona kuti gulu lankhondo lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo.
8 Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa pa phiri la Gilibowa. 9 Iwo anamuvula zovala zake, natenga mutu wake ndi zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo. 10 Iwo anayika zida zake zankhondo mʼnyumba zopembedzera milungu yawo ndipo anapachika mutu wake mʼnyumba ya Dagoni.
11 Pamene anthu onse okhala ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli, 12 anthu awo onse olimba mtima anapita kukatenga mitembo ya Sauli ndi ana ake ndipo anabwera nayo ku Yabesi. Anakwirira mafupa awo pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.
13 Sauli anafa chifukwa anali wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova, pakuti anakafunsira nzeru kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, 14 sanafunsire nzeruzo kwa Yehova. Choncho Yehova anamupha ndi kupereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese.
Yesu Chitsanzo Chathu
12 Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. 2 Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu. 3 Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima. 4 Polimbana ndi uchimo, simunafike mpaka pokhetsa magazi.
Mulungu Amalanga Ana ake
5 Kodi mwayiwala mawu olimbitsa mtima aja, amene Mulungu anayankhula kwa inu ngati ana ake? Mawuwo ndi awa:
“Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye
ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula.
6 Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda
ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.”
7 Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? 8 Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. 9 Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo? 10 Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima. 11 Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.
12 Nʼchifukwa chake limbitsani manja anu otopa ndi mawondo anu ogowoka. 13 Muziyenda mʼnjira zowongoka, kuti iwo amene akukutsatirani ngakhale ndi olumala ndi ofowoka asapunthwe ndi kugwa koma adzilimbikitsidwa.
Chenjezo kwa Okana Mulungu
14 Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye. 15 Yangʼanitsitsani kuti wina aliyense asachiphonye chisomo cha Mulungu ndiponso kuti pasaphuke muzu wamkwiyo umene udzabweretsa mavuto ndi kudetsa ambiri. 16 Yangʼanitsitsani kuti pasakhale wina wachigololo. Kapena wosapembedza ngati Esau, amene chifukwa cha chakudya cha kamodzi kokha anagulitsa ukulu wake. 17 Monga inu mukudziwa, pambuyo pake pamene anafuna kuti adalitsidwe anakanidwa. Sanapezenso mpata woti asinthe maganizo, ngakhale anafuna madalitsowo ndi misozi.
18 Inu simunafike ku phiri limene mungathe kulikhudza, loyaka moto wa mdima bii, la mphepo yamkuntho; 19 limene pali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mawu. Anthu amene amamva mawuwo anapempha kuti asawayankhulenso mawu ena. 20 Iwo anachita mantha ndi lamulo lija lakuti, “Ngakhale nyama ikangokhudza phirilo, iphedwe ndi miyala.” 21 Maonekedwenso a Mose anali woopsa kwambiri, ngakhale Mose yemwe anati, “Ine ndinachita mantha ndi kunjenjemera.”
22 Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba. Mwafika mu msonkhano wa angelo osangalala osawerengeka. 23 Mwafika mu mpingo wa ana oyamba kubadwa, amene mayina awo analembedwa kumwamba. Inu mwafika kwa Mulungu, woweruza anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama ndi osandutsidwa kukhala angwiro. 24 Kwa Yesu mʼkhalapakati wa pangano latsopano, ndiponso mwafika ku magazi owazidwa amene amayankhula mawu abwino kuposa magazi a Abele.
25 Chenjerani kuti musakane kumvera amene akuyankhula nanu. Anthu amene anakana kumvera iye amene anawachenjeza uja pa dziko lapansi pano, sanapulumuke ku chilango ayi, nanga tsono ife tidzapulumuka bwanji ngati tikufulatira wotichenjeza wochokera kumwamba? 26 Pa nthawiyo mawu ake anagwedeza dziko lapansi, koma tsopano Iye walonjeza kuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza osati dziko lapansi lokha komanso thambo.” 27 Mawu akuti, “Kamodzi kenanso,” akuonetsa kuchotsedwa kwa zimene zitha kugwedezeka, zonse zolengedwa, kotero kuti zimene sizingatheke kugwedezeka zitsale.
28 Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha. 29 Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.
Tsoka kwa Osalabadira Kanthu
6 Tsoka kwa amene simukulabadira kanthu ku Ziyoni,
ndiponso kwa inu amene mukukhala mwamtendere pa Phiri la Samariya,
inu anthu otchuka ochokera ku mtundu wa anthu omveka,
kumene Aisraeli amafikako!
2 Pitani ku mzinda wa Kaline mukawuyangʼane;
mukapitenso ku Hamati-raba mzinda waukulu uja,
ndipo mukatsikirenso ku Gati kwa Afilisti.
Kodi mizinda imeneyi ndi yopambana maufumu anu awiriwa?
Kodi dziko lawo ndi lalikulu kupambana lanu?
3 Inu simulabadirako kuti tsiku loyipa lidzafika,
zochita zanu zimafulumizitsa ulamuliro wankhanza.
4 Mumagona pa mabedi owakongoletsa ndi minyanga ya njovu,
mumagona pa mipando yanu ya wofuwofu.
Mumadya ana ankhosa onona
ndi ana angʼombe onenepa.
5 Mumayimba azeze anu ndi kumangopeka
nyimbo pa zingʼwenyengʼwenye ngati Davide.
6 Mumamwera vinyo mʼzipanda zodzaza
ndipo mumadzola mafuta abwino kwambiri,
koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa Yosefe.
7 Nʼchifukwa chake inu mudzakhala mʼgulu la anthu oyamba kupita ku ukapolo;
maphwando ndi zikondwerero zanu zidzatheratu.
Yehova Amanyansidwa ndi Kunyada kwa Israeli
8 Ambuye Yehova walumbira mʼdzina lake. Yehova Mulungu Wamphamvuzonse walengeza kuti,
“Ndimanyansidwa ndi kunyada kwa Yakobo,
ndimadana ndi nyumba zake zaufumu;
Ine ndidzawupereka mzindawu
pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.”
9 Ngati anthu khumi otsala adzabisala mʼnyumba imodzi, nawonso adzafa ndithu. 10 Ndipo ngati mʼbale wake wa wina wakufayo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mitembo mʼnyumbamo nʼkufunsa aliyense amene akubisalabe mʼnyumbamo kuti, “Kodi uli ndi wina wamoyo mʼmenemo?” Ndipo munthu wobisalayo ndi kuyankha kuti, “Ayi,” mʼbaleyo adzanena kuti, “Khala chete! Ife tisayerekeze kutchula dzina la Yehova.”
11 Pakuti Yehova walamula kuti
nyumba zikuluzikulu Iye adzazigamulagamula,
ndipo nyumba zazingʼono zidzasanduka maduka okhaokha.
12 Kodi akavalo amathamanga pa thanthwe?
Kodi wina amatipula ndi ngʼombe mʼnyanja?
Koma chiweruzo cholungama mwachisandutsa kukhala zinthu zakupha
ndipo chipatso cha chilungamo mwachisandutsa kukhala chowawa.
13 Inu amene mukunyadira kuti munagonjetsa Lo Debara
ndipo mukunena kuti, “Kodi sitinatenge Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?”
14 Koma Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akulengeza kuti,
“Inu nyumba ya Israeli, ndidzakudzutsirani mtundu wina wa anthu
umene udzakuzunzani
kuchokera ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha Araba.”
Mariya Acheza kwa Elizabeti
39 Nthawi imeneyo anakonzeka ndipo anapita mofulumira ku mudzi wa ku mapiri a dziko la Yudeya, 40 kumene anakalowa mʼnyumba ya Zakariya nalonjera Elizabeti. 41 Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. 42 Anafuwula ndi mawu akulu kuti, “Ndiwe wodala pakati pa akazi, ndipo ndi wodala mwana amene udzabereke! 43 Koma nʼchifukwa chiyani andikomera mtima kuti amayi a Ambuye anga abwere kwa ine? 44 Nthawi yomwe ndinamva mawu akulonjera kwanu, mwana anatakataka mʼmimba mwanga chifukwa cha chimwemwe. 45 Wodala iye amene wakhulupirira kuti chimene Ambuye wanena kwa iye chidzakwaniritsidwa!”
Nyimbo ya Mariya
46 Ndipo Mariya anati:
“Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
47 Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48 pakuti wakumbukira
kudzichepetsa kwa mtumiki wake.
Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
49 pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,
dzina lake ndi loyera.
50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye
kufikira mibadomibado.
51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;
Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,
koma wakweza odzichepetsa.
53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino
koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,
pokumbukira chifundo chake.
55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse
monga ananena kwa makolo athu.”
56 Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu ndipo kenaka anabwerera kwawo.
Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi
57 Itakwana nthawi yoti Elizabeti abereke, anabereka mwana wamwamuna. 58 Anansi ndi abale ake anamva kuti Ambuye anamuchitira chifundo chachikulu ndipo anakondwera naye pamodzi.
59 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu anabwera ndi mwana kuti adzachitidwe mdulidwe, ndipo anafuna kumupatsa dzina la abambo ake Zakariya, 60 koma amayi ake anayankhula nati, “Ayi, atchulidwe kuti Yohane.”
61 Iwo anati kwa iye, “Palibe mmodzi mwa abale ake amene ali ndi dzina limeneli.”
62 Pamenepo anapanga zizindikiro kwa abambo ake kuti adziwe dzina limene akanakonda kumutcha mwanayo. 63 Iye anapempha poti alembepo, ndipo chodabwitsa kwa aliyense analemba kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” 64 Nthawi yomweyo pakamwa pake panatsekuka ndi lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula, nayamika Mulungu. 65 Anansi onse anachita mantha kwambiri, ndipo ku madera onse a kumapiri a Yudeya, anthu anayankhula zinthu zonsezi. 66 Aliyense amene anamva izi anadabwa nazo nafunsa kuti, “Kodi mwana uyu adzakhala wotani?” Pakuti dzanja la Ambuye lili pa iye.
Nyimbo ya Zakariya
67 Abambo ake, Zakariya, anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenera kuti,
68 “Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli
chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.
69 Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife
mu nyumba ya mtumiki wake Davide.
70 (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera),
71 chipulumutso kuchoka kwa adani athu
ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,
72 kuonetsa chifundo kwa makolo athu
ndi kukumbukira pangano lake loyera,
73 lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu:
74 kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu,
ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha,
75 mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse.
76 “Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba;
pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake,
77 kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso
kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,
78 chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu,
ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba,
79 kuwalira iwo okhala mu mdima
ndi mu mthunzi wa imfa,
kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere.”
80 Ndipo mwanayo anakula nakhala wamphamvu mu mzimu; ndipo anakhala ku chipululu mpaka pamene anaonekera poyera mu Israeli.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.