M’Cheyne Bible Reading Plan
Sauli Ayesanso Kupha Davide
19 Sauli anawuza mwana wake Yonatani ndi nduna zake zonse kuti aphe Davide. Koma Yonatani amamukonda kwambiri Davide. 2 Choncho anawuza Davide kuti, “Abambo anga Sauli akufuna kukupha. Tsono uchenjere. Mmawa upite ukabisale ndipo ukakhale komweko. 3 Ine ndidzapita ndi kukayima pafupi ndi abambo anga ku munda kumene iwe ukabisale. Ndipo ndidzayankhula ndi abambo anga za iwe ndipo chilichonse chimene ndikamve ndidzakuwuza.”
4 Tsono Yonatani anakanena zabwino za Davide kwa abambo ake Sauli ndipo anati, “Mfumu musachimwire mtumiki wanu Davide, sanakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino kwambiri. 5 Iye anayika moyo wake pa chiswe pamene anapha Mfilisiti uja. Choncho Yehova anachita zazikulu popambanitsa Aisraeli pa nkhondo. Inu munaona zonsezo ndipo munakondwera. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa pofuna kupha Davide?”
6 Sauli anamvera mawu a Yonatani ndipo analumbira kuti, “Pali Yehova, Davide sadzaphedwa.”
7 Pambuyo pake Yonatani anayitana Davide namuwuza zonsezi. Choncho Yonatani anabwera naye Davide kwa Sauli ndipo ankamutumikira Sauliyo monga kale.
8 Panabukanso nkhondo ina ndipo Davide anapita ndi kukamenyana ndi Afilisti. Iye anawakantha mwamphamvu kotero kuti Afilisti anathawa.
9 Tsiku lina mzimu woyipa uja unafikanso pa Sauli. Nthawi imeneyi nʼkuti Sauli uja ali mʼnyumba mwake, mkondo uli mʼdzanja lake ndi Davide akuyimba zeze, 10 Sauli anafuna kumubaya Davide ndi kumukhomera kukhoma, koma Davide anapewa mkondowo kotero Sauli anakabaya pa khoma. Usiku womwewo Davide anathawa.
11 Usiku womwewo Sauli anatumiza anthu ku nyumba ya Davide kuti akamubisalire ndi kumupha mmamawa. Koma Mikala mkazi wake anamuchenjeza nati, “Ngati usiku uno supulumutsa moyo wako, mawa udzaphedwa.” 12 Choncho Mikala anamutulutsira Davide pa zenera, ndipo anathawa ndi kupulumuka. 13 Kenaka Mikala anatenga fano naligoneka pa bedi nayika pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwa fanolo ndipo analifunditsa nsalu.
14 Pamene amithenga a Sauli aja anafika kuti akamugwire Davide, Mikala anati, “Davide akudwala.”
15 Koma Sauli anatumanso anthuwo kuti akamuone Davide, nati, “Mubwere naye kuno ali pa bedi pomwepo kuti ndidzamuphe.” 16 Koma pamene anthuwo analowa, anangoona fano pa bedipo ndi pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwake.
17 Tsono Sauli anafunsa Mikala kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandinamiza chotere polola kuti mdani wanga athawe?”
Mikala anayankha kuti, “Davide anandiwuza kuti, ‘Ukapanda kutero ndikupha.’ ”
18 Choncho Davide anathawa napulumuka. Pambuyo pake anapita kwa Samueli ku Rama nakamuwuza zonse zimene Sauli anamuchita. Kenaka iye ndi Samueli anapita kukakhala ku Nayoti. 19 Sauli anamva kuti, “Davide ali ku Nayoti ku Rama.” 20 Choncho iye anatumiza anthu kuti akamugwire Davide. Koma anaona gulu la aneneri likulosera ndi Samueli akuwatsogolera. Pomwepo Mzimu wa Mulungu unawafikira ndipo nawonso anayamba kulosera. 21 Sauli atamva zimenezi anatumizanso anthu ena, koma nawonso anayamba kulosa. Anatumanso anthu ena kachitatu, koma nawonso anayamba kulosa. 22 Pomaliza Sauli mwini wake ananyamuka kupita ku Rama ndipo anafika ku chitsime chachikulu cha ku Seku. Ndipo anafunsa, “Samueli ndi Davide ali kuti?”
Munthu wina anamuyankha kuti, “Ali ku Nayoti ku Rama.”
23 Choncho Sauli anapita ku Nayoti ku Rama. Koma Mzimu wa Mulungu unafikanso pa iye ndipo ankalosa akuyenda mpaka anafika ku Nayoti. 24 Nayenso anavula zovala zake nayamba kulosa pamaso pa Samueli. Kenaka anagona wamaliseche tsiku lonse ndi usiku wonse. Nʼchifukwa chake anthu amati, “Kodi Sauli alinso mmodzi wa aneneri?”
1 Paulo, woyitanidwa mwachifuniro cha Mulungu kuti akhale mtumwi wa Khristu Yesu ndi mʼbale wathu Sositene.
2 Kupita ku mpingo wa Mulungu ku Korinto, kwa oyeretsedwa mwa Khristu Yesu ndi oyitanidwa kukhala opatulika ndiponso kwa onse amene amapemphera mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu mʼdziko lonse lapansi, amene ndi Ambuye wawo ndi wathunso.
3 Landirani chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu.
Kuthokoza
4 Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu chifukwa cha chisomo chake chopatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu. 5 Pakuti mwa Iye mwalemekezedwa mʼnjira iliyonse, mʼkuyankhula kwanu konse ndi mʼkudziwa kwanu konse, 6 chifukwa umboni wathu pa za Khristu unatsimikizidwa mwa inu. 7 Choncho inu simusowa mphatso yauzimu iliyonse pamene mukudikira mofunitsitsa kuti Ambuye athu Yesu Khristu avumbulutsidwe. 8 Adzakulimbikitsani mpaka kumapeto kuti mudzakhale wopanda mlandu pa tsiku lobwera Ambuye athu Yesu Khristu. 9 Mulungu amene wakuyitanani inu mu chiyanjano ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu ngokhulupirika.
Kugawikana mu Mpingo
10 Ndidandaulira inu, abale, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu kuti nonsenu muvomerezane wina ndi mnzake kuti pasakhale kugawikana pakati panu ndi kuti mukhale amodzi kwenikweni mu nzeru ndi mʼmaganizo. 11 Abale anga, ena a ku nyumba ya Kloe andidziwitsa kuti pali mkangano pakati panu. 12 Chimene ndikutanthauza ndi ichi: wina amati, “Ndimatsatira Paulo,” wina, “Ndimatsatira Apolo,” wina, “Ndimatsatira Kefa,” winanso, “Ndimatsatira Khristu.”
13 Kodi Khristu wagawikana? Kodi Paulo anapachikidwa pa mtanda chifukwa cha inu? Kodi munabatizidwa mʼdzina la Paulo? 14 Ine ndikuyamika kuti sindinabatizepo mmodzi mwa inu kupatula Krispo ndi Gayo, 15 mwakuti palibe amene anganene kuti anabatizidwa mʼdzina langa. 16 (Inde, ine ndinabatizanso a mʼbanja la Stefano, koma sindikumbukira ngati ndinabatizanso wina aliyense). 17 Pakuti Khristu sananditume ine kudzabatiza, koma kudzalalikira Uthenga Wabwino, osati ndi mawu anzeru za umunthu, kuopa kuti mtanda wa Khristu ungakhale wopanda mphamvu.
Khristu ndiye Nzeru ndi Mphamvu za Mulungu
18 Pakuti uthenga wa mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa uthengawu ndi mphamvu ya Mulungu. 19 Pakuti kwalembedwa kuti,
“Ine ndidzawononga nzeru za anthu anzeru;
luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
20 Munthu wanzeru ali kuti? Munthu wozama ndi maphunziro ali kuti? Munthu wodziwa zakuya zamakono ali kuti? Kodi Mulungu sanazipusitse nzeru za dziko lapansi? 21 Tsono poti mwa nzeru za Mulungu dziko lapansi mu nzeru zake silinamudziwe Iye, Mulungu amakondweretsedwa kuti kudzera mu chopusa cha zomwe zinalalikidwa apulumutse iwo amene akhulupirira. 22 Ayuda amafuna zizindikiro zodabwitsa ndipo Agriki amafunafuna nzeru, 23 koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa. Chitsa chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi chopusa kwa a mitundu ina. 24 Koma kwa iwo amene Mulungu anawayitana, Ayuda ndi Agriki omwe, Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndi nzeru za Mulungu. 25 Pakuti za Mulungu zooneka ngati zopusa, ndi za nzeru kuposa nzeru za munthu, ndipo za Mulungu zooneka ngati zofowoka, zili ndi mphamvu kuposa mphamvu za munthu.
26 Abale taganizirani mmene munalili musanayitanidwe. Si ambiri a inu munali a nzeru, si ambiri a inu munali a mphamvu zamakopedwe. Si ambiri a inu munali obadwa pa ulemerero. 27 Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu. 28 Anasankha zinthu zapansipansi ndi zopeputsidwa za dziko la pansi lino, zinthu zimene kulibe, kuti asukulutse zimene zilipo, 29 kuti munthu asanyade pamaso pa Mulungu. 30 Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso. 31 Choncho poti zinalembedwa kuti, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.”
4 Haa! Golide wathimbirira,
golide wosalala wasinthikiratu!
Amwazamwaza miyala yokongola ya kumalo opatulika
pamphambano ponse pa mzinda.
2 Haa! Ana a Ziyoni amtengowapatali
amene kale anali ngati golide,
tsopano ali ngati miphika ya dothi,
ntchito ya owumba mbiya!
3 Ngakhale nkhandwe zimapereka bere
kuyamwitsa ana ake,
koma anthu anga asanduka ankhanza
ngati nthiwatiwa mʼchipululu.
4 Lilime la mwana lakangamira kukhosi
chifukwa cha ludzu,
ana akupempha chakudya,
koma palibe amene akuwapatsa.
5 Iwo amene kale ankadya zonona
akupemphetsa mʼmisewu ya mu mzinda.
Iwo amene kale ankavala zokongola
tsopano akugona pa phulusa.
6 Kuyipa kwa anthu anga kunali kwakukulu
kuposa anthu a ku Sodomu,
amene anawonongedwa mʼkamphindi kochepa
popanda owathandiza.
7 Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundana
ndi oyera kuposa mkaka.
Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi,
maonekedwe awo ngati miyala ya safiro.
8 Koma tsopano maonekedwe awo ndi akuda kuposa mwaye;
palibe angawazindikire mʼmisewu ya mu mzinda.
Khungu lawo lachita makwinyamakwinya pa mafupa awo;
lawuma gwaa ngati nkhuni.
9 Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposa
amene anafa ndi njala;
chifukwa chosowa chakudya cha mʼmunda
iwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa.
10 Amayi achifundo afika
pophika ana awo enieni,
ndiwo anali chakudya chawo pamene anthu
anga anali kuwonongeka.
11 Yehova wakwaniritsa ukali wake;
wagwetsa pansi mkwiyo wake woopsa.
Ndipo wayatsa moto mʼZiyoni
kuti uwononge maziko ake.
12 Mafumu a pa dziko lapansi sanakhulupirire,
kapena wina aliyense wokhala pa dziko lonse,
kuti adani kapena ankhondo akhoza kulowa
pa zipata za Yerusalemu.
13 Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri ake
ndi mphulupulu za ansembe ake,
amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo.
14 Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzinda
ngati anthu osaona.
Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazi
palibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo.
15 Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!”
“Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!”
Akamathawa ndi kumangoyendayenda,
pakati pa anthu a mitundu yonse amati,
“Asakhalenso ndi ife.”
16 Yehova mwini wake wawabalalitsa;
Iye sakuwalabadiranso.
Ansembe sakulandira ulemu,
akuluakulu sakuwachitira chifundo.
17 Ndiponso maso athu atopa nʼkuyangʼana,
chithandizo chosabwera nʼkomwe,
kuchokera pa nsanja zathu tinadikirira mtundu
wa anthu umene sukanatipulumutsa.
18 Anthu ankalondola mapazi athu,
choncho sitikanayenda mʼmisewu yathu mu mzinda.
Chimaliziro chathu chinali pafupi, masiku athu anali owerengeka,
chifukwa chimaliziro chathu chinali chitafika.
19 Otilondola akuthamanga kwambiri
kuposa ziwombankhanga mu mlengalenga;
anatithamangitsa mpaka ku mapiri
ndi kutibisalira mʼchipululu.
20 Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo,
anakodwa mʼmisampha yawo.
Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wake
pakati pa mitundu ya anthu.
21 Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu.
Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi.
Koma iwenso chikho chidzakupeza;
udzaledzera mpaka kukhala maliseche.
22 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha;
Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo.
Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu,
ndi kuyika poyera mphulupulu zako.
Salimo la Davide.
35 Inu Yehova, mulimbane nawo amene akulimbana nane;
mumenyane nawo amene akumenyana nane.
2 Tengani chishango ndi lihawo;
dzukani ndipo bwerani mundithandize.
3 Tengani mkondo ndi nthungo,
kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa.
Uzani moyo wanga kuti,
“Ine ndine chipulumutso chako.”
4 Iwo amene akufunafuna moyo wanga
anyozedwe ndi kuchita manyazi;
iwo amene akukonza kuti moyo wanga uwonongeke
abwerere mʼmbuyo mochititsa mantha.
5 Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo
pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa.
6 Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera
pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.
7 Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa
ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,
8 chiwonongeko chiwapeza modzidzimutsa
ukonde umene iwo abisa uwakole,
agwere mʼdzenje kuti awonongedwe.
9 Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova
ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.
10 Thupi langa lidzafuwula mokondwera,
“Ndani angafanane nanu Yehova?
Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri,
osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”
11 Mboni zopanda chisoni zinayimirira,
zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
12 Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino
ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.
13 Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli
ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya.
Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,
14 ndinayendayenda ndi kulira maliro,
kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga.
Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima
kukhala ngati ndikulira amayi anga.
15 Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala;
ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa.
Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.
16 Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe;
anandikukutira mano awo.
17 Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana?
Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo,
moyo wanga wopambana ku mikango.
18 Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu;
pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.
19 Musalole adani anga onyenga
akondwere chifukwa cha masautso anga;
musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa
andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.
20 Iwowo sayankhula mwamtendere,
koma amaganizira zonamizira
iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.
21 Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa!
Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”
22 Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete.
Ambuye musakhale kutali ndi ine.
23 Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza!
Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
24 Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga.
Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.
25 Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!”
Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”
26 Onse amene amakondwera ndi masautso anga
achite manyazi ndi kusokonezeka.
Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana,
avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
27 Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa,
afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo.
Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke,
Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
28 Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu
ndi za matamando anu tsiku lonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.