M’Cheyne Bible Reading Plan
3 Iyi ndi mitundu ya anthu yomwe Yehova anayisiya kuti ayese nayo Aisraeli amene sanadziwe kumenya nkhondo mu Kanaani 2 (Yehova anachita izi kuti Aisraeli onse aphunzire kumenya nkhondo; makamaka amene nʼkale lonse sanadziwe kumenya nkhondo. 3 Mitundu ya anthuyo ndi: Mafumu asanu a Afilisti, Akanaani onse, Asidoni, ndi Ahivi amene ankakhala ku mapiri a Lebanoni kuyambira ku phiri la Baala-Herimoni mpaka ku Lebo Hamati. 4 Iwowa Yehova anawasiya kuti aziyesa nawo Aisraeli kuti aone ngati angamvere malamulo a Yehova, amene anapatsa makolo awo kudzera mwa Mose.
5 Choncho Aisraeli anakhala pakati pa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. 6 Tsono Aisraeli aja amalola ana awo aamuna ndi aakazi kuti azikwatira ndi kukwatiwa ndi anthu amitundu ina. Kenaka anayamba kupembedza milungu yawo.
Otanieli
7 Aisraeli anachita zinthu zoyipira Yehova. Iwowa anayiwala Yehova Mulungu wawo ndi kumatumikira Abaala ndi Asera. 8 Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeliwo ndipo anawagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraeli anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zisanu ndi zitatu. 9 Koma pamene Aisraeliwo analirira kwa Yehova, Iye anawawutsira mpulumutsi, Otanieli mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. Iyeyu ndiye anawapulumutsa. 10 Mzimu wa Yehova unatsika pa iye, choncho anasanduka mtsogoleri wa Israeli. Iye anapita kukamenya nkhondo, ndipo Yehova anapereka Kusani-Risataimu mfumu ya Aaramu mʼmanja mwake. Choncho anayigonjetsa. 11 Ndipo mʼdzikomo munakhala mtendere zaka makumi anayi. Kenaka Otanieli mwana wa Kenazi anamwalira.
Ehudi
12 Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. Tsono Yehova anapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya Mowabu kuti alimbane ndi Aisraeli aja popeza anachita zinthu zoyipira Yehova. 13 Egiloniyo anamemeza Aamori ndi Aamaleki kupita kukamenyana ndi Israeli, ndipo analanda Yeriko, mzinda wa migwalangwa. 14 Aisraeli anatumikira ngati akapolo Egiloni mfumu ya Mowabu kwa zaka 18.
15 Aisraeli analiranso kwa Yehova, ndipo Iye anawawutsira mpulumutsi, Ehudi. Iyeyu anali mwana wa Gera, munthu wamanzere, wa fuko la Benjamini. Aisraeli ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, kudzera kwa Ehudi. 16 Ndipo Ehudi anapanga lupanga lakuthwa kuwiri lotalika masentimita makumi asanu, ndipo anamangirira lupangalo pa ntchafu yake ya kumanja mʼkati mwa zovala zake. 17 Iye anakapereka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, amene anali munthu wonenepa kwambiri. 18 Ehudi atapereka msonkhowo, anawuza anthu amene ananyamula msonkhowo kuti azipita. 19 Iye mwini anabwerera pamalo a miyala yozokotedwa ku Giligala ndipo anati, “Zikomo mfumu, ine ndili ndi mawu achinsinsi kuti ndikuwuzeni.”
Mfumuyo inawuza onse amene amayitumikira kuti akhale chete, ndipo kenaka anawatulutsa.
20 Kenaka Ehudi anayandikira pafupi ndi mfumuyo, ndipo iyo inakhala yokha mʼchipinda chapamwamba, mozizira bwino. Tsono Ehudi anati, “Ndili ndi mawu ochokera kwa Mulungu woti ndikuwuzeni.” Mfumuyo itadzuka pa mpando wake waufumu, 21 Ehudi ndi dzanja lake lamanzere, anasolola lupanga pa ntchafu yake ya kumanja ndi kubaya nalo mfumuyo pa mimba. 22 Lupanga linalowa mʼmimba pamodzi ndi chogwirira chake. Mafuta anaphimba lupangalo popeza silinatulutsidwe mʼmimbamo. Ndiponso matumbo anatuluka. 23 Kenaka Ehudi anatuluka panja pa khonde, atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda chapamwambacho.
24 Ehudi atachoka, atumiki a mfumu aja anabwera, ndipo ataona kuti zitseko za chipinda chapamwamba zinali zokhoma anaganiza kuti mwina mfumu ikudzithandiza mʼkatimo. 25 Iwo anadikira nthawi yayitali koma popanda chochitika. Koma ataona kuti mfumuyo sikutsekulabe zitseko za chipindacho, iwo anatenga makiyi ndi kutsekula zitsekozo, ndipo anangoona mbuye wawo atagwera pansi, ali wakufa.
26 Ehudi anathawa pamene iwo ankadikira. Iye anadzera ku malo a miyala yozokotedwa kuja ndi kuthawa kupita ku Seiri. 27 Atafika kumeneko, anayimba lipenga ku dziko la ku mapiri la Efereimu. Iye akutsogolera, Aisraeli onse anatsika naye pamodzi kuchoka ku mapiriko.
28 Iye anawawuza kuti, “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu mʼmanja mwanu.” Choncho anthuwo anamutsatira, nalanda madooko a Yorodani opita ku Mowabu. Iwo sanalole kuti wina aliyense awoloke. 29 Nthawi imeneyo anapha Amowabu pafupifupi 10,000. Ophedwawo anali anthu amphamvu komanso odziwa kumenya nkhondo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anathawa. 30 Tsiku limenelo Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Israeli, ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 80.
Samugara
31 Ehudi atamwalira, panabwera Samugara mwana wa Anati. Iye anapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ngʼombe. Nayenso anapulumutsa Israeli.
Mawu a Stefano
7 Kenaka mkulu wa ansembe anafunsa Stefano kuti, “Kodi zimene akukunenerazi ndi zoona?”
2 Stefano anayankha kuti, “Abale ndi makolo, tamverani! Mulungu waulemerero anaoneka kwa kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani. 3 Mulungu anati, ‘Tuluka mʼdziko lako, siya abale ako, ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.’
4 “Ndipo iye anatulukadi mʼdziko la Akaldeya ndi kukakhala ku Harani. Atamwalira abambo ake, Mulungu anamuchotsa kumeneko ndi kumubweretsa mʼdziko lino limene inu mukukhalamo tsopano. 5 Mulungu sanamupatse cholowa kuno, ngakhale kadera kakangʼono kadziko. Koma Mulungu anamulonjeza kuti adzapereka dziko lino kwa iye ndi kwa zidzukulu zake, ngakhale kuti pa nthawi imeneyi analibe mwana. 6 Mulungu anayankhula motere kwa iye: ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo, ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400.’ 7 Mulungu anati, ‘Ine ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo, ndipo pambuyo pake akadzatuluka mʼdzikolo adzandipembedza Ine pamalo pano.’ 8 Kenaka Mulungu anachita pangano la mdulidwe ndi Abrahamu. Ndipo Abrahamu, anabereka Isake, namudula ali ndi masiku asanu ndi atatu. Ndipo Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka makolo khumi ndi awiri aja.
9 “Makolo athu anachita nsanje ndi Yosefe ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo ku Igupto. Koma Mulungu anali naye 10 ndipo anamupulumutsa iye kumasautso ake onse. Mulungu anamupatsa Yosefe nzeru ndi chisomo pamaso pa Farao mfumu ya ku Igupto, kotero mfumuyo inamuyika iye kukhala nduna yayikulu ya dziko la Igupto ndiponso nyumba yake yonse yaufumu.
11 “Kenaka munalowa njala mʼdziko la Kanaani, kotero kuti anthu anavutika kwambiri, ndipo makolo athu sanathe kupeza chakudya. 12 Pamene Yakobo anamva kuti ku Igupto kunali tirigu, iye anatuma makolo athu ulendo woyamba. 13 Pa ulendo wawo wachiwiri, Yosefe anadziwulula kwa abale akewo ndipo Farao anadziwa za banja la Yosefe. 14 Izi zinachitika, Yosefe anayitanitsa abambo ake Yakobo ndi banja lonse, onse pamodzi analipo 75. 15 Motero Yakobo anapita ku Igupto, kumene iye ndiponso makolo athu anamwalira. 16 Mitembo yawo anayinyamula ndi kupita nayo ku Sekemu kumene inayikidwa mʼmanda amene Abrahamu anagula kochokera kwa ana a Hamori ku Sekemuko.
17 “Nthawi itayandikira yakuti Mulungu achite zimene analonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu unakula ndi kuchuluka kwambiri mu Igupto. 18 Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto. 19 Mfumuyo inachita mwachinyengo ndi mtundu wathu ndi kuwazunza kuti ataye ana awo akhanda kuti afe.
20 “Pa nthawi imeneyo Mose anabadwa, ndipo anali wokongola kwambiri. Iye analeredwa mʼnyumba ya abambo ake kwa miyezi itatu. 21 Atakamutaya, mwana wamkazi wa Farao anamutola nakamulera ngati mwana wake. 22 Mose anaphunzira nzeru zonse za Aigupto, ndipo anali wamphamvu mʼmawu ndi ntchito zake.
23 “Mose ali ndi zaka makumi anayi, anaganizira zokayendera abale ake Aisraeli. 24 Iye ataona mmodzi wa iwo akuzunzidwa ndi Mwigupto, anatchinjiriza Mwisraeliyo, namupha Mwiguptoyo. 25 Mose anaganiza kuti abale ake adzazindikira kuti Mulungu anamuyika kuti awapulumutse koma iwo sanazindikire. 26 Mmawa mwake Mose anaona Aisraeli awiri akukangana. Iye anayesa kuwayanjanitsa ponena kuti, ‘Amuna inu, ndinu abale; chifukwa chiyani mukufuna kupwetekana?’
27 “Koma munthu amene amavutitsa mnzakeyo anakankha Mose ndipo anati, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza. 28 Kodi ukufuna kundipha monga momwe unaphera Mwigupto uja dzulo?’ 29 Mose atamva mawu awa anathawira ku Midiyani, kumene anakhala mlendo ndipo anabereka ana amuna awiri.
30 “Ndipo patapita zaka makumi anayi mngelo anaonekera kwa Mose mʼmalawi amoto pa chitsamba mʼchipululu pafupi ndi Phiri la Sinai. 31 Iye ataona zimenezi, anadabwa. Akupita kuti akaonetsetse pafupi, Mose anamva mawu a Ambuye: 32 ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.’ Mose ananjenjemera chifukwa cha mantha ndipo sanalimbe mtima kuyangʼananso.
33 “Ndipo Ambuye anati kwa Mose, ‘Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika. 34 Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse. Tsopano tiye ndikutume ku Igupto.’
35 “Uyu ndi Mose yemwe uja amene Aisraeli anamukana ndi kunena kuti, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza?’ Iyeyo anatumidwa ndi Mulungu mwini kuti akakhale wowalamulira ndiponso mpulumutsi, mothandizidwa ndi mngelo amene anamuonekera pa chitsamba. 36 Iye anawatulutsa mu Igupto ndipo anachita zodabwitsa ndi zizindikiro zozizwitsa mu Igupto, pa Nyanja Yofiira, ndiponso mʼchipululu kwa zaka makumi anayi.
37 “Uyu ndi Mose uja amene anati kwa Aisraeli, ‘Mulungu adzawutsa pakati pa abale anu mneneri ngati ine.’ 38 Iyeyu anali mʼgulu la Aisraeli mʼchipululu pamodzi ndi mngelo amene anamuyankhula pa phiri la Sinai ndiponso makolo athu; ndipo Mose analandira mawu amoyo kuti atipatse ife.
39 “Koma makolo athu anakana kumumvera iye. Iwo anamukana iye ndipo mʼmitima mwawo anatembenukira ku Igupto. 40 Iwo anati kwa Aaroni, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitsogolera kutuluka mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira. 41 Iyi ndi nthawi imene anapanga fano la mwana wangʼombe. Anapereka nsembe kwa fanoli nachita chikondwerero kulemekeza ntchito ya manja awo. 42 Koma Mulungu anawafulatira, nawapereka kuti apembedze zolengedwa zakumwamba. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la aneneri kuti,
“ ‘Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja
munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?’
43 Ayi, inu mwanyamula tenti ya Moloki
ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani,
mafano amene munapanga kuti muziwapembedza.
Chifukwa chake, Ine ndidzakutumizani kutali, kupitirira dziko la Babuloni.
44 “Makolo athu anali ndi tenti ya msonkhano pakati pawo mʼchipululu. Anayipanga monga momwe Mulungu anawuzira Mose, molingana ndi chithunzi chimene Mose anachiona. 45 Makolo athu, atayilandira Tentiyo, anabwera nayo motsogozedwa ndi Yoswa pamene analanda dziko la mitundu imene Mulungu anayipirikitsa pamaso pawo. Tentiyo inakhala mʼdzikomo mpaka nthawi ya Davide, 46 amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu ndipo anapempha kuti amʼmangire nyumba Mulungu wa Yakobo. 47 Koma anali Solomoni amene anamanga nyumbayo.
48 “Komatu, Wammwambamwambayo sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi anthu. Monga mneneri akunena kuti,
49 “ ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu,
ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga.
Kodi mudzandimangira nyumba yotani?
Akutero Ambuye.
Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?
50 Kodi si dzanja langa linapanga zonsezi?’
51 “Anthu wokanika inu, osachita mdulidwe wa mu mtima ndi a makutu ogontha! Inu ofanana ndi makolo anu. Nthawi zonse mumakana kumvera Mzimu Woyera: 52 Kodi analipo mneneri amene makolo anu sanamuzunze? Iwo anapha ngakhale amene ananeneratu za kubwera kwa Wolungamayo. Ndipo tsopano inu munamupereka ndi kumupha Iye. 53 Inu amene munalandira Malamulo amene anaperekedwa ndi angelo ndipo simunawamvere.”
Kuphedwa kwa Stefano
54 Atamva zimenezi, iwo anakwiya kwambiri ndipo anamukukutira mano. 55 Koma Stefano, wodzaza ndi Mzimu Woyera, anayangʼana kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu atayimirira ku dzanja lamanja la Mulungu. 56 Stefano anati, “Taonani, ndikuona kumwamba kotsekuka ndiponso Mwana wa Munthu atayimirira ku dzanja la manja la Mulungu.”
57 Koma iwo anatseka mʼmakutu mwawo, ndipo anafuwula kolimba, onse anathamangira kwa iye, 58 anamukokera kunja kwa mzinda ndipo anayamba kumugenda miyala. Mboni zinasungitsa zovala zawo kwa mnyamata otchedwa Saulo.
59 Akumugenda miyala, Stefano anapemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” 60 Ndipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.
Tsiku la Masautso
16 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, 2 “Usadzakwatire ndi kubereka ana aamuna kapena aakazi malo ano 3 pakuti ana aamuna ndi ana aakazi obadwira mʼdziko muno, komanso amayi awo ndi abambo awo amene anabereka anawo mʼdziko muno, 4 adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzawalira maliro kapena kuyikidwa mʼmanda koma adzakhala ngati ndowe zotayikira pansi. Ena adzaphedwa ku nkhondo ndipo ena adzafa ndi njala. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo.”
5 Yehova akuti, “Usalowe mʼnyumba ya maliro; usapite kukalira maliro kapena kukapepesa, chifukwa Ine ndawachotsera madalitso anga, chikondi changa ndi chifundo changa.” 6 Akuluakulu ndi angʼonoangʼono omwe adzafa mʼdziko muno. Sadzayikidwa mʼmanda kapena kuliridwa, ndipo palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi lake chifukwa cha iwo. 7 Palibe amene adzapereka chakudya kutonthoza amene akulira maliro, ngakhale kuti womwalirayo ndi abambo ake kapena amayi ake.
8 “Ndipo usalowe mʼnyumba mmene muli madyerero, nʼkukhala pansi ndi kudya ndi kumwa nawo. 9 Pakuti Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Pa nthawi yanu, inu mukuona ndidzathetsa mawu achimwemwe ndi achisangalalo ndiponso mawu a mkwati ndi mkwatibwi pa malo ano.’
10 “Ukawawuza anthu awa zinthu zonsezi akakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wanena kuti tsoka lalikulu lotere lidzatigwere? Kodi talakwa chiyani? Kodi tamuchimwira tchimo lotani Yehova Mulungu wathu?’ 11 Pamenepo ukawawuze kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti makolo anu anandisiya Ine,’ akutero Yehova, ‘ndi kutsatira milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Iwo anandisiya Ine ndipo sanasunge lamulo langa. 12 Komanso inu munachimwa kwambiri kupambana makolo anu. Aliyense wa inu akutsatira zoyipa ndi mtima wake wokanikawo mʼmalo mondimvera Ine. 13 Choncho Ine ndidzakubalalitsani mʼdziko muno ndi kukulowetsani mʼdziko limene inu ndi makolo anu simunalidziwe. Kumeneko mukatumikira milungu ina usana ndi usiku, ndipo sadzakuchitirani chifundo.’ ”
14 Yehova akuti, “Komabe masiku akubwera pamene anthu polumbira sadzatinso, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto,’ 15 koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku mayiko onse kumene anawabalalitsirako.’ Pakuti ndidzawabwezera ku dziko limene ndinalipereka kwa makolo awo.”
16 Yehova akuti, “Koma tsopano ndidzayitana adani okhala ngati asodzi ambiri, ndipo adzawagwira ngati nsomba. Izi zitatha adani enanso okhala ngati alenje ambiri, adzawasaka pa phiri lililonse, pa chitunda chilichonse ndiponso mʼmapanga onse a mʼmatanthwe. 17 Maso anga akuona makhalidwe awo onse; sanabisike pamaso panga. Palibe tchimo limene sindikulidziwa. 18 Ndidzawalanga mowirikiza chifukwa cha kuyipa kwawo ndi tchimo lawo. Ndidzatero chifukwa ayipitsa dziko langa ndi mafano awo amene ali ngati mitembo, ndiponso adzaza cholowa changa ndi mafano awo onyansa.”
19 Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga ndi linga langa,
pothawirapo panga nthawi ya masautso,
anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu
kuchokera ku mathero onse a dziko lapansi ndipo adzanena kuti,
“Makolo anthu anali ndi milungu yonama,
anali ndi mafano achabechabe amene sanawathandize.
20 Kodi anthu nʼkudzipangira milungu?
Atati atero ndiye kuti imeneyo ikhala milungu yachabechabe.”
21 “Choncho Ine ndidzawaphunzitsa,
kokha kano kuti adziwe
za mphamvu yanga ndi za nyonga zanga.
Pamenepo adzadziwa kuti
dzina langa ndi Yehova.
Yesu Achiritsa Munthu Wofa Ziwalo
2 Patapita masiku pangʼono, Yesu atalowanso mu Kaperenawo, zinamveka kuti wabwera ali mʼnyumba. 2 Choncho anthu ambiri anasonkhana kotero kuti panalibenso malo, ngakhale ndi pa khomo pomwe, ndipo Iye anawalalikira mawu. 3 Amuna anayi anabwera, atanyamula munthu wofa ziwalo. 4 Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo. 5 Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati kwa wofa ziwaloyo, “Mwana, machimo ako akhululukidwa.”
6 Ndipo ena mwa aphunzitsi amalamulo anakhala pansi pomwepo, namaganiza mʼmitima mwawo kuti, 7 “Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?”
8 Nthawi yomweyo Yesu anadziwa mu mzimu wake kuti izi ndi zimene ankaganiza mʼmitima yawo, ndipo anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukuganiza zinthu izi? 9 Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’ 10 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo.” Anati kwa wofa ziwaloyo, 11 “Ndikuwuza iwe, imirira, tenga mphasa yako ndipo pita kwanu.” 12 Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, “Sitinaonepo zinthu ngati izi!”
Kuyitanidwa kwa Levi
13 Yesu anatulukanso napita kumbali ya nyanja. Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye, ndipo anayamba kuliphunzitsa. 14 Pamene ankayendabe, anaona Levi mwana wa Alufeyo atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anamuwuza kuti, “Tsate Ine.” Ndipo Levi anayimirira namutsata Iye.
15 Yesu atakalandira chakudya ku nyumba kwa Levi, amisonkho ambiri ndi “ochimwa” ankadya naye pamodzi ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri amene anamutsatira. 16 Pamene aphunzitsi amalamulo a Afarisi anamuona akudya ndi “ochimwa” ndi amisonkho, anafunsa ophunzira ake kuti, “Chifukwa chiyani amadya ndi olandira msonkho ndi ochimwa?”
17 Yesu atamva zimenezi, anawawuza kuti, “Anthu amene ali bwino safuna singʼanga koma odwala. Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa.”
Za Kusala Kudya
18 Ndipo ophunzira a Yohane ndi a Afarisi amasala kudya. Anthu ena anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Zitheka bwanji kuti ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma anu satero?”
19 Yesu anayankha nati, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya bwanji pamene iye ali nawo pamodzi? Iwo sangatero, pamene iye ali nawo pamodzi. 20 Koma nthawi idzafika pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya.
21 “Palibe amene amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale. Ngati atatero, chigamba chatsopanocho chidzazomola chovala chakalecho, kukulitsa chibowocho. 22 Ndipo palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba akale a vinyo. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba a vinyo ndipo vinyoyo pamodzi ndi matumbawo zidzawonongeka. Ayi, satero, amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso.”
Yesu Mbuye wa Sabata
23 Tsiku lina la Sabata, Yesu amadutsa pakati pa minda ya tirigu, ndipo ophunzira ake amayenda naye limodzi, nayamba kubudula ngala za tiriguyo. 24 Afarisi anati kwa Iye, “Taonani, chifukwa chiyani akuchita chosaloledwa ndi lamulo pa Sabata?”
25 Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali osowa ndi anamva njala? 26 Pa nthawi ya Abiatara mkulu wa ansembe, iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndi kudya buledi wopatulika amene amaloledwa kuti adye ndi ansembe okha. Ndipo anapereka wina kwa anzake.”
27 Pamenepo anawawuza kuti, “Sabata linapangidwira munthu, osati munthu kupangidwira Sabata. 28 Choncho Mwana wa Munthu ali Ambuye ngakhale wa Sabata.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.