Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 17

Hoseya Mfumu Yotsiriza ya Israeli

17 Mʼchaka cha 12 cha Ahazi mfumu ya Yuda, Hoseya mwana wa Ela anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka zisanu ndi zinayi. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi mafumu a Israeli amene ankalamulira iye asanalowe ufumuwo.

Salimenezeri mfumu ya ku Asiriya anabwera kudzathira nkhondo Hoseya amene anali pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iyeyo. Koma mfumu ya ku Asiriya inazindikira kuti Hoseya akuwukira, pakuti Hoseyayo anali atatumiza nthumwi kwa So mfumu ya Igupto ndiponso analeka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, monga ankachitira chaka ndi chaka. Choncho Salimenezeri anagwira Hoseya ndi kumuyika mʼndende. Mfumu ya ku Asiriya inapita kukathira nkhondo dziko lonse la Israeli ndipo inapita mpaka ku Samariya ndipo inazinga mzindawo kwa zaka zitatu. Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya, mfumu ya ku Asiriya inalanda Samariya ndipo inatenga Aisraeli ndi kupita nawo ku Asiriya. Anakawakhazika ku Hala ndi Habori mʼmbali mwa mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi.

Israeli Apita ku Ukapolo chifukwa cha Tchimo

Zonsezi zinachitika chifukwa Aisraeli anachimwira Yehova Mulungu wawo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto pansi pa ulamuliro wa Farao mfumu ya Igupto. Iwo ankapembedza milungu ina, ndiponso ankatsatira miyambo ya anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika mʼdzikomo pamodzinso ndi miyambo yonse imene mafumu a Israeli anayambitsa. Ndipo Aisraeli ankachita zoyipa mwamseri kutsutsana ndi Yehova Mulungu wawo. Kuchokera ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa, mʼmizinda yawo yonse anamangamo malo opembedzeramo mafano. 10 Anayimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya mafano a Asera pa phiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. 11 Pa malo aliwonse opembedzera mafano, anthuwa ankafukiza lubani monga momwe ankachitira anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika. Iwo anachita zinthu zoyipa zomwe zinaputa mkwiyo wa Yehova. 12 Ndipo iwowo ankapembedza mafano ngakhale Yehova ananena kuti, “Musadzachite zimenezi.” 13 Yehova anachenjeza Israeli ndi Yuda kudzera mwa aneneri ake onse ndi alosi kuti, “Lekani mchitidwe wanu woyipawo. Mverani malamulo anga ndi malangizo anga potsatira zonse zolembedwa mʼmalamulo a Mose, zimene ndinalamulira makolo anu kuti azimvere, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.”

14 Koma anthuwa sanamvere ndipo anawumitsa khosi ngati momwe analili makolo awo, amene sanadalire Yehova Mulungu wawo. 15 Anakana malangizo ake ndi pangano anachita ndi makolo awo ndipo ananyoza zochenjeza za Yehova. Iwo anatsatira mafano achabechabe nasanduka achabechabe. Anthuwa anatsanzira mitundu ya anthu owazungulira ngakhale kuti Yehova anawalamula kuti, “Musamachite zomwe iwo amachita,” koma iwo anachita zomwe Yehova anawaletsa.

16 Iwowo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wawo, nadzipangira mafano awiri osungunula a ana angʼombe ndiponso fano la Asera, napembedza zonse zamlengalenga ndi kutumikira Baala. 17 Ndipo anadutsitsa mʼmoto ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo ankawombeza mawula, namachitanso zanyanga ndipo anadzipereka kuchita zoyipa pamaso pa Yehova namukwiyitsa.

18 Choncho Yehova anakwiya nawo kwambiri Aisraeli ndipo anawachotsa pamaso pake. Palibe amene anatsala kupatula fuko la Yuda lokha. 19 Yuda nayenso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wawo. Iwo ankatsatira machitidwe amene Israeli anayambitsa. 20 Motero Yehova anakana Aisraeli onse. Iye anawazunza nawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha mpaka Iye atawachotseratu pamaso pake.

21 Yehova atangʼamba Israeli kumuchotsa ku nyumba ya Davide, Aisraeliwo anasankha Yeroboamu mwana wa Nebati kukhala mfumu yawo. Yeroboamu ananyengerera Aisraeli kuti asatsatire Yehova ndipo anawachimwitsa tchimo lalikulu. 22 Aisraeli anakakamira machimo onse amene Yeroboamu anachita ndipo sanawasiye 23 mpaka pamene Yehova anawachotsa pamaso pake monga anawachenjezera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri. Choncho Aisraeli anachotsedwa mʼdziko lawo kupita ku ukapolo ku Asiriya ndipo ali komweko mpaka lero lino.

Anthu Achilendo Akhala mu Samariya

24 Mfumu ya ku Asiriya inabweretsa anthu a ku Babuloni, Kuta, Awa, Hamati ndi a ku Sefaravaimu kudzawakhazika mʼmizinda ya Samariya kulowa mʼmalo mwa Aisraeli. Iwo anatenga Samariya ndi kukhala mʼmizinda yake. 25 Iwo atayamba kukhala kumeneko, sanapembedze Yehova choncho Yehova anatumiza mikango pakati pawo ndipo inapha ena mwa iwo. 26 Tsono mfumu ya ku Asiriya inawuzidwa za nkhaniyi kuti, “Anthu amene munawatumiza ndi kuwakhazika mʼmizinda ya Samariya sakudziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna. Choncho Iye watumiza mikango pakati pawo imene ikuwapha chifukwa anthuwo sadziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna.”

27 Tsono mfumu ya ku Asiriya inalamula kuti, “Tengani wansembe mmodzi mwa amene munawagwira ukapolo, mupite naye kumeneko ndipo akakhale komweko nakaphunzitse anthu zimene Mulungu wa dzikolo amafuna.” 28 Choncho mmodzi mwa ansembe amene anawatenga ku Samariya anabwera kudzakhala ku Beteli ndipo ankaphunzitsa anthuwo kupembedza Yehova.

29 Koma mtundu uliwonse wa anthu unkapangabe mafano a milungu yawoyawo mʼmizinda yambiri imene anthuwo ankakhala, ndipo anayika milunguyo mʼnyumba za milungu zimene anthu a ku Samariya anamanga ku malo opembedzera mafano. 30 Anthu a ku Babuloni anapanga Sukoti-Benoti, anthu a ku Kuti anapanga Nerigali, ndipo anthu a ku Hamati anapanga Asima; 31 Aava anapanga Nibihazi ndi Taritaki, ndipo Asefaravaimu ankawotcha ana awo pa moto ngati nsembe kwa Adirameleki ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu. 32 Iwo ankapembedza Yehova, koma ankadzisankhira okha pakati pawo anthu wamba kuti akhale ansembe awo ku nyumba za milungu za ku malo opembedzera mafano. 33 Iwowo ankapembedza Yehova, komanso ankatumikira milungu yawo molingana ndi miyambo ya mitundu ya kumene ankachokera.

34 Mpaka lero lino iwo akupitirizabe kuchita zimene ankachita poyamba. Sapembedza Yehova kapenanso kutsata malangizo ake ndi malamulo ake, chiphunzitso chake monga mwa malamulo amene Yehova anawapereka kwa zidzukulu za Yakobo, amene anamutcha Israeli. 35 Pamene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli, Iye anawalamula kuti, “Musapembedze milungu ina kapena kuyigwadira iyo, kuyitumikira kapena kupereka nsembe kwa iyoyo. 36 Koma Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndiye amene muyenera kumupembedza. 37 Muyenera kusamalitsa nthawi zonse kusunga malangizo anga ndi malemba anga, chiphunzitso ndi malamulo amene anakulemberani. Musapembedze milungu ina. 38 Musayiwale pangano limene ndinapangana nanu ndipo musamapembedze milungu ina. 39 Mʼmalo mwake muzipembedza Yehova Mulungu wanu pakuti ndiye amene adzakulanditsani mʼdzanja la adani anu onse.”

40 Komabe iwo sanamvere ndipo anapitiriza kuchita zomwe ankachita kale. 41 Ngakhale anthuwo ankapembedza Yehova, ankatumikiranso mafano awo. Mpaka lero lino ana awo ndi zidzukulu zawo zikupitiriza kuchita zomwe ankachita makolo awo.

Tito 3

Kuchita Ntchito Zabwino

Uwakumbutse anthu kuti azigonjera oweruza ndi olamulira, aziwamvera ndi kukhala okonzeka kuchita chilichonse chabwino. Asamachitire chipongwe aliyense, asamakangane, akhale ofatsa ndipo oganizira ena, ndipo nthawi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.

Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake. Koma kukoma mtima ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu chitaonekera, Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa mowolowamanja kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu, kuti titalungamitsidwa mwachisomo chake, tikhale olowamʼmalo okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Mawuwa ndi okhulupirika ndipo ine ndikufuna kuti iwe utsindike zinthu izi, kuti amene akhulupirira Mulungu adzipereke kuchita ntchito zabwino. Zinthu izi ndi zabwino kwambiri ndi zopindulitsa kwa aliyense.

Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kuwerengawerenga mndandanda wa mibado ya makolo, mikangano ndi mitsutso pa za Malamulo, chifukwa zimenezi ndi zosapindulitsa ndi zopanda pake. 10 Munthu woyambitsa mipatuko umuchenjeze koyamba, ndiponso umuchenjeze kachiwiri. Kenaka umupewe. 11 Iwe udziwe kuti munthu wotero ngosokoneza ndi wochimwa, ndipo akudzitsutsa yekha.

Mawu Otsiriza

12 Ndikadzamutuma Artema kapena Tukiko kwanuko, udzayesetse kundipeza ku Nikapoli, chifukwa ndatsimikiza kukhala kumeneko pa nthawi yozizira. 13 Uyesetse chilichonse ungathe kuthandiza Zena katswiri wa malamulo ndi Apolo, kuti apitirize ulendo wawo, ndipo uwonetsetse asasowe kanthu. 14 Anthu athu aphunzire kudzipereka pogwira ntchito zabwino, nʼcholinga chakuti athandize zinthu zimene zikufunika msangamsanga. Ndipo asakhale moyo osapindulitsa.

15 Onse amene ali ndi ine akupereka moni. Upereke moni kwa amene amatikonda ife mʼchikhulupiriro.

Chisomo chikhale ndi inu nonse.

Hoseya 10

10 Israeli anali mpesa wotambalala;
    anabereka zipatso zambiri.
Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka,
    anawonjezera kumanga maguwa ansembe.
Pamene dziko lake linkatukuka,
    anakongoletsa miyala yake yopatulika.
Mtima wawo ndi wonyenga
    ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo.
Yehova adzagumula maguwa awo ansembe
    ndi kuwononga miyala yawo yopatulika.

Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu
    chifukwa sitinaope Yehova.
Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu,
    kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”
Mafumu amalonjeza zambiri,
    amalumbira zabodza
    pochita mapangano.
Kotero maweruzo amaphuka
    ngati zitsamba zakupha mʼmunda umene walimidwa.
Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha
    chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni.
Anthu ake adzalirira fanolo,
    chimodzimodzinso ansembe ake adamawo,
amene anakondwera ndi kukongola kwake,
    chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.
Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya
    ngati mphatso kwa mfumu yayikulu.
Efereimu adzachititsidwa manyazi
    chifukwa cha mafano ake amitengo.
Samariya ndi mfumu yake adzatengedwa kupita kutali
    ngati kanthambi koyenda pa madzi.
Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa.
    Ili ndiye tchimo la Israeli.
Minga ndi mitungwi zidzamera
    ndi kuphimba maguwa awo ansembe.
Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!”
    ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”

“Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya,
    ndipo wakhala uli pomwepo.
Kodi nkhondo sinagonjetse anthu
    ochita zoyipa ku Gibeya?
10 Pamene ndifunire, ndidzalanga anthuwo;
    mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa kudzalimbana nawo,
    kuwayika mʼndende chifukwa cha uchimo wawo waukulu.
11 Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwa
    amene amakonda kupuntha tirigu,
choncho Ine ndidzayika goli
    mʼkhosi lake lokongolalo.
Ndidzasenzetsa Efereimu goli,
    Yuda ayenera kulima,
    ndipo Yakobo ayenera kutipula.
12 Mufese nokha chilungamo
    ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika.
Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo;
    pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova,
mpaka Iye atabwera
    kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.
13 Koma inu munadzala zolakwa,
    mwakolola zoyipa;
    mwadya chipatso cha chinyengo.
Chifukwa mumadalira mphamvu zanu
    ndiponso ankhondo anu ochulukawo,
14 phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu anga
    kotero kuti malinga anu onse adzawonongeka,
monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo;
    pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.
15 Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli
    chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu.
Tsiku limeneli likadzafika,
    mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.

Masalimo 129-131

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

129 “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,”
    anene tsono Israeli;
“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,
    koma sanandipambane.
Anthu otipula analima pa msana panga
    ndipo anapangapo mizere yayitali:
Koma Yehova ndi wolungama;
    Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”

Onse amene amadana ndi Ziyoni
    abwezedwe pambuyo mwamanyazi.
Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba,
    umene umafota usanakule;
sungadzaze manja a owumweta
    kapena manja a omanga mitolo.
Odutsa pafupi asanene kuti,
    “Dalitso la Yehova lili pa inu;
    tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

130 Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
    Ambuye imvani mawu anga.
Makutu anu akhale tcheru kumva
    kupempha chifundo kwanga.

Inu Yehova, mukanamawerengera machimo,
    Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?
Koma kwa Inu kuli chikhululukiro;
    nʼchifukwa chake mumaopedwa.

Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera,
    ndipo ndimakhulupirira mawu ake.
Moyo wanga umayembekezera Ambuye,
    kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
    inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,

Yembekeza Yehova, iwe Israeli,
    pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika
    ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.
Iye mwini adzawombola Israeli
    ku machimo ake onse.

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Davide.

131 Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza,
    maso anga siwonyada;
sinditengeteka mtima
    ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.
Koma moyo wanga ndawutontholetsa
    ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa,
    moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa.

Yembekeza Yehova, iwe Israeli,
    kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.