Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Samueli 19

19 Yowabu anawuzidwa kuti, “Mfumu ikulira maliro a Abisalomu.” Ndipo kwa asilikali onse chipambano cha tsiku limenelo chinasandulika maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake. Ankhondo analowa mu mzinda mwakachetechete tsiku limenelo ngati momwe amalowera anthu mwamanyazi chifukwa athawa ku nkhondo. Mfumu inaphimba nkhope yake ndipo inalira mofuwula, “Iwe mwana wanga Abisalomu! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”

Kenaka Yowabu analowa mʼnyumba ya mfumu nafika kwa mfumuyo ndipo anati, “Lero mwachititsa manyazi asilikali anu onse, amene apulumutsa moyo wanu ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu. Inu mumakonda amene amadana nanu ndipo mumadana ndi amene amakukondani. Inuyo mwaonetsa lero poyera kuti simusamala za atsogoleri anu a nkhondo ndi asilikali awo. Ine ndikuona kuti inu mukanakondwera ngati Abisalomu akanakhala ndi moyo lero, tonsefe titafa. Tsopano pitani mukawalimbikitse asilikali anu. Ine ndikulumbira mwa Yehova kuti ngati inu simupita palibe munthu amene adzatsale ali ndi inu polowa dzuwa. Ichi chidzakhala choyipa kwambiri kuposa zovuta zonse zimene zinakugwerani kuyambira muli mnyamata mpaka lero.”

Kotero mfumu inanyamuka ndipo inakhala pa mpando wake pa chipata. Pamene asilikali anawuzidwa kuti, “Mfumu yakhala pa chipata,” onse anabwera kwa iye.

Davide Abwerera ku Yerusalemu

Nthawi imeneyi nʼkuti Aisraeli atathawira ku nyumba zawo. Pakati pa mafuko onse a Israeli, anthu amakangana ndipo amati, “Mfumu inatipulumutsa mʼmanja mwa adani anthu. Iye ndi amene anatilanditsa mʼdzanja la Afilisti. Koma tsopano wathawa mʼdziko muno chifukwa cha Abisalomu. 10 Ndipo Abisalomu amene ife tinamudzoza kuti atilamulire wafa pa nkhondo. Tsono nʼchifukwa chiyani simukunena kanthu za kubweretsanso mfumu?”

11 Mfumu Davide inatumiza uthenga uwu kwa ansembe Zadoki ndi Abiatara, “Funsani akuluakulu a Yuda, ‘Nʼchifukwa chiyani inu mukukhala otsiriza kuyitana mfumu ku nyumba yake yaufumu, pakuti zimene zikunenedwa mu Israeli yense zamveka kwa mfumu ndi onse amene akukhala nayo. 12 Inu ndinu abale anga enieni, mafupa anga ndi mnofu wanga. Nʼchifukwa chiyani inuyo mukukhala otsiriza kubweretsa mfumu?’ 13 Ndipo munene kwa Amasa, ‘Kodi iwe si mʼbale wanga weniweni? Mulungu andilange, andilange kwambiri ngati kuyambira tsopano sukhala mtsogoleri wa ankhondo anga kulowa mʼmalo mwa Yowabu.’ ”

14 Davide anakopa mitima ya anthu onse a Yuda ndipo anthuwo anakhala ngati munthu mmodzi. Iwo anatumiza mawu kwa mfumu, “Bwererani inu ndi anthu anu onse.” 15 Kotero mfumu inabwerera ndipo inakafika mpaka ku Yorodani.

Tsono anthu a ku Yuda anabwera ku Giligala kuti akakumane ndi mfumu ndi kumuwolotsa Yorodani. 16 Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, anabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide. 17 Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a fuko la Benjamini pamodzi ndi Ziba, wantchito wa banja la Sauli ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndi antchito ake makumi awiri. Iwo anathamangira ku Yorodani kumene kunali mfumu. 18 Iwo anawoloka mtsinje kukatenga banja lonse la mfumu ndi kuchita zonse zimene mfumuyo imafuna.

Pamene Simei mwana wa Gera anawoloka Yorodani, anagwa pansi chafufumimba pamaso pa mfumu, 19 ndipo anati, “Mbuye wanga musaganizire za kulakwa kwanga. Musakumbukire zolakwa zimene mtumiki wanu anakuchitirani tsiku limene mbuye wanga mfumu mumachoka mu Yerusalemu. Mfumu musazikumbukirenso zimenezi. 20 Pakuti ine mtumiki wanu ndazindikira kuti ndachimwa. Koma lero ndabwera ngati woyamba wa nyumba ya Yosefe yonse kudzakumana nanu mbuye wanga mfumu.”

21 Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati, “Kodi Simei saphedwa chifukwa cha ichi? Iye anatukwana wodzozedwa wa Yehova.”

22 Davide anayankha kuti, “Kodi inu ana a Zeruya, ndikuchitireni chiyani? Lero lino iwe wakhala mdani wanga! Kodi wina aphedwe lero mu Israeli? Kodi ine sindikudziwa kuti lero ndine mfumu mu Israeli?” 23 Ndipo mfumu inati kwa Simei, “Iwe Simei suphedwa.” Ndipo mfumuyo inalonjeza ndi lumbiro.

24 Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli, nayenso anabwera kudzakumana ndi mfumu. Kuyambira tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere, iye sanasambe mapazi kaya kumeta ndevu kapena kuchapa zovala zake. 25 Pamene anafika kuchokera ku Yerusalemu kudzakumana ndi mfumu, mfumu inamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunapite nane Mefiboseti?”

26 Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga mfumu, pakuti ine wantchito wanu ndine wolumala. Ndinati, ‘Andikonzere chishalo cha bulu wanga ndipo ndidzakwera kuti ndipite ndi mfumu.’ Koma Ziba wantchito wanga anandilakwitsa. 27 Ndipo wayankhula zosinjirira za ine mtumiki wanu kwa inu mbuye wanga mfumu. Mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu ndipo chitani chimene chikukomerani. 28 Zidzukulu zonse za agogo anga sizinayenera chilichonse koma imfa kuchokera kwa inu mbuye wanga mfumu, koma inu munapereka malo kwa mtumiki wanu pakati pa amene amadya pa tebulo lanu. Tsono ine ndili ndi chiyaninso kuti ndipitirize kudandaula kwa mfumu?”

29 Mfumu inayankha kuti, “Uneneranji zambiri? Ine ndikulamula kuti iwe ndi Ziba mugawane minda.”

30 Mefiboseti anati kwa mfumu, “Muloleni atenge zonse, pakuti tsopano mbuye wanga mwafika kwanu mu mtendere.”

31 Barizilai Mgiliyadi anabweranso kuchokera ku Rogelimu kudzawoloka Yorodani ndi mfumu ndi kumuperekeza kuchokera kumeneko. 32 Tsono Barizilai anali wokalamba kwambiri, wa zaka makumi asanu ndi atatu. Iye ndi amene anapereka zinthu kwa mfumu pamene anali ku Mahanaimu pakuti anali wolemera kwambiri. 33 Mfumu inati kwa Barizilai, “Woloka nane ndipo ukakhale ndi ine mu Yerusalemu ndipo ineyo ndidzakusamalira.”

34 Barizilai anayankha mfumu kuti, “Kodi zakhala zaka zingati zoti ndikhale ndi moyo, kuti ndipite ku Yerusalemu ndi mfumu? 35 Ine tsopano ndili ndi zaka 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa? Kodi mtumiki wanu angathe kuzindikira kukoma kwa zimene akudya ndi kumwa? Kodi ndingathe kumva kuyimba kwa amuna ndi akazi? Nʼchifukwa chiyani wantchito wanu akakhale ngati katundu kwa mbuye wanga mfumu? 36 Koma ine mtumiki wanu ndingoyenda pangʼono kuti ndiwoloke Yorodani pamodzi ndi mfumu. Amfumu mungandipatsirenji mphotho yotere? 37 Muloleni, mtumiki wanu abwerere, kuti ndikafere kwathu pafupi ndi manda a abambo ndi amayi anga. Koma nayu mtumiki wanu Kimuhamu. Muloleni iye awoloke nanu mbuye wanga mfumu. Mumuchitire chilichonse chimene chikukomereni!”

38 Mfumu inati, “Kimuhamu adzawoloka ndi ine, ndipo ndidzamuchitira iye chilichonse chimene chidzakondweretsa iwe. Ndipo chilichonse chimene udzandipempha ine ndidzakuchitira.”

39 Kotero anthu onse anawoloka Yorodani ndipo kenaka mfumu inawoloka. Mfumu inapsompsona Barizilai ndi kumupatsa madalitso ndipo Barizilaiyo anabwerera kwawo.

40 Pamene mfumu inawolokera ku Giligala, Kimuhamu anawoloka naye. Ankhondo onse a Yuda ndi theka la ankhondo a Israeli onse anaperekeza mfumu.

41 Kenaka Aisraeli onse amabwera kwa mfumu nʼkumati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani abale athu, anthu a ku Ayuda, anakubani mfumu, nawoloka nanu Yorodani inu ndi banja lanu, pamodzi ndi anthu ake onse?”

42 Ayuda onse anayankha Aisraeli kuti, “Ife timachita zimenezi chifukwa mfumu ndi mʼbale wathu. Nʼchifukwa chiyani inu mwapsa mtima ndi zimenezi? Kodi ife tinadya chakudya chilichonse cha mfumu? Kodi chilipo chimene ife tatenga kukhala chathu?”

43 Aisraeli anayankha Ayuda kuti, “Ife ndi magawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo kuwonjezera apo, ife tili ndi zinthu zambiri mwa Davide kuposa inu. Tsono nʼchifukwa chiyani mukutichita chipongwe? Kodi ife si amene tinayamba kunena za kubweretsa mfumu yathu?”

Koma anthu a Yuda anayankha mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israeli.

2 Akorinto 12

Masomphenya a Paulo ndi Minga ya Mʼthupi Mwake

12 Ndiyenera kupitiriza kudzitamandira. Ngakhale palibe choti ndipindule, ndipitiriza kufotokoza za masomphenya ndi mavumbulutso ochokera kwa Ambuye. Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. Ndipo ndikumudziwa munthu ameneyu. Sindikudziwa ngati zinachitika mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. Munthuyu anatengedwa kupita ku paradizo. Ndipo anamva zinthu zosatheka kuneneka, zinthu zimene munthu saloledwa kunena. Ndidzatamanda za munthu ngati ameneyu, koma sindidzadzitamandira ine mwini kupatula za kufowoka kwanga. Ngakhale nditafuna kudzitamandira, sindingakhale chitsiru, chifukwa ndikunena zoona. Koma ndimapewa kuti pasapezeke munthu wondiganizira moposera chimene ndili chifukwa cha zimene ndimachita kapena kuyankhula, kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza. Katatu konse ndinapempha Ambuye kuti andichotsere. Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. 10 Tsono, chifukwa cha Khristu, ndimakondwera pamene ndili wofowoka, pamene akundinyoza, pamene ndikumva zowawa, ndi pamene akundizunza ndi kundisautsa. Pakuti pamene ndili wofowoka ndiye kuti ndili wamphamvu.

Paulo Akhudzidwa ndi Akorinto

11 Ndadzisandutsa wopusa, koma inu mwandichititsa zimenezi. Ndinu amene munayenera kundichitira umboni. Ngakhale kuti sindine kanthu, koma sindine wochepetsetsa kwa “atumwi apamwamba” aja. 12 Ndinapirira pokuonetserani zizindikiro za mtumwi weniweni, pochita pakati panu zizindikiro, zodabwitsa ndi ntchito zamphamvu. 13 Kodi inu munaoneka ochepa motani ku mipingo ina, kupatula kuti sindinali cholemetsa kwa inu? Mundikhululukire cholakwa chimenechi!

14 Ndakonzeka tsopano kudzakuyenderani kachitatu, ndipo sindidzakhala cholemetsa kwa inu chifukwa ndikungofuna inuyo osati zinthu zanu. Pakuti ana sasamalira makolo koma makolo ndiwo asamalira ana. 15 Motero ndidzakondwera kukupatsani zanga zonse zimene ndili nazo ndi kudziperekanso ine mwini chifukwa cha inu. Kodi ine ndikamakukondani kwambiri chotere, inuyo mudzandikonda pangʼono? 16 Ena mwa inu amavomereza kuti sindinali cholemetsa. Komabe ena amaganiza kuti ndine wochenjera, ndipo ndinakuchenjererani. 17 Kodi ndinakudyerani masuku pamutu kudzera mwa wina aliyense amene ndinamutumiza kwa inu? 18 Ndinamupempha Tito kuti abwere kwanuko ndipo ndinamutumiza pamodzi ndi mʼbale wathu. Kodi kapena Tito anakudyerani masuku pamutu? Kodi iye ndi ine sitinachite zinthu mofanana ndi Mzimu mmodzi yemweyo?

19 Kodi mukuyesa kuti nthawi yonseyi takhala tikudzitchinjiriza tokha? Takhala tikuyankhula pamaso pa Mulungu monga anthu amene ali mwa Khristu; ndipo abwenzi okondedwa, chilichonse chimene timachita ndi chofuna kukulimbikitsani. 20 Pakuti ndikuona kuti pamene ndibwera sindidzakupezani monga mmene ndikufunira kuti muzikhalira, ndipo simungadzandione monga mmene mukufunira kundionera. Ndikuopa kuti pangadzakhale mkangano, nsanje, kupserana mitima, kugawikana, ugogodi, miseche, kudzitukumula ndi chisokonezo. 21 Ndikuopa kuti pamene ndidzabwerenso, Mulungu adzandichepetsa pamaso panu, ndipo ndidzamva chisoni ndi ambiri amene anachimwa kale ndipo sanalape zonyansa, zachigololo ndi zilakolako zoyipa zimene anachita.

Ezekieli 26

Za Chilango cha Turo

26 Pa chaka cha khumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’ Nʼchifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulangani, inu anthu a ku Turo. Ndidzakuyitanirani anthu a mitundu ina kuti adzakulangeni monga momwe mafunde amawombera pa Nyanja. Anthuwo adzawononga makoma a Turo ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake ndipo ndidzamusandutsa thanthwe losalala. Udzakhala poyanikapo makoka pakati pa nyanja. Ine Ambuye Yehova ndayankhula zimenezo. Udzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina. Anthu okhala ku mtunda adzasakazidwa ndi lupanga. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Iwe Turo, ndidzakubweretsera Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto pamodzi ndi akavalo ndiponso magaleta, anthu okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo. Anthu okhala ku mtunda adzawapha ndi lupanga. Adzapanga mitumbira yankhondo ndi kukukwezera zishango kuti alimbane nawe. Adzagwetsa makoma ako ndi zida zogumulira khoma ndi kugwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake. 10 Akavalo ake adzakhala ochuluka kwambiri kotero kuti adzakukwirira ndi fumbi lawo. Makoma ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo, ngolo ndi magaleta pamene iye adzalowa pa zipata monga mmene amalowera mu mzinda umene makoma ake agwetsedwa. 11 Akavalo ake adzapondaponda mʼmisewu yako yonse ndi ziboda zawo. Adzapha anthu ako ndi lupanga. Mizati yako yolimba idzagwetsedwa. 12 Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja. 13 Choncho ndidzathetsa phokoso la nyimbo zanu, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso. 14 Ndidzakusandutsa thanthwe losalala, ndipo udzakhala malo woyanikapo makoka a nsomba. Sudzamangidwanso, pakuti Ine Yehova ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.

15 “Ine Ambuye Yehova ndikukuwuza, iwe mzinda wa Turo, kuti zilumba zidzagwedezeka pakumva za kugwa kwako ndiponso poona anthu opweteka akubuwula ndipo anthu akuphedwa pakati pako. 16 Pamenepo mafumu a mʼmbali mwa nyanja adzatsika pa mipando yawo yaufumu. Adzayika pambali mikanjo yawo ndi kuvala zovala zawo zamakaka. Adzachita mantha ndipo adzakhala pansi akunjenjemera kosalekeza. Adzathedwa nzeru poona zimene zakugwera. 17 Pamenepo adzayimba nyimbo yokudandaula ndipo adzati kwa iwe:

“ ‘Nʼkuchita kuwonongeka chotere, iwe mzinda wotchuka,
    wodzaza ndi anthu a ku nyanja!
Unali wamphamvu pa nyanja,
    iwe ndi nzika zako;
unkaopseza anthu onse amene
    ankakhala kumeneko.
18 Tsopano mayiko a mʼmbali mwa nyanja akunjenjemera
    chifukwa cha kugwa kwako;
okhala pa zilumba nawonso agwidwa ndi mantha aakulu
    chifukwa cha kugwa kwako.’

19 “Mawu a Ine Ambuye Yehova ndi awa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mizinda imene anthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama a mʼnyanja, madzi amphamvu woti akumize. 20 Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ine ndidzakusunga ku dzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene anafa kale motero sudzabwererako kukhala pakati pa anthu amoyo. 21 Ine ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna, koma sudzapezekanso, akutero Ambuye Yehova.”

Masalimo 74

Ndakatulo ya Asafu.

74 Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu?
    Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?
Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale,
    fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola,
    phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala.
Tembenuzani mapazi kuloza ku mabwinja awa amuyaya
    chiwonongeko ichi chonse mdani wabweretsa pa malo opatulika.

Adani anu anabangula pa malo pamene Inu munkakumana nafe;
    anayimika mbendera zawo monga zizindikiro zachigonjetso.
Iwo anachita ngati anthu oti anyamula mbendera zawo
    kuti adule mitengo mʼnkhalango.
Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo
    zonse zimene tinapachika.
Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi;
    anadetsa malo okhalamo dzina lanu.
Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.”
    Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo.
Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa;
    palibe aneneri amene atsala
    ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.

10 Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu?
    Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya?
11 Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja?
    Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!

12 Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale;
    Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi.
13 Ndinu amene munagawa nyanja ndi mphamvu yanu;
    munathyola mitu ya zirombo za mʼmadzi.
14 Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani
    ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu.
15 Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje,
    munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse.
16 Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso;
    Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi.
17 Ndinu amene munakhazikitsa malire onse a dziko lapansi;
    munakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.

18 Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova,
    momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.
19 Musapereke moyo wa nkhunda yanu ku zirombo zakuthengo;
    nthawi zonse musayiwale miyoyo ya anthu anu osautsidwa.
20 Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko
    asanduka mochitira zachiwawa zochuluka.
21 Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi;
    osauka ndi osowa atamande dzina lanu.

22 Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu;
    kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse.
23 Musalekerere phokoso la otsutsana nanu,
    chiwawa cha adani anu, chimene chikumveka kosalekeza.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.