M’Cheyne Bible Reading Plan
Mwambo wa Mdulidwe pa Giligala
5 Mafumu onse a Aamori, a kummawa kwa Yorodani ndi mafumu onse a Akanaani a mʼmbali mwa Nyanja anamva momwe Yehova anawumitsira Yorodani pamene Aisraeli ankawoloka. Choncho anachita mantha ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraeliwo.
2 Tsono Yehova anati kwa Yoswa, “Panga mipeni ya miyala ndipo uchitenso mwambo wa mdulidwe pa Aisraeli.” 3 Choncho Yoswa anapanga mipeni ya miyala ndi kuchita mdulidwe Aisraeli ku Gibeyati Haaraloti.
4 Chifukwa chimene Yoswa anachitira izi ndi ichi: Onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto, amuna onse amene anali oyenera kumenya nkhondo anatha kufa mʼchipululu atatuluka mʼdziko la Igupto. 5 Anthu onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto anali atachita mwambo wa mdulidwe, koma onse amene anabadwira mʼchipululu, pa ulendo wochoka ku Igupto, sanachite. 6 Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa. 7 Koma ana awo amene analowa mʼmalo mwawo ndiwo amene Yoswa anawachita mdulidwe popeza sanachite pamene anali pa ulendo wawo mʼchipululu muja. 8 Atamaliza kuchita mdulidwe uja, anthu onse anakakhala ku misasa yawo kudikira kuti zilonda zipole.
9 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Kuyambira tsopano anthu a ku Igupto sadzakunyozaninso.” Nʼchifukwa chake malowa anatchedwa Giligala mpaka lero.
10 Akupumulabe ku Giligala kuja mʼchigwa cha Yeriko, Aisraeli anachita chikondwerero cha Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo. 11 Mmawa mwake ndi pamene anayamba kudya zakudya za mʼdziko la Kanaani. Anaphika buledi wopanda yisiti ndi kukazinga tirigu tsiku lomwelo. 12 Atangodya chakudya cha mʼdzikomo, mana anasiya kugwa, ndipo sanapezekenso. Kuyambira nthawi imeneyo Aisraeli anayamba kudya chakudya cha mʼdziko la Kanaani.
Kugwa kwa Makoma a Yeriko
13 Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo mwadzidzidzi anaona munthu atayima patsogolo pake ndi lupanga losolola mʼdzanja lake. Yoswa anapita pamene panali munthuyo ndipo anamufunsa kuti, “Kodi uli mbali yathu kapena ya adani athu?”
14 Iye anayankha kuti “Sindili mbali iliyonse. Ndabwera monga mkulu wa asilikali a Yehova.” Pomwepo Yoswa anadzigwetsa chafufumimba kupereka ulemu, ndipo anamufunsa, “Kodi mbuye wanga muli ndi uthenga wotani kwa mtumiki wanu?”
15 Mkulu wa asilikali a Yehova uja anayankha kuti, “Vula nsapato zako, pakuti wayima pa malo wopatulika.” Ndipo Yoswa anachitadi zimene anawuzidwazo.
6 Tsono mzinda wa Yeriko unali utatsekedwa kuti Aisraeli asalowe. Palibe amene amatuluka kapena kulowa.
2 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Taona ndapereka Yeriko, pamodzi ndi mfumu yake ndi ankhondo ake mʼmanja mwako. 3 Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse muzizungulira mzindawu masiku asanu ndi limodzi, kamodzi pa tsiku. 4 Ansembe asanu ndi awiri, atanyamula malipenga a nyanga za nkhosa zazimuna, akhale patsogolo pa Bokosi la Chipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzazungulire mzindawu kasanu ndi kawiri ansembe akuliza malipenga. 5 Ansembe adzalize malipenga kosalekeza. Tsono anthu onse akadzamva kuliza kumeneku adzafuwule kwambiri, ndipo makoma a mzindawo adzagwa. Zikadzatero ankhondo adzalowe mu mzindawo.”
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
132 Inu Yehova, kumbukirani Davide
ndi mavuto onse anapirira.
2 Iye analumbira kwa Yehova
ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,
3 “Sindidzalowa mʼnyumba mwanga
kapena kugona pa bedi langa:
4 sindidzalola kuti maso anga agone,
kapena zikope zanga ziwodzere,
5 mpaka nditamupezera malo Yehova,
malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”
6 Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata,
tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:
7 “Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo;
tiyeni tikamulambire pa mapazi ake.
8 ‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira,
Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
9 Ansembe anu avekedwe chilungamo;
anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’ ”
10 Chifukwa cha Davide mtumiki wanu,
musakane wodzozedwa wanu.
11 Yehova analumbira kwa Davide,
lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha:
“Mmodzi wa ana ako
ndidzamuyika pa mpando waufumu;
12 ngati ana ako azisunga pangano langa
ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa,
pamenepo ana awo adzakhala pa mpando
wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”
13 Pakuti Yehova wasankha Ziyoni,
Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo:
14 “Awa ndi malo anga opumapo ku nthawi za nthawi;
ndidzakhala pano pa mpando waufumu, pakuti ndakhumba zimenezi.
15 Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri;
anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya.
16 Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso,
ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe.
17 “Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide
ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
18 Ndidzaveka adani ake manyazi,
koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala.”
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
133 Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu
pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!
2 Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu,
otsikira ku ndevu,
ku ndevu za Aaroni,
oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake.
3 Zili ngati mame a ku Heremoni
otsikira pa Phiri la Ziyoni.
Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso,
ndiwo moyo wamuyaya.
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
134 Bwerani, mutamande Yehova, inu atumiki onse a Yehova,
amene mumatumikira usiku mʼnyumba ya Yehova.
2 Kwezani manja anu mʼmalo opatulika
ndipo mutamande Yehova.
3 Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
akudalitseni kuchokera mʼZiyoni.
Chiweruzo ndi Chipulumutso
65 “Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu;
ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze.
Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine,
ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’
2 Tsiku lonse ndatambasulira manja anga
anthu owukira aja,
amene amachita zoyipa,
natsatira zokhumba zawo.
3 Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsa
mopanda manyazi.
Iwo amapereka nsembe mʼminda
ndi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.
4 Amakatandala ku manda
ndipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika.
Amadya nyama ya nkhumba,
ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa.
5 Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire,
chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’
Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga,
ngati moto umene umayaka tsiku lonse.
6 “Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo;
sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthu
chifukwa cha machimo awo
7 ndi a makolo awo,”
akutero Yehova.
“Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapiri
ndi kundinyoza Ine pa zitunda zawo,
Ine ndidzawalanga kwathunthu potsata
zimene anachita kale.”
8 Yehova akuti,
“Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesa
ndipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo,
popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’
Inenso chifukwa cha mtumiki wanga;
sindidzawononga onse.
9 Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo,
ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo.
Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi,
ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.
10 Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa,
ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombe
kwa anthu anga ondifunafuna Ine.
11 “Koma inu amene mumasiya Yehova
ndi kuyiwala phiri langa lopatulika,
amene munamukonzera Gadi chakudya
ndi kuthirira Meni chakumwa,
12 ndidzakuperekani ku lupanga ngati nsembe,
ndipo nonse mudzaphedwa;
chifukwa simunayankhe pamene ndinakuyitanani,
ndinayankhula koma simunamvere.
Munachita zoyipa pamaso panga
ndipo munasankha kuchita zoyipa zomwe sindikondwera nazo.”
13 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti,
“Atumiki anga adzadya,
koma inu mudzakhala ndi njala;
atumiki anga adzamwa,
koma inu mudzakhala ndi ludzu;
atumiki anga adzakondwa,
koma inu mudzakhala ndi manyazi.
14 Atumiki anga adzayimba
mosangalala,
koma inu mudzalira kwambiri
chifukwa chovutika mu mtima
ndipo mudzalira mofuwula chifukwa mudzamva kuwawa mu mtima.
15 Anthu anga osankhidwa
adzatchula dzina lanu potemberera.
Ambuye Yehova adzakuphani,
koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.
16 Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomo
adzachita zimenezo kwa Mulungu woona;
ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomo
adzalumbira mwa Mulungu woona.
Pakuti mavuto akale adzayiwalika
ndipo adzachotsedwa pamaso panga.
Chilengedwe Chatsopano
17 “Taonani, ndikulenga
mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.
Zinthu zakale sizidzakumbukika,
zidzayiwalika kotheratu.
18 Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya
chifukwa cha zimene ndikulenga,
pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa
ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
19 Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu
ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.
Kumeneko sikudzamvekanso kulira
ndi mfuwu wodandaula.
20 “Ana sadzafa ali akhanda
ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse.
Wamngʼono mwa iwo
adzafa ali ndi zaka 100.
Amene adzalephere kufika zaka 100
adzatengedwa kukhala
wotembereredwa.
21 Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo,
adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.
22 Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo,
kapena kudzala ndi ena nʼkudya.
Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo
wautali ngati mitengo.
Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito
ya manja awo nthawi yayitali.
23 Sadzagwira ntchito pachabe
kapena kubereka ana kuti aone tsoka;
chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova,
iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.
24 Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe.
Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.
25 Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi.
Mkango udzadya udzu monga ngʼombe,
koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka.
Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala
chinthu chopweteka kapena chowononga,”
akutero Yehova.
Fanizo la Wofesa Mbewu
13 Tsiku lomwelo Yesu anatuluka mʼnyumba ndipo anakhala mʼmbali mwa nyanja. 2 Magulu a anthu anasonkhana mozungulira ndipo Iye analowa mʼbwato nakhala pansi ndipo anthu onse anayimirira ku mtunda. 3 Pamenepo Iye anawawuza zinthu zambiri mʼmafanizo ndi kuti, “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. 4 Akufesa, zina zinagwera mʼmbali mwa njira ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. 5 Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. 6 Koma dzuwa litakwera, mbewu zinapserera ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. 7 Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. 8 Koma mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala zipatso 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa. 9 Amene ali ndi makutu amve.”
10 Ophunzira anabwera kwa Iye ndikumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani Inu mukuyankhula kwa anthu mʼmafanizo?”
11 Iye anayankha kuti, “Nzeru zakudziwa zinsinsi za ufumu wakumwamba zapatsidwa kwa inu koma osati kwa iwo. 12 Aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zowonjezera ndipo iye adzakhala nazo zambiri. Aliyense amene alibe, ngakhale zimene ali nazo adzamulanda. 13 Ichi ndi chifukwa chake ndimayankhula kwa iwo mʼmafanizo:
“Ngakhale akupenya koma saona,
ngakhale akumva koma samvetsetsa kapena kuzindikira.
14 Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa:
“ ‘Kumva mudzamva koma osamvetsetsa.
Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu.
15 Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika,
mʼmakutu mwawo ndi mogontha,
ndipo atsinzina
kuti asaone kanthu.
Mwina angapenye ndi maso awo,
angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,
Ineyo nʼkuwachiritsa.’
16 Koma maso anu ndi odala chifukwa amapenya ndi makutu anu chifukwa amamva. 17 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama anafuna kuona zimene inu mukupenya koma sanazione ndi kumva zimene inu mukumva koma sanazimve.
Tanthauzo la Fanizo la Wofesa
18 “Tamverani tsono zimene fanizo la wofesa litanthauza: 19 Pamene aliyense akumva uthenga wa ufumu koma sawuzindikira, woyipayo amabwera ndi kuchotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Iyi ndi mbewu yofesedwa mʼmbali mwa njira. 20 Zimene zinafesedwa pa malo amiyala ndi munthu amene amamva mawu ndi kuwalandira msanga ndi chimwemwe. 21 Koma popeza alibe muzu, iwo amakhala nthawi yochepa. Pamene vuto kapena zunzo libwera chifukwa cha mawu, iye amagwa mofulumira. 22 Zimene zinafesedwa pakati pa minga, ndi munthu amene amamva mawu koma nkhawa za moyo uno ndi chinyengo cha chuma zimalepheretsa mawuwo kuti abale chipatso. 23 Koma zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino, ndi munthu amene amamva mawu ndipo amawazindikira. Iye amabala zipatso zokwanira 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.”
Fanizo la Namsongole
24 Yesu anawawuza fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi munthu amene anafesa mbewu zabwino mʼmunda mwake. 25 Koma aliyense akugona usiku mdani wake anabwera ndi kufesa namsongole pakati pa tirigu ndipo anachoka. 26 Pamene tirigu anamera ndi kutulutsa ngala, namsongole anaonekanso.
27 “Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, ‘Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?’
28 “Iye anayankha kuti, ‘Ndi mdani amene anachita izi.’
“Antchito anamufunsa iye kuti, ‘Kodi mufuna kuti tipite tikamuzule?’
29 “Iye anakana nati, ‘Ayi. Chifukwa pamene mukuzula namsongoleyo mwina inu mungazulire pamodzi ndi tirigu. 30 Zisiyeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Pa nthawi imeneyo ndidzawuza okolola kuti: Poyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga mʼmitolo kuti atenthedwe, kenaka sonkhanitsani tirigu ndi kumuyika mʼnkhokwe yanga.’ ”
Fanizo la Mbewu ya Mpiru ndi Yisiti
31 Iye anawawuza fanizo lina kuti, “Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. 32 Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.”
33 Iye anawawuzanso fanizo lina nati: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza mu ufa wambiri mpaka wonse unafufuma.”
34 Yesu anayankhula zinthu zonsezi kwa gulu la anthu mʼmafanizo ndipo Iye sananene kalikonse kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. 35 Kotero zinakwaniritsidwa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri kuti,
“Ndidzatsekula pakamwa panga ndi mafanizo,
ndidzawulula zinthu zobisika
chiyambire kukhazikidwa kwa dziko lapansi.”
Yesu Awatanthauzira Fanizo la Namsongole
36 Kenaka Iye anasiya gulu la anthu ndi kukalowa mʼnyumba. Ophunzira ake anapita kwa Iye nati, “Timasulireni fanizo la namsongole mʼmunda.”
37 Iye anayankha nati, “Munthu amene anafesa mbewu yabwino ndi Mwana wa Munthu. 38 Munda ndi dziko lapansi ndipo mbewu yabwino ndi ana a ufumu. Namsongole ndi ana a woyipayo. 39 Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo.
40 “Monga momwe namsongole azulidwa ndi kutenthedwa ndi moto, momwemonso kudzakhala pakutha kwa dziko. 41 Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa. 42 Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano. 43 Pamenepo olungama adzawala ngati dzuwa mu ufumu wa Atate awo. Amene ali ndi makutu amve.”
Fanizo la Chuma Chobisika ndi la Ngale
44 “Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo.
45 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. 46 Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.”
Fanizo la Khoka
47 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi khoka limene linaponyedwa mʼnyanja ndipo linakola mitundu yonse ya nsomba. 48 Litadzaza, asodzi analikokera ku mtunda. Pomwepo anakhala pansi nasonkhanitsa nsomba zabwino mʼmadengu koma zoyipa anazitaya. 49 Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. 50 Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
51 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi mwamvetsetsa zonsezi?”
Iwo anayankha kuti, “Inde.”
52 Iye anawawuza kuti, “Chifukwa chake mphunzitsi aliyense wa malamulo amene walangizidwa za ufumu wakumwamba ali ngati mwini nyumba amene amatulutsa chuma chatsopano komanso chakale.”
Amupeputsa Yesu ku Nazareti
53 Yesu atatsiriza mafanizowa anachoka kumeneko. 54 Atafika ku mudzi kwawo anayamba kuphunzitsa mʼmasunagoge awo ndipo iwo anadabwa nati, “Munthu uyu anayitenga kuti nzeru iyi ndi mphamvu zodabwitsazi? 55 Kodi si mwana wa wopala matabwa? Kodi dzina la amayi ake si Mariya ndipo kodi abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi? 56 Kodi alongo ake onse sali ndi ife? Tsono ndi kuti kumene anazitenga zinthu izi?” 57 Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye.
Koma Yesu anawawuza kuti, “Mneneri sapatsidwa ulemu ku mudzi kwawo ndi ku nyumba kwawo.”
58 Ndipo Iye sanachite zodabwitsa zambiri kumeneko chifukwa cha kusowa kwa chikhulupiriro kwawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.