Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 29-30

Afilisti Akana Davide

29 Afilisti anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, ndipo Israeli anamanga misasa yawo pa chitsime cha Yezireeli. Pamene atsogoleri a Afilisti ankatsogolera magulu awo ankhondo a miyandamiyanda, Davide ndi ankhondo ake ankayenda pambuyo pamodzi ndi Akisi. Tsono atsogoleri a Afilisti aja anafunsa kuti, “Kodi Ahebri awa akufuna chiyani?”

Akisi anayankha kuti, “Uyu ndi Davide, mtumiki wa Sauli mfumu ya Israeli. Iye wakhala ndi ine kwa masiku ndithu, kapena titi zaka ndipo kuyambira tsiku limene anachoka kwa Sauli mpaka lero, ine sindinapeze cholakwa mwa iye.”

Koma atsogoleri a ankhondo a Afilisti anamukwiyira Akisi kwambiri ndipo anati, “Mubweze munthuyu kuti abwerere ku malo amene unamupatsa. Iye asapite nafe ku nkhondo kuopa kuti angadzasanduke mdani wathu. Kodi iyeyu adzadziyanjanitsa bwanji ndi mbuye wake? Iyeyutu adzadziyanjanitsa ndi mbuye wake pakupha anthu ali panowa? Paja ameneyu ndi Davide yemwe ankamuvinira namuyimbira kuti,

“ ‘Sauli wapha anthu 1,000
    koma Davide wapha miyandamiyanda?’ ”

Kotero Akisi anayitana Davide ndipo anamuwuza kuti, “Pali Yehova wamoyo, iwe wakhala wodalirika ndipo chikanakhala chinthu chabwino kuti uzimenya nkhondo pamodzi nane popeza chibwerere iwe kuno ine sindinapeze cholakwa chilichonse ndi iwe. Koma atsogoleri enawa ndiwo sakukufuna. Tsono bwerera. Upite mu mtendere kuopa kuti ungachite kanthu kena koyipira atsogoleri a Afilistiwa.”

Davide anafunsa Akisi kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza cholakwa chotani mwa ine mtumiki wanu chiyambire kukutumikirani mpaka lero? Tsono chifukwa chiyani sindingapite kukamenya nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?”

Akisi anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti ndiwe wangwiro ngati mngelo wa Mulungu. Komabe atsogoleri a ankhondo a Afilisti akuti, ‘Davide asapite nafe ku nkhondo.’ 10 Tsono udzuke mmamawa, pamodzi ndi ankhondo ako amene unabwera nawo, ndipo unyamuke kukangocha.”

11 Choncho Davide ndi anthu ake anadzuka mmamawa kubwerera ku dziko la Afilisti. Koma Afilistiwo anapita ku Yezireeli.

Davide Amenyana ndi Aamaleki

30 Pa tsiku lachitatu, Davide ndi anthu ake anakafika ku Zikilagi. Tsono anapeza Aamaleki atawononga kale dera la Negevi ndi Zikilagi. Anathira nkhondo mzinda wa Zikilagi ndi kuwutentha ndi moto. Anatenga akazi ndi onse amene anali mʼmenemo akuluakulu ndi angʼono omwe kuti akakhale akapolo. Sanaphe aliyense koma anawatenga amoyo napita nawo.

Davide ndi anthu ake atafika ku Zikilagi anapeza kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo, amuna ndi akazi atengedwa ukapolo. Kotero Davide ndi anthu ake analira mofuwula mpaka analibenso mphamvu zolirira. Akazi awiri a Davide, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli anatengedwanso. Davide anavutika kwambiri mu mtima mwake chifukwa anthu amakamba zoti amuponye miyala popeza aliyense anali ndi chisoni pokumbukira ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anapeza mphamvu mwa Yehova Mulungu wake.

Kenaka Davide anawuza wansembe Abiatara, mwana wa Ahimeleki kuti, “Ndipatse efodi ija.” Abiatara anabwera nayo efodiyo. Tsono Davide anapempha nzeru kwa Yehova nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondoli? Kodi ndidzawapambana?”

Yehova anayankha kuti, “Litsatire, iwe udzawapambana ndithu ndipo udzapulumutsa anthu ako.”

Davide pamodzi ndi anthu ake 600 aja ananyamuka nafika ku mtsinje wa Besori. Kumeneko anasiyako anthu ena. 10 Davide ndi anthu ake 400 anapitirira kuwalondola Aamaleki aja. Koma anthu ena 200 anatsala popeza anatopa moti sakanatha kuwoloka mtsinje wa Besori uja.

11 Anthu amene anali ndi Davide anapeza Mwigupto mʼmunda wina ndipo anabwera naye kwa Davide. Iwo anamupatsa madzi kuti amwe ndi chakudya kuti adye. 12 Anamupatsanso chidutswa cha keke yankhuyu ndi makeke awiri a mphesa zowumika kuti adye. Atadya anapezanso mphamvu popeza anakhala masiku atatu wosadya kapena kumwa kanthu kalikonse.

13 Davide anafunsa kuti, “Kodi ndiwe yani, ndipo ukuchokera kuti?”

Iye anayankha kuti, “Ine ndine Mwigupto, kapolo wa Mwamaleki. Mbuye wanga anandisiya nditayamba kudwala masiku atatu apitawo. 14 Ife tinathira nkhondo dera la kummwera kwa mayiko a Akereti, dera la Yuda, ndi dera la kummwera kwa mayiko a Kalebe. Mzinda wa Zikilagi tinawutentha ndi moto.”

15 Davide anamupempha kuti, “Kodi unganditsogolere kumene kuli gulu lankhondoli?”

Iye anayankha kuti, “Mukandilonjeza molumbira kuti simudzandipha kapena kundipereka kwa mbuye wanga, ine ndikulondolerani kumene kuli gululo.”

16 Mwigupto uja anaperekeza Davide. Tsono Aamaleki anali atamwazikana ponseponse. Iwo ankadya, kumwa ndi kuvina chifukwa cha zofunkha zambiri zimene anatenga ku dziko la Afilisti ndi ku dziko la Ayuda. 17 Tsono Davide anawakantha kuyambira madzulo atsikulo mpaka madzulo a tsiku linalo. Palibe anapulumuka kupatula anyamata 400 amene anakwera pa ngamira nʼkuthawa. 18 Choncho Davide analanditsa zinthu zonse zimene Aamaleki aja anatenga. Anapulumutsanso akazi ake awiri aja. 19 Palibe chimene chinasowa anthu onse, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, mnyamata mpaka mtsikana anapulumutsidwa. Davide anapulumutsa chilichonse chimene anafunkha Aamaleki aja. 20 Anapulumutsanso nkhosa ndi ngʼombe zonse. Tsono anthu ankakusa ziwetozo namati, “Izi ndizo zofunkha za Davide.”

21 Davide anafika ku malo kumene kunali anthu 200 otopa kwambiri aja amene sanathe kutsagana naye koma anangokhala ku mtsinje wa Besori. Tsono ananyamuka kuti akumane ndi Davide pamodzi ndi anthu amene anali naye. Davide anawayandikira nawalonjera. 22 Tsono anthu ena oyipa mtima achabechabe mwa amene anatsagana ndi Davide aja anati, “Popeza awa sanapite nafe, sitiwapatsako zofunkha zimene tapulumutsazi, kupatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake azipita.”

23 Koma Davide anawayankha kuti, “Ayi, abale anga, musachite zimenezi ndi zinthu zimene Yehova watipatsa. Iye watisunga ndi kupereka mʼmanja mwathu gulu la ankhondo limene linabwera kudzalimbana nafe. 24 Ndani angakumvereni zimene mukunenazi? Gawo la munthu amene anapita kukamenya nkhondo likhale lofanana ndi la munthu amene anatsala pano kuyangʼanira katundu wathu. Pasakhale kusiyana kulikonse.” 25 Choncho Davide anakhazikitsa ngati lamulo mʼchitidwe woterewu pakati pa Aisraeli kuyambira tsiku limenelo mpaka lero.

26 Davide atafika ku Zikilagi, anatumiza zina mwa zofunkhazo kwa akuluakulu a Yuda, amene anali abwenzi ake. Anati, “Nayi mphatso yanu yochokera pa zofunkha za adani a Yehova.”

27 Iye anatumiza mphatsozo kwa anthu a ku Beteli, Ramoti-Negavi, Yatiri, 28 Aroeri, Sifimoti, Esitemowa 29 Rakala, mizinda ya fuko la Ayerahimeeli, mizinda ya fuko la Akeni, 30 a ku Horima, Borasani, Ataki, 31 Hebroni pamodzi ndi onse a kumalo kumene Davide ndi anthu ake anakhala akuyendayendako.

1 Akorinto 10

Chenjezo Kuchokera Mʼmbiri ya Israeli

10 Pakuti sindikufuna kuti inu mukhale osadziwa zenizeni, abale, kuti makolo athu anatsogozedwa ndi mtambo ndikuti onse anawoloka nyanja. Ndipo onse anabatizidwa mwa Mose mu mtambo ndi mʼnyanja. Onse anadya chakudya chimodzi chauzimu ndipo anamwa chakumwa chimodzi chauzimu; popeza anamwa kuchokera mʼthanthwe lomwe anayenda nalo, ndipo thanthwe limeneli linali Khristu. Ngakhale zinali choncho, Mulungu sanakondwere ndi ambiri a iwo, motero ambiri mwa iwo anafera mʼchipululu.

Tsono zinthu izi zinachitika kuti zikhale chitsanzo, kuti ife tisayike mitima yathu pa zinthu zoyipa monga anachitira makolo athuwo. Musakhale anthu opembedza mafano, monga analili ena mwa iwo. Pakuti zalembedwa kuti, “Anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.” Tisachite chigololo monga ena mwa iwo anachitira ndipo tsiku limodzi anafapo anthu 23,000. Tisamuyese Khristu, monga ena mwa iwo anachitira ndipo anaphedwa ndi njoka. 10 Ndipo osamawiringula, monga ena mwa iwo anachitira naphedwa ndi mngelo wowononga.

11 Zinthu izi zinawachitikira kuti zikhale chitsanzo ndipo zinalembedwa kuti zikhale chenjezo kwa ife, amene tiyandikira nthawi ya kutha kwa zonse. 12 Choncho, ngati mukuganiza kuti mwayima mwamphamvu, samalani mungagwe! 13 Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.

Maphwando a Mafano ndi Mgonero wa Ambuye

14 Choncho abwenzi anga okondedwa, lekani kupembedza mafano. 15 Ndikuyankhula kwa a anthu anzeru zawo, nokha muweruze pa zimene ndikunenazi. 16 Pamene tidalitsa chikho cha Mgonero wa Ambuye, mothokoza Mulungu, kodi sitikugawana magazi a Khristu? Nanga buledi amene timanyemayo, kodi sitikugawana thupi la Khristu? 17 Pakuti buledi ndi mmodzi yekha, ifenso ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, popeza tonse timagawana buledi mmodzi yemweyo.

18 Taganizirani zimene amachita Aisraeli. Kodi onse amene amadya zoperekedwa nsembe, samachita nawo miyambo ya pa guwapo? 19 Kodi ndikutanthauza kuti nsembe zoperekedwa kwa mafano ndi kanthu konse, kapena kuti mafano ndi kanthu konse? 20 Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo. 21 Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda. 22 Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?

Ufulu wa Munthu Wokhulupirira

23 Mutha kunena kuti, “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zili za phindu. “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zimathandiza. 24 Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.

25 Idyani nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 26 Popeza kuti, “Dziko lapansi ndi la Ambuye ndi zonse za mʼmenemo ndi zake.”

27 Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 28 Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima. 29 Ndikunena za chikumbumtima cha winayo osati chanu. Tsono mungafunse kuti, nʼchifukwa chiyani ufulu wanga ukuphwanyidwa chifukwa cha chikumbumtima cha munthu wina? 30 Ngati ndikuyamika Mulungu chifukwa cha chakudya, nanga munthu angandinyoze bwanji pa zinthu zomwe ndayamikira nazo Mulungu?

31 Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. 32 Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu. 33 Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.

Ezekieli 8

Kupembedza Mafano Mʼnyumba ya Mulungu

Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, mʼchaka chachisanu ndi chimodzi, ndinakhala mʼnyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Tsono mphamvu za Ambuye Yehova zinandifikira. Nditayangʼana ndinangoona chinthu chooneka ngati munthu. Kuchokera pamene pamaoneka ngati chiwuno chake kumatsika mʼmunsi anali ngati moto, ndipo kuchokera mʼchiwuno kukwera mmwamba amaoneka mowala ngati mkuwa wonyezimira. Iye anatambasula chinthu chooneka ngati dzanja ndipo anagwira tsitsi la pamutu panga. Nthawi yomweyo Mzimu unandikweza mlengalenga. Tsono ndikumachita ngati ndikuona Mulungu kutulo, Mzimu uja unapita nane ku Yerusalemu nundiyika pa khomo la chipata chamʼkati choyangʼana kumpoto. Kumeneko kunali fano limene limaputa mkwiyo wa Mulungu. Kumeneko ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ngati momwe ndinaonera mʼmasomphenya mʼchigwa muja.

Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayangʼana kumpoto.” Choncho ndinayangʼana kumpoto ndipo ndinaona pa khomo la chipata pafupi ndi guwa lansembe ndinaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija.

Ndipo Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimene akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene Aisraeli akuchita kuno, zinthu zondichotsa Ine kumalo anga opatulika? Koma iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri.”

Kenaka Iye anandipititsa ku khomo lolowera ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Nditayangʼanitsitsa ndinangoona dzenje pa khomapo. Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano bowola pa khomapo.” Ndinabowoladi pa khomapo ndipo ndinapezapo khomo.

Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Lowa, ndipo ona zinthu zonyansa zimene akuchita pamenepa.” 10 Motero Ine ndinalowa ndi kuyangʼana, ndipo ndinaona pa makoma onse zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwawa pansi, za nyama zonyansa ndiponso za mafano onse amene Aisraeli ankapembedza. 11 Patsogolo pa zimenezi panayima akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Aisraeli, ndipo Yaazaniya mwana wa Safani anali atayima pakati pawo. Aliyense wa iwo anali ndi chofukizira lubani mʼdzanja lake ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkafuka.

12 Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Aisraeli akuchita mu mdima, aliyense akupembedza fano lakelake mʼnyumbamo? Iwo akuti, ‘Yehova sakutiona; Yehova walisiya dziko!’ 13 Iye anandiwuzanso kuti, ‘Iwe udzawaonanso akuchita zinthu zonyansa kwambiri.’ ”

14 Kenaka anapita nane pa khomo la ku khomo la chipata cha Nyumba ya Mulungu choyangʼana kumpoto, ndipo kumeneko ndinaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wawo wotchedwa Tamuzi. 15 Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi? Iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri kuposa izi.”

16 Kenaka Iye anapita nane mʼkati mwa bwalo la Nyumba ya Yehova. Kumeneko ku khomo lolowera ku Nyumba ya Yehova pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna 25. Anafulatira Nyumba ya Mulungu wa Yehova ndipo nkhope zawo zinaloza kummawa, ndipo ankapembedza dzuwa choyangʼana kummawa.

17 Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waziona zimenezi? Kodi nʼchinthu chopepuka kuti anthu a ku Yuda azichita zonyansa zimene akuchitazi pano? Kodi afike mpaka pomafalitsa za ndewu mʼdziko lonse? Iwotu akuwutsa ukali wanga. Akundipsetsa mtima ndi zochita zawo! 18 Choncho Ine ndidzawalanga ndili wokwiya. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka. Ngakhale atandifuwulira mʼmakutu mwanga sindidzawamvera.”

Masalimo 46-47

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali.

46 Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
    thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,
    ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,
    ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.

Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,
    malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;
    Mulungu adzawuthandiza mmawa.
Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa;
    Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.

Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova,
    chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.
Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;
    Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo;
    amatentha zishango ndi moto.
10 Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;
    ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;
    ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”

11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

47 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;
    fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;
    Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;
    anayika anthu pansi pa mapazi athu.
Iye anatisankhira cholowa chathu,
    chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.
            Sela

Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,
    Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;
    imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.

Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;
    imbirani Iye salimo la matamando.
Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;
    Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana
    monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;
    Iye wakwezedwa kwakukulu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.