Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 3

Solomoni Apempha Nzeru

Solomoni anachita ubale ndi Farao mfumu ya ku Igupto ndipo anakwatira mwana wake wamkazi. Mkaziyo anabwera naye mu Mzinda wa Davide mpaka anatsiriza kumanga nyumba yaufumu ndi Nyumba ya Yehova ndiponso khoma lozungulira Yerusalemu. Koma anthu ankaperekabe nsembe ku malo achipembedzo osiyanasiyana chifukwa chakuti mpaka pa nthawi imeneyo Dzina la Yehova anali asanalimangire nyumba. Solomoni anaonetsa chikondi chake pa Yehova poyenda motsatira malamulo a abambo ake Davide, kupatula kuti ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo osiyanasiyana achipembedzo.

Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe popeza kumeneko ndiye kunali malo oposa malo ofunika kwambiri pachipembedzo. Kumeneko Solomoni anapereka nsembe zopsereza 1,000 pa guwa lansembe. Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”

Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.

“Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi. Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga. Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”

10 Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi. 11 Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo, 12 Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako. 13 Kuwonjeza apo, ndidzakupatsa zimene sunazipemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti pa masiku onse a moyo wako sipadzakhala mfumu yofanana nawe. 14 Ndipo ngati udzayenda mʼnjira zanga ndi kumvera malamulo anga ndiponso malangizo anga monga abambo ako Davide anachitira, ndidzakupatsa moyo wautali.” 15 Kotero Solomoni anadzuka ndipo anazindikira kuti anali maloto.

Iye anabwerera ku Yerusalemu nakayimirira patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Ambuye ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Kenaka anakonzera phwando atumiki ake onse.

Kuweruza Kolungama

16 Nthawi ina amayi awiri adama anabwera kwa mfumu ndipo anayima pamaso pake. 17 Mmodzi mwa amayiwo anati, “Mbuye wanga, mayi uyu ndi ine timakhala nyumba imodzi. Ine ndinabala mwana tili limodzi ndi mnzangayu. 18 Tsiku lachitatu ine nditabala mwana, mnzangayunso anabereka mwana wake. Tinalipo awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe wina aliyense.

19 “Nthawi ya usiku mwana wa mnzangayu anafa chifukwa anamugonera. 20 Tsono iyeyu anadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga ku mimba kwanga pamene ine mdzakazi wanu ndinali mʼtulo. Anamuyika mwanayo ku mimba kwake ndi kuyika mwana wake wakufayo ku mimba kwanga. 21 Mmawa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga ndinapeza kuti ndi wakufa! Koma kutacha nditamuyangʼanitsitsa ndinaona kuti si mwana amene ine ndinabala.”

22 Koma mayi winayo anati, “Ayi! Mwana wamoyoyu ndi wanga, mwana wakufayu ndi wako.”

Koma mayi woyambayo analimbikira kuti. “Ayi! Mwana wakufayu ndi wako; wamoyoyu ndi wanga.” Motero akaziwa anatsutsana pamaso pa mfumu.

23 Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’ ”

24 Pamenepo mfumu inati, “Patseni lupanga.” Ndipo anabwera nalo lupanga kwa mfumu. 25 Tsono mfumu inagamula kuti, “Muduleni pakati mwana wamoyoyu ndipo wina mumupatse gawo limodzi, gawo linalo mumupatse winayo.”

26 Mayi amene mwana wake anali moyo anagwidwa ndi chisoni chifukwa cha mwana wakeyo ndipo anawuza mfumu kuti, “Chonde mbuye wanga, mupatseni mnzangayu mwana wamoyoyu! Musamuphe!”

Koma winayo anati, “Ayi, asandipatse ine kapena iwe. Muduleni pakati!”

27 Choncho mfumu inagamula kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mayi woyambayu. Musamuphe, iyeyu ndiye mayi wake wa mwanayu.”

28 Pamene Aisraeli onse anamva za chigamulo chimene mfumu inapereka, anaopa mfumuyo kwambiri, chifukwa anaona kuti mfumu inali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu zoweruzira mwachilungamo.

Aefeso 1

Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu.

Kulembera oyera mtima a ku Efeso, okhulupirika mwa Khristu Yesu:

Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.

Madalitso Auzimu mwa Khristu

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu. Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake, Iye anakonzeratu kuti ife titengedwe ngati ana mwa Yesu Khristu, molingana ndi kukonda kwake ndi chifuniro chake. Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda. Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu chimene anatipatsa mosawumira. Mwa nzeru zonse ndi chidziwitso, Iye watiwululira chifuniro chake chimene chinali chobisika, chimene anachikonzeratu mwa Khristu, molingana ndi kukoma mtima kwake. 10 Chimene anakonza kuti chichitike nʼchakuti, ikakwana nthawi yake asonkhanitsa pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za kumwamba ndi pa dziko lapansi.

11 Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake, 12 nʼcholinga chakuti, ife amene tinali oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu, tiyamike ulemerero wake. 13 Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza. 14 Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.

Kuyamika ndi Kupemphera

15 Choncho, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chanu mwa Ambuye Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse, 16 ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga. 17 Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni. 18 Ndimapempheranso kuti maso a mitima yanu atsekuke ndi cholinga choti mudziwe chiyembekezo chimene Iye anakuyitanirani, chuma cha ulemerero chomwe chili mwa anthu oyera mtima. 19 Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu zake zazikulu koposa zimene zili mwa ife amene timakhulupirira. Mphamvuyi ndi yofanana ndi mphamvu yoposa ija 20 imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba. 21 Anamukhazika pamwamba pa ulamuliro onse ndi mafumu, mphamvu ndi ufumu, ndiponso pamwamba pa dzina lililonse limene angalitchule, osati nthawi ino yokha komanso imene ikubwerayo. 22 Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo, 23 umene ndi thupi lake, chidzalo cha Iye amene adzaza chilichonse mu njira iliyonse.

Ezekieli 34

Abusa a Israeli

34 Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa? Mumadya chambiko, mumadziveka zovala zaubweya, ndi kupha nyama zonenepa, koma simusamalira nkhosazo. Simunalimbitse nkhosa zofowoka, kapena kuchiritsa zodwala, kapena kumanga mabala a nkhosa zopweteka. Simunabweze zosochera kapena kufunafuna zotayika. Munaziweta mozunza ndi mwankhanza. Kotero zinabalalika chifukwa zinalibe mʼbusa, ndipo pamene zinabalalika zinakhala chakudya cha zirombo zonse zakuthengo. Nkhosa zanga zinayendayenda mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zazitali. Zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo palibe amene anazilondola kapena kuzifunafuna.

“ ‘Choncho Inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. Pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Wamphamvuzonse, ndithu, nkhosa zanga zinajiwa ndi zirombo zakuthengo, zinasanduka chakudya cha zirombo chifukwa panalibe abusa. Abusa anga sanafunefune nkhosa zanga. Iwo ankangosamala za iwo okha mʼmalo mosamala nkhosa zanga. Chifukwa chake, inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. 10 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndayipidwa nanu, inu abusa. Ndidzakulandani nkhosa zanga ndipo simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito ya ubusa kuti musamangodzidyetsa nokha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwanu ndipo simudzazidyanso.

11 “ ‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira. 12 Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima. 13 Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuzisonkhanitsa kuchokera ku mayiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lawo. Ndidzaziwetera ku mapiri a Israeli, mʼmbali mwa mitsinje ndi kumalo kumene kumakhala anthu. 14 Ndidzaziwetera kumalo a msipu wabwino. Mapiri okwera a Israeli adzakhala malo azidyetserako. Kumeneko zidzapumula ku abusa abwino a msipu ndipo zizidzadyadi msipu wonenepetsa pa mapiri a Israeli. 15 Ine mwini wake ndidzaziweta nkhosa zanga ndi kuzilola kuti zipumule. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 16 Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo.

17 “ ‘Kunena za inu, nkhosa zanga, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zazimuna ndi mbuzi zazimuna. 18 Kodi sikukukwanirani kudya msipu wabwino kuti muzichita kuponderezanso msipu umene simunadyewo? Kodi simukhutira ndi kumwa madzi abwino kuti muzinka mudetsanso madzi otsalawo ndi mapazi anu? 19 Kodi nkhosa zanga zidye zimene mwazipondaponda ndi kumwa madzi amene mwawadetsa ndi mapazi anu?

20 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Taonani, Ine mwini wake ndidzaweruza pakati pa nkhosa zonenepa ndi nkhosa zowonda. 21 Popeza zofowoka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nʼkuzimwazira kutali, 22 tsono Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso. 23 Ndidzaziyikira mʼbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala. Adzakhala mʼbusa wawo. 24 Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wake ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu pakati pa nkhosazo. Ine Yehova ndayankhula.

25 “ ‘Ndidzapangana nazo pangano la mtendere. Ndidzachotsa mʼdzikomo zirombo zolusa. Choncho nkhosa zanga zidzakhala mu mtendere mu chipululu ngakhalenso mʼthengo. 26 Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso. 27 Mitengo ya mʼminda idzabereka zipatso zake, ndipo nthaka idzakhala ndi zokolola zake. Anthu adzakhala mwamtendere mʼdziko lawo. Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzathyola magoli awo ndi kuwapulumutsa kuchoka mʼmanja mwa amene anawagwira ukapolo. 28 Anthu amitundu ina sadzawafunkhanso ndipo sadzadyedwa ndi zirombo zakuthengo. Adzakhala mwamtendere ndipo palibe amene adzawaopseze. 29 Ndidzawapatsa zokolola zochuluka motero kuti sadzavutikanso ndi njala. Anthu a mitundu ina sadzawanyozanso. 30 Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wawo ndili nawo pamodzi, ndipo kuti iwo, Aisraeli, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 31 Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimazidyetsa. Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.’ ”

Masalimo 83-84

Nyimbo. Salimo la Asafu.

83 Inu Mulungu musakhale chete;
    musangoti phee, Mulungu musangoti duu.
Onani adani anu akuchita chiwawa,
    amene amadana nanu autsa mitu yawo.
Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu;
    Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.
Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu
    kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”

Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu;
    Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:
Matenti a Edomu ndi Aismaeli,
    Mowabu ndi Ahagiri,
Agebala, Aamoni ndi Aamaleki,
    Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.
Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo
    kupereka mphamvu kwa ana a Loti.
            Sela

Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani,
    monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.
10 Amene anawonongedwa ku Endori
    ndi kukhala ngati zinyalala.
11 Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu
    ana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna,
12 amene anati, “Tiyeni tilande dziko
    la msipu la Mulungu.”

13 Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga,
    ngati mankhusu owuluka ndi mphepo.
14 Monga moto umatentha nkhalango,
    kapena malawi a moto kuyatsa phiri,
15 kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho,
    ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe.
16 Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi
    kuti adzafunefune dzina lanu Yehova.

17 Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse;
    awonongeke mwa manyazi.
18 Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova,
    ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora.

84 Malo anu okhalamo ndi okomadi,
    Inu Yehova Wamphamvuzonse!
Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,
    kufuna mabwalo a Yehova;
Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira
    Mulungu wamoyo.

Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo,
    ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa,
    kumene amagonekako ana ake
pafupi ndi guwa lanu la nsembe,
    Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Odala amene amakhala mʼNyumba yanu;
    nthawi zonse amakutamandani.
            Sela

Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu,
    mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.
Pamene akudutsa chigwa cha Baka,
    amachisandutsa malo a akasupe;
    mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.
Iwo amanka nakulirakulira mphamvu
    mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.

Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse;
    mvereni Inu Mulungu wa Yakobo.
            Sela
Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu;
    yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.

10 Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi
    kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;
Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga
    kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;
    Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;
Iye sawamana zinthu zabwino
    iwo amene amayenda mwangwiro.

12 Inu Yehova Wamphamvuzonse,
    wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.