M’Cheyne Bible Reading Plan
Mngelo wa Yehova ku Bokimu
2 Mngelo wa Yehova anapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala ndipo anati kwa Aisraeli, “Ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndikukulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo anu. Ndinati ‘Sindidzaswa pangano langa ndi inu, 2 ndipo inu musadzachite pangano ndi anthu a dziko lino, koma mudzaphwanye maguwa awo ansembe.’ Koma inu simunamvere lamulo langa. Chifukwa chiyani mwachita zimenezi? 3 Ndikukuwuzani tsopano kuti sindithamangitsa nzikazo pamene inu mukufika. Ndidzawasandutsa kukhala adani anu ndipo milungu yawo idzakhala ngati msampha kwa inu.”
4 Mngelo wa Mulungu atayankhula izi kwa Aisraeli, onse analira mokweza, 5 ndipo anatcha malowo kuti Bokimu (kutanthauza kuti Olira). Pamenepo anapereka nsembe kwa Yehova.
Agonjetsedwa Chifukwa Chosamvera
6 Yoswa atawuza Aisraeli kuti achoke, iwo anapita kukatenga dzikolo, aliyense dera lake. 7 Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a moyo wa Yoswa. Atamwalira Yoswa, Aisraeli anatumikirabe Yehova nthawi yonse ya moyo wa akuluakulu amene anaona zazikulu zimene Yehova anawachitira.
8 Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110. 9 Ndipo anamuyika mʼmanda a mʼdziko lake, ku Timnati-Heresi mʼdziko la mapiri la Efereimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.
10 Mʼbado onse utapita kukakhala ndi anthu a mtundu awo, kenaka panauka mʼbado wina umene sunadziwe Yehova ngakhale ntchito zazikulu zimene Yehova anachitira Aisraeli. 11 Choncho Aisraeli anayamba kuchita zinthu zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anatumikira Abaala. 12 Iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa ku Igupto. Ndipo anatsatira ndi kupembedza milungu yosiyanasiyana ya anthu amene anawazungulira. Motero Aisraeli anakwiyitsa Yehova. 13 Iwo anasiya Yehova ndi kumatumikira Baala ndi Asiteroti. 14 Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse. 15 Nthawi zonse Aisraeli ankati akapita ku nkhondo, Yehova amalimbana nawo kuti agonjetsedwe, monga ananenera molumbira kuti zidzaterodi. Choncho iwo anali pa mavuto aakulu.
16 Choncho Yehova anawawutsira atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankasakaza zinthu zawo. 17 Komabe iwo sanawamvere atsogoleri awowo popeza ankapembedza milungu ina ndi kumayigwadira. Iwo anapatuka msangamsanga mu njira imene ankayendamo makolo awo. Iwo aja ankamvera malamulo a Yehova, koma mʼbado uwu ayi. 18 Nthawi zonse Yehova akawautsira mtsogoleri, Iye amakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankawapulumutsa Aisraeliwo mʼmanja mwa adani awo mʼnthawi imene anali moyo. Yehova ankawamvera chisoni Aisraeli pamene ankabuwula chifukwa cha anthu owazunza ndi kuwasautsa. 19 Koma nthawi zonse mtsogoleri akamwalira, Aisraeli ankabwerera mʼmbuyo. Iwo amadzisandutsa oyipa kupambana makolo awo popeza ankatsata milungu ina, kuyitumikira ndi kumayigwadira. Anakana kusiya makhalidwe awo oyipa ndi njira zawo zamakani.
20 Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeli ndipo anati, “Chifukwa mtundu uwu waswa pangano limene ndinakhazikitsa ndi makolo awo ndipo sanandimvere, 21 Inenso sindidzapirikitsanso mtundu uli wonse wa anthu amene Yoswa anawasiya pomwalira. 22 Ndidzatero kuti ndiwayese Aisraeli ndi kuona ngati adzasamala kuyenda mʼnjira ya Ine Yehova monga momwe ankachitira makolo awo.” 23 Choncho Yehova anayileka mitundu imeneyi ndipo sanayithamangitse kapena kuyipereka mʼmanja mwa Yoswa.
Asankha Atumiki Asanu ndi Awiri
6 Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku. 2 Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya. 3 Choncho abale, sankhani pakati panu anthu asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi anzeru. Ife tidzawapatsa udindo oyangʼanira. 4 Koma ife tidzadzipereka kuti tizipemphera ndi kulalikira mawu.”
5 Mawu amenewa anakondweretsa gulu lonse la anthu. Iwo anasankha, Stefano, munthu wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndiponso Mzimu Woyera; anasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanora, Timo, Parmena ndi Nikolao amene anatembenuka mtima ndi kulowa Chiyuda kuchokera kwa Antiokeya. 6 Iwo anapereka anthuwa kwa atumwi amene anawapempherera ndi kuwasanjika manja.
7 Ndipo Mawu a Mulungu anapitirira kufalikira. Chiwerengero cha ophunzira mu Yerusalemu chinakula mofulumira ndipo ansembe ochuluka anakhulupirira.
Ayuda Agwira Stefano
8 Stefano, munthu wodzazidwa ndi chisomo cha Mulungu ndi mphamvu anachita zodabwitsa ndiponso zizindikiro zazikulu pakati pa anthu. 9 Panauka mtsutso kuchokera kwa anthu a ku Kurene ndi a ku Alekisandriya komanso a ku dera la Silisiya ndi Asiya, otchedwa a Sunagoge ya Mfulu. Anthu amenewa anayamba kutsutsana ndi Stefano. 10 Koma iwo sanathe kumugonjetsa chifukwa iye ankayankhula ndi nzeru zimene Mzimu Woyera anamupatsa.
11 Iwo ananyengerera anthu ena mwamseri kuti anene kuti, “Ife tinamva Stefano akuchitira chipongwe Mose ndiponso Mulungu.”
12 Motero anawutsa mitima ya anthu, akulu ndi aphunzitsi amalamulo. Anamugwira Stefano ndi kumubweretsa ku Bwalo Lalikulu. 13 Iwo anabweretsa mboni zonama zimene zinati, “Munthu uyu akupitirirabe kuyankhula mawu onyoza malo oyera ndi malamulo. 14 Pakuti tinamumva akunena kuti Yesu uja wa ku Nazareti adzawononga malo ano ndiponso kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”
15 Onse amene anakhala pansi Mʼbwalo Lalikulu anamuyangʼanitsitsa Stefano, ndipo anaona kuti nkhope yake ikuwala ngati ya mngelo.
15 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samueli akanayima pamaso panga kupempherera anthu awa, Ine sindikanawachitira chisoni. Achotseni ndipo ndisawaonenso! Aleke apite! 2 Ndipo ngati akufunsa iwe kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ uwawuze kuti, ‘Yehova akuti,
“ ‘Oyenera kufa adzafa;
oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga;
oyenera kufa ndi njala adzafa ndi njala;
oyenera kupita ku ukapolo adzapita ku ukapolo.’
3 “Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga. 4 Ndidzawasandutsa kukhala chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a dziko lapansi chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda anachita mu Yerusalemu.
5 “Kodi adzakumvera chisoni ndani, Yerusalemu?
Kodi adzakulira ndani?
Kodi ndani amene adzapatuka kufunsa za moyo wako?
6 Inu mwandikana Ine,” akutero Yehova.
“Inu mukubwererabe mʼmbuyo.
Choncho Ine ndidzakukanthani.
Ndatopa ndi kukuchitirani chifundo.
7 Ine ndidzakubalalitsani kukuchotsani mʼmizinda ya mʼdzikomo
monga mmene amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero.
Anthu anga ndinawaliritsa ndi kuwawononga
chifukwa sanasinthe makhalidwe awo oyipa.
8 Ndinachulukitsa amayi awo amasiye
kupambana mchenga wa kunyanja.
Amayiwo ndinawawonongera ana awo aamuna
dzuwa lili pamutu.
Mwadzidzidzi ndinawagwetsera
kuwawa mtima ndi mantha.
9 Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka
ndipo akupuma wefuwefu.
Dzuwa lake lalowa ukanali usana;
anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru.
Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo
kuti awaphe ndi lupanga,”
akutero Yehova.
10 Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine,
munthu amene ndikutsutsana ndi kulimbana ndi anthu pa dziko lonse!
Ine sindinakongoze kapena kukongola kanthu,
komatu aliyense akunditemberera.
11 Yehova anati,
“Ndithudi, Ine ndidzakulanditsa kuti upeze bwino.
Ndithudi, adani ako adzakupempha pa nthawi ya tsoka
ndi ya mavuto awo.
12 “Palibe munthu amene angathe kudula chitsulo,
makamaka chitsulo chochokera kumpoto chosakaniza ndi mkuwa.
13 Anthu ako ndi chuma chako
ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro,
chifukwa cha machimo anu onse
a mʼdziko lanu lonse.
14 Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu
mʼdziko limene inu simulidziwa,
chifukwa mkwiyo wanga wayaka ngati moto
umene udzakutenthani.”
15 Ine ndinati, “Inu Yehova, mumadziwa zonse;
kumbukireni ndi kundisamalira.
Ndilipsireni anthu ondizunza.
Ndilezereni mtima musandilande moyo wanga.
Onani momwe ndi kuvutikira chifukwa cha Inu.
16 Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino.
Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala.
Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse,
ndimadziwika ndi dzina lanu.
17 Sindinakhale nawo mʼgulu la anthu amadyera,
sindinasangalale nawo anthu amenewo.
Ndinakhala ndekha chifukwa choti dzanja lanu linali pa ine
ndipo munadzaza mu mtima mwanga ndi mkwiyo.
18 Nanga nʼchifukwa chiyani mavuto anga sakutha?
Bwanji chilonda changa sichikupola?
Kodi inu mudzakhala ngati mtsinje wowuma nthawi yachilimwe,
kapena ngati kasupe wopanda madzi?”
19 Tsono Yehova anandiyankha kuti,
“Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso
ndipo udzakhalanso mtumiki wanga.
Ngati udzayankhula mawu oyenera osati achabechabe,
udzakhalanso mneneri wanga.
Anthu adzabwera kwa iwe
ndipo sipadzafunika kuti iwe upite kwa iwo.
20 Ndidzakusandutsa ngati khoma lolimba
ngati mkuwa kwa anthu awa.
Adzalimbana nawe
koma sadzakugonjetsa,
pakuti Ine ndili nawe
kukulanditsa ndi kukupulumutsa,”
akutero Yehova.
21 “Ndidzakupulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza.”
Yohane Mʼbatizi Akonza Njira
1 Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, 2 monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya:
“Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,
amene adzakonza njira yanu,”
3 “Mawu a wofuwula mʼchipululu,
‘Konzani njira ya Ambuye,
wongolani njira zake.’ ”
4 Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo. 5 Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani. 6 Yohane amavala zovala zopangidwa ndi ubweya wangamira, ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wamthengo. 7 Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake. 8 Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”
Kubatizidwa ndi Kuyesedwa kwa Yesu
9 Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. 10 Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda. 11 Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”
12 Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu, 13 ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.
Yesu Alengeza za Uthenga Wabwino
14 Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, 15 “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba
16 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi. 17 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 18 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
19 Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo. 20 Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.
Yesu Atulutsa Mzimu Woyipa
21 Iwo anapita ku Kaperenawo, ndipo tsiku la Sabata litafika, Yesu analowa mʼsunagoge nayamba kuphunzitsa. 22 Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo. 23 Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti, 24 “Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”
25 Yesu anadzudzula chiwandacho mwamphamvu nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye!” 26 Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.
27 Anthu anadabwa kwambiri kotero kuti anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Ichi nʼchiyani? Chiphunzitso chatsopano ndi ulamuliro! Iye akulamula, ngakhale mizimu yoyipa ikumumvera.” 28 Mbiri yake inafalikira kudera lonse la Galileya mofulumira.
Yesu Achiritsa Anthu Ambiri
29 Atangochoka mu sunagoge, Yesu pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane anakalowa mʼnyumba ya Simoni ndi Andreya. 30 Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye. 31 Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira.
32 Madzulo omwewo dzuwa litalowa anthu anabweretsa kwa Yesu anthu onse odwala ndi ogwidwa ndi ziwanda. 33 Anthu onse a mʼmudzimo anasonkhana pa khomo, 34 Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye.
Yesu Apemphera Kumalo a Yekha
35 Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera. 36 Simoni ndi anzake anapita kokamufunafuna Iye, 37 ndipo atamupeza, anamuwuza kuti, “Aliyense akukufunani!”
38 Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.” 39 Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda.
Yesu Achiritsa Wakhate
40 Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
41 Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” 42 Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.
43 Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti, 44 “Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.” 45 Mʼmalo mwake anapita nayamba kuyankhula momasuka, nafalitsa mbiriyo. Zotsatira zake, Yesu sanathe kulowa mʼmudzi moonekera, koma anakhala kunja kumalo kopanda anthu. Komabe anthu amabwera kwa Iye kuchokera kulikonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.