M’Cheyne Bible Reading Plan
Kugonjetsedwa kwa Mafumu a Kumpoto
11 Yabini, mfumu ya Hazori, inamva zimene zinachitikazi. Tsono inatumiza uthenga kwa Yobabu mfumu ya Madoni, ndiponso kwa mafumu a ku Simironi ndi Akisafu. 2 Inatumizanso uthenga kwa mafumu a kumpoto, kumapiri, ndi mʼchigwa cha Yorodani kummwera kwa nyanja ya Kinereti, ndiponso kumadzulo mʼmbali mwa nyanja pafupi ndi Dori. 3 Inatumizanso uthenga kwa Akanaani amene ankakhala kummawa ndi kumadzulo kwa Yorodani. Uthenga unapitanso kwa Aamori, Ahiti, Aperezi ndi Ayebusi amene amakhala mʼdziko la ku mapiri ndiponso kwa Ahivi amene ankakhala mʼmunsi mwa phiri la Herimoni ku chigwa cha Mizipa. 4 Mafumuwo anabwera pamodzi ndi ankhondo awo onse. Gulu la ankhondo linali lalikulu ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Analinso ndi akavalo ndi magaleta ambiri. 5 Mafumu onsewa anasonkhana pamodzi ndipo anamanga misasa yawo ku mtsinje wa Meromu, kuti amenyane ndi Israeli.
6 Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzawapereka kuti muwaphe. Akavalo awo muwadule matsinde ndipo magaleta awo muwatenthe ndi moto.”
7 Kotero Yoswa pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo anafika kwa adani awo aja ku mtsinje wa Meromu modzidzimutsa ndi kuwathira nkhondo. 8 Yehova anawapereka mʼmanja mwa Israeli mwakuti anawagonjetseratu ndi kuwapirikitsa njira yonse mpaka ku Sidoni Wamkulu ndi ku Misirefoti Maimu, ndiponso kummawa ku chigwa cha Mizipa. Onse anaphedwa popanda wopulumuka. 9 Yoswa anawachita zimene Yehova analamula. Iye anadula matsinde a akavalo awo ndi kutentha magaleta awo.
10 Pambuyo pake Yoswa anabwera nalanda mzinda wa Hazori ndi kupha mfumu yake. (Nthawi imeneyo mzinda wa Hazori unali wopambana mizinda ina yonse). 11 Anapha aliyense wa mu mzindamo popanda wotsala wamoyo, ndipo mzinda wa Hazori anawutentha ndi moto.
12 Yoswa analanda mizinda yonse ndi mafumu ake. Anthu onse anaphedwa ndi lupanga monga momwe analamulira Mose, mtumiki wa Yehova. 13 Israeli sanatenthe mizinda yomangidwa pa zitunda, kupatula mzinda wa Hazori, umene Yoswa anawutentha. 14 Aisraeli anatenga zinthu zonse za mʼmizindayi pamodzi ndi ziweto kuti zikhale zawo, koma anapha anthu onse ndi lupanga osasiyako ndi mmodzi yemwe wamoyo. 15 Monga momwe Yehova analamulira mtumiki wake Mose, nayenso Mose analamulira Yoswa ndipo Yoswa anachita chilichonse chimene Yehova analamulira Mose.
16 Kotero Yoswa analanda dziko lonse: dziko la ku mapiri, dera lonse la Negevi, chigawo chonse cha Goseni, ndi chigwa chake chonse, chigwa cha Yorodani, dziko lonse la lamapiri la Israeli pamodzi ndi chigwa chake chomwe. 17 Dziko lolandidwalo linayambira ku phiri la Halaki limene linali ku Seiri mpaka ku Baala-Gadi mʼchigwa cha Lebanoni, kumunsi kwa phiri la Herimoni. Yoswa anagwira ndi kupha mafumu a dziko lonselo 18 atachita nawo nkhondo kwa nthawi yayitali. 19 Palibe ngakhale ndi mfumu imodzi yomwe imene inachita mgwirizano wa mtendere ndi Aisraeli kupatula Ahivi okhala ku Gibiyoni. Koma mizinda ina yonse anachita kuyigonjetsa pa nkhondo. 20 Yehova anali atawumitsa mitima yawo kuti alimbane ndi Aisraeli kuti aphedwe popanda kuchitiridwa chifundo. Izi ndi zimene Yehova analamula Mose kuti zichitidwe.
21 Pa nthawi imeneyi Yoswa anapita kukawononga Aanaki okhala mʼdziko lija la ku mapiri ku Hebroni, Debri, Anabu komanso madera onse a ku mapiri a Yuda ndi Israeli. Yoswa anawawononga onse pamodzi ndi mizinda yawo. 22 Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsalako mʼdziko lonse la Israeli; komabe ku Gaza, ku Gati ndi Asidodi kokha ndi kumene anatsalako pangʼono. 23 Choncho Yoswa anagonjetsa dziko lonse monga momwe Yehova analamulira Mose. Tsono Yoswa analipereka kwa Aisraeli kuti likhale lawo, fuko lililonse gawo lake.
Anthu onse anapumula, osamenyanso nkhondo.
Salimo la Davide.
144 Atamandike Yehova Thanthwe langa,
amene amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;
zala zanga kumenya nkhondo.
2 Iye ndiye Mulungu wanga wachikondi ndi malo anga otetezedwa,
linga langa ndi mpulumutsi wanga,
chishango changa mmene ine ndimathawiramo,
amene amagonjetsa mitundu ya anthu pansi panga.
3 Inu Yehova, munthu nʼchiyani kuti mumamusamalira,
mwana wa munthu kuti muzimuganizira?
4 Munthu ali ngati mpweya;
masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.
5 Ngʼambani mayiko akumwamba, Inu Yehova, ndipo tsikani pansi;
khudzani mapiri kuti atulutse utsi.
6 Tumizani zingʼaningʼani ndi kubalalitsa adani;
ponyani mivi yanu ndi kuwathamangitsa.
7 Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba;
landitseni ndi kundipulumutsa,
ku madzi amphamvu,
mʼmanja mwa anthu achilendo,
8 amene pakamwa pawo ndi podzala ndi mabodza,
amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.
9 Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano Inu Mulungu;
ndidzakuyimbirani nyimbo pa zeze wa nsambo khumi,
10 kwa Iye amene amapambanitsa mafumu,
amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.
11 Landitseni ndi kundipulumutsa,
mʼmanja mwa anthu achilendo,
amene pakamwa pawo ndi podzaza ndi mabodza,
amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.
12 Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo
adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino,
ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala
zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.
13 Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza
ndi zokolola za mtundu uliwonse.
Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda
pa mabusa athu.
14 Ngʼombe zathu zidzanyamula katundu wolemera.
Sipadzakhala mingʼalu pa makoma,
sipadzakhalanso kupita ku ukapolo,
mʼmisewu mwathu simudzakhala kulira chifukwa cha mavuto.
15 Odala anthu amene adzalandira madalitso awa;
odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.
Palibe Munthu Wolungama
5 “Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu,
mudzionere nokha,
funafunani mʼmabwalo ake.
Ngati mungapeze munthu mmodzi
amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi,
ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.
2 Ngakhale anthu akulumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’
komabe akungolumbira mwachinyengo.”
3 Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona?
Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka;
munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro.
Anawumitsa mitima yawo ngati mwala
ndipo anakaniratu kulapa.
4 Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe;
anthu ochita zopusa.
Sadziwa njira ya Yehova,
sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.
5 Tsono ndidzapita kwa atsogoleri
ndi kukayankhula nawo;
ndithu iwo amadziwa njira ya Yehova,
amadziwa zomwe Mulungu wawo amafuna.”
Koma ayi, iwonso anathyola goli la Yehova
ndipo anadula msinga zawo.
6 Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha,
mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga,
kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawo
kuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamo
pakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulu
ndipo abwerera mʼmbuyo kwambiri.
7 Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita?
Ana anu andisiya Ine
ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse.
Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa,
komabe iwo anachita chigololo
namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.
8 Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa,
aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake.
9 Tsono ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?”
akutero Yehova.
“Kodi nʼkuleka kuwulipsira
mtundu woterewu?
10 “Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga,
koma musakayiwononge kotheratu.
Sadzani nthambi zake
pakuti anthu amenewa si a Yehova.
11 Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yuda
onse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.”
12 Iwowa ankanama ponena za Yehova kuti,
“Yehova sangachite zimenezi!
Choyipa sichidzatigwera;
sitidzaona nkhondo kapena njala.
13 Mawu a aneneri azidzangopita ngati mphepo;
ndipo mwa iwo mulibe uthenga wa Yehova.
Choncho zimene amanena zidzawachitikira okha.”
14 Chifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akuti,
“Popeza kuti anthu awa ayankhula mawu amenewa,
tsono mawu anga ndidzawasandutsa moto mʼkamwa mwako
ndipo anthu awa ndidzawasandutsa nkhuni zimene moto udzapserezeretu.
15 Inu Aisraeli,” Yehova akuti,
“Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali,
ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo,
mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa,
zimene akunena inu simungazimvetse.
16 Zida zawo za nkhondo zapha anthu ambirimbiri;
onsewo ndi ankhondo amphamvu okhaokha.
17 Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu,
adzapha ana anu aamuna ndi aakazi;
adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu,
adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu.
Ndi malupanga awo adzagwetsa
mizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.
18 “Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova. 19 Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”
20 “Lengeza izi kwa ana a Yakobo
ndipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti,
21 Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru,
inu amene maso muli nawo koma simupenya,
amene makutu muli nawo koma simumva.
22 Kodi simuyenera kuchita nane mantha?”
Akutero Yehova.
“Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga?
Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,
malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo.
Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo;
mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
23 Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira;
andifulatira ndipo andisiyiratu.
24 Sananenepo mʼmitima mwawo kuti,
‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu.
Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika.
Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
25 Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi;
ndipo machimo anu akumanitsani zabwino.
26 “Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa
amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame
ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.
27 Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo
ngati zikwere zodzaza ndi mbalame.
Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera.
28 Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala.
Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire;
saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino,
sateteza ufulu wa anthu osauka.
29 Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
Kodi ndisawulipsire
mtundu woterewu?
Akutero Yehova.
30 “Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambiri
chachitika mʼdzikomo:
31 Aneneri akunenera zabodza,
ndipo ansembe akuvomerezana nawo,
ndipo anthu anga akukonda zimenezi.
Koma mudzatani potsiriza?
Za Kuthetsa Ukwati
19 Yesu atatsiriza kunena zinthu zimenezi, anachoka ku Galileya ndi kupita ku chigawo cha Yudeya mbali ina ya mtsinje wa Yorodani. 2 Magulu akulu a anthu anamutsatira Iye, ndipo iwo anachiritsidwa pomwepo.
3 Afarisi ena anabwera kwa Iye kudzamuyesa. Anamufunsa Iye nati, “Kodi ndikololedwa kuti mwamuna amuleke mkazi wake pa chifukwa china chilichonse?”
4 Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge kuti pachiyambi Mulungu analenga iwo, ‘mwamuna ndi mkazi?’ 5 Ndipo anati, ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ 6 Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse.”
7 Ndipo iwo anamufunsa nati, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa?”
8 Yesu anayankha kuti, “Mose anakulolezani kuti muzisudzula akazi anu chifukwa cha kuwuma mitima kwanu. Koma sizinali chotere kuyambira pachiyambi. 9 Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere nakakwatira mkazi wina, achita chigololo.”
10 Ophunzira ake anati kwa Iye, “Ngati umu ndi mmene zilili pa mwamuna ndi mkazi, kuli bwino kusakwatira.”
11 Yesu anayankha kuti, “Si aliyense amene angavomere chiphunzitso ichi, koma kwa okhawo amene achimvetsetsa. 12 Pakuti ena ndi akuti sangakwatire chifukwa anabadwa motero, ena ali motero chifukwa chofulidwa ndi anthu ndipo ena anawukana ukwati chifukwa cha ufumu wakumwamba. Iye amene angalandire ichi alandire.”
Yesu Adalitsa Ana
13 Pamenepo anabwera nawo ana kwa Yesu kuti awasanjike manja ndi kuwapempherera. Koma ophunzira ake anadzudzula amene anabweretsa anawo.
14 Yesu anati, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa.” 15 Atasanjika manja ake pa anawo, anachokapo.
Mnyamata Wolemera ndi Ufumu wa Mulungu
16 Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?”
17 Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.”
18 Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?”
Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama, 19 lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.”
20 Mnyamatayo anati, “Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?”
21 Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.”
22 Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri.
23 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. 24 Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.”
25 Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, “Nanga angapulumuke ndani?”
26 Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”
27 Petro anamuyankha Iye kuti, “Ife tinasiya zonse ndi kukutsatirani Inu! Nanga tsono ife tidzalandira chiyani?”
28 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli. 29 Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha. 30 Koma ambiri amene ali oyambirira adzakhala omalizira, ndipo ambiri amene ndi omalizira adzakhala oyambirira.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.