Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yoswa 6:6-27

Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anayitana ansembe ndipo anawawuza kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano cha Yehova ndipo ansembe asanu ndi awiri anyamule malipenga. Iwowa akhale patsogolo pake.” Ndipo analamulira anthu kuti, “Yambani kuyenda! Yendani mozungulira mzinda ndipo ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi la Yehova.”

Mofanana ndi mmene Yoswa anayankhulira kwa anthu aja, ansembe asanu ndi awiri anapita patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Yehova akuliza malipenga a nyanga za nkhosa zija, ndipo Bokosi la Chipangano cha Yehova limabwera pambuyo pawo. Ankhondo amayenda patsogolo pa ansembe amene amayimba malipenga, ndiponso gulu lina pambuyo pa Bokosilo. Nthawi yonseyi nʼkuti malipenga akulira. 10 Koma Yoswa nʼkuti atalamulira anthu kuti, “Musafuwule, musakweze mawu anu kapena kuyankhula mpaka tsiku limene ndidzakuwuzani kuti mufuwule. Pamenepo mudzafuwule!” 11 Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anazungulira mzindawo kamodzi. Kenaka anthu anabwerera ku msasa wawo kukagona.

12 Yoswa anadzuka mmawa tsiku linalo ndipo ansembe ananyamula Bokosi la Yehova. 13 Ansembe asanu ndi awiri onyamula malipenga asanu ndi awiri anakhala patsogolo pa Bokosi la Yehova akuyimba malipenga. Ankhondo anali patsogolo pawo ndipo gulu lina linatsatira Bokosi la Yehova. Apa nʼkuti malipenga akulira. 14 Tsiku lachiwiri anazunguliranso mzinda kamodzi ndi kubwerera ku misasa. Iwo anachita izi kwa masiku asanu ndi limodzi.

15 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, anadzuka mʼbandakucha ndipo anazungulira mzindawo kasanu ndi kawiri. Ndi pa tsiku lokhali limene anazungulira mzindawu kasanu ndi kawiri. 16 Pomwe amazungulira kachisanu ndi chiwiri, ansembe akuliza malipenga mokweza, Yoswa analamulira anthu kuti “Fuwulani pakuti Yehova wakupatsani mzindawu! 17 Mzindawu ndi zonse zimene zili mʼmenemo muziwononge. Rahabe yekha, mayi wadama, ndi aliyense amene ali pamodzi naye mʼnyumba mwake asaphedwe, chifukwa anabisa anthu odzazonda, amene ife tinawatuma 18 Koma musatenge kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa. Mukadzangotenga kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa, mudzaputa mavuto, misasa ya Israeli idzawonongedwa. 19 Zonse za siliva ndi golide, ziwiya zamkuwa ndi zachitsulo, ndi zake za Yehova ndipo ziyenera kukasungidwa mosungiramo chuma chake.”

20 Ansembe analiza malipenga. Anthu atamva kulira kwa malipenga, anafuwula kwambiri ndipo makoma a Yeriko anagwa. Choncho ankhondo anabwera ku mzinda uja nawulanda. 21 Iwo analowa mu mzindawo nawononga ndi lupanga chilichonse chamoyo kuyambira amuna, akazi, ana ndi akulu, ngʼombe, nkhosa ndi abulu.

22 Yoswa anawuza anthu awiri amene anakazonda dziko aja kuti, “Pitani ku nyumba ya mkazi wadama uja ndipo mukamutulutse iye pamodzi ndi onse amene ali naye ndipo mukabwere nawo kuno, munamulumbirira.” 23 Choncho iwo anapita nakatenga Rahabe, abambo ake ndi amayi ake, abale ake ndi onse amene anali naye. Iwo anatulutsa banja lake lonse ndipo analiyika kuseri kwa msasa wa Aisraeli.

24 Kenaka iwo anawotcha mzinda wonse ndi chilichonse chimene chinali mʼmenemo, kupatulapo zasiliva ndi zagolide pamodzi ndi ziwiya zamkuwa ndi zachitsulo zimene anakaziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha Yehova. 25 Koma Yoswa sanaphe Rahabe, mkazi wadamayo pamodzi ndi banja lake ndi onse amene anali naye, chifukwa anabisa anthu amene iye anawatuma kukazonda Yeriko. Zidzukulu zake za Rahabeyo zikukhala pakati pa Aisraeli mpaka lero.

26 Pa nthawi imeneyo Yoswa anapereka chenjezo motemberera kuti, “Akhale wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzamangenso mzinda uwu wa Yeriko:

“Aliyense amene adzayike maziko ake,
    mwana wake wamwamuna wachisamba adzafa,
aliyense womanga zipata zake
    mwana wake wamngʼono adzafa.”

27 Motero Yehova anali ndi Yoswa, ndipo mbiri yake inafalikira dziko lonse.

Masalimo 135-136

135 Tamandani Yehova.

Tamandani dzina la Yehova;
    mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova,
    mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.

Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino;
    imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,
Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake,
    Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.

Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu,
    kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.
Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera,
    kumwamba ndi dziko lapansi,
    ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi,
    amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula
    ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.

Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,
    ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.
Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto,
    kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.
10 Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu
    ndi kupha mafumu amphamvu:
11 Sihoni mfumu ya Aamori,
    Ogi mfumu ya Basani,
    ndi maufumu onse a ku Kanaani;
12 ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa,
    cholowa cha anthu ake Aisraeli.

13 Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya,
    mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.
14 Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa,
    ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.

15 Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide,
    opangidwa ndi manja a anthu.
16 Pakamwa ali napo koma sayankhula
    maso ali nawo, koma sapenya;
17 makutu ali nawo, koma sakumva
    ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.
18 Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo,
    chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.

19 Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova;
    inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;
20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova;
    Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.
21 Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni,
    amene amakhala mu Yerusalemu.

Tamandani Yehova.
136 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino.
Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
Yamikani Mulungu wa milungu.
Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
Yamikani Ambuye wa ambuye,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Iye yekhayo amene amachita zodabwitsa zazikulu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
Amene anapanga miyuni ikuluikulu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
Dzuwa lilamulire usana,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
Mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

10 Amene anakantha ana woyamba kubadwa a Igupto,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
11 Natulutsa Israeli pakati pawo,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
12 Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

13 Amene anagawa Nyanja Yofiira pakati,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
14 Nadutsitsa Israeli pakati pa nyanjayo,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
15 Koma anakokolola Farao ndi ankhondo ake mʼNyanja Yofiira,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

16 Amene anatsogolera anthu ake mʼchipululu
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
17 Amene anakantha mafumu akuluakulu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
18 Napha mafumu amphamvu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
19 Siloni mfumu ya Aamori,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
20 Ogi mfumu ya Basani,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
21 Napereka dziko lawo ngati cholowa,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
22 Cholowa cha mtumiki wake Israeli;
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

23 Amene anatikumbukira ife anthu opeputsidwa,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
24 Amene anatimasula kwa adani athu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
25 Amene amapereka chakudya kwa cholengedwa chilichonse,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

26 Yamikani Mulungu wakumwamba,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Yesaya 66

Chiweruzo ndi Chiyembekezo

66 Yehova akuti,

“Kumwamba ndi mpando wanga waufumu
    ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.
Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire,
    ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?
Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi,
    motero zonsezi ndi zanga?”
            Akutero Yehova.

“Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu:
    amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima,
    ndipo amamvera mawu anga.
Koma aliyense amene amapereka nsembe ngʼombe yayimuna
    amaphanso munthu,
ndipo aliyense amene amapereka mwana wankhosa,
    amaphanso galu.
Aliyense amene amapereka nsembe chopereka cha chakudya
    amaperekanso magazi a nkhumba.
Ndipo amene amafukiza lubani pa guwa lansembe la chikumbutso
    amapembedzanso fano.
Popeza iwo asankha njira zawozawo,
    ndiponso kusangalatsidwa ndi zonyansa zawo.
Inenso ndawasankhira chilango chowawa
    ndipo ndidzabweretsa pa iwo zimene amaziopa zija.
Pakuti pamene ndinawayitana palibe amene anayankha,
    pamene ndinayankhula palibe amene anatchera khutu.
Anachita zoyipa pamaso panga
    ndi kusankha kuchita zimene zimandinyansa zija.”

Imvani mawu a Yehova,
    inu amene mumanjenjemera ndi mawu ake:
“Abale anu amene amakudani,
    ndi kukuchotsani pakati pawo chifukwa cha dzina langa, amanena kuti,
‘Yehova alemekezeke
    kuti ife tione chimwemwe chanu!’
    Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.
Imvani mfuwu mu mzinda,
    imvani phokoso mʼNyumba ya Mulungu!
Limenelo ndi liwu la Yehova,
    kulanga adani ake onse.

“Mzinda uli ngati amayi apakati amene asanayambe kumva zowawa
    wachira kale;
asanayambe kumva ululu,
    wabala kale mwana wamwamuna.
Ndani anamvapo zinthu zoterezi?
    Ndani anazionapo zinthu zoterezi?
Kodi dziko nʼkupangika tsiku limodzi,
    kapena mtundu wa anthu nʼkubadwa tsiku limodzi?
Komatu Ziyoni atangoyamba kumva zowawa
    nthawi yomweyo anabereka ana ake.
Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira,
    koma osalola kuti abaledi mwana?” akutero Yehova.
“Kodi ndingatseke mimba
    pa nthawi yoti abeleke?” akutero Mulungu wako.
10 “Kondwera nayeni Yerusalemu ndipo musangalale chifukwa cha Iye,
    inu nonse amene mumakonda Yerusalemu,
kondwera nayeni kwambiri,
    nonse amene mumamulira.
11 Pakuti mudzagawana naye ulemerero wake
    ngati kuyamwa ndi kukhuta mkaka wambiri
wa mʼmawere
    a chitonthozo chake.”

12 Yehova akuti,

“Ndidzamupatsa mtendere ngati mtsinje wa madzi,
    ndiponso chuma cha anthu a mitundu ina ngati mtsinje wosefukira.
Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene amayi ake amunyamulira pambalipa,
    kapena kumufungata pa miyendo yake.
13 Monga momwe amayi amasangalatsira mwana wawo,
    moteronso Ine ndidzakusangalatsani;
    ndipo mudzasangalala chifukwa cha Yerusalemu.”

14 Mukadzaona zimenezi mitima yanu idzakondwera. Mudzabiriwira ngati udzu.
    Zimenezi zidzakulimbikitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu.
Mudzadziwa kuti ndimathandiza amene amanditumikira
    ndi kuti ndimakwiyira adani anga.
15 Taonani, Yehova akubwera ngati moto,
    ndipo magaleta ake ali ngati kamvuluvulu;
Iye adzaonetsa mkwiyo wake nadzalanga adani ake
    ndi malawi amoto.
16 Pakuti Yehova adzalanga anthu onse
    ndi moto ndi lupanga,
    Yehova adzapha anthu ambiri.

17 Yehova akuti, “Amene amadzipatula ndi kudziyeretsa okha kuti apite ku minda, ali ndi mtsogoleri awo, nʼkumadya nyama ya nkhumba, mbewa ndi zinthu zina zonyansa, onsewa adzafera limodzi.”

18 “Ndipo Ine, chifukwa cha zochita zawo ndi maganizo awo, ndili pafupi kubwera kudzasonkhanitsa mitundu yonse ya anthu ndi ziyankhulo zonse. Iwo adzabwera ndi kuona ulemerero wanga.

19 “Ndidzayika chizindikiro pakati pawo, ndipo ndidzatumiza ena mwa iwowa amene anapulumuka kuti apite kwa anthu a mitundu ina inu ku Tarisisi, ku Libiya ndi ku Ludi (akatswiri a mauta) ku Tubala ndi Grisi, ndi ku mayiko akutali a mbali mwa nyanja amene sanamvepo za mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina. 20 Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo. 21 Ndipo ndidzasankha ena mwa iwonso kukhala ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova.

22 “Monga momwe mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ndidzapanga zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, ndi chonchonso dzina lanu ndi zidzukulu zanu zidzakhalire.” Akutero Yehova. 23 “Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala pa mwezi watsopano ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Yehova. 24 “Akamachoka adzaona mitembo ya anthu amene anandiwukira Ine. Mphutsi zawo sizidzafa, kapena moto wawo sudzazimitsidwa. Anthu a mitundu ina yonse powaona adzanyansidwa nawo.”

Mateyu 14

Kuphedwa kwa Yohane Mʼbatizi

14 Pa nthawi imeneyo Mfumu Herode anamva za mbiri ya Yesu. Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.”

Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo. Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.” Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri.

Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri. Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe. Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.” Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe; 10 ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende. 11 Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake. 12 Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu.

Yesu Adyetsa Anthu 5,000

13 Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda. 14 Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo.

15 Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”

16 Yesu anawayankha kuti, “Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.”

17 Iwo anayankha kuti, “Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri.”

18 Koma Iye anati, “Bweretsani kwa Ine.” 19 Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu. 20 Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri. 21 Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.

Yesu Ayenda pa Nyanja

22 Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo. 23 Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha. 24 Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo.

25 Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja. 26 Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo analira chifukwa cha mantha.

27 Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, “Limbani mtima! Ndine, musaope.”

28 Petro anayankha nati, “Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo.”

29 Iye anati, “Bwera.”

Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu. 30 Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!”

31 Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati, “Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?”

32 Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka. 33 Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”

34 Atawoloka, anafika ku Genesareti. 35 Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye. 36 Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.