M’Cheyne Bible Reading Plan
Kugawa kwa Madera Otsala a Dziko
18 Atagonjetsa dziko lonse Aisraeli anasonkhana ku Silo ndipo anayimikako tenti ya msonkhano. 2 Koma pa nthawiyo nʼkuti mafuko asanu ndi awiri a Aisraeli asanalandire cholowa chawo.
3 Ndipo Yoswa anati kwa Aisraeli, “Kodi mudikira mpaka liti kuti mulowe ndi kulanda dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani? 4 Sankhani amuna atatu kuchokera ku fuko lililonse ndipo ine ndidzawatuma kuti akayendere dzikolo ndi kukalilembera bwino kuti ndiligawe kukhala lawo. Akatero, abwererenso kwa ine. 5 Aligawe dzikolo mʼzigawo zisanu ndi ziwiri; fuko la Yuda lidzakhale ndi dziko lake la kummwera ndi nyumba ya Yosefe ikhalebe mʼdziko lawo la kumpoto. 6 Mudzalembe mawu ofotokoza za zigawo zisanu ndi ziwiri za dzikolo, ndi kubwera nawo kwa ine. Tsono ineyo ndidzakuchitirani maere pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 7 Alevi asakhale ndi dziko pakati panu, chifukwa gawo lawo ndi kutumikira Yehova pa ntchito ya unsembe. Ndipo Gadi, Rubeni ndi theka la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo kummawa kwa Yorodani. Mose mtumiki wa Yehova ndiye anawapatsa.”
8 Anthuwo akupita kukalembera dzikolo, Yoswa anawalangiza kuti, “Pitani mukayendere ndi kulembera dzikolo. Kenaka mukabwere kwa ine, ndidzakuchitirani maere kuno ku Silo pamaso pa Yehova.” 9 Ndipo anthu anachoka ndi kukayendera dziko lonse. Iwo analemba bwinobwino mʼbuku za dzikolo, mzinda ndi mzinda. Analigawa magawo asanu ndi awiri, ndipo anabwerera kwa Yoswa ku misasa ya ku Silo. 10 Pambuyo pake Yoswa anawachitira maere ku Silo pamaso pa Yehova, ndipo fuko lililonse la Israeli analigawira dziko lake.
Dziko la Benjamini
11 Maere anagwera mabanja a fuko la Benjamini. Dziko limene anapatsidwa linali pakati pa fuko la Yuda ndi fuko la Yosefe:
12 Mbali ya kumpoto malire awo anayambira ku Yorodani nalowera chakumpoto kwa matsitso a ku Yeriko kulowera cha kumadzulo kwa dziko la ku mapiri ndi kukafika ku chipululu cha Beti-Aveni. 13 Kuchokera kumeneko malirewo analoza ku Luzi nadutsa mʼmbali mwa mapiri kummwera kwa Luzi (ndiye Beteli) ndipo anatsika mpaka ku Ataroti Adari, ku mapiri a kummwera kwa Beti-Horoni wa Kumunsi.
14 Ndipo malirewo analowanso kwina, analunjika kummwera kuchokera kumadzulo kwake kwa phiri loyangʼanana ndi Beti-Horoni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati Baala (ndiye Kiriati Yearimu), mzinda wa anthu a fuko la Yuda. Amenewa ndiye anali malire a mbali ya kumadzulo.
15 Malire a kummwera anayambira mʼmphepete mwenimweni mwa Kiriati Yearimu napita kumadzulo mpaka kukafika ku akasupe a Nefitowa. 16 Malire anatsikira mʼmphepete mwa phiri loyangʼanana ndi chigwa cha Beni Hinomu, kumpoto kwa chigwa cha Refaimu. Anapitirira kutsikira ku chigwa cha Hinomu kummwera kwa chitunda cha Ayebusi mpaka ku Eni Rogeli. 17 Kenaka anakhotera kumpoto kupita ku Eni-Semesi, kupitirira mpaka ku Geliloti amene amayangʼanana ndi pokwera pa Adumimu. Kenaka malire anatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni. 18 Anabzola cha kumpoto kwa chitunda cha Beti Araba ndi kutsikabe mpaka ku chigwa cha Yorodani. 19 Anabzolanso cha kumpoto kwa chitunda cha Beti-Hogila kukafika cha kumpoto ku gombe la Nyanja ya Mchere kumene mtsinje wa Yorodani umathirirako, cha kummwera kwenikweni. Awa anali malire a kummwera.
20 Yorodani ndiye anali malire a mbali ya kummawa.
Awa anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira.
21 Mabanja a fuko la Benjamini anali ndi mizinda iyi;
Yeriko, Beti-Hogila, Emeki Kezizi, 22 Beti-Araba, Zemaraimu, Beteli 23 Avimu, Para, Ofiri, 24 Kefari-Amoni, Ofini ndi Geba, mizinda khumi ndi awiri ndi midzi yake
25 Panalinso Gibiyoni, Rama, Beeroti, 26 Mizipa, Kefira, Moza 27 Rekemu, Iripeeli, Tarala, 28 Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake.
Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo.
Dziko la Simeoni
19 Maere achiwiri anagwera mabanja a fuko la Simeoni. Dziko lawo linali mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda. 2 Dzikolo linaphatikiza zigawo izi:
Beeriseba (ndi Seba), Molada, 3 Hazari-Suwali, Bala, Ezemu, 4 Elitoladi, Betuli, Horima, 5 Zikilagi, Beti-Marikaboti, Hazari-Susa, 6 Beti-Lebaoti ndi Saruheni. Yonse pamodzi inali mizinda 13 ndi midzi yawo.
7 Panalinso mizinda inayi iyi: Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani pamodzi ndi midzi yawo. 8 Dzikolo linaphatikizanso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baalati-Beeri, ndiye kuti Rama wa kummwera.
Ili ndi dziko limene mabanja a fuko la Simeoni analandira kukhala lawo. 9 Cholowa cha fuko la Simeoni chinatengedwa kuchokera ku gawo la Yuda chifukwa fuko la Yuda linali lalikulu kwambiri. Izi zinachititsa fuko la Simeoni kukhala mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda.
Dziko la Zebuloni
10 Maere achitatu anagwera mabanja a fuko la Zebuloni:
Malire a dziko lawo anafika mpaka ku Saridi. 11 Malirewo anakwera kupita cha kumadzulo ku Marala nakafika ku Dabeseti ndi ku mtsinje wa kummawa kwa Yokineamu. 12 Kuchokera ku mbali ina ya Saridi malire anakhota kupita kummawa ku malire a Kisiloti-Tabori mpaka ku Daberati nakwera mpaka ku Yafiya. 13 Kuchokera kumeneko anabzola kulowa cha kummawa mpaka ku Gati-Heferi ndi ku Eti Kazini ndi kumaloza ku Neya njira ya ku Rimoni. 14 Mbali ya kumpoto malirewo analoza ku Hanatoni ndipo anakathera ku chigwa cha Ifita Eli. 15 Anaphatikizapo Katati, Nahalala, Simironi, Idala ndi Betelehemu. Mizinda yonse inakwana khumi ndi iwiri pamodzi ndi midzi yake.
16 Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndi imene mabanja a fuko la Zebuloni analandira.
Dziko la Isakara
17 Maere achinayi anagwera mabanja a fuko la Isakara. 18 Dziko lawo linaphatikiza zigawo izi:
Yezireeli, Kesuloti, Sunemu, 19 Hafaraimu, Sioni, Anaharati, 20 Rabiti, Kisoni, Ebezi, 21 Remeti, Eni Ganimu, Eni Hada ndi Beti-Pazezi. 22 Malirewa anakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi Beti-Semesi ndipo anakathera ku Yorodani. Mizinda yonse inalipo 16 ndi midzi yake.
23 Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Isakara.
Dziko la Aseri
24 Maere achisanu anagwera mabanja a fuko la Aseri. 25 Gawo lawo linaphatikiza
Helikati, Hali, Beteni, Akisafu, 26 Alameleki, Amadi ndi Misali. Kumadzulo malire anafika ku Karimeli ndi Sihori Libinati. 27 Kenaka anakhotera kummawa kulowera ku Beti-Dagoni nafika ku dziko la Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifita Eli, ndipo anapita kumpoto ku Beti-Emeki ndi Neieli. Anapitirirabe kumpoto mpaka kukafika ku Kabuli, 28 Ebroni, Rehobu, Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni Wamkulu. 29 Kenaka malirewo anakhotera ku Rama ndi kupita ku mzinda wotetezedwa wa ku Turo. Kuchokera pamenepo malirewo anakhota kupita ku Hosa nakatulukira ku Nyanja, mʼchigawo cha Akizibu, 30 Uma, Afeki ndi Rehobu. Mizinda yonse inalipo 22 pamodzi ndi midzi yake.
31 Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Aseri.
Dziko la Nafutali
32 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera mabanja a fuko la Nafutali.
33 Malire awo anayambira ku Helefu mpaka ku mtengo wa thundu wa ku Zaananimu, ndipo anapitirira nʼkukafika ku Adami Nekebu, Yabineeli mpaka ku Lakumi ndi kukathera ku Yorodani. 34 Tsono malirewo anakhotera kumadzulo kupita ku Azinoti-Tabori. Kuchoka kumeneko anapita ku Hukoki, modutsa Zebuloni cha kummwera, Aseri cha kumadzulo ndi mtsinje wa Yorodani cha kummawa. 35 Mizinda yotetezedwa inali Zidimi, Zeri, Hamati, Rakati, Kinereti, 36 Adama, Rama, Hazori, 37 Kedesi, Ederi, Eni Hazori, 38 Yironi, Migidali Eli, Horemu, Beti-Anati ndi Beti-Semesi. Yonse pamodzi inalipo mizinda 19 ndi midzi yake.
39 Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yawo ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Nafutali.
Dziko la Dani
40 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera mabanja a fuko la Dani. 41 Gawo lawo linaphatikiza mizinda iyi:
Zora, Esitaoli, Iri Semesi, 42 Saalabini, Ayaloni, Itira, 43 Eloni, Timna, Ekroni, 44 Eliteke, Gibetoni, Baalati, 45 Yehudi, Beni Beraki, Gati-Rimoni, 46 Me-Yarikoni ndi Rakoni, pamodzi ndi dera loyangʼanana ndi Yopa.
47 Anthu a fuko la Dani atalandidwa dziko lawo, anapita kukathira nkhondo Lesemu. Iwo anapha anthu ake onse, nawulandiratu mzindawo, kuwusandutsa wawo ndi kumakhalamo. Tsono anatcha mzindawo dzina loti Dani popeza ndilo linali dzina la kholo lawo.
48 Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Dani.
Dziko la Yoswa
49 Atatha kugawana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, Aisraeli anamupatsa Yoswa mwana wa Nuni chigawo chake. 50 Potsata zimene Yehova anawalamula, anamupatsa mzinda wa Timnati-Sera umene anawupempha. Mzindawu unali mʼdziko lamapiri la Efereimu. Iye anawumanga mzindawu ndi kukhazikikako.
51 Wansembe Eliezara, Yoswa ndi atsogoleri a mabanja onse a Israeli anagawa dziko lija zigawozigawo pogwiritsa ntchito maere pamaso pa Yehova. Izi zinachitika ku Silo pa khomo la tenti ya msonkhano. Choncho anamaliza kugawa dzikolo.
149 Tamandani Yehova.
Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.
2 Israeli asangalale mwa mlengi wake;
anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.
3 Atamande dzina lake povina
ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.
4 Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake;
Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.
5 Oyera mtima asangalale mu ulemu wake
ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.
6 Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo,
ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,
7 kubwezera chilango anthu a mitundu ina,
ndi kulanga anthu a mitundu yonse,
8 kumanga mafumu awo ndi zingwe,
anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,
9 kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo
Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse.
Tamandani Yehova.
150 Tamandani Yehova.
Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika;
mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.
2 Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu;
mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.
3 Mutamandeni poyimba malipenga,
mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.
4 Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina,
mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.
5 Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga,
mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.
6 Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova.
Tamandani Yehova.
9 Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi,
ndi maso anga ngati kasupe wa misozi!
Ndikanalira usana ndi usiku
kulirira anthu anga amene aphedwa.
2 Ndani adzandipatsa malo
ogona mʼchipululu
kuti ndiwasiye anthu anga
ndi kuwachokera kupita kutali;
pakuti onse ndi achigololo,
ndiponso gulu la anthu onyenga.
3 “Amapinda lilime lawo ngati uta.
Mʼdzikomo mwadzaza
ndi mabodza okhaokha
osati zoonadi.
Amapitirirabe kuchita zoyipa;
ndipo sandidziwa Ine.”
Akutero Yehova.
4 “Aliyense achenjere ndi abwenzi ake;
asadalire ngakhale abale ake.
Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu.
Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi.
5 Aliyense amamunamiza mʼbale wake
ndipo palibe amene amayankhula choonadi.
Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza;
amalimbika kuchita machimo.
6 Iwe wakhalira mʼchinyengo
ndipo ukukana kundidziwa Ine,”
akutero Yehova.
7 Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa.
Kodi ndingachite nawonso
bwanji chifukwa cha machimo awo?
8 Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa;
limayankhula zachinyengo.
Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake,
koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.
9 Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
akutero Yehova.
‘Kodi ndisawulipsire
mtundu wotere wa anthu?’ ”
10 Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri
ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu.
Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako,
ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe.
Mbalame zamlengalenga zathawa
ndipo nyama zakuthengo zachokako.
11 Ndipo Yehova anati, “Ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala bwinja,
malo okhalamo ankhandwe;
ndipo ndidzawononga mizinda ya Yuda
kotero kuti palibe munthu amene adzakhalemo.”
12 Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”
13 Yehova anati, “Nʼchifukwa chakuti anthuwa analeka kutsata malamulo anga amene ndinawapatsa; sanandimvere kapena kuwasamala. 14 Mʼmalo mwake, anatsatira zolakwa za mʼmitima yawo; anapembedza Abaala ngati momwe makolo awo anawaphunzitsira.” 15 Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu. 16 Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”
17 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere;
itanani akazi odziwa kulira bwino.”
18 Anthu akuti, “Abwere mofulumira
kuti adzatilire
mpaka mʼmaso mwathu mutatuluka misozi
ndi kuti msidze zathu zinyowe ndi madzi.
19 Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti,
‘Aa! Ife tawonongeka!
Tachita manyazi kwambiri!
Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu
chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’ ”
20 Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova;
tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova.
Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni;
aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.
21 Imfa yatifikira kudzera mʼmazenera athu
ndipo yalowa mʼnyumba zathu zotetezedwa;
yapha ana athu mʼmisewu,
ndi achinyamata athu mʼmabwalo.
22 Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti,
“ ‘Mitembo ya anthu
idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda,
ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola,
popanda munthu woyitola.’ ”
23 Yehova akuti,
“Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake,
kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake,
kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake,
24 koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi:
kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa,
kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo,
chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi.
Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,”
akutero Yehova.
25 “Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe. 26 Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”
Yesu Adzudzula Aphunzitsi Amalamulo ndi Afarisi
23 Pamenepo Yesu anati kwa magulu a anthu ndi ophunzira ake: 2 “Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi amakhala pa mpando wa Mose. 3 Choncho muziwamvera ndi kuchita chilichonse chimene akuwuzani. Koma musachite zimene amachita, popeza sachita zimene amaphunzitsa. 4 Amamanga akatundu olemera nawayika pa mapewa a anthu, koma iwo eni safuna kuwanyamula.
5 “Ntchito zawo amachita ndi cholinga chakuti anthu awaone. Amadzimangirira timaphukusi tikulutikulu ta Mawu a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono komanso amatalikitsa mphonje za mikanjo yawo. 6 Amakonda malo aulemu pa maphwando ndi malo ofunika kwambiri mʼmasunagoge. 7 Amakondwera ndi kupatsidwa moni mʼmisika ndi kutchulidwa kuti ‘Aphunzitsi.’
8 “Koma inu simuyenera kutchulidwa ‘Aphunzitsi,’ popeza muli naye Mbuye mmodzi ndipo inu nonse ndinu abale. 9 Ndipo musamatchule wina aliyense pansi pano kuti ‘Atate,’ pakuti muli ndi Atate mmodzi, ndipo ali kumwamba. 10 Komanso musamatchedwenso ‘Mtsogoleri,’ pakuti muli naye Mtsogoleri mmodzi amene ndi Khristu. 11 Wamkulu pakati panu adzakhala wokutumikirani. 12 Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.
Tsoka kwa Aphunzitsi Amalamulo ndi Afarisi
13 “Tsoka kwa inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumatseka pa khomo la kumwamba kuti anthu asalowemo. Eni akenu simulowamo komanso simulola kuti ena amene akufuna kulowa kuti alowe. 14 Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumawadyera akazi amasiye chuma chawo, kwinaku nʼkumanamizira kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa.
15 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumayenda maulendo ambiri pa mtunda ndi pa nyanja kuti mutembenuze munthu mmodzi, ndipo akatembenuka, mumamusandutsa kukhala mwana wa gehena kawiri kuposa inu.
16 “Tsoka kwa inu, atsogoleri akhungu! Mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula Nyumba ya Mulungu, zilibe kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula ndalama zagolide za mʼNyumbayo, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’ 17 Inu akhungu opusa! Chopambana nʼchiyani: ndalama zagolide, kapena Nyumba imene imayeretsa golideyo? 18 Ndiponso mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula guwa lansembe, sizitanthauza kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula mphatso ya paguwa lansembe, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’ 19 Inu anthu akhungu! Chopambana nʼchiyani: mphatso, kapena guwa limene limayeretsa mphatsoyo? 20 Chifukwa chake, iye amene alumbira kutchula guwa alumbira pa ilo ndi pa chilichonse chili pamenepo. 21 Ndipo iye wolumbira potchula Nyumba ya Mulungu alumbira pa Nyumbayo ndi pa Iye amene amakhala mʼmenemo. 22 Ndipo iye wolumbira kutchula kumwamba alumbira kutchula mpando waufumu wa Mulungu ndi pa Iye wokhalapo.
23 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumapereka chakhumi cha timbewu tonunkhira ndi cha timbewu tokometsera chakudya. Koma mwasiya zofunikira kwambiri za mʼmalamulo monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Muyenera kuchita zomalizirazi komanso osasiya zoyambazo. 24 Atsogoleri akhungu inu! Mumachotsa kantchentche mu chakumwa chanu koma mumameza ngamira.
25 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumayeretsa kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkatimo mwadzaza ndi dyera ndi kusadziretsa. 26 Afarisi akhungu! Poyamba tsukani mʼkati mwa chikho ndi mbale, ndipo kunja kwake kudzakhalanso koyera.
27 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Muli ngati ziliza pa manda zowala kunja zimene zimaoneka zokongola koma mʼkatimo mwadzaza mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zina zonse. 28 Chimodzimodzinso, kunja mumaoneka kwa anthu kuti ndinu olungama koma mʼkatimo ndinu odzaza ndi chinyengo ndi zoyipa zina.
29 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumamanga ziliza za aneneri ndi kukongoletsa manda a olungama. 30 Ndipo mumati, ‘Ngati tikanakhala mʼmasiku a makolo athu sitikanakhetsa nawo magazi a aneneri.’ 31 Potero mukutsimikiza kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri. 32 Dzazani inu muyeso wa uchimo wa makolo anu!
33 “Njoka inu! Ana amamba! Mudzachithawa bwanji chilango cha gehena? 34 Choncho ndi kutumizirani aneneri ndi anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena a iwo mudzawapha ndi kuwapachika; ena mudzawakwapula mʼmasunagoge anu ndi kuwafunafuna kuchokera mudzi wina kufikira wina. 35 Ndipo magazi onse a olungama amene anakhetsedwa pansi pano, kuyambira magazi a Abele, olungama kufikira Zakariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, adzakhala pa inu. 36 Zoonadi, ndikuwuzani kuti zonsezi zidzafika pa mʼbado uno.
37 “Haa! Yerusalemu, Yerusalemu, iwe amene umapha aneneri ndi kugenda miyala amene atumidwa kwa iwe, kawirikawiri ndimafuna kusonkhanitsa ana ako, monga nkhuku imasonkhanitsira ana ake pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune. 38 Taona, nyumba yako yasiyidwa ya bwinja. 39 Chifukwa chake ndikuwuza kuti simudzandionanso kufikira pamene mudzati, ‘Wodala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye.’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.