Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 1-2

Mbiri ya Makolo Kuchokera pa Adamu Mpaka pa Abrahamu

Mpaka pa Ana a Nowa

Adamu, Seti, Enosi Kenani, Mahalaleli, Yaredi, Enoki, Metusela, Lameki, Nowa.

Ana a Nowa,

Semu, Hamu ndi Yafeti.

Fuko la Yafeti

Ana aamuna a Yafeti anali:

Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.

Ana aamuna a Gomeri anali:

Asikenazi, Rifati ndi Togarima

Ana aamuna a Yavani anali:

Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.

Fuko la Hamu

Ana aamuna a Hamu anali:

Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani

Ana aamuna a Kusi anali:

Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka

Ana aamuna a Raama anali:

Seba ndi Dedani.

10 Kusi anali abambo a Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu

kwambiri pa dziko lapansi.

11 Igupto ndiye kholo la

Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, 12 Apaturusi, Akasilu (kumene kunachokera Afilisti) ndi Akafitori.

13 Kanaani anabereka mwana wake wachisamba Sidoni,

ndipo anaberekanso Ahiti, 14 Ayebusi, Aamori, Agirigasi 15 Ahivi, Aariki, Asini 16 Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.

Fuko la Semu

17 Ana aamuna a Semu anali:

Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.

Ana aamuna a Aramu anali:

Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.

18 Aripakisadi anabereka Sela

ndipo Selayo anabereka Eberi:

19 Eberi anabereka ana aamuna awiri:

wina anamutcha Pelegi, chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.

20 Yokitani anabereka

Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, 21 Hadoramu, Uzali, Dikila 22 Obali, Abimaeli, Seba, 23 Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.

24 Semu, Aripakisadi, Sela

25 Eberi, Pelegi, Reu

26 Serugi, Nahori, Tera

27 ndi Abramu (amene ndi Abrahamu).

Banja la Abrahamu

28 Ana a Abrahamu ndi awa:

Isake ndi Ismaeli.

Zidzukulu za Hagara

29 Zidzukulu zake zinali izi:

Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli, kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, 30 Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema, 31 Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Awa anali ana a Ismaeli.

Zidzukulu za Ketura

32 Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu anali awa:

Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa.

Ana a Yokisani ndi awa:

Seba ndi Dedani

33 Ana aamuna a Midiyani anali,

Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.

Onsewa anali zidzukulu za Ketura.

Zidzukulu za Sara

34 Abrahamu anabereka Isake.

Ana a Isake anali awa:

Esau ndi Israeli.

Ana a Esau

35 Ana aamuna a Esau anali awa:

Elifazi, Reueli, Yeusi, Yolamu ndi Kora.

36 Ana a Elifazi anali awa:

Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi:

Amene anabereka ndi Timna: Amaleki.

37 Ana a Reueli anali awa:

Nahati, Zera, Sama ndi Miza.

Anthu a ku Seiri ku Edomu

38 Ana a Seiri anali awa:

Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, Disoni, Ezeri ndi Disani.

39 Ana aamuna a Lotani anali awa:

Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.

40 Ana aamuna a Sobala anali awa:

Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.

Ana aamuna a Zibeoni anali awa:

Ayiwa ndi Ana.

41 Mwana wa Ana anali

Disoni.

Ana a Disoni anali awa:

Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani

42 Ana aamuna a Ezeri anali awa:

Bilihani, Zaavani ndi Yaakani.

Ana aamuna a Disani anali awa:

Uzi ndi Arani.

Mafumu a ku Edomu

43 Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:

Bela mwana wa Beori, mzinda wake ankawutcha Dinihaba.

44 Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.

45 Yobabu atamwalira, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa ufumu mʼmalo mwake.

46 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.

47 Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka analowa ufumu mʼmalo mwake.

48 Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje analowa ufumu mʼmalo mwake.

49 Sauli atamwalira, Baala-Hanani mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.

50 Pamene Baala-Hanani anamwalira, Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli mwana wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. 51 Hadadi anamwaliranso.

Mafumu a ku Edomu anali:

Timna, Aliva, Yeteti, 52 Oholibama, Ela, Pinoni, 53 Kenazi, Temani, Mibezari, 54 Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu.

Ana a Israeli

Ana a Israeli anali awa:

Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni, Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi ndi Aseri.

Yuda Mpaka pa Ana a Hezironi

Ana a Hezironi

Ana a Yuda anali awa:

Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha. Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.

Ana a Perezi anali awa:

Hezironi ndi Hamuli.

Ana a Zera anali awa:

Zimuri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo asanu.

Mwana wa Karimi anali

Akani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa.

Mwana wa Etani anali

Azariya.

Ana amene anabadwa kwa Hezironi anali:

Yerahimeeli, Ramu ndi Kelubai.

Kuchokera kwa Ramu Mwana wa Hezironi

10 Ramu anabereka

Aminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda. 11 Naasoni anabereka Salima, Salima anabereka Bowazi, 12 Bowazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Yese.

13 Yese anabereka

Eliabu mwana wake woyamba, wachiwiri Abinadabu, wachitatu Simea, 14 wachinayi Netaneli, wachisanu Radai, 15 wachisanu ndi chimodzi Ozemu ndi wachisanu ndi chiwiri Davide. 16 Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli. 17 Abigayeli anali amayi ake a Amasa amene abambo ake anali Yeteri wa fuko la Ismaeli.

Kalebe Mwana wa Hezironi

18 Kalebe mwana wa Hezironi anabereka ana mwa Azuba mkazi wake (ndi mwa Yerioti). Ana a mkaziyo anali awa: Yeseri, Sobabu ndi Aridoni. 19 Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri. 20 Huri anabereka Uri ndipo Uri anabereka Bezaleli.

21 Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu. 22 Segubu anabereka Yairi, amene anali ndi mizinda 23 ku Giliyadi. 23 (Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi.

24 Atamwalira Hezironi ku Kalebe Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anamuberekera Asihuri abambo a Tekowa.

Yerahimeeli Mwana wa Hezironi

25 Ana a Yerahimeeli, mwana woyamba wa Hezironi anali:

Ramu, mwana wake woyamba, Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya. 26 Yerahimeeli anali ndi mkazi wina amene dzina lake linali Atara, amene anali amayi a Onamu.

27 Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerahimeeli, anali awa:

Maazi, Yamini ndi Ekeri.

28 Ana a Onamu anali awa:

Shamai ndi Yada.

Ana a Shamai anali awa:

Nadabu ndi Abisuri.

29 Mkazi wa Abisuri anali Abihaili, amene anamuberekera Ahibani ndi Molidi.

30 Ana a Nadabu anali awa:

Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana.

31 Ana a Apaimu anali awa:

Isi, amene anabereka Sesani.

Sesani anabereka Ahilai.

32 Ana a Yada, mʼbale wa Samai, anali awa:

Yereri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana.

33 Ana a Yonatani anali awa:

Peleti ndi Zaza.

Amenewa anali adzukulu a Yerahimeeli.

34 Sesani sanabereke ana aamuna koma aakazi okhaokha.

Iye anali ndi wantchito wa ku Igupto, dzina lake Yariha. 35 Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yariha wantchito wake kuti amukwatire ndipo anamuberekera Atayi.

36 Atayi anali abambo ake a Natani,

Natani anali abambo ake a Zabadi,

37 Zabadi anali abambo a Efilali,

Efilali anali abambo a Obedi,

38 Obedi anali abambo a Yehu,

Yehu anali abambo a Azariya,

39 Azariya anali abambo a Helezi,

Helezi anali abambo a Eleasa,

40 Eleasa anali abambo ake a Sisimai,

Sisimai anali abambo a Salumu,

41 Salumu anali abambo a Yekamiya,

Yekamiya anali abambo a Elisama.

Mabanja a Kalebe

42 Ana a Kalebe mʼbale wa Yerahimeeli anali awa:

Mesa mwana wachisamba, anali abambo a Zifi, ndipo mwana wake Maresa anali abambo a Hebroni.

43 Ana a Hebroni anali awa:

Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema. 44 Sema anali abambo ake Rahamu ndipo Rahamu anali abambo a Yorikeamu. Rekemu anali abambo a Samai. 45 Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali abambo a Beti Zuri.

46 Efai, mzikazi wa Kalebe, anali amayi a Harani, Moza ndi Gazezi. Harani anali abambo a Gazezi.

47 Ana a Yahidai anali awa:

Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efai ndi Saafi.

48 Maaka mzikazi wa Kalebe anali mayi Seberi ndi Tirihana. 49 Iye anaberekanso Saafi abambo a Madimena ndi Seva abambo a Makibena ndi Gibeya. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa. 50 Izi zinali zidzukulu za Kalebe.

Ana a Huri mwana wachisamba wa Efurata anali awa:

Sobala abambo a Kiriati Yearimu, 51 Salima abambo a Betelehemu ndi Harefu abambo ake a Beti-Gadera.

52 Zidzukulu za Sobala abambo a Kiriati Yearimu zinali izi:

Harowe, theka la banja la Manahati, 53 ndipo mabanja a Kiriati-Yeyarimu anali awa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati ndi Aesitaoli anachokera kwa amenewa.

54 Zidzukulu za Salima zinali izi:

Betelehemu, Anetofati, Atiroti-Beti-Yowabu, theka la banja la Manahati, Azori, 55 ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu.

Ahebri 8

Mkulu wa Ansembe wa Pangano Latsopano

Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu Waulemerero kumwamba. Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.

Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu, ndipo kunali koyenera kuti wansembe wathunso akhale nʼkanthu kopereka. Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo. Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.

Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake. Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati,

“Masiku akubwera,” akutero Yehova,
    “pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
    ndiponso nyumba ya Yuda.
Silidzakhala ngati pangano
    limene ndinachita ndi makolo awo,
pamene ndinawagwira padzanja
    nʼkuwatulutsa ku Igupto
chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija
    ndipo Ine sindinawasamalire,
            akutero Ambuye.
10 Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli:
    Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye,
Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo,
    ndi kulemba mʼmitima mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo,
    ndipo iwo adzakhala anthu anga.
11 Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake,
    kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye
chifukwa onse adzandidziwa,
    kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.
12 Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo,
    ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

13 Ponena kuti, pangano “latsopano” Mulungu wapanga pangano loyamba lija kukhala lotha ntchito, ndipo chilichonse chimene chayamba kutha ntchito ndi kukalamba, chili pafupi kuchokeratu.

Amosi 2

Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Mowabu akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu,
    mpaka kuwasandutsa phulusa,
Ine ndidzatumiza moto pa Mowabu,
    umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Keriyoti.
Mowabu adzafera pakati pa nkhondo yoopsa,
    mʼkati mwa mfuwu wa nkhondo ndi kuliza malipenga.
Ndidzawononga wolamulira wake
    ndi kupha akuluakulu onse amene ali pamodzi ndi iye,”
            akutero Yehova.

Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Popeza iwo akana lamulo la Yehova
    ndipo sanasunge malangizo ake,
popeza asocheretsedwa ndi milungu yabodza,
    milungu imene makolo awo ankayitsatira,
Ine ndidzatumiza moto pa Yuda,
    umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu.”

Chilango cha Anthu a ku Israeli

Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Israeli akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Iwo amagulitsa anthu olungama ndi siliva,
    ndi osauka ndi nsapato.
Amapondereza anthu osauka
    ngati akuponda fumbi,
    ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa.
Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo,
    ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera.
Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe
    pa zovala zimene anatenga ngati chikole.
Mʼnyumba ya mulungu wawo
    amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu.

“Ine ndinawononga Aamori pamaso pawo,
    ngakhale iwo anali anthu ataliatali ngati mikungudza
    ndiponso amphamvu ngati mitengo ya thundu.
Ndinawononga zipatso zawo
    ndiponso mizu yawo.

10 “Ine ndinakutulutsani ku Igupto,
    ndipo ndinakutsogolerani mʼchipululu kwa zaka makumi anayi,
    kudzakupatsani dziko la Aamori.
11 Ine ndinawutsanso ena mwa ana ako kuti akhale aneneri,
    ndi ena mwa anyamata ako kuti akhale anaziri.
Kodi si choncho, inu Aisraeli?”
            akutero Yehova.
12 “Koma inu munawamwetsa vinyo anaziri aja,
    ndipo munalamula aneneri kuti asanenere.

13 “Tsono Ine ndidzakupsinjani
    monga imapsinjikira ngolo imene yadzaza ndi tirigu.
14 Munthu waliwiro sadzatha kuthawa,
    munthu wamphamvu sadzakhalanso ndi nyonga,
    wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.
15 Munthu wa uta sadzalimbika,
    msilikali wothamanga kwambiri sadzapulumuka,
    ndipo wokwera pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake.
16 Ngakhale asilikali olimba mtima kwambiri
    adzathawa ali maliseche pa tsikulo,”
            akutero Yehova.

Masalimo 145

Salimo la matamando la Davide.

145 Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga;
    ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.
Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku
    ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.

Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse;
    ukulu wake palibe angawumvetsetse.
Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina;
    Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.
Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu,
    ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.
Iwo adzafotokoza za mphamvu ya ntchito zanu zoopsa kwambiri,
    ndipo ine ndidzalengeza za ntchito zanu zazikulu.
Adzakondwerera kuchuluka kwa ubwino wanu,
    ndi kuyimba mwachimwemwe za chilungamo chanu.

Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo,
    wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.
Yehova ndi wabwino kwa onse;
    amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.
10 Zonse zimene munazipanga zidzakutamandani, Inu Yehova;
    oyera mtima adzakulemekezani.
11 Iwo adzafotokoza za ulemerero wa ufumu wanu
    ndi kuyankhula za mphamvu yanu,
12 kuti anthu onse adziwe za machitidwe anu amphamvu
    ndi ulemerero wokongola wa ufumu wanu.
13 Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,
    ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse.

Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse
    ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.
14 Yehova amagwiriziza onse amene akugwa
    ndipo amakweza onse otsitsidwa.
15 Maso a onse amayangʼana kwa Inu,
    ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera.
16 Mumatsekula dzanja lanu
    ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.

17 Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,
    ndi wokonda zonse zimene anazipanga.
18 Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana,
    onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.
19 Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa;
    amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.
20 Yehova amayangʼana onse amene amamukonda
    koma adzawononga anthu onse oyipa.

21 Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova.
    Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyera
    ku nthawi za nthawi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.