Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 5-6

Fuko la Rubeni

Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa, ndipo ngakhalenso Yuda anali wamphamvu kwambiri pakati pa abale ake, ndi kuti wolamulira anachokera mwa iye, ulemu wa mwana woyamba kubadwa unaperekedwa kwa Yosefe) ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli ndi awa:

Hanoki, Palu, Hezironi, ndi Karimi.

Ana a Yoweli anali awa:

Semaya, Gogi,

Simei, Mika,

Reaya, Baala,

ndiponso Beeri, amene Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri anamugwira ukapolo. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni anali Beeri.

Abale awo mwa mabanja awo, potsata mndandanda wa mʼbado wawo, ndi awa:

Yeiyeli, mtsogoleri, Zekariya, ndiponso Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoweli. Iwo ankakhala ku Aroeri mpaka ku Nebo ndi Baala-Meoni. Iwo anakhala cha kummawa mpaka kukafika polowera mʼchipululu cha mbali ina ya Mtsinje wa Yufurate, chifukwa ziweto zawo zinaswana kwambiri mʼdziko la Giliyadi.

10 Pa nthawi ya Sauli anachita nkhondo ndi Ahagiri ndi kuwagonjetsa. Tsono iwo anakhala mʼmatenti a Ahagiri ku dera lonse la kummawa kwa Giliyadi.

Fuko la Gadi

11 Anthu a fuko la Gadi anakhala moyandikana ndi fuko la Rubeni ku Basani mpaka ku Saleka:

12 Mtsogoleri wawo ku Basani anali Yoweli, wachiwiri anali Safamu, kenaka Yanayi ndi Safati.

13 Abale awo mwa mabanja awo anali awa:

Mikayeli, Mesulamu, Seba, Yorayi, Yakani, Ziya ndi Eberi, onse ali asanu ndi awiri.

14 Amenewa ndiwo anali ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikayeli, mwana wa Yesisayi, mwana wa Yahido, mwana wa Buzi.

15 Ahi mwana wa Abdieli, mwana wa Guni, anali mtsogoleri wa banja la makolo awo.

16 Fuko la Gadi linakhala ku Giliyadi, ku Basani ndi midzi yozugulira, madera onse a msipu a ku Saroni mpaka kumene amalekezera.

17 Mayina onsewa analembedwa potsata mndandanda wa mibado yawo pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu mfumu ya Yuda ndi Yeroboamu mfumu ya Israeli.

18 Mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la Manase, anali ndi anthu 44, 760 okonzeka kulowa usilikali; anthu amatupi amphamvu, amene amatha kugwiritsa ntchito chishango ndi lupanga, amene amatha kugwiritsa ntchito uta, amene anaphunzitsidwa kumenya nkhondo. 19 Iwo anachita nkhondo ndi Ahagiri, Yeturi, Nafisi ndi Nodabu. 20 Iwowo anathandizidwa polimbana nawo ndipo Mulungu anapereka Ahagiri mʼmanja mwawo; popeza iwo anafuwulira kwa Mulungu pa nkhondopo. Iye anayankha mapemphero awo chifukwa anamudalira. 21 Choncho iwo analanda ziweto za Ahagiri: ngamira 50,000, nkhosa ndi mbuzi 250,000 ndi abulu 2,000. Ndiponso anagwira akapolo 100,000, 22 enanso ambiri anaphedwa, chifukwa nkhondoyo inali ya Mulungu. Ndipo iwo anakhala mʼdzikomo mpaka pa nthawi ya ukapolo.

Theka la Fuko la Manase

23 Theka la fuko la Manase linkakhala ku dziko la kummawa kuyambira ku Basani mpaka ku Baala-Herimoni, kumene ndi ku Seniri (Phiri la Herimoni) ndipo anthuwo anali ochuluka kwambiri.

24 Atsogoleri a mabanja awo anali awa: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya ndi Yahidieli. Iwo anali asilikali olimba mtima, anthu otchuka, ndiponso atsogoleri a mabanja awo. 25 Koma iwo anali osakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo ndipo anadzipereka okha kwa milungu ya anthu okhala mʼdzikomo amene Mulungu anawawononga pamene iwowo ankafika. 26 Kotero Mulungu wa Israeli anayika mkwiyo mwa Puli mfumu ya Asuri (ameneyu ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri) amene anatenga fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase kupita nawo ku ukapolo. Iye anapita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, kumene ali mpaka lero lino.

Fuko la Levi

Ana a Levi anali awa:

Geresoni, Kohati ndi Merari.

Ana a Kohati anali awa:

Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.

Ana a Amramu anali awa:

Aaroni, Mose ndi Miriamu.

Ana a Aaroni anali awa:

Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara

Eliezara anabereka Finehasi,

Finehasi anabereka Abisuwa,

Abisuwa anabereka Buki,

Buki anabereka Uzi.

Uzi anabereka Zerahiya,

Zerahiya anabereka Merayoti,

Merayoti anabereka Amariya,

Amariya anabereka Ahitubi.

Ahitubi anabereka Zadoki,

Zadoki anabereka Ahimaazi.

Ahimaazi anabereka Azariya,

Azariya anabereka Yohanani,

10 Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu),

11 Azariya anabereka Amariya,

Amariya anabereka Ahitubi,

12 Ahitubi anabereka Zadoki,

Zadoki anabereka Salumu,

13 Salumu anabereka Hilikiya,

Hilikiya anabereka Azariya,

14 Azariya anabereka Seraya,

ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.

15 Yehozadaki anagwidwa ukapolo pamene Yehova analola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo Yuda ndi Yerusalemu.

16 Ana a Levi anali awa:

Geresomu, Kohati ndi Merari.

17 Mayina a ana a Geresomu ndi awa:

Libini ndi Simei.

18 Ana a Kohati anali awa:

Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.

19 Ana a Merari anali awa:

Mahili ndi Musi.

Mayina a mabanja a fuko la Levi olembedwa potsata makolo awo ndi awa:

20 Ana a Geresomu ndi awa:

Libini, Yehati,

Zima, 21 Yowa,

Ido, Zera

ndi Yeaterai.

22 Zidzukulu za Kohati ndi izi:

Aminadabu, Kora,

Asiri, 23 Elikana,

Ebiyasafu, Asiri,

24 Tahati, Urieli,

Uziya ndi Sauli.

25 Zidzukulu za Elikana ndi izi:

Amasai, Ahimoti,

26 Elikana, Zofai,

Nahati, 27 Eliabu,

Yerohamu, Elikana

ndi Samueli.

28 Ana a Samueli ndi awa:

Mwana wake woyamba anali Yoweli,

wachiwiri anali Abiya.

29 Zidzukulu za Merari ndi izi:

Mahili, Libini,

Simei, Uza,

30 Simea, Hagiya

ndi Asaya.

Oyimba mʼNyumba ya Mulungu

31 Awa ndi anthu amene Davide anawayika kuti aziyangʼanira mayimbidwe mʼNyumba ya Yehova, Bokosi la Chipangano litabwera kudzakhala mʼmenemo. 32 Iwo ankatumikira akuyimba nyimbo pa khomo la malo opatulika, tenti ya msonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu. Iwo ankagwira ntchito zawo potsata malamulo amene anawapatsa.

33 Mayina a anthuwo, pamodzi ndi ana awo, anali awa:

Ochokera ku banja la Kohati:

Hemani, katswiri woyimba,

anali mwana wa Yoweli, mwana wa Samueli,

34 mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu,

mwana wa Elieli, mwana wa Towa,

35 mwana wa Zufi, mwana wa Elikana,

mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,

36 mwana wa Elikana, mwana wa Yoweli,

mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,

37 mwana wa Tahati, mwana wa Asiri,

mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,

38 mwana wa Izihari, mwana wa Kohati,

mwana wa Levi, mwana wa Israeli;

39 ndi Asafu mʼbale wake, amene ankatumikira ku dzanja lake lamanja:

Asafu anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,

40 mwana wa Mikayeli, mwana wa Baaseya,

mwana wa Malikiya, 41 mwana wa Etini,

mwana wa Zera, mwana wa Adaya,

42 mwana wa Etani, mwana wa Zima,

mwana Simei, 43 mwana wa Yahati,

mwana wa Geresomu, mwana wa Levi;

44 ndipo abale awo ena anali a banja la Merari amene amatumikira ku dzanja lake lamanzere:

Etani anali mwana wa Kisi, mwana wa Abidi,

mwana wa Maluki, 45 mwana wa Hasabiya,

mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,

46 mwana wa Amizi, mwana wa Bani,

mwana wa Semeri, 47 mwana wa Mahili,

mwana wa Musi, mwana wa Merari,

mwana wa Levi.

48 Abale awo Alevi anapatsidwa ntchito zina zonse ku malo opatulika ku nyumba ya Mulungu. 49 Koma Aaroni ndi zidzukulu zake anali amene amapereka nsembe pa guwa lansembe zopsereza ndi pa guwa lansembe zofukiza pamodzi ndi zonse zimene zimachitika ku malo opatulika kwambiri, kuchita mwambo wopepesera Israeli, potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu anawalamulira.

50 Ana a Aaroni ndi zidzukulu zake anali awa:

Eliezara, Finehasi,

Abisuwa, 51 Buki,

Uzi, Zerahiya,

52 Merayoti, Amariya,

Ahitubi, 53 Zadoki

ndi Ahimaazi.

54 Malo amene iwo anapatsidwa kuti likhale dziko lawo ndi awa: (Malowa anapatsidwa kwa zidzukulu za Aaroni zimene zinali za banja la Kohati, chifukwa malo oyamba kugawidwa anali awo).

55 Iwo anapatsidwa Hebroni mʼdziko la Yuda ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. 56 Koma minda ndi midzi yozungulira mzindawo zinapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune.

57 Kotero zidzukulu za Aaroni zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako), ndi Libina, Yatiri, Esitemowa, 58 Hileni, Debri, 59 Asani, Yuta ndi Beti-Semesi pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. 60 Ndipo ku fuko la Benjamini anapatsidwa Gibiyoni, Geba, Alemeti ndi Anatoti, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.

Mizinda imene anapatsidwa ku banja la Kohati onse pamodzi inalipo 13.

61 Zidzukulu zotsala za Kohati anazigawira midzi khumi kuchokera ku mabanja a fuko la theka la Manase.

62 Zidzukulu za Geresomu banja ndi banja zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Isakara, Aseri ndi Nafutali, ndi gawo lina la fuko la Manase limene lili ku Basani.

63 Zidzukulu za Merari banja ndi banja zinapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.

64 Kotero Aisraeli anapatsa Alevi mizindayi ndi madera a msipu ozungulira malowa. 65 Kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini anawapatsa mizinda imene inawatchula kale mayina.

66 Mabanja ena a Kohati anapatsidwanso malo kuchokera ku fuko la Efereimu.

67 Kuchokera ku dziko lamapiri la Efereimu anapatsidwa Sekemu (mzinda wopulumukirako) ndi Gezeri, 68 Yokineamu, Beti-Horoni, 69 Ayaloni ndi Gati-Rimoni, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira.

70 Ndipo kuchokera ku theka la fuko la Manase, Aisraeli anapereka Aneri ndi Bileamu pamodzi ndi madera odyetsera ziweto kwa mabanja ena onse a Kohati.

71 Ageresomu analandira malo awa:

Kuchokera ku theka la fuko la Manase,

analandira Golani ku Basani ndiponso Asiteroti, ndi malo awo odyetsera ziweto;

72 Kuchokera ku fuko la Isakara

analandira Kedesi, Daberati, 73 Ramoti ndi Anemu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

74 kuchokera ku fuko la Aseri

analandira Masala, Abidoni, 75 Hukoki ndi Rehobu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

76 ndipo kuchokera ku fuko la Nafutali

analandira Kedesi ku Galileya, Hamoni ndi Kiriyataimu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.

77 Amerari (Alevi ena onse) analandira madera awa:

kuchokera ku fuko la Zebuloni,

iwo analandira Yokineamu, Karita, Rimono ndi Tabori, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

78 Kuchokera ku fuko la Rubeni kutsidya kwa Yorodani, kummawa kwa Yeriko,

analandira Bezeri ku chipululu, Yaza, 79 Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

80 ndipo kuchokera ku fuko la Gadi

analandira Ramoti ku Giliyadi, Mahanaimu, 81 Hesiboni ndi Yazeri, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.

Ahebri 10

Yesu Nsembe ya Anthu Onse

10 Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza. Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo. Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka. Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.

Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati,

“Simunafune nsembe kapena zopereka,
    koma thupi munandikonzera.
Simunakondwere nazo nsembe zopsereza
    ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.
Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine,
    Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ ”

Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe. Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri. 10 Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.

11 Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo. 12 Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu. 13 Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake. 14 Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.

15 Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,

16 “Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo
    atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo,
    ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”

17 Ndipo akutinso:

“Sindidzakumbukiranso konse
    machimo awo ndi zolakwa zawo.”

18 Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.

Kulimbika Mtima ndi Kupirira pa Chikhulupiriro

19 Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake. 21 Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu. 22 Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera. 23 Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. 24 Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. 25 Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.

26 Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. 27 Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu 28 Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu. 29 Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo? 30 Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” 31 Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.

32 Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri. 33 Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere. 34 Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.

35 Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu. 36 Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza. 37 Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe,

Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi.
38 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
    Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha,
    Ine sindidzakondwera naye.

39 Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.

Amosi 4

Israeli Sanabwerere kwa Mulungu

Imvani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basani, okhala pa Phiri la Samariya,
    inu akazi amene mumapondereza anthu osauka ndi kuzunza anthu osowa
    ndi kumanena kwa amuna anu kuti, “Tipatseni zakumwa!”
Ambuye Yehova, mwa kuyera mtima kwake walumbira kuti,
    “Nthawi idzafika ndithu
pamene adzakukokani ndi ngowe,
    womaliza wa inu adzakokedwa ndi mbedza.
Mudzatulukira mʼmingʼalu ya pa khoma
    aliyense payekhapayekha,
    ndipo mudzatayidwa ku Harimoni,”
            akutero Yehova.
“Bwerani ku Beteli mudzachimwe;
    ndi ku Giligala kuti mudzapitirize kuchimwa.
Bweretsani nsembe zanu mmawa uliwonse,
    bweretsani chakhumi chanu masiku atatu aliwonse.
Wotchani buledi wokhala ndi yisiti ngati nsembe yachiyamiko
    ndi kumanyadira poyera za zopereka zanu zaufulu.
Inu Aisraeli, zinyadireni nsembezo,
    pakuti izi ndi zimene mumakonda kuchita,”
            akutero Ambuye Yehova.

“Ndine amene ndinakusendetsani milomo mʼmizinda yanu yonse,
    ndipo munasowa chakudya mʼmizinda yanu.
    Komatu inu simunabwerere kwa Ine,”
            akutero Yehova.

“Ndinenso amene ndinamanga mvula
    patangotsala miyezi itatu kuti mukolole.
Ndinagwetsa mvula pa mzinda wina,
    koma pa mzinda wina ayi,
mvula inkagwa pa munda wina;
    koma sinagwe pa munda wina ndipo mbewu zinawuma.
Anthu ankayenda mzinda ndi mzinda kufuna madzi,
    koma sanapeze madzi okwanira kumwa.
    Komabe inu simunabwerere kwa Ine,”
            akutero Yehova.

“Nthawi zambiri ndinakantha mbewu zanu ndiponso minda ya mpesa,
    ndinayikantha ndi chinsikwi ndiponso ndi chiwawu.
Dzombe linawononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi.
    Komabe inu simunabwerere kwa Ine,”
            akutero Yehova.

10 “Ine ndinabweretsa miliri pakati panu
    monga ndinachitira ku Igupto.
Ndinapha anyamata anu ndi lupanga,
    ndinapereka akavalo anu kwa adani.
Ndinakununkhitsani fungo la mitembo lochokera mʼmisasa yanu ya nkhondo.
    Komatu inu simunabwerere kwa Ine,”
            akutero Yehova.

11 “Ndinawononga ena mwa inu
    monga ndinawonongera Sodomu ndi Gomora.
Inu munali ngati chikuni choyaka chimene chafumulidwa pa moto.
    Komabe inu simunabwerere kwa Ine,”
            akutero Yehova.

12 “Choncho izi ndi zimene ndidzakuchitire iwe Israeli,
    chifukwa ndidzakuchitira zimenezi,
    konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Israeli.”

13 Iye amene amawumba mapiri,
    amalenga mphepo,
    ndipo amawululira munthu za mʼmaganizo ake,
Iye amene amasandutsa usana kuti ukhale mdima,
    ndipo amayenda pa zitunda za dziko lapansi,
    dzina lake ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.

Masalimo 148-150

148 Tamandani Yehova.

Tamandani Yehova, inu a kumwamba,
    mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
Mutamandeni, inu angelo ake onse,
    mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,
    mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba
    ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
Zonse zitamande dzina la Yehova
    pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.
Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;
    analamula ndipo sizidzatha.

Tamandani Yehova pa dziko lapansi,
    inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,
inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,
    mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,
inu mapiri ndi zitunda zonse,
    inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,
10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,
    inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.
11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,
    inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.
12 Inu anyamata ndi anamwali,
    inu nkhalamba ndi ana omwe.

13 Onsewo atamande dzina la Yehova
    pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;
    ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
14 Iye wakwezera nyanga anthu ake,
    matamando a anthu ake onse oyera mtima,
    Aisraeli, anthu a pamtima pake.

Tamandani Yehova.
149 Tamandani Yehova.

Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
    matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.

Israeli asangalale mwa mlengi wake;
    anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.
Atamande dzina lake povina
    ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.
Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake;
    Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.
Oyera mtima asangalale mu ulemu wake
    ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.

Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo,
    ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,
kubwezera chilango anthu a mitundu ina,
    ndi kulanga anthu a mitundu yonse,
kumanga mafumu awo ndi zingwe,
    anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,
kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo
    Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse.

Tamandani Yehova.
150 Tamandani Yehova.

Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika;
    mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.
Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu;
    mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.
Mutamandeni poyimba malipenga,
    mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.
Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina,
    mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.
Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga,
    mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.

Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova.

Tamandani Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.