Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 6

Nkhwangwa Iyandama pa madzi

Ana a aneneri anati kwa Elisa, “Taonani malo amene timakhala ndi inu atichepera kwambiri. Tiloleni tipite ku Yorodani kumene aliyense wa ife akadule mtengo umodzi, kuti timange malo woti tizikhalamo.”

Ndipo Elisa anati, “Pitani.”

Mmodzi wa iwo anati, “Chonde mulole kutsagana nawo atumiki anu.”

Elisa anayankha kuti, “Ndipita nanu.” Ndipo anapita nawo.

Anapita ku Yorodani nayamba kudula mitengo. Pamene wina ankadula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka nigwera mʼmadzi. Iye anafuwula kuti, “Mayo! Mbuye wanga! Popeza ndi yobwereka!”

Ndipo munthu wa Mulungu uja anafunsa, “Yagwera pati?” Pamene anamuonetsa malowo, Elisa anadula kamtengo nakaponya pamenepo, ndipo nkhwangwayo inayandama. Elisa anati, “Itenge.” Ndipo munthuyo anatambalitsa dzanja lake nayitenga.

Elisa Achititsa Khungu Ankhondo a ku Aramu

Tsono mfumu ya ku Aramu inali pa nkhondo ndi Israeli. Itakambirana ndi atsogoleri ake ankhondo inati, “Ndidzamanga misasa yanga pamalo akutiakuti.”

Munthu wa Mulungu anatumiza mawu kwa mfumu ya ku Israeli kuti “Musamale podutsa malo akuti, chifukwa Aaramu akupita kumeneko.” 10 Choncho mfumu ya ku Israeli inatuma anthu kumalo kumene munthu wa Mulunguyo ananena. Nthawi ndi nthawi Elisa ankachenjeza mfumu, kotero kuti ankakhala tcheru ku malo amenewo.

11 Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri mfumu ya ku Aramu. Mfumuyo inayitanitsa atsogoleri ake ankhondo ndipo inawafunsa kuti, “Kodi simungandiwuze munthu amene pakati pathu pano ali mbali ya mfumu ya ku Israeli?”

12 Mmodzi mwa atsogoleri a ankhondowo anati, “Palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu, inu mbuye wanga, koma Elisa mneneri amene ali ku Israeli amawuza mfumu ya ku Israeli mawu enieni amene inu mumayankhula ku chipinda kwanu.”

13 Choncho mfumu inalamula kuti, “Pitani, kafufuzeni kumene akukhala kuti ine nditume anthu kukamugwira.” Anthuwo anabweretsa mawu oti, “Taonani, Elisa ali ku Dotani.” 14 Ndipo mfumu inatumizako magaleta ndi akavalo ndiponso gulu lankhondo lamphamvu. Anapita usiku nakawuzungulira mzindawo.

15 Mtumiki wa munthu wa Mulungu atadzuka mmamawa ndi kutuluka panja, gulu la ankhondo pamodzi ndi akavalo ndi magaleta anali atazungulira mzindawo. Mtumikiyo anafunsa kuti, “Kalanga mbuye wanga, tidzachita chiyani?”

16 Mneneri anamuyankha kuti, “Usachite mantha. Amene ali mbali yathu ndi ambiri kupambana amene ali mbali yawo.”

17 Ndipo Elisa anapemphera kuti, “Inu Yehova tsekulani maso ake kuti aone.” Pamenepo Yehova anatsekula maso a mtumikiyo, ndipo anayangʼana naona kuti phiri lonse linali lodzaza ndi akavalo ndi magaleta a moto atazungulira Elisa.

18 Pamene adaniwo ankabwera kudzalimbana naye, Elisa anapemphera kwa Yehova kuti, “Achititseni khungu anthu awa.” Kotero Yehova anawachititsa khungu monga anapemphera Elisa.

19 Elisa anawawuza ankhondowo kuti, “Njira si imeneyi ndipo mzinda sumenewunso. Tsateni, ndipo ndidzakutengerani kwa munthu amene mukumufunayo.” Ndipo anawatengera ku Samariya.

20 Atalowa mu mzinda wa Samariya, Elisa anati, “Yehova tsekulani maso a anthu awa kuti aone.” Choncho Yehova anatsekula maso awo ndipo anangoona kuti ali mʼkati mwenimweni mwa Samariya.

21 Mfumu ya ku Israeli itawaona, inafunsa Elisa kuti, “Abambo anga, kodi ndiwaphe? Kodi ndiwaphe?”

22 Elisa anayankha kuti, “Musawaphe. Kodi mungaphe anthu amene munawagwira pogwiritsa ntchito lupanga ndi uta? Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa kenaka apite kwa mbuye wawo.” 23 Choncho anawakonzera mphwando lalikulu, ndipo atatsiriza kudya ndi kumwa, anawatumiza kwawo ndipo anabwerera kwa mbuye wawo. Kotero magulu a ankhondo a ku Aramu analeka kuthira nkhondo dziko la Israeli.

Njala mu Mzinda wa Samariya

24 Patapita nthawi, Beni-Hadadi mfumu ya Aramu anasonkhanitsa gulu lake lonse la ankhondo, napita kukazungulira mzinda wa Samariya. 25 Mu mzinda wa Samariya munali njala yoopsa. Ndipo taonani, Aaramu anazungulira mzindawu kwa nthawi yayitali kotero kuti mutu wa bulu ankawugulitsa ndalama za siliva 80, ndipo magalamu 200 a zitosi za nkhunda ankawagulitsa pa mtengo wa masekeli asanu.

26 Pamene mfumu inkayenda pa khoma la mzindawo, mayi wina anafuwulira mfumuyo kuti, “Thandizeni mbuye wanga mfumu!”

27 Mfumu inayankha kuti, “Ngati Yehova sakuthandiza iwe, ine thandizo lako ndingalipeze kuti? Kuchokera ku malo opunthira tirigu kodi? Kuchokera kumalo opsinyira mphesa kodi?” 28 Pamenepo mfumuyo inafunsa mayiyo kuti, “Kodi chakuvuta nʼchiyani?”

Iye anayankha kuti, “Mayi uyu anandiwuza kuti, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye lero, ndipo mawa tidzadya mwana wangayu.’ 29 Choncho tinaphika mwana wanga ndi kumudya. Tsiku lotsatira lakelo ine ndinati, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye,’ koma iye anabisa mwana wakeyo.”

30 Mfumu itamva mawu a mayiyo, inangʼamba mkanjo wake. Pamene inkayenda pa khoma, anthu anayangʼana, ndipo anaona zovala zamʼkati, pakuti anavala chiguduli. 31 Mfumuyo inati, “Mulungu andilange, andilange kwambiri ndikapanda kudula mutu wa Elisa mwana wa Safati lero!”

32 Tsono Elisa nʼkuti atakhala mʼnyumba mwake, ndipo akuluakulu anali naye limodzi. Mfumu inatuma munthu wina kuti imutsogolere, koma asanafike, Elisa anawuza akuluakuluwo kuti, “Kodi simukuona momwe wopha munthu uja watumizira munthu wina kuti adzadule mutu wanga? Taonani mthengayo akafika, mutseke chitseko ndipo muchigwiritsitse kuti asalowe. Kodi ndikumvawo pambuyo pake si mgugu wa mbuye wake?”

33 Elisa akuyankhulabe ndi anthuwo, taonani, wamthengayo anafika kwa iye. Ndipo mfumu inati, “Mavuto amenewa ndi ochokera kwa Yehova. Kodi nʼchifukwa chiyani ine ndiyenera kudikira thandizo lochokera kwa Yehova?”

1 Timoteyo 3

Zowayenereza Oyangʼanira ndi Atumiki

Mawu woona ndi awa: Ngati munthu akufunitsitsa atakhala woyangʼanira, ndiye kuti akufuna ntchito yabwino. Tsono woyangʼanira ayenera kukhala munthu wopanda chotsutsika nacho, mwamuna wa mkazi mmodzi yekha, woganiza bwino, wodziretsa, waulemu, wosamala bwino alendo, wodziwa kuphunzitsa. Asakhale chidakwa, asakhale wandewu, koma wofatsa, asakhale wokonda mikangano, kapena wokonda ndalama. Akhale wodziwa kusamala bwino banja lake ndi kulera ana ake bwino, kuti akhale omvera ndi aulemu weniweni. (Ngati munthu sadziwa kusamala banja lake lomwe, angathe bwanji kusamala mpingo wa Mulungu?) Asakhale wongotembenuka mtima kumene kuopa kuti angadzitukumule napezeka pa chilango monga Satana. Ayeneranso kukhala munthu wambiri yabwino ndi akunja, kuti anthu asamutonze nagwa mu msampha wa Satana.

Momwemonso atumiki, akhale anthu oyenera ulemu, woona mtima, osakhala okonda zoledzeretsa, osakonda kupeza zinthu mwachinyengo. Ayenera kugwiritsa mozama choonadi cha chikhulupiriro ndi kukhala ndi chikumbumtima chabwino. 10 Ayambe ayesedwa kaye, ndipo ngati palibe kanthu kowatsutsa, aloleni akhale atumiki.

11 Momwemonso, akazi akhale olemekezeka, osasinjirira koma oganiza bwino ndi odalirika pa chilichonse.

12 Mtumiki akhale wokhulupirika kwa mkazi wake ndipo ayenera kukhala wosamalira bwino ana ake ndi onse a pa khomo pake. 13 Iwo amene atumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndipo amakhala chitsimikizo chachikulu cha chikhulupiriro chawo mwa Khristu Yesu.

Cholinga cha Malangizo a Paulo

14 Ngakhale ndili ndi chiyembekezo choti ndifika komweko posachedwapa, ndikukulemberani malangizo awa. 15 Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi. 16 Mosakayikira, chinsinsi cha chikhulupiriro chathu chachikulu:

Khristu anaonekera ali ndi thupi la munthu,
    Mzimu anamuchitira umboni,
angelo anamuona,
    analalikidwa pakati pa mitundu yonse,
dziko lapansi linamukhulupirira,
    anatengedwa kupita kumwamba mwa ulemerero.

Danieli 10

Masomphenya a Danieli a Munthu

10 Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya.

Pa nthawi imeneyi, ine Danieli ndinalira kwa masabata atatu. Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu.

Pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, nditayima mʼmbali mwa mtsinje waukulu wa Tigirisi, ndinakweza maso ndipo ndinaona kuti pafupi ndi ine panali munthu wochokera ku Ufazi atavala zovala zosalala ndi lamba wa golide woyengeka bwino mʼchiwuno mwake. Thupi lake linali ngati mwala wonyezimira, nkhope yake ngati chiphaliwali, maso ake ngati muni wowala, manja ndi miyendo yake ngati mkuwa wowala, ndipo mawu ake ngati liwu la chikhamu cha anthu.

Ine Danieli ndinali ndekha pamene ndinaona masomphenyawa; anthu amene anali ndi ine sanawaone, koma anadzazidwa ndi mantha kotero kuti anathawa ndi kukabisala. Choncho ndinatsala ndekha, ndikuonetsetsa masomphenya a ulemererowa. Ndiye nkhope yanga inasinthika, ndinalefuka, ndipo ndinalibenso mphamvu. Kenaka ndinamva iye akuyankhula, ndipo pamene ndinkamvetsera, ndinagwa chafufumimba ndi kugona tulo tofa nato.

10 Dzanja linandikhudza ndi kundinyamula ndipo ndinachita ngati kuwerama pa mawondo manja atagwira pansi. 11 Iye anati, “Danieli, iwe wokondedwa kwambiri, imirira ndipo uganizire mosamala mawu ndiyankhule kwa iwe, popeza tsopano ndatumidwa kwa iwe.” Atanena izi kwa ine ndinayimirira monjenjemera.

12 Ndipo iye anapitiriza nati, “Usachite mantha Danieli. Kuyambira tsiku loyamba pamene unatsimikiza mtima kuti umvetse zinthuzi ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, pempho lako linamveka ndipo ndabwera kudzayankha mapemphero akowo. 13 Koma mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya ananditchingira pa masiku 21, kenaka Mikayeli, mmodzi mwa angelo akuluakulu anadza kudzandithandiza chifukwa ndinakhala komweko ndi mafumu a ku Peresiya. 14 Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.”

15 Pa nthawi yomwe ankanena izi kwa ine, ndinazolika nkhope yanga pansi kusowa chonena. 16 Kenaka wina wa maonekedwe ngati munthu anakhudza milomo yanga, ndipo ndinatsekula pakamwa panga ndi kuyamba kuyankhula. Ndinati kwa amene anayima patsogolo panga, “Ine ndasweka mtima chifukwa cha masomphenyawa mbuye wanga, ndipo ndalefuka. 17 Kodi ine mtumiki wamba wa mbuye wanga ndingathe bwanji kuyankhula ndi inu mbuye wanga? Mphamvu zanga zatha, ndipo ndikulephera kupuma.”

18 Kenaka wooneka ngati munthu uja anandikhudzanso ndipo anandipatsa mphamvu. 19 Iye anati, “Usachite mantha, munthu wokondedwa kwambiriwe. Mtendere ukhale ndi Iwe ndipo ukhale wolimba.”

Atayankhula nane, ndinalimbikitsidwa ndipo ndinati, “Yankhulani Mbuye wanga, popeza mwandipatsa mphamvu.”

20 Ndipo iye anati, “Kodi ukudziwa chifukwa chimene ndabwerera kwa iwe? Ndiyamba ndabwerera kukamenyana ndi mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya, ndipo ndikakanthana naye, kenaka mtsogoleri wa ufumu wa Grisi adzabwera. 21 Koma ndikuwuza zimene zalembedwa mʼbuku la zoona koma palibe wondithandiza kulimbana nawo kupatula Mikayeli, kalonga wako.”

Masalimo 119:1-24

Alefu

119 Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa,
    amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova.
Odala ndi amene amasunga malamulo ake,
    amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.
Sachita cholakwa chilichonse;
    amayenda mʼnjira zake.
Inu mwapereka malangizo
    ndipo ayenera kutsatidwa kwathunthu.
Aa! Ndikanakonda njira zanga zikanakhala zokhazikika
    pa kumvera zophunzitsa zanu!
Pamenepo ine sindikanachititsidwa manyazi,
    poganizira malamulo anu onse.
Ndidzakutamandani ndi mtima wolungama,
    pamene ndikuphunzira malamulo anu olungama.
Ndidzamvera zophunzitsa zanu;
    musanditaye kwathunthu.

Beti

Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?
    Akawasamala potsata mawu anu.
10 Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse;
    musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.
11 Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga
    kuti ndisakuchimwireni.
12 Mutamandike Inu Yehova;
    phunzitseni malamulo anu.
13 Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse
    amene amachokera pakamwa panu.
14 Ndimakondwera potsatira malamulo anu
    monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri.
15 Ndimalingalira malangizo anu
    ndipo ndimaganizira njira zanu.
16 Ndimakondwera ndi malamulo anu;
    sindidzayiwala konse mawu anu.

Gimeli

17 Chitirani zokoma mtumiki wanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo;
    kuti tsono ndisunge mawu anu.
18 Tsekulani maso anga kuti ndithe kuona
    zinthu zodabwitsa mʼmalamulo anu.
19 Ine ndine mlendo pa dziko lapansi;
    musandibisire malamulo anu.
20 Moyo wanga wafowoka polakalaka
    malamulo anu nthawi zonse.
21 Inu mumadzudzula onyada, otembereredwa,
    amene achoka pa malamulo anu.
22 Mundichotsere chitonzo ndi mnyozo
    pakuti ndimasunga malamulo anu.
23 Ngakhale mafumu akhale pamodzi kundinyoza,
    mtumiki wanu adzalingalirabe zophunzitsa zanu.
24 Malamulo anu amandikondweretsa;
    ndiwo amene amandilangiza.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.