Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Oweruza 9

Abimeleki

Abimeleki mwana wa Yeru-Baala anapita ku Sekemu kwa abale a amayi ake ndi kukawawuza iwowo ndi fuko lonse la banja la abambo a amayi ake kuti, “Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno, ‘Chabwino ndi chiyani kwa inu kuti ana onse makumi asanu ndi awiri a Yeru-Baala azikulamulirani, kapena kuti azikulamulirani ndi munthu mmodzi basi?’ Kumbukirani kuti ine ndine mʼbale wanu weniweni.”

Abale a amayi akewo anamuyankhulira mawu amenewa kwa nzika zonse za ku Sekemu, ndipo mitima ya anthu onse inali pa Abimeleki chifukwa anati, “Uyu ndi mʼbale wathu,” Tsono anamupatsa ndalama zasiliva 70 za mʼnyumba ya chipembedzo ya Baala Beriti. Ndi ndalama zimenezi Abimeleki analemba anthu achabechabe ndi osasamala kuti azimutsatira. Anapita ku Ofiri ku mudzi kwa abambo ake ndipo anapha abale ake makumi asanu ndi awiri, ana a Yeru-Baala pa mwala umodzi. Koma Yotamu yemwe anali wamngʼono mwa onsewo anapulumuka chifukwa anabisala. Tsono nzika za ku Sekemu ndi za ku Beti-Milo zinapita kukasonkhana ku mtengo wa thundu pafupi ndi chipilala cha ku Sekemu kuti akalonge Abimeleki ufumu.

Yotamu atamva izi anapita kukayima pamwamba pa phiri la Gerizimu ndipo anafuwula nati, “Tandimverani inu anthu a ku Sekemu, kuti Mulungu akumvereninso. Tsiku lina mitengo inapita kukadzoza mfumu yawo. Tsono mitengoyo inati kwa mtengo wa olivi, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’ ”

“Koma mtengo wa olivi uja unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye mafuta angawa amene amalemekezera nawo milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo?’ ”

10 Apo mitengo inawuza mtengo wa mkuyu kuti, “Bwera ndiwe ukhale mfumu yathu.”

11 Koma mtengo wa mkuyu unayankha kuti, “Kodi ndisiye chipatso changa chokoma ndi chozunachi kuti ndizikalamulira mitengo?”

12 Kenaka mitengo ija inawuza mtengo wamphesa kuti, “Bwera ndiwe kuti ukhale mfumu yathu.”

13 Koma mtengo wamphesa unayankha kuti, “Kodi ine ndisiye vinyo wangayu, amene amasangalatsa milungu ndi anthu omwe kuti ndizikalamulira mitengo?”

14 Pomaliza mitengo yonse inawuza mkandankhuku kuti, “Bwera ndipo ukhale mfumu yathu.”

15 Mkandankhuku uja unayankha kuti, “Ngati mukufunadi kuti mudzoze ine kuti ndikhale mfumu yanu, bwerani mudzabisale mu mthunzi mwangamu, koma ngati simutero, moto utuluka kwa ine ndi kupsereza mikungudza ya ku Lebanoni.”

16 Yotamu anatinso, “Kodi mukuti munaonetsadi kuona mtima ndi kukhulupirika podzoza Abimeleki kukhala mfumu? Kodi mukuti munachitira ulemu Yeru-Baala ndi banja lake poganizira ntchito zimene anachita? 17 Kodi suja abambo anga anakumenyerani nkhondo ndi kuyika moyo wawo pa chiswe kuti akupulumutseni mʼmanja mwa Amidiyani? 18 Koma lero inu mwawukira banja la abambo anga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndiponso mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mdzakazi wake kuti akhale wolamulira anthu a ku Sekemu chifukwa ndi mʼbale wanu. 19 Tsono ngati mukuti zimene mwachitira Yeru-Baala ndi banja lake mwazichita moona mtima ndiponso mokhulupirika, ndiye mukondwere ndi Abimeleki, nayenso akondwere nanu! 20 Koma ngati sichoncho moto utuluke mwa Abimeleki ndi kupsereza anthu a ku Sekemu ndi Beti-Milo, ndipo moto utulukenso mwa anthu a ku Sekemu ndi Beti-Milo, ndi kupsereza Abimeleki!”

21 Kenaka Yotamu anathawira ku Beeri nakakhala komweko chifukwa ankaopa Abimeleki mʼbale wake.

22 Abimeleki atalamulira Israeli zaka zitatu, 23 Mulungu anayika chidani pakati pa Abimelekiyo ndi anthu a ku Sekemu, motero kuti anthu a ku Sekemu anawukira Abimeleki. 24 Mulungu anachita zimenezi kuti zoyipa zimene anachitira ana aamuna 70 a Yeru-Baala aja zimubwerere, ndi kuti magazi awo akhale pa Abimeleki mʼbale wawo ndi pa anthu a ku Sekemu amene anamulimbikitsa mtima kuti aphe abale akewo. 25 Choncho anthu a ku Sekemu anayika anthu omubisalira pamwamba pa mapiri. Tsono iwo ankalanda anthu odutsa mʼnjira imeneyo zinthu zawo ndipo Abimeleki anamva zimenezi.

26 Gaali mwana wa Ebedi anasamukira ku Sekemu ndi abale ake, ndipo anthu a ku Sekemuko anamukhulupirira iye. 27 Anthuwo anapita ku munda kukathyola mphesa ndi kuzifinya, ndipo anachita chikondwerero mʼnyumba ya milungu yawo. Anthuwo akudya ndi kumwa, ankatemberera Abimeleki. 28 Ndipo Gaali mwana wa Ebedi anati “Kodi Abimeleki ndi ndani, ndipo nʼchifukwa chiyani akutilamulira ife Asekemu? Kodi iyeyu si mwana wa Yeru-Baala ndipo womuthandiza wake si Zebuli? Tiyeni titumikire anthu a ku Hamori, kholo la fuko la Sekemu! Nanga nʼchifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki? 29 Anthu a mu mzindawo akanakhala pansi pa ulamuliro wanga, ndikanamuchotsa Abimelekiyu. Ndikanamuwuza Abimeleki kuti, ‘Wonjeza ankhondo ako ndipo ubwere tidzamenyane!’ ”

30 Zebuli amene ankalamulira mzindawo atamva zimene Gaali mwana wa Ebadi ananena, anakwiya kwambiri. 31 Anatumiza amithenga kwa Abimeleki, kukanena kuti, “Gaali mwana wa Ebedi ndi abale ake abwera ku Sekemu ndipo akuwutsa mitima ya anthu a mu mzindawo kuti akuwukireni inu. 32 Nʼchifukwa chake usiku womwe uno inu ndi anthu anu mupite, mukabisale mʼminda. 33 Mmawa dzuwa likutuluka, mudzuke ndi kukathira nkhondo mzindawo. Gaali ndi anthu amene ali naye akamadzabwera kuti alimbane ndi inu, inu mudzathane nawo monga mmene mungachitire.”

34 Choncho Abimeleki ndi ankhondo ake onse anadzuka usiku nakabisalira mzinda wa Sekemu mʼmagulu anayi. 35 Gaali mwana wa Ebedi anatuluka nakayima pa khomo pa chipata cha mzinda pamene Abimeleki ndi ankhondo ake anatuluka ku malo kumene anabisala kuja.

36 Gaaliyo atawaona, anawuza Zebuli kuti, “Taona anthu akutsika kuchoka pamwamba pa mapiri.”

Koma Zebuli anayankha kuti, “Zimene mukuonazo ndi zithunzi za mapiri chabe osati anthu.”

37 Koma Gaaliyo anayankhulanso kuti, “Taona anthu akutsika kuchokera pakati pa phiri, ndipo gulu lina likubwera kuchokera ku mtengo wa thundu wa owombeza mawula.”

38 Ndipo Zebuli anamufunsa iye kuti, “Pakamwa pako paja pali kuti tsopano, iwe amene umanena kuti, Abimeleki ndaninso kuti ife timutumikire? Kodi amenewa si anthu aja umawanyozawa? Tsopano tuluka ukamenyane nawo.”

39 Choncho Gaaliyo anatuluka akutsogolera anthu a ku Sekemu kukamenyana ndi Abimeleki. 40 Koma Abimeleki anamuthamangitsa ndipo Gaala anathawa. Ambiri a ankhondo ake anagwa napwetekeka njira yonse mpaka ku chipata cha mzinda. 41 Abimeleki anakhala ku Aruma, ndipo Zebuli anathamangitsa Gaali pamodzi ndi abale ake, kuwatulutsa mu Sekemu.

42 Mmawa mwake anthu a ku Sekemu anapangana zopita ku minda, ndipo Abimeleki anamva zimenezi. 43 Tsono Abimeleki anatenga anthu ake, nawagawa magulu atatu ndi kukabisala mʼminda. Ataona anthu akutuluka mu mzindawo, iye anapita kukalimbana nawo ndipo onsewo anawapha. 44 Abimeleki pamodzi ndi magulu ake anathamangira kutsogolo nakawakhalira pa chipata cha mzinda. Ndipo magulu awiri ena aja anathamangira anthu amene anali mʼminda ndi kuwapha onse. 45 Abimeleki anawuthira nkhondo mzindawo tsiku lonse. Kenaka anawulanda ndi kupha nzika zonse za mu mzindamo. Anawuwonongeratu mzindawo nawuwaza mchere.

46 Anthu a mu nsanja ya Sekemu atamva zimenezi, anakalowa mu linga la nyumba yopembedzeramo Baala-Beriti. 47 Abimeleki anamva kuti anthu ena asonkhana kumeneko. 48 Choncho Abimeleki pamodzi ndi anthu ake onse anapita ku phiri la Zalimoni. Kumeneko anatenga nkhwangwa nadula nthambi za mitengo. Ananyamula nthambi zija pa phewa pake. Tsono anawuza anthu aja kuti, “Zimene mwaona ine ndikuchita, inunso mufulumire kuchita monga ndachitiramu.” 49 Tsono aliyense anadula nthambi zake, natsatira Abimeleki. Anakawunjika nthambi zija pa linga paja, kenaka ndi kuliyatsa moto. Choncho anthu onse a ku nsanja ya Sekemu anafa. Analipo anthu pafupifupi 1,000, amuna ndi akazi.

50 Kenaka Abimeleki anapita ku Tebezi. Anakawuzungulira mzindawo ndi kuwulanda. 51 Koma mu mzindamo munali nsanja yolimba. Anthu onse a mu mzindamo amuna ndi akazi anathawira mu nsanjayo, nadzitsekera mʼkati. Ndipo anakwera ku denga la nsanjayo. 52 Abimeleki anapita ku nsanjayo nathira nkhondo. Anafika pafupi ndi chitseko cha nsanja ija kuti ayitenthe. 53 Koma mkazi wina anaponya mwala wa mphero pa mutu wa Abimeleki ndi kuswa chibade cha mutuwo.

54 Mwamsanga Abimeleki anayitana mnyamata womunyamulira zida za nkhondo namuwuza kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuti anthu asadzanene kuti, ‘Mkazi ndiye anamupha.’ ” Choncho wantchito wake anamubayadi mpaka kutulukira kunja lupangalo ndipo anafa. 55 Aisraeli ataona kuti Abimeleki wafa, anapita kwawo.

56 Mmenemu ndi mmene Mulungu analipsirira tchimo la Abimeleki limene anachitira abambo ake pakupha abale ake 70 aja. 57 Mulungu anawalanganso anthu a ku Sekemu chifukwa cha kuyipa kwawo konse. Ndipo matemberero a Yotamu mwana wa Yeru-Baala anawagweradi.

Machitidwe a Atumwi 13

Barnaba ndi Saulo Atumidwa ndi Mpingo

13 Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.” Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.

Ku Kupro

Barnaba ndi Saulo motumidwa ndi Mzimu Woyera, anapita ku Selukeya ndipo kuchokera kumeneko anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. Pamene anafika ku Salamisi, analalikira Mawu a Mulungu mʼMasunagoge a Ayuda. Iwo anali ndi Yohane monga wowatumikira.

Iwo anayenda pa chilumba chonse mpaka anafika ku Pafo, kumeneko anapezanako ndi Myuda, wamatsenga amene analinso mneneri wonama dzina lake Barayesu. Iyeyu, amathandiza mkulu wa boma, Sergio Paulo. Mkulu wa bomayu, munthu wanzeru, anayitana Barnaba ndi Saulo chifukwa anafuna kumva Mawu a Mulungu. Koma Elima wamatsengayo, (Elima tanthauzo lake ndi wamatsenga), anatsutsana nawo ndipo anafuna kumuletsa mkulu wa bomayo kuti asakhulupirire. Koma Saulo, amenenso amatchedwa Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera anamuyangʼanitsitsa Elima ndipo anati, 10 “Iwe ndiwe mwana wa mdierekezi ndiponso mdani wa chilungamo! Ndiwe wodzaza ndi chinyengo cha mtundu uliwonse ndi kuchenjera konse. Kodi sudzaleka kupotoza njira zolungama za Ambuye? 11 Tsopano dzanja la Ambuye likukutsutsa iwe. Udzakhala wosaona ndipo kwa kanthawi sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.”

Nthawi yomweyo khungu ndi mdima zinamugwera ndipo anafunafuna munthu woti amugwire dzanja kuti amutsogolere. 12 Pamene mkulu wa bomayo anaona zimene zinachitika anakhulupirira pakuti anadabwa ndi chiphunzitso cha Ambuye.

Antiokeya wa ku Pisidiya

13 Kuchokera ku Pafo, Paulo ndi anzake anayenda pa sitima ya pamadzi kupita ku Perga wa ku Pamfiliya, kumeneko Yohane anawasiya nabwerera ku Yerusalemu. 14 Kuchokera ku Perga anapita ku Pisidiya wa ku Antiokeya. Pa tsiku la Sabata analowa mʼsunagoge, nakhala pansi. 15 Atawerenga mawu a mʼMalamulo ndi Aneneri, akulu a sunagoge anawatumizira mawu ndi kuti, “Abale ngati muli ndi mawu olimbikitsa nawo anthuwa, nenani.”

16 Atayimirira, Paulo anakweza dzanja lake ndi kuti, “Inu Aisraeli ndiponso inu a mitundu ina amene mumapembedza Mulungu, tandimverani! 17 Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu. 18 Ndipo Iye anapirira khalidwe lawo mʼchipululu kwa zaka makumi anayi. 19 Mulungu anawagonjetsera mitundu isanu ndi iwiri ya ku Kanaani ndipo anapereka dzikolo kwa Israeli kuti likhale lawo. 20 Izi zonse zinatenga zaka 450.

“Zitatha izi, Mulungu anawapatsa oweruza mpaka nthawi ya mneneri Samueli. 21 Kenaka anthu anapempha kuti awapatse mfumu, ndipo anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, wa fuko la Benjamini amene analamulira zaka makumi anayi. 22 Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’

23 “Kuchokera mwa zidzukulu za munthu ameneyu, Mulungu anawutsa Yesu kukhala Mpulumutsi wa Aisraeli, monga analonjezera. 24 Yesu asanabwere, Yohane analalikira kwa anthu onse Aisraeli za kutembenuka mtima ndi ubatizo. 25 Pamene Yohane amatsiriza ntchito yake anati: ‘Mukuganiza kuti ine ndine yani? Ine sindine ameneyo ayi, koma Iye akubwera pambuyo panga, amene ine sindine woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.’

26 “Abale, ana a Abrahamu, ndiponso inu a mitundu ina amene mumaopa Mulungu, Iye watumiza uthenga wachipulumutsowo kwa ife. 27 Anthu a ku Yerusalemu ndi atsogoleri awo sanazindikire Yesu, komabe pomuweruza Yesu anakwaniritsa mawu a Aneneri amene amawerengedwa Sabata lililonse. 28 Ngakhale sanapeze chifukwa choti afe, anapempha Pilato kuti amuphe. 29 Atachita zonse zimene zinalembedwa za Iye, iwo anamuchotsa pa mtengo ndipo anamuyika mʼmanda. 30 Koma Mulungu anamuukitsa, 31 ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa amene anayenda naye kuchokera ku Galileya mpaka ku Yerusalemu. Iwowa tsopano ndi mboni zake kwa anthu a Israeli.

32 “Ife tikukuwuzani Uthenga Wabwino; umene Mulungu analonjeza makolo athu. 33 Iye wakwaniritsa zimenezi kwa ife ana awo, poukitsa Yesu kuchokera kwa akufa. Monga zinalembedwa mu Salimo lachiwiri kuti,

“Iwe ndiwe mwana wanga;
    lero ine ndakhala Atate ako.”

34 Zakuti Mulungu anamuukitsa kuti asawole konse, zinanenedwa mʼmawu awa:

“ ‘Ine, ndidzakupatsa madalitso opatulika ndi odalirika amene ndinalonjeza Davide.’

35 Nʼchifukwa chakenso zinalembedwa mu Salimo lina kuti,

“ ‘Simudzalekerera woyera wanu kuti awole.’

36 “Pakuti pamene Davide anatsiriza kutumikira Mulungu mu mʼbado wake, anamwalira, iye anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo thupi lake linawola. 37 Koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa sanawole ayi.

38 “Nʼchifukwa chake, abale anga, dziwani kuti mwa Yesu chikhululukiro cha machimo chikulalikidwa. 39 Kudzera mwa Iye aliyense amene akhulupirira, alungamitsidwa kuchoka ku tchimo lililonse limene silingachoke ndi Malamulo a Mose. 40 Samalani kuti zimene aneneri akunena zisakuchitikireni inu:

41 “ ‘Onani, inu anthu onyoza,
    dabwani ndipo wonongekani,
chifukwa ine ndidzachita china chake mʼmasiku anu,
    inu simudzazikhulupirira
    ngakhale wina atakufotokozerani!’ ”

42 Pamene Paulo ndi Barnaba amatuluka mʼSunagoge, anthu anawapempha kuti adzapitirize kuyankhula zinthu zimenezi Sabata linalo. 43 Atatha mapemphero, Ayuda ambiri ndi anthu odzipereka otembenukira ku Chiyuda anatsatira Paulo ndi Barnaba, iwo anayankhula ndi anthuwo ndipo anawapempha kuti apitirire mʼchisomo cha Mulungu.

44 Pa Sabata linalo pafupifupi anthu onse a mu mzindawo anasonkhana kudzamva Mawu a Ambuye. 45 Pamene Ayuda anaona gulu la anthu, anachita nsanje ndipo anayankhula zamwano kutsutsana ndi zimene Paulo amanena.

46 Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina. 47 Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife:

“ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina,
    kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ”

48 Anthu a mitundu ina atamva izi, anakondwa ndipo analemekeza Mawu Ambuye; ndipo onse amene anawasankha kuti alandire moyo osatha anakhulupirira.

49 Mawu a Ambuye anafalikira mʼchigawo chonse. 50 Koma Ayuda anawutsa mitima ya akazi otchuka opembedza Mulungu ndi akulu a mu mzindamo. Iwo anabweretsa mazunzo kwa Paulo ndi Barnaba ndipo anawathamangitsa mʼchigawo chawo. 51 Tsono iwo anasasa fumbi la ku mapazi awo powatsutsa, ndipo anapita ku Ikoniya. 52 Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndiponso ndi Mzimu Woyera.

Yeremiya 22

Chiweruzo kwa Mafumu Oyipa

22 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndipo ukayiwuze kuti, ‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi. Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano. Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo. Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’ ”

Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi:

“Ngakhale iwe uli ngati Giliyadi kwa Ine,
    ngati msonga ya phiri la Lebanoni,
komabe ndidzakusandutsa chipululu,
    ngati mizinda yopanda anthu.
Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge,
    munthu aliyense ali ndi zida zake,
ndipo adzadula mikungudza yako yokongola
    nadzayiponya pa moto.

“Pamene anthu a mitundu ina adzadutsa pa mzinda umenewu adzafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere pa mzinda waukuluwu?’ Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’ ”

10 Musayilire mfumu Yosiya, musamuyimbire nyimbo womwalirayo;
    mʼmalo mwake, mulire kwambiri chifukwa cha Yehowahazi amene wapita ku ukapolo,
chifukwa sadzabwereranso
    kapena kuonanso dziko lake lobadwira.

11 Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso. 12 Iyeyo adzafera ku ukapoloko. Sadzalionanso dziko lino.”

13 “Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo,
    womanga zipinda zake zosanja monyenga,
pogwiritsa ntchito abale ake mwathangata,
    osawapatsa malipiro a ntchito yawo.
14 Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikulu
    ya zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.’
Kotero ndidzapanga mazenera akuluakulu,
    ndi kukhomamo matabwa a mkungudza
    ndi kukongoletsa ndi makaka ofiira.

15 “Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambiri
    zingachititse iwe kukhala mfumu?
Ganiza za abambo ako. Suja anali ndi zonse zakudya ndi zakumwa.
    Abambo ako ankaweruza molungama ndi mosakondera,
    ndipo zonse zinkawayendera bwino.
16 Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa,
    ndipo zonse zinkamuyendera bwino.
Kodi zimenezi sindiye tanthauzo la kudziwa Ine?”
    akutero Yehova.
17 “Koma maso ako ndi mtima sizili penanso,
    koma zili pa phindu lachinyengo,
pa zopha anthu osalakwa
    ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.”

18 Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti,

“Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti,
    ‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga!
Anthu ake sadzamulira maliro kuti,
    Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’
19 Adzayikidwa ngati bulu,
    kuchita kumuguguza ndi kukamutaya
    kunja kwa zipata za Yerusalemu.”

20 “Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko,
    mawu anu akamveke mpaka ku Basani.
Mulire mofuwula muli ku Abarimu
    chifukwa abwenzi ako onse awonongeka.
21 Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere.
    Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’
Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono.
    Simunandimvere Ine.
22 Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse,
    ndipo abwenzi anu adzatengedwa ku ukapolo.
Pamenepo mudzachita manyazi ndi kunyozedwa
    chifukwa cha zoyipa zanu zonse.
23 Inu amene mumakhala mʼnyumba ya ku Lebanoni,
    amene munamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza,
mudzabuwula kwambiri pamene zowawa zidzakugwerani,
    zonga za mkazi pa nthawi yake yochira!

24 “Pali Ine wamoyo, akutero Yehova, ngakhale iwe, Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ukanakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikanakuvula nʼkukutaya. 25 Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake. 26 Iwe pamodzi ndi amayi ako amene anakubereka ndidzakupititsani ku dziko lachilendo. Ngakhale inu simunabadwire kumeneko, komabe mudzafera komweko. 27 Simudzabwereranso ku dziko limene mudzafuna kubwerera.”

28 Kodi Yehoyakini wakhala ngati mbiya yonyozeka,
    yosweka imene anthu sakuyifunanso?
Kodi nʼchifukwa chake iye pamodzi ndi ana ake,
    achotsedwa nʼkutayidwa ku dziko limene iwo sakulidziwa?
29 Iwe dziko, dziko, dziko,
    Imva mawu a Yehova!
30 Yehova akuti,
“Munthu ameneyu mumutenge ngati wopanda ana,
    munthu amene sadzakhala wochita bwino pamoyo wake wonse,
pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake zomwe zidzachita bwino.
    Palibe amene adzathe kukhala pa mpando waufumu wa Davide
    ndi kulamulira Yuda.”

Marko 8

Yesu Adyetsa Anthu 4,000

Mʼmasiku amenewo gulu lina lalikulu la anthu linasonkhana. Popeza iwo analibe chakudya, Yesu anayitana ophunzira ake nati kwa iwo, “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala ali ndi Ine masiku atatuwa ndipo alibe chakudya. Ngati nditawawuza kuti apite kwawo ali ndi njala, iwo adzakomoka mʼnjira chifukwa ena a iwo achokera kutali.”

Ophunzira ake anayankha nati, “Kodi ndi kuti kuthengo kuno kumene munthu angapeze buledi okwanira kuwadyetsa?”

Yesu anafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?”

Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”

Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero. Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo, 10 analowa mʼbwato pamodzi ndi ophunzira ake napita ku dera la Dalamanuta.

11 Afarisi anabwera nayamba kumufunsa Yesu. Pomuyesa Iye, anamufunsa za chizindikiro chochokera kumwamba. 12 Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.” 13 Ndipo anawasiya, nalowanso mʼbwato ndi kuwolokera tsidya lina.

Yisiti wa Afarisi ndi Herode

14 Ophunzira anayiwala kutenga buledi, kupatula buledi mmodzi yekha amene anali naye mʼbwato. 15 Yesu anawachenjeza kuti, “Samalani ndipo onetsetsani yisiti wa Afarisi ndi wa Herode.”

16 Iwo anakambirana wina ndi mnzake ndipo anati, “Ndi chifukwa choti tilibe buledi.”

17 Yesu atadziwa zokambirana zawo anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe buledi? Kodi inu simukuonabe kapena kuzindikira? Kodi mitima yanu ndi yowumitsidwa? 18 Kodi muli ndi maso ndipo simukuona, ndi makutu ndipo mukulephera kumva? Kodi simukukumbukira? 19 Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”

Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.”

20 “Ndipo pamene ndinagawa malofu asanu ndi awiri a buledi, kwa anthu 4,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”

Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”

21 Iye anawafunsa kuti, “Kodi simumvetsetsabe?”

Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosaona ku Betisaida

22 Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze. 23 Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?”

24 Iye anakweza maso nati, “Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.”

25 Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino. 26 Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, “Usapite mʼmudzimo.”

Petro Avomereza Khristu

27 Yesu ndi ophunzira ake anapita ku midzi yozungulira Kaisareya wa Filipo. Ali panjira, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati ndine yani?”

28 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneri.”

29 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?”

Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.”

30 Yesu anawachenjeza kuti asawuze wina aliyense za Iye.

Yesu Aneneratu za Imfa Yake

31 Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.” 32 Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula.

33 Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”

Njira ya Mtanda

34 Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. 35 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. 36 Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? 37 Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? 38 Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.