M’Cheyne Bible Reading Plan
24 Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu. 2 Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye 3 ndipo ananena uthenga wake:
“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,
uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka,
4 uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,
yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,
yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere:
5 “Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo,
misasa yako, iwe Israeli!
6 “Monga zigwa zotambalala,
monga minda mʼmbali mwa mtsinje,
monga aloe wodzalidwa ndi Yehova,
monga mikungudza mʼmbali mwa madzi.
7 Madzi adzayenderera mʼmitsuko yake;
mbewu zake zidzakhala ndi madzi ambiri.
“Mfumu yake idzakhala yamphamvu kuposa Agagi;
ufumu wake udzakwezedwa.
8 “Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto
ali ndi mphamvu ngati za njati.
Amawononga mitundu yomuwukira
ndi kuphwanya mafupa awo,
amalasa ndi mivi yake.
9 Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi,
monga mkango waukazi, adzamuputa ndani?
“Amene adalitsa iwe, adalitsike
ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”
10 Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka. 11 Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”
12 Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine, 13 kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena? 14 Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.”
Uthenga Wachinayi wa Balaamu
15 Ndipo iye ananena uthenga wake nati,
“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,
uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka.
16 Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,
amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba,
amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,
amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka:
17 “Ndikumuona iye koma osati tsopano;
ndikumupenya iye koma osati pafupi.
Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo;
ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli.
Iye adzagonjetsa Mowabu
ndi kugonjetsa ana onse a Seti.
18 Edomu adzagonjetsedwa;
Seiri, mdani wake, adzawonongedwa
koma mphamvu za Israeli zidzachuluka.
19 Wolamulira adzachokera mwa Yakobo
ndipo adzawononga otsala a mu mzindamo.”
Uthenga Wachisanu wa Balaamu
20 Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu:
“Aamaleki anali oyamba mwa mitundu ya anthu
koma potsiriza pake adzawonongeka.”
Uthenga Wachisanu ndi Chimodzi wa Balaamu
21 Kenaka anaonanso Akeni ndipo ananena uthenga wake,
“Malo amene mukukhalamo ndi otetezedwa,
chisa chanu chinayikidwa pa thanthwe;
22 komabe inu Akeni mudzawonongedwa,
pamene Asuri adzakutengeni ukapolo.”
Uthenga Wachisanu ndi Chiwiri wa Balaamu
23 Ndipo ananenanso uthenga wina kuti,
“Aa, ndani adzakhala ndi moyo Mulungu akachita zimenezi?
24 Sitima zapamadzi zidzabwera kuchokera ku madooko a Kitimu;
kupondereza Asuri ndi Eberi,
koma iwonso adzawonongeka.”
25 Pamenepo Balaamu ananyamuka ndi kubwerera kwawo ndipo Balaki anapitanso njira yake.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo.
66 Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!
2 Imbani ulemerero wa dzina lake;
kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.
3 Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu!
Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri
kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.
4 Dziko lonse lapansi limaweramira inu;
limayimba matamando kwa Inu;
limayimba matamando pa dzina lanu.”
Sela.
5 Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,
ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.
6 Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma,
iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi.
Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.
7 Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya,
maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina.
Anthu owukira asadzitukumule.
8 Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,
mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
9 Iye watchinjiriza miyoyo yathu
ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
10 Pakuti Inu Mulungu munatiyesa;
munatiyenga ngati siliva.
11 Inu mwatilowetsa mʼndende
ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
12 Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu;
ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi,
koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.
13 Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza
ndi kukwaniritsa malumbiro anga.
14 Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza
ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.
15 Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu
ndi chopereka cha nkhosa zazimuna;
ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi.
Sela
16 Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu.
Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.
17 Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga,
matamando ake anali pa lilime panga.
18 Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga
Ambuye sakanamvera;
19 koma ndithu Mulungu wamvetsera
ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.
20 Matamando akhale kwa Mulungu
amene sanakane pemphero langa
kapena kuletsa chikondi chake pa ine!
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo.
67 Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa,
achititse kuti nkhope yake itiwalire.
2 Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi,
chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.
3 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
4 Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe,
pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo
ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.
5 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
6 Nthaka yabereka zokolola zake;
tidalitseni Mulungu wathu.
7 Mulungu atidalitse
kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.
14 Yehova adzachitira chifundo Yakobo;
adzasankhanso Israeli
ndi kuwalola kuti akhalenso mʼdziko lawo.
Alendo adzabwera kudzakhala nawo
ndi kudziphatika okha kukhala ngati a mʼnyumba ya Yakobo.
2 Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli
ku dziko lawo.
Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja
kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova.
Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo.
Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.
3 Yehova akadzakupumitsani ku zowawa ndi mavuto, ndiponso kuntchito yakalavulagaga imene ankakugwiritsani, 4 mudzayankhula monyogodola mfumu ya Babuloni kuti,
Wopsinja uja watha!
Ukali wake uja watha!
5 Yehova wathyola chikwapu cha anthu oyipa,
Iye waphwanya ndodo ya olamulira.
6 Mfumu ya ku Babuloni inkakantha mitundu ya anthu mwaukali
powamenya kosalekeza,
Iyo inkagonjetsa anthu a mitundu ina mwaukali
ndikuwazunza kosalekeza.
7 Koma tsopano mayiko onse ali pa mpumulo ndi pa mtendere;
ndipo akuyimba mokondwa.
8 Ngakhale mitengo ya payini ndi mikungudza ya ku Lebanoni
ikuyimba za iwe mokondwa ndipo ikuti,
“Chigwetsedwere chako pansi,
palibe wina anabwera kudzatigwetsa.”
9 Ku manda kwatekeseka
kuti akulandire ukamabwera;
mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri
a dziko lapansi, yadzutsidwa.
Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu
ayimiritsidwa pa mipando yawo.
10 Onse adzayankha;
adzanena kwa iwe kuti,
“Iwenso watheratu mphamvu ngati ife;
Iwe wafanana ndi ife.”
11 Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda,
pamodzi ndi nyimbo za azeze ako;
mphutsi zayalana pogona pako
ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi.
12 Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba,
iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha!
Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi,
Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!
13 Mu mtima mwako unkanena kuti,
“Ndidzakwera mpaka kumwamba;
ndidzakhazika mpando wanga waufumu
pamwamba pa nyenyezi za Mulungu;
ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako,
pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
14 Ndidzakwera pamwamba pa mitambo;
ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.”
15 Koma watsitsidwa mʼmanda
pansi penipeni pa dzenje.
16 Anthu akufa adzakupenyetsetsa
nadzamalingalira za iwe nʼkumati,
“Kodi uyu ndi munthu uja anagwedeza dziko lapansi
ndi kunjenjemeretsa maufumu,
17 munthu amene anasandutsa dziko lonse chipululu,
amene anagwetsa mizinda yake
ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwawo?”
18 Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemu
aliyense mʼmanda akeake.
19 Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako,
ngati nthambi yowola ndi yonyansa.
Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa;
amene anabayidwa ndi lupanga,
anatsikira mʼdzenje lamiyala
ngati mtembo woponderezedwa.
20 Sudzayikidwa nawo mʼmanda mwaulemu,
chifukwa unawononga dziko lako
ndi kupha anthu ako.
Zidzukulu za anthu oyipa
sizidzakumbukika nʼpangʼono pomwe.
21 Konzani malo woti muphere ana ake aamuna
chifukwa cha machimo a makolo awo;
kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi
ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda yawo.
22 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni.
Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo.
Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,”
akutero Yehova.
23 “Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungu
ndiponso dambo lamatope;
ndidzawusesa ndi tsache lowononga,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Za Kulangidwa kwa Asiriya
24 Yehova Wamphamvuzonse walumbira kuti,
“Ndithudi, monga ndaganizira ndidzachitadi choncho,
ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.
25 Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa;
ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga;
ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga,
ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”
26 Izi ndizo ndakonza kuti zichitike pa dziko lonse lapansi,
ndatambasula dzanja pa anthu a mitundu yonse.
27 Pakuti Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza, ndipo ndani angamuletse?
Dzanja lake latambasulidwa ndipo ndani angalibweze?
Za Kulangidwa kwa Afilisti
28 Uthenga uwu unabwera chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira:
29 Musakondwere inu Afilisti nonse
kuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa;
chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri,
ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.
30 Osaukitsitsa adzapeza chakudya
ndipo amphawi adzakhala mwamtendere.
Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala,
ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.
31 Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda!
Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse!
Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto,
ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.
32 Kodi tidzawayankha chiyani
amithenga a ku Filisitiya?
“Yehova wakhazikitsa Ziyoni,
ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”
2 Choncho, lekani zoyipa zonse, chinyengo chilichonse, chiphamaso, nsanje ndi kusinjirira kulikonse. 2 Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu, 3 pakuti tsopano mwalawadi kuti Ambuye ndi wabwino.
Mwala wa Moyo ndi Anthu Osankhidwa
4 Pamene mukubwera kwa Iye, amene ndi Mwala wa moyo, umene anthu anawukana, koma Mulungu anawusankha kuti ndi wa mtengowapatali, 5 inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu. 6 Pakuti mʼMalemba mwalembedwa kuti,
“Taonani, ndikuyika mwala wa maziko mu Ziyoni,
wosankhika ndi wamtengowapatali.
Amene akhulupirira Iye
sadzachititsidwa manyazi.”
7 Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira,
“Mwala umene amisiri anawukana
wasanduka mwala wa maziko,
8 ndi
“Mwala wopunthwitsa anthu
ndiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.”
Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo.
9 Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa. 10 Kale simunali anthu ake, koma tsopano ndinu anthu a Mulungu. Kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.
11 Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu. 12 Khalani moyo wabwino pakati pa anthu osapembedza kuti ngakhale atakusinjirirani kuti mumachita zoyipa, iwowo akaona ntchito zanu zabwino, adzalemekeza Mulungu pa tsiku lomwe Iye adzatiyendere.
Kugonjera Olamulira
13 Gonjerani maulamuliro onse chifukwa cha Ambuye. Kaya ndi mfumu, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro waukulu, 14 kaya ndi mabwanamkubwa, pakuti watumidwa ndi mfumu kuti alange onse amene amachita zoyipa ndi kuyamikira onse amene amachita zabwino. 15 Pakuti Mulungu akufuna kuti pochita ntchito zabwino muthetse kuyankhula mosazindikira ndi mopusa. 16 Mukhale monga mfulu, koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo ngati chophimbira zoyipa; mukhale monga atumiki a Mulungu. 17 Chitirani ulemu aliyense, kondani abale okhulupirira, wopani Mulungu, ndipo chitirani mfumu ulemu.
Akapolo
18 Inu akapolo, gonjerani ambuye anu ndi kuwachitira ulemu, osati kwa iwo okha amene ndi abwino ndi omvetsa zinthu, komanso kwa amene ndi ankhanza. 19 Pakuti ndi chinthu chokoma ngati munthu apirira mu zowawa zimene sizinamuyenera chifukwa chodziwa kuti Mulungu alipo. 20 Kodi pali choti akuyamikireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira, mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu. 21 Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake.
22 “Iye sanachite tchimo
kapena kunena bodza.”
23 Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama. 24 Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa. 25 Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.