M’Cheyne Bible Reading Plan
Mayina a Mafumu Ogonjetsedwa
12 Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:
2 Sihoni mfumu ya Aamori,
amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi. 3 Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.
4 Ogi mfumu ya mzinda wa Basani,
amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi. 5 Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.
6 Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.
7 Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. 8 Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:
9 mfumu ya Yeriko | imodzi |
mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli | imodzi |
10 mfumu ya Yerusalemu | imodzi |
mfumu ya Hebroni | imodzi |
11 mfumu ya Yarimuti | imodzi |
mfumu ya Lakisi | imodzi |
12 mfumu ya Egiloni | imodzi |
mfumu ya Gezeri | imodzi |
13 mfumu ya Debri | imodzi |
mfumu ya Gederi | imodzi |
14 mfumu ya Horima | imodzi |
mfumu ya Aradi | imodzi |
15 mfumu ya Libina | imodzi |
mfumu ya Adulamu | imodzi |
16 mfumu ya Makeda | imodzi |
mfumu ya Beteli | imodzi |
17 mfumu ya Tapuwa | imodzi |
mfumu ya Heferi | imodzi |
18 mfumu ya Afeki | imodzi |
mfumu ya Lasaroni | imodzi |
19 mfumu ya Madoni | imodzi |
mfumu ya Hazori | imodzi |
20 mfumu ya Simuroni Meroni | imodzi |
mfumu ya Akisafu | imodzi |
21 mfumu ya Taanaki | imodzi |
mfumu ya Megido | imodzi |
22 mfumu ya Kadesi | imodzi |
mfumu ya Yokineamu ku Karimeli | imodzi |
23 mfumu ya Dori ku Nafoti Dori | imodzi |
mfumu ya Goyini ku Giligala | imodzi |
24 mfumu ya Tiriza | imodzi |
mafumu onse pamodzi analipo 31. |
Mayiko Otsala Oyenera Kulandidwa
13 Yoswa atakalamba Yehova anamuwuza kuti, Iwe tsopano wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa lilipobe lalikulu.
2 “Madera amene atsala ndi awa: chigawo chonse cha Afilisti ndi Agesuri 3 kuchokera ku mtsinje wa Sihori kummawa kwa Igupto mpaka kumpoto kwa dziko la Ekroni. Madera onse amawerengedwa kuti ndi a Akanaani ngakhale amalamulidwa ndi mafumu asanu a Afilisti a ku Gaza, Asidodi, Asikeloni, Gati, Ekroni ndi Agiti, komanso ku Avimu ku chigawo cha kumpoto. 4 Dziko lina la Akanaani ndi Ameara limene lili mʼmanja mwa Asidoni mpaka ku Afeki, dziko limene linachitana malire ndi dziko la Aamori. 5 Palinso dziko lonse la Gebala ndi Lebanoni cha kummawa kuyambira ku Baala-Gadi pa tsinde pa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo Hamati.
6 “Palinso anthu okhala mʼchigawo cha ku mapiri kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Misirefoti-Maimu, Ine ndidzawapirikitsa pamene Aisraeli azidzalowa. Tsono uwagawire Aisraeli dziko limeneli kuti likhale cholowa chawo monga momwe ndakulamulira. 7 Tsopano ugawire dziko limeneli mafuko asanu ndi anayi ndiponso theka la fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”
Kugawidwa kwa Dziko la Kummawa kwa Yorodani
8 Anthu a fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi pamodzi ndi theka lina la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa. Cholowa chawocho chinali kummawa kwa mtsinje wa Yorodani.
9 Dziko lawolo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikizanso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba mpaka ku Diboni. 10 Linkaphatikizanso mizinda yonse ya mfumu Sihoni ya Aamori, imene inkalamulira mu Hesiboni, mpaka ku malire a Aamoni. 11 Dzikoli linaphatikizanso Giliyadi, dziko la anthu a ku Gesuri ndi Maaka, phiri lonse la Herimoni ndi dziko lonse la Basani mpaka ku Saleka. 12 Linaphatikizanso dziko la mfumu Ogi ya ku Basani imene imalamulira kuchokera ku Asiteroti ndi Ederi. Iye yekha ndiye anali mfumu ya Arefaimu amene anapulumuka. Mose anali atawagonjetsa anthu amenewa ndi kuwathamangitsira kutali. 13 Koma Aisraeli sanathamangitse anthu a ku Gesuri ndi Maaka, kotero iwowa amakhalabe pakati pawo mpaka lero.
14 Koma Mose sanapereke dziko kwa fuko la Alevi popeza zopereka zopatulika zimene anthu ankapereka kwa Yehova, Mulungu wa Israeli, ndizo zinali cholowa chawo monga Yehova anawalonjezera.
15 Mose anapereka gawo lina la dziko kwa mabanja a fuko la Rubeni.
16 Dziko lawo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, mʼmudzi wa pakati pa chigwa, ndiponso dera lonse lokwera mpaka ku Medeba. 17 Dzikolo linaphatikizanso Hesiboni ndi mizinda yake yonse, komanso mizinda monga Diboni, Bamoti Baala, Beti-Baala-Meoni, 18 Yahaza, Kedemoti, Mefaati. 19 Kiriataimu, Sibima, Zereti-Sahari, pa phiri limene lili mʼchigwa, 20 Beti-Peori, ku matsitso a Pisiga, ndiponso Beti-Yesimoti. 21 Dzikolo linaphatikizanso mizinda yonse ya ku madera okwera ndiponso dziko lonse la mfumu Sihoni ya Aamori amene ankalamulira kuchokera ku Hesiboni. Mose anamugonjetsa iye pamodzi ndi mafumu a Amidiyani awa: Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu amene anagwirizana ndi Sihoni. Onsewa analamulira dzikolo ngati nduna za Sihoni. 22 Kuwonjezera pa amene anaphedwa ndi nkhondo, Aisraeli anapha ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori, amene amachita za matsenga. 23 Malire a fuko la Rubeni anali mtsinje wa Yorodani. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake zinapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni kuti akhale cholowa chawo.
24 Dera limene Mose anapereka kwa mabanja a fuko la Gadi ndi ili:
25 Dziko la Yazeri, mizinda yonse ya mu Giliyadi ndiponso theka la dziko la Amori kukalekezera ku Aroeri, kufupi ndi Raba; 26 ndiponso kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Ramati-Mizipa, ndi Betonimu; ndiponso kuyambira ku Mahanaimu mpaka ku dziko la Debri. 27 Mu chigwa cha Yorodani analandiramo Beti-Haramu, Beti-Nimira, Sukoti ndi Zafoni pamodzi ndi dziko lonse la mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. Malire ake a ku madzulo anali mtsinje wa Yorodani kufikira ku Nyanja ya Kinereti, kumpoto. 28 Mizinda ndi midzi imeneyi inali cholowa cha mabanja a fuko la Gadi.
29 Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko limeneli kwa theka la mabanja a fuko la Manase kuti likhale cholowa chawo.
30 Derali linayambira ku Mahanaimu kuphatikizapo dziko lonse la mfumu Ogi, Mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi mizinda 60 ya ku Yairi, ku Basaniko. 31 Derali linaphatikizanso theka la Giliyadi pamodzi ndi Asiteroti ndi Ederi, mizinda yayikulu ya mfumu Ogi wa Basani. Mizinda imeneyi inapatsidwa kwa mabanja a Makiri, mwana wa Manase kuti ikhale cholowa cha theka la ana a Makiri, malinga ndi mabanja awo.
32 Umu ndi mmene Mose anagawira malo a mʼchigwa cha Yorodani, kummawa kwa Yeriko, ku tsidya kwa Yorodani. 33 Komatu Mose sanapereke malo kwa fuko la Levi. Mose anawawuza kuti zopereka zimene anthu ankapereka kwa Yehova ndizo cholowa chawo.
Salimo la matamando la Davide.
145 Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga;
ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.
2 Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku
ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.
3 Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse;
ukulu wake palibe angawumvetsetse.
4 Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina;
Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.
5 Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu,
ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.
6 Iwo adzafotokoza za mphamvu ya ntchito zanu zoopsa kwambiri,
ndipo ine ndidzalengeza za ntchito zanu zazikulu.
7 Adzakondwerera kuchuluka kwa ubwino wanu,
ndi kuyimba mwachimwemwe za chilungamo chanu.
8 Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo,
wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.
9 Yehova ndi wabwino kwa onse;
amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.
10 Zonse zimene munazipanga zidzakutamandani, Inu Yehova;
oyera mtima adzakulemekezani.
11 Iwo adzafotokoza za ulemerero wa ufumu wanu
ndi kuyankhula za mphamvu yanu,
12 kuti anthu onse adziwe za machitidwe anu amphamvu
ndi ulemerero wokongola wa ufumu wanu.
13 Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,
ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse.
Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse
ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.
14 Yehova amagwiriziza onse amene akugwa
ndipo amakweza onse otsitsidwa.
15 Maso a onse amayangʼana kwa Inu,
ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera.
16 Mumatsekula dzanja lanu
ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.
17 Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,
ndi wokonda zonse zimene anazipanga.
18 Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana,
onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.
19 Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa;
amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.
20 Yehova amayangʼana onse amene amamukonda
koma adzawononga anthu onse oyipa.
21 Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova.
Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyera
ku nthawi za nthawi.
Kuzingidwa kwa Yerusalemu
6 “Thawani, inu anthu a ku Benjamini!
Tulukani mu Yerusalemu!
Lizani lipenga ku Tekowa!
Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu!
Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto,
ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu.
2 Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri,
kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?
3 Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo;
adzamanga matenti awo mowuzinga,
ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.”
4 Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo!
Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano.
Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka,
ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika.
5 Tsono nyamukani kuti tiwuthire nkhondo mzindawu usiku uno
ndi kuwononga malinga ake!”
6 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Dulani mitengo
ndipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu.
Mzinda umenewu uyenera kulangidwa;
wadzaza ndi kuponderezana.
7 Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi
ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake.
Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo;
nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.
8 Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro,
kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokere
ndi kusandutsa dziko lako kukhala bwinja
mopanda munthu wokhalamo.”
9 Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti,
“Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli,
monga momwe amachitira populula mphesa.
Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe
monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”
10 Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza?
Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve?
Makutu awo ndi otsekeka
kotero kuti sangathe kumva.
Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo;
sasangalatsidwa nawo.
11 Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,
ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova.
Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu
ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi;
pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa,
pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.
12 Nyumba zawo adzazipereka kwa ena,
pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo.
Ndidzatambasula dzanja langa kukantha
anthu okhala mʼdzikomo,”
akutero Yehova.
13 “Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,
onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba;
aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,
onse amachita zachinyengo.
14 Amapoletsa zilonda za anthu anga
pamwamba pokha.
Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’
pamene palibe mtendere.
15 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo?
Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe;
sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe.
Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;
adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,”
akutero Yehova.
16 Yehova akuti,
“Imani pa mphambano ndipo mupenye;
kumeneko ndiye kuli njira zakale,
funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo,
ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’
17 Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni
ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’
koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’
18 Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina;
yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano,
chimene chidzawachitikire anthuwo.
19 Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi,
ndikubweretsa masautso pa anthu awa.
Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo.
Iwowa sanamvere mawu anga
ndipo anakana lamulo langa.
20 Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba,
kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali?
Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira;
nsembe zanu sizindikondweretsa.”
21 Choncho Yehova akuti,
“Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa.
Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa;
anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”
22 Yehova akunena kuti,
“Taonani, gulu lankhondo likubwera
kuchokera kumpoto;
mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka
kuchokera kumathero a dziko lapansi.
23 Atenga mauta ndi mikondo;
ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo.
Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja.
Akwera pa akavalo awo
ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo,
kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”
24 A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo,
ndipo manja anthu alefukiratu.
Nkhawa yatigwira,
ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.
25 Musapite ku minda
kapena kuyenda mʼmisewu,
pakuti mdani ali ndi lupanga,
ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.
26 Inu anthu anga, valani ziguduli
ndipo gubudukani pa phulusa;
lirani mwamphamvu
ngati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha,
pakuti mwadzidzidzi wowonongayo
adzabwera kudzatipha.
27 “Iwe Yeremiya, ndakuyika kuti ukhale choyesera zitsulo.
Uwayese anthu anga
monga ungayesere chitsulo
kuti uwone makhalidwe awo.
28 Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukira
ndipo akunka nanena zamiseche.
Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo.
Onse amangochita zoyipa zokhazokha.
29 Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri;
mtovu watha kusungunuka ndi moto.
Koma ntchito yosungunulayo sikupindula
chifukwa zoyipa sizikuchokapo.
30 Iwo ali ngati siliva wotayidwa,
chifukwa Yehova wawakana.”
Fanizo la Aganyu Mʼmunda wa Mphesa
20 “Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa. 2 Anagwirizana kuwalipira dinari monga malipiro a tsiku limodzi ndipo anawatumiza mʼmunda wake wamphesa.
3 “Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala. 4 Anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa, ndipo ndidzakulipirani malipiro oyenera.’ 5 Ndipo anapita.
“Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi. 6 Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’
7 “Iwo anayankha kuti, ‘Chifukwa palibe munthu amene watilemba ganyu.’
“Iye anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa.’
8 “Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’
9 “Antchito amene anawalemba ganyu pa 5 koloko masana anafika ndipo aliyense analandira dinari. 10 Ndipo atabwera kwa amene analembedwa poyamba anayembekezera kuti alandira zambiri. Koma aliyense wa iwo analandira dinari. 11 Atalandira, anayamba kuderera kwa mwini mundayo. 12 Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’
13 “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari? 14 Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe. 15 Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’
16 “Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.”
Yesu Anenanso za Imfa Yake
17 Tsopano pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, anatengera pambali ophunzira ake khumi ndi awiriwo nati kwa iwo, 18 “Tikupita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo adzamuweruza kuti aphedwe, 19 ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!”
Pempho la Mkazi wa Zebedayo
20 Amayi a ana a Zebedayo anabwera ndi ana ake kwa Yesu, nagwada pansi namupempha Iye.
21 Yesu anawafunsa kuti, “Mukufuna chiyani?”
Amayiwo anati, “Lolani kuti ana anga awiriwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja ndi wina ku dzanja lanu lamazere mu ufumu wanu.”
22 Yesu anawawuza kuti, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwera chikho chimene ndidzamwera Ine?”
Iwo anayankha nati, “Inde tingathe.”
23 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga.”
24 Ophunzira khumi aja, anawapsera mtima abale awiriwo. 25 Yesu anawayitana onse pamodzi nati, “Mukudziwa kuti olamulira a mitundu ina ali ndi mphamvu pa iwo, ndipo akuluakulu awo amawalamulira. 26 Siziyenera kutero ndi inu. Mʼmalo mwake, aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu akhale wotumikira wanu. 27 Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu. 28 Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”
Yesu Achiritsa Anthu Awiri Osaona
29 Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata. 30 Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”
31 Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”
32 Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?”
33 Anamuyankha nati, “Ambuye, tikufuna tione!”
34 Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.