Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Samueli 15

Abisalomu Akonzekera Zowukira

15 Patapita nthawi, Abisalomu anadzipezera galeta ndi akavalo pamodzi ndi amuna makumi asanu amene amathamanga patsogolo pake. Iye amadzuka mmamawa ndi kuyima pa njira yopita ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi zodandaula zopita nazo kwa mfumu kuti akaweruze, Abisalomu amamuyitana iye ndi kumufunsa kuti, “Kodi ukuchokera ku limodzi mwa mafuko a Israeli?” Kenaka Abisalomu amanena kwa iye kuti, “Taona, madandawulo ako ndi abwino ndi oyenera, koma palibe woyimira mfumu woti akumvere.” Ndipo Abisalomu amawonjezera kunena kuti, “Ine ndikanangosankhidwa kukhala woweruza mʼdziko muno bwenzi munthu aliyense amene ali ndi madandawulo kapena milandu akubwera kwa ine ndipo ndikanaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.”

Ndipo nthawi zonse amati munthu akasendera pafupi ndi kumugwandira, Abisalomu amatambalitsa dzanja lake, kumuyimiritsa munthuyo ndi kupsompsona. Abisalomu amachitira izi Aisraeli onse amene amabwera kwa mfumu kuti adzaweruzidwe ndipo Abisalomuyo anagwira mtima anthu a mu Israeli.

Patapita zaka zinayi Abisalomu anati kwa mfumu, “Loleni ndipite ku Hebroni kuti ndikakwaniritse lonjezo limene ndinachita kwa Yehova. Pamene mtumiki wanu amakhala ku Gesuri ku Aramu, anachita lonjezo ili: ‘Ngati Yehova adzandibweretsadi ku Yerusalemu, ndidzapembedza Yehovayo mu Hebroni.’ ”

Mfumu inati kwa iye, “Pita mu mtendere” Kotero iye anapita ku Hebroni.

10 Ndipo Abisalomu anatuma amithenga ake mwamseri kwa mafuko onse a Israeli kukanena kuti, “Mukangomva kulira kwa malipenga pamenepo munene kuti, ‘Abisalomu ndiye mfumu mu Hebroni.’ ” 11 Anthu 200 ochokera mu Yerusalemu anapita naye Abisalomu. Iwo anayitanidwa monga alendo ndipo anapita osadziwa chilichonse pa nkhaniyi. 12 Pamene Abisalomu amapereka nsembe, iye anayitanitsanso Ahitofele Mgiloni, mlangizi wa Davide, wa ku Gilo, kotero kuwukiraku kunakula kwambiri, ndipo anthu otsatira Abisalomu anapitirira kuchuluka.

Davide Athawa Abisalomu

13 Munthu wina anabweretsa uthenga ndi kudzamuwuza Davide kuti, “Mitima ya Aisraeli onse ili pa Abisalomu.”

14 Ndipo Davide anati kwa akuluakulu ake amene anali mu Yerusalemu. “Bwerani! Tiyeni tithawe, mwina palibe adzapulumuke kwa Abisalomu. Tiyeni tichoke msanga, mwina iye adzabwera msanga ndi kutipitirira, nʼkuwononga ife ndi mzinda wathu ndi lupanga.”

15 Akuluakulu a mfumu anamuyankha kuti, “Antchito anu ndi okonzeka kuchita chilichonse chimene mbuye wathu mfumu mukufuna kuchita.”

16 Mfumu inanyamuka pamodzi ndi banja lake lonse. Koma iye anasiya azikazi khumi kuti azisamalira nyumba yaufumu. 17 Kotero mfumu inanyamuka pamodzi ndi anthu onse oyitsatira, ndipo anayima pamalo pena chapatalipo. 18 Ankhondo ake onse anayamba kuyenda pamaso pa Davide, ndipo Akereti ndi Apeleti, pamodzinso ndi Agiti okwanira 600 amene anamutsata kuchokera ku Gati, nawonso anayenda pamaso pake.

19 Mfumu inati kwa Itai Mgiti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ukupita ndi ife? Bwerera ndipo ukakhale ndi mfumu Abisalomu. Iwe ndiwe mlendo munthu wothawa kwawo. 20 Wangobwera dzulo lomweli, lero ndikutenge kuti uziyendayenda ndi ife, pamene ine sindikudziwa kumene ndikupita? Bwerera, ndipo tenga abale ako. Chifundo ndi kukhulupirika zikhale nawe.”

21 Koma Itai anayankha mfumu kuti, “Pali Yehova wamoyo, kulikonse kumene mbuye wanga mfumu mudzakhala, kaya ndi moyo kapena imfa, mtumiki wanu adzakhala komweko.”

22 Davide anati kwa Itai, “Tiye pita nafe” Kotero Itai Mgiti anayenda pamodzi ndi anthu ake ndi mabanja amene anali naye.

23 Anthu onse a madera ozungulira analira mofuwula pamene anthu onsewo amadutsa. Mfumunso inawoloka chigwa cha Kidroni, ndipo anthu onse anayenda kulowera ku chipululu.

24 Zadoki anali nawonso, ndipo Alevi onse amene anali naye ananyamula Bokosi la Chipangano la Mulungu. Iwo anayika pansi Bokosi la Mulungulo ndipo Abiatara ankapereka nsembe mpaka pamene anthu onse anamaliza kutuluka mu mzinda.

25 Kenaka mfumu inati kwa Zadoki, “Tenga Bokosi la Mulungu ubwerere nalo mu mzinda. Ngati ndidzapeza chifundo pamaso pa Yehova, adzandibweretsa kuti ndilionenso ndi malo ake okhalamo. 26 Koma iye anati, ‘Akapanda kukondwera nane,’ chabwino, andichite chimene chimukomere.”

27 Mfumu inatinso kwa wansembe Zadoki, “Kodi siwe mlosi? Bwerera mu mzinda mwamtendere pamodzi ndi mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiatara. Iwe ndi Abiatara tengani ana anu awiri. 28 Ine ndidzadikira powolokera Yorodani ku chipululu mpaka nditalandira mawu ochokera kwa iwe ondiwuza mmene zilili zinthu.” 29 Kotero Zadoki ndi Abiatara ananyamula Bokosi la Mulungu lija nabwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo anakakhala kumeneko.

30 Koma Davide anapitirira ndi kukakwera phiri la Olivi akupita nalira. Anafunda kumutu koma sanavale nsapato. Anthu onse amene anali naye anafundanso kumutu, ndipo nawonso amalira pamene amapita. 31 Tsono Davide anamva kuti, “Ahitofele ali pakati pa anthu owukira pamodzi ndi Abisalomu.” Choncho Davide anapemphera, “Inu Yehova, musandutse uphungu wa Ahitofele ukhale uchitsiru.”

32 Davide atafika pamwamba pa phiri pomwe anthu ankapembedzerapo Mulungu, Husai Mwariki anadzakumana naye atangʼamba mkanjo wake ndi kudzithira fumbi kumutu. 33 Davide anati kwa iye, “Ngati iwe upite ndi ine, udzakhala chondilemetsa. 34 Koma ngati ubwerera ku mzinda ndi kukanena kwa Abisalomu kuti, ‘Inu mfumu ine ndidzakhala wantchito wanu.’ Mʼmbuyomu ndinali wantchito wa abambo anu koma tsopano ndidzakhala wantchito wanu. Ukatero udzandithandiza kulepheretsa malangizo a Ahitofele. 35 Kodi ansembe, Zadoki ndi Abiatara, sakukhala nawe kumeneko? Ukawawuze zonse zimene umamva mʼnyumba yaufumu. 36 Ana awo awiri, Ahimaazi wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiatara ali nawo pamodzi, uzikawatuma kwa ine ndi china chilichonse chimene ukamve.”

37 Ndipo Husai bwenzi la Davide anafika ku Yerusalemu pamene Abisalomu amalowa mu mzinda.

2 Akorinto 8

Kulimbikitsa Zopereka

Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu. Choncho tinamupempha Tito kuti atsirize poti nʼkuti atayamba kale ntchito yachisomoyi pakati panu. Popeza pa zinthu zonse munachita bwino, monga pachikhulupiriro, poyankhula, pachidziwitso, pakhama lambiri ndi pachikondi chanu pa ife, onetsetsani kuti muchitenso bwino pachisomo ichi chopereka.

Sindikukulamulirani, koma ndikufuna kuona ngati chikondi chanu nʼchoona pofananitsa ndi changu cha anthu ena. Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemera, koma chifukwa cha inuyo anasanduka wosauka, kuti umphawi wakewo, inuyo mulemere.

10 Ndipo nawa malangizo anga pa zoyenera inu kuchita pa nkhaniyi. Chaka chatha munali oyamba, osati ongofuna kupereka kokha komanso okhala ndi mtima ofuna kupereka. 11 Tsopano tsirizani ntchitoyi, ndipo changu chanu chofunitsitsa kugwira ntchitoyi ndi kuyitsiriza chichitike molingana ndi zimene muli nazo. 12 Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe.

13 Cholinga chathu sikuti tipeputse ena pamene inuyo mukuvutika, koma kuti pakhale kufanana. 14 Zambiri zimene muli nazo pakati panu muthandize nazo osowa, kuti nawonso akadzakhala nazo zambiri adzakuthandizeni pa zosowa zanu. Cholinga nʼkuchita mofanana, 15 monga kwalembedwa kuti, “Iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere.”

Tito Atumidwa ku Korinto

16 Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa Tito changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu. 17 Pakuti Tito sanangovomera kokha pempho lathu, koma yekha anafunitsitsa kwambiri kubwera kwa inu mwa iye yekha. 18 Ndipo tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale amene mipingo yonse yamuyamikira chifukwa cha utumiki wake wa Uthenga Wabwino. 19 Chowonjezera china nʼchakuti anasankhidwa ndi mipingo kuti atiperekeze pamene ife tikukapereka zopereka, zimene tikuchita pofuna kupereka ulemu kwa Ambuye mwini ndi kuonetsa kufunitsitsa kwathu pothandiza. 20 Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi. 21 Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu.

22 Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi wachangu ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu. 23 Kunena za Tito, ndiye mnzanga ndi wogwira naye ntchito pakati panu. Kunena za abale athu, ndiwo oyimirira mipingo ndi olemekezetsa Khristu. 24 Choncho anthu amenewa atsimikizireni za chikondi chanu ndipo adziwe chifukwa chimene ife timakunyadirani, kuti mipingo yonse iwone chimenechi.

Ezekieli 22

Machimo a Yerusalemu

22 Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza mzinda uwo wa anthu akupha anzawo? Tsono uwudzudzule chifukwa cha machitidwe ake onse onyansa ndipo unene kuti, ‘Ambuye akuti: Iwe mzinda umene wadzigwetsa wekha mʼtsoka pa kukhetsa magazi pakati pako ndi kudziyipitsa popanga mafano, wapezekatu wolakwa chifukwa cha magazi amene wakhetsa, ndipo wadziyipitsa chifukwa cha mafano amene wapanga. Choncho wachepetsa masiku ako, ndipo zaka zako zafika kumapeto. Nʼchifukwa chake ndalola kuti anthu a mitundu ina akunyoze ndiponso kuti anthu a mayiko onse akuseke. Mayiko amene ali pafupi ndi mayiko omwe ali kutali adzakunyoza, iwe mzinda wa mbiri yoyipa, wodzaza ndi chiwawa.

“ ‘Taona momwe aliyense wa atsogoleri a Israeli amagwiritsira mphamvu zake kupha anthu. Mu mzindamo anthu amanyoza abambo ndi amayi awo. Iwo amapondereza alendo ndi kuzunza ana amasiye ndi akazi amasiye. Wanyoza zinthu zanga zopatulika ndi kuyipitsa Masabata anga. Mwa iwe muli anthu onenera anzawo zabodza kuti aphedwe. Mwa iwe mulinso amene amadyera zansembe pa mapiri a chipembedzo. Enanso amachita zonyansa. 10 Mwa iwe muli ena ogonana ndi akazi a abambo awo, muli enanso amene amavuta akazi pamene ali woyipitsidwa ndi msambo. 11 Ena amachita chigololo ndi akazi a anzawo, ndipo ena, mopanda manyazi, amayipitsa mkazi wa mwana wawo. Palinso ena amene amayipitsa alongo awo, ana aakazi a abambo awo. 12 Mwa iwe muli anthu amene amalandira ziphuphu kuti aphe anzawo; ena amachita katapira ndi kupeza phindu loposera muyeso; enanso amapeza phindu mwachinyengo poopseza anzawo. Ndipo mwandiyiwala Ine, akutero Ambuye Yehova.

13 “ ‘Koma Ine ndachita kuwomba mʼmanja kuti phuu nʼkudabwa chifukwa cha phindu lachinyengo limene mwapeza ndiponso chifukwa cha kuphana kumene kumachitika pakati panu. 14 Kodi mtima wako udzakhala wolimbabe kapena manja ako adzakhalabe amphamvu ndikadzatsiriza kukulanga iwe? Ine Yehova ndayankhula, ndipo ndidzazichitadi. 15 Ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukumwazirani ku mayiko onse. Umu ndi mmene ndidzachotsere zoyipa zako. 16 Udzanyozedwa pamaso pa anthu a mitundu ina. Pambuyo pake udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

17 Yehova anandiyankhula nati: 18 “Iwe mwana wa munthu, Aisraeli asanduka chinthu cha chabechabe kwa Ine. Onse ali ngati mkuwa, chitini, chitsulo ndi mtovu zotsala mʼngʼanjo atayeretsa siliva. 19 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Pakuti nonse mwasanduka chinthu cha chabechabe, Ine ndidzakusonkhanitsani mu Yerusalemu. 20 Monga momwe anthu amasonkhanitsira siliva, mkuwa, chitsulo, mtovu ndi chitini mʼngʼanjo ndi kusonkhetsa moto kuti azisungunule, motero Inenso ndidzakusonkhanitsani ndili wokwiya ndi waukali, ndipo ndidzakuyikani mʼkati mwa mzinda, ndikukusungunurani. 21 Ndidzakusonkhanitsani mu mzindamo ndi kukoleza moto wa mkwiyo wanga, ndipo inu mudzasungunuka mu mzindamo. 22 Monga siliva amasungunulidwa mʼngʼanjo, kotero inunso mudzasungunuka mʼkati mwa mzinda ndipo Inu mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakukwiyirani.’ ”

23 Yehova anandiyankhulanso nati, 24 “Iwe mwana wa munthu, uza dziko la Israeli kuti, ‘Iwe ndiwe dziko losayeretsedwa, ndiponso losavumbidwa ndi mvula chifukwa cha mkwiyo wanga.’ 25 Atsogoleri ake mu mzindamo ali ngati mkango wobangula pogwira nyama. Apha anthu, alanda chuma ndi zinthu za mtengowapatali, ndiponso asandutsa amayi ambiri kukhala amasiye. 26 Ansembe ake amaphwanya lamulo langa ndi kuyipitsa zinthu zanga zopatulika. Sasiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba. Saphunzitsa anthu kusiyana kwa zinthu zoyenera pa chipembedzo ndi zinthu zosayenera. Sasamalira za kusunga masabata anga. Motero Ine ndimanyozedwa pakati pawo. 27 Atsogoleri ake ali ngati mimbulu yokhadzula nyama; amakhetsa magazi ndi kupha anthu kuti apeze phindu loyipa. 28 Aneneri ake amabisa zonsezi monga muja amachitira anthu popaka njereza. Amazimphimba ndi zabodza zimene aona mʼmasomphenya awo ndi zonama za mʼmawula awo. Iwo amati, ‘Ambuye Yehova akuti,’ pamene Ine Yehova sindinayankhule. 29 Anthu a mʼdzikomo amasautsa anzawo ndi kulanda anthu osowa. Amazunza anthu osauka ndi amphawi. Amavutitsa alendo posawachitira zinthu mwachilungamo.

30 “Ndinafunafuna munthu pakati pawo woti amange linga, woti ayimirire dziko pamaso panga kundipepesa kuti ndisaliwononge, koma sindinamupeze. 31 Nʼchifukwa chake ndawakwiyira kwambiri. Ndawawonongeratu ndi mkwiyo wanga woyaka ngati moto. Ndawalanga molingana ndi zimene anachita. Akutero Ambuye Yehova.”

Masalimo 69

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.”

69 Pulumutseni Inu Mulungu,
    pakuti madzi afika mʼkhosi
Ine ndikumira mʼthope lozama
    mʼmene mulibe popondapo.
Ndalowa mʼmadzi ozama;
    mafunde andimiza.
Ndafowoka ndikupempha chithandizo;
    kummero kwanga kwawuma gwaa,
mʼmaso mwanga mwada
    kuyembekezera Mulungu wanga.
Iwo amene amadana nane popanda chifukwa
    ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga;
ambiri ndi adani anga popanda chifukwa,
    iwo amene akufunafuna kundiwononga.
Ndikukakamizidwa kubwezera
    zomwe sindinabe.

Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu,
    kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.

Iwo amene amadalira Inu
    asanyozedwe chifukwa cha ine,
    Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
Iwo amene amafunafuna Inu
    asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine,
    Inu Mulungu wa Israeli.
Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu,
    ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga.
Ndine mlendo kwa abale anga,
    munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga;
pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa
    ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.
10 Pamene ndikulira ndi kusala kudya,
    ndiyenera kupirira kunyozedwa;
11 pomwe ndavala chiguduli,
    anthu amandiseweretsa.
12 Iwo amene amakhala pa chipata amandinena,
    ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa.

13 Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye,
    pa nthawi yanu yondikomera mtima;
mwa chikondi chanu chachikulu
    Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.
14 Mundilanditse kuchoka mʼmatope,
    musalole kuti ndimire,
pulumutseni ine kwa iwo
    amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama.
15 Musalole kuti chigumula chindimeze,
    kuya kusandimeze
    ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza.
16 Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu;
    mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.
17 Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu,
    ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.
18 Bwerani pafupi ndi kundilanditsa;
    ndiwomboleni chifukwa cha adani anga.

19 Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera,
    kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.
20 Mnyozo waswa mtima wanga
    ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse;
ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni,
    koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.
21 Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa
    ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.

22 Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha;
    chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe.
23 Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso
    ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale.
24 Khuthulirani ukali wanu pa iwo;
    mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.
25 Malo awo akhale wopanda anthu
    pasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo.
26 Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza
    ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.
27 Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo,
    musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.
28 Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo
    ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.

29 Ndikumva zowawa ndi kuzunzika;
    lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze.

30 Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo,
    ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.
31 Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe,
    kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.
32 Wosauka adzaona ndipo adzasangalala,
    Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!
33 Yehova amamvera anthu osowa
    ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.

34 Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye,
    nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,
35 pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni
    ndi kumanganso mizinda ya Yuda,
anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;
36     ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo,
    ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.