M’Cheyne Bible Reading Plan
Kugonjetsedwa kwa Ogi Mfumu ya ku Basani
3 Kenaka tinakhota ndi kumayenda mokwera mtunda ndi njira yolowera ku Basani. Ndipo Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anakumana nafe ndipo anamenyana nafe ku Ederi. 2 Yehova anati kwa ine, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.”
3 Choncho Yehova Mulungu wathu anapereka mʼmanja mwathu Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo. Tinawakantha onsewo osasiya ndi mmodzi yemwe. 4 Pa nthawi imeneyo tinatenga mizinda yake yonse. Pa mizinda 60, panalibe ndi umodzi womwe umene sitinawalande, mʼdera lonse la ufumu wa Ogi ku Basani chimene ndi chigawo cha Arigobu. 5 Mizinda yonseyi inali yotetezedwa ndi malinga ataliatali wokhala ndi zitseko ndi zitsulo, komabe panali midzi ina yambiri imene inalibe malinga. 6 Tinawawonongeratu monga momwe tinachitira Sihoni, mfumu ya ku Hesiboni. Tinawononga mzinda uliwonse, amayi, amuna ndi ana omwe. 7 Koma tinafunkha ziweto ndi katundu wawo yense.
8 Choncho pa nthawi imeneyi tinalanda kwa mafumu awiri Aamori, dera la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku khwawa la Arinoni mpaka ku Phiri la Herimoni. 9 (Asidoni amatcha Herimoni kuti Siriyoni, pamene Aamori amalitcha Seniri). 10 Tinalanda mizinda yonse ya ku mapiri, ku Giliyadi, Basani mpaka ku Saleka ndi Ederi, mizinda ya mu ufumu wa Ogi wa ku Basani. 11 (Ogi, mfumu ya ku Basani, anali yekhayo amene anatsala mwa mtundu wa anthu ataliatali a Chirefai. Bedi lake linali lachitsulo ndipo lalitali kuposa mamita anayi. Mulifupi mwake munali mamita awiri. Bedilo likanalipo ku Raba kwa Aamori).
Kugawana Dziko
12 Dziko limene tinalanda nthawi imeneyo, ndinapatsa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi dera la kumpoto kwa Aroeri cha mʼmphepete mwa khwawa la Arinoni kuphatikizapo theka la dziko lamapiri la Giliyadi ndi mizinda yake. 13 Theka la fuko la Manase ndinalipatsa dziko lonse lotsala la Giliyadi ndi Basani yense yemwe ndi dera la ufumu wa Ogi. (Chigawo chonse cha Arigobu mu Basani chinkadziwika kuti ndi dziko la Arefai. 14 Yairi, mdzukulu wa Manase, anatenga chigawo chonse cha Arigobu mpaka ku malire a Agesuri ndi Amaakati. Anatcha chigawochi dzina lake, moti mpaka lero Basani amatchedwa Havoti Yairi). 15 Ndipo ndinapereka Giliyadi kwa Makiri. 16 Koma kwa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi ndinapereka chigawo chochokera ku Giliyadi kutsetsereka mpaka ku khwawa la Arinoni (pakati pa khwawalo ndiye panali malire) ndi kupitirira mpaka ku mtsinje wa Yaboki umene ndi malire Aamoni. 17 Malire ake a chakumadzulo anali Yorodani ku Araba, kuchokera ku Kinereti mpaka ku Nyanja ya Araba (Nyanja ya Mchere), mʼmunsi mwa matsitso a Pisiga.
18 Ndinakulamulirani nthawi imene ija kuti, “Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili kuti likhale lanu. Koma amuna amphamvu onse ali ndi zida zankhondo, awoloke kutsogolera abale anu Aisraeli. 19 Koma akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu (ndikudziwa kuti muli ndi ziweto zambiri) zikhoza kumakhalabe mʼmizinda imene ndakupatsani, 20 mpaka Yehova atapereka mpumulo kwa abale anu, nawonso atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa patsidya pa Yorodani, monga wachitira ndi inu. Kenaka, aliyense wa inu akhoza kudzabwerera ku dziko limene ndinakupatsani.”
Mose Aletsedwa Kuwoloka Yorodani
21 Nthawi imeneyo ndinamulamula Yoswa kuti, “Waona wekha ndi maso ako zonse zimene Yehova Mulungu wako anachitira mafumu awiriwa. Yehova adzachita zomwezo ndi mafumu ena onse kumene mukupitako. 22 Musawaope chifukwa Yehova Mulungu mwini adzakumenyerani nkhondo.”
23 Nthawi imeneyo ndinachonderera Yehova kuti, 24 “Ambuye Mulungu, mwayamba tsopano kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu. Ndi mulungu uti ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene angachite ntchito zozizwitsa zimene mumachita? 25 Mundilole ndipite ndi kukaona dziko labwinolo kutsidya kwa Yorodani dziko la mapiri abwinowo ndi Lebanoni.”
26 Koma chifukwa cha inu, Yehova anakwiya nane osandimvera. Yehova anati, “Basi pakwana, usayankhulenso ndi ine zimenezi. 27 Pita pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo uyangʼane kumadzulo, kumpoto, kummwera ndi kummawa. Ulione dzikolo ndi maso ako pakuti suwoloka Yorodaniyu. 28 Koma langiza Yoswa ndipo umulimbikitse ndi kumupatsa mphamvu pakuti adzatsogolera anthu awa kuwoloka ndipo adzawathandiza kuti atenge dziko limene ulioneli.” 29 Ndipo tinakhala mʼchigwa pafupi ndi Beti-Peori.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
85 Yehova munakomera mtima dziko lanu;
munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.
2 Munakhululukira mphulupulu za anthu anu
ndi kuphimba machimo awo onse.
Sela
3 Munayika pambali ukali wanu wonse
ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa.
4 Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.
5 Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?
6 Kodi simudzatitsitsimutsanso,
kuti anthu anu asangalale mwa Inu?
7 Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova,
ndipo tipatseni chipulumutso chanu.
8 Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena;
Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake,
koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.
9 Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye,
kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.
10 Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi;
chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.
11 Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi,
ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.
12 Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino,
ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.
13 Wolungama amapita patsogolo pake
ndi kukonza njira za mapazi ake.
Tsoka kwa Amene Amadalira Igupto
31 Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo,
amene amadalira akavalo,
nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondo
ndiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo,
koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli,
kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.
2 Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga,
ndipo sasintha chimene wanena.
Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa,
komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.
3 Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu;
akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu.
Yehova akangotambasula dzanja lake,
amene amapereka chithandizo adzapunthwa,
amene amalandira chithandizocho adzagwa;
onsewo adzathera limodzi.
4 Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi:
“Monga mkango kapena msona wamkango umabangula
ukagwira nyama yake,
ndipo suopsedwa kapena kusokonezeka
ndi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo,
momwemonso palibe chingaletse
Yehova Wamphamvuzonse
kubwera kudzatchinjiriza
phiri la Ziyoni ndi zitunda zake.
5 Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake,
Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu;
ndi kumupulumutsa,
iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa.”
6 Inu Aisraeli, bwererani kwa Iye amene munamuwukira kwakukulu. 7 Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.
8 “Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu.
Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga.
Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awo
adzagwira ntchito yathangata.
9 Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha,
ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi mantha
kusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.”
Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni,
ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.
Mawu Oyamba
1 Vumbulutso lochokera kwa Yesu Khristu, limene Mulungu anamupatsa kuti aonetse atumiki ake zimene zinayenera kuchitika posachedwa. Iye anatuma mngelo wake kuti adziwitse mtumiki wake Yohane, 2 amene akuchitira umboni chilichonse chimene anachiona. Awa ndi Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu. 3 Ngodala munthu amene awerenga mawu oneneratu zamʼtsogolo ndi iwo amene amamva ndi kusunga zolembedwa mʼbukuli pakuti nthawi yayandikira.
Malonje kwa Mipingo Isanu ndi Iwiri
4 Ndine Yohane,
Kupita ku mipingo isanu ndi iwiri ya mʼchigawo cha Asiya.
Chisomo ndi mtendere kwa inu, kuchokera kwa Iye amene ali, amene analipo ndi amene akubwera ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala patsogolo pa mpando wake waufumu, 5 ndiponso kuchokera kwa Yesu Khristu mboni yokhulupirika, woyamba kuukitsidwa, ndi wolamulira mafumu a dziko lapansi.
Kwa Iye amene amatikonda ndipo watimasula ku machimo athu ndi magazi ake, 6 ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni.
7 “Onani akubwera ndi mitambo,”
ndipo “Aliyense adzamuona,
ndi amene anamubaya omwe.”
Ndipo anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi “adzalira chingʼangʼadza chifukwa cha Iye.”
Zidzakhaladi momwemo, Ameni.
8 “Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”
Wina Wokhala ngati Mwana wa Munthu
9 Ine Yohane mʼbale wanu ndi mnzanu mʼmasautso ndi mu ufumu ndi mukupirira kwambiri, zomwe ndi zathu mwa Yesu, ndinali pa chilumba cha Patimo chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu. 10 Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga, 11 amene anati, “Lemba mʼbuku zimene ukuziona ndipo uzitumize ku mipingo isanu ndi iwiri ya ku Efeso, Simurna, Pergamo, Tiyatira, Sarde, Filadefiya ndi ku Laodikaya.”
12 Nditatembenuka kuti ndione amene amandiyankhulayo, ndinaona zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. 13 Pakati pa zoyikapo nyalezo ndinaona wina wooneka ngati Mwana wa Munthu atavala mkanjo wofika kumapazi ake ndipo anamangirira lamba wagolide pa chifuwa pake. 14 Tsitsi lake linali loyera ngati thonje, kuyera ngati matalala, ndipo maso ake amawala ngati malawi amoto. 15 Mapazi ake anali ngati chitsulo choti chili mʼngʼanjo yamoto, ndipo mawu ake anali ngati mkokomo wamadzi othamanga. 16 Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri.
17 Nditamuona ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Kenaka Iye anasanjika dzanja lake lamanja pa ine nati, “Usachite mantha. Ndine Woyamba ndi Wotsiriza. 18 Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.
19 “Chomwecho, lemba zimene waona, zimene zilipo panopa ndi zimene zidzachitike mʼtsogolo. 20 Tanthauzo la nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene waziona mʼdzanja langa lamanja ndi la zoyikapo nyale zagolide zisanu ndi ziwiri ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndi angelo a mipingo isanu ndi iwiri ija, ndipo zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zija ndi mipingo isanu ndi iwiri ija.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.